Malo a ku Dziko Lolonjezedwa
Gerizimu ‘Pa Phiri Iri Tinalambira’
MKAZI wa ku Samariya pachitsime. Kodi mawu amenewo samakukumbutsani chochitika chothutsa mtima chakuchitira umboni kwa Yesu mwamwaŵi kwa mkazi pa ‘Chitsime cha Yakobo’ ku Sukari, mzinda wa Samariya? Kodi mukakondwa kuwonjezera chidziŵitso chanu cha chochitika chokhala ndi tanthauzo chimenecho?—Yohane 4:5-14.
Tawonani mapiri aŵiri pamwambapo, amene ali pafupifupi makilomita 50 kumpoto kwa Yerusalemu.a Chakumanzere (kummwera) kuli Gerizimu wodzala mitengo; akasupe ake ochuluka amathandiza kukukhala kwake wachonde ndi wokongola. Kulamanja (kumpoto) kuli Ebala, wokhala pamwamba pang’ono koma wamathanthwe ambiri ndi wosabala.
Pakati pawo pali chigwa cha chonde cha Sekemu. Kumbukirani kuti pamene bwenzi la Mulungu Abramu (pambuyo pake anadzatchedwa Abrahamu) anayenda kudutsa Dziko Lolonjezedwa, anaima pa Sekemu. Panopa anamangira Yehova guwa lansembe, amene anali atangowonekera kumene kwa iye nalonjeza kupatsa dziko limeneli kwa mbewu yake. (Genesis 12:5-7) Ndimalo oyenerera chotani nanga kupangira lonjezo lotero, pakati penipeni pa dzikolo! Liri pamwamba penipeni pa Gerizimu kapena Ebala, khololo likanakhoza kuwona mbali zazikulu za Dziko Lolonjezedwa. Mzinda wa Sekemu (Nablus wamakono) unali phata lofunika, popeza unali pamsewu wodzera paphiri wochokera kumpoto kumka kummwera pafupi ndi msewu wochokera kummawa kumka kumadzulo pakati pa m’mphepete mwanyanja ndi Chigwa cha Yordano.
Guwa lansembe la Abrahamu linali chochitika cha chipembedzo chimodzi chokha chodziŵika panopa. Pambuyo pake, Yakobo anagula malo m’chigawo chino napitiriziramo kulambira kowona. Iye anakumbanso kapena kulipirira kukumbidwa kwa chitsime chakuya, pafupi ndi tsinde la Gerizimu. Zaka mazana ambiri pambuyo pake mkazi wa ku Samariya anauza Yesu kuti: ‘Kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi . . . anamwamo.’ Madzi ake angakhale anali ochokera m’kasupe, chimene chingakhale chifukwa chake mtumwi Yohane anachitcha ‘kasupe wa Yakobo.’
Kutchulidwa kwa kulambira kowona kogwirizanitsidwa ndi Gerizimu ndi Ebala kuyenera kukukumbutsaninso kuti Yoswa anabweretsa Israyeli pano, monga momwe Mose analamulirira. Yoswa anamanga guwa lansembe pa Ebala. Tayerekezerani theka la anthuwo patsogolo pa Gerizimu ndipo otsalawo kukhala ataimirira pafupi ndi Ebala pamene Yoswa amaŵerenga ‘chilamulo, madalitso ndi matemberero.’ (Yoswa 8:30-35; Deuteronomo 11:29) Zaka zambiri pambuyo pake, Yoswa anabwerera ndipo m’kudandaulira kwake komalizira anati: “Koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.” Anthu anachita pangano lakuchita mofananamo. (Yoswa 24:1, 15-18, 25) Koma kodi iwo akaterodi?
Yankho lingakuthandizeni kuzindikira kukambitsirana kwa Yesu ndi mkazi wa ku Samariya. Mwawona nanga, kulambira kowona kochitidwa ndi Abrahamu, Yakobo, ndi Yoswa sikunapitirizebe muno m’Samariya.
Mafuko khumi akumpoto atapanduka, anatembenukira kukulambira mwana wang’ombe. Chotero Yehova analola Asuri kugonjetsa chigawo chimenechi mu 740 B.C.E. Iwo anatenga unyinji wa anthuwo, mmalo mwawo akumaloŵetsamo alendo ochokera m’mbali zina za Chifumu cha Asuri, olambira milungu yachilendo. Ena akunja amenewo mwachiwonekere anakwatirana ndi Aisrayeli naphunzira ziphunzitso zina zakulambira kowona, monga ngati mdulidwe. Koma chotulukapo cha mpangidwe wakulambira kwa Asamariya sichinalidi chokondweretsa kotheratu kwa Mulungu.—2 Mafumu 17:7-33.
M’kulambira kwawo kosanganiza, Asamariya anavomereza monga Malemba Opatulika mabukhu asanu okha oyamba olembedwa ndi Mose, Pentateuch. Pafupifupi zaka za zana lachinayi B.C.E., iwo anamanga kachisi pa Phiri la Gerizimu, motsutsana ndi kachisi wa Mulungu m’Yerusalemu. M’kupita kwanthaŵi kachisi wa pa Gerizimu anaperekedwa kwa Zeu (kapena, Jupiter) ndipo potsirizira pake anawonongedwa. Komabe, kulambira kwa Asamariya kunapitirizabe kukhala ndi phata lake pa Gerizimu.
Kufikira lerolino, Asamariya amachitira phwando lachaka ndi chaka la Paskha pa Gerizimu. Ana ankhosa angapo amaphedwa. Nkhosa zophedwazo zimanyikidwa mndoŵa za madzi oŵira kotero kuti ubweya wake uthotholedwe, ndiyeno nyamayo nkuphikidwa m’maenje kwa maola angapo. Pakati pa usiku Asamariya mazana angapo, ocholuka ochokera ku Yerusalemu, amadya mgonero wawo wa paskha. Kulamanzere, mungathe kuwona mkulu wa ansembe waku Samariya, mutu wake ngwophimbidwa, akuchititsa phwando la Paskha pa Phiri la Gerizimu.
Kumbukirani zimene mkazi wa ku Samariya anauza Yesu kuti: “Makolo athu analambira m’phiri ili.” Yesu anawongolera mkaziyo, nawongoleranso ife. ‘Ikudza nthaŵi, imene simudzalambira Atate kapena m’phiri ili, kapena m’Yerusalemu. . . . Koma ikudza nthaŵi, ndipo tsopano iripo, imene olambira owona adzalambira Atate mumzimu ndi m’chowonadi.’—Yohane 4:20-24.
[Mawu a M’munsi]
a Mungathe kupenda chithunzithunzi chimenechi pa mlingo wokulirapo mu Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1993.
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Garo Nalbandian
Garo Nalbandian