Mulungu Samaiŵala ‘Chikondi Chimene Munachiwonetsera ku Dzina Lake’
‘MULUNGU sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachiwonetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.’ (Ahebri 6:10) Mawu amtumwi Paulo amenewa ngowona kwa Mboni za Yehova Kummaŵa kwa Yuropu. Zikumatumikira mokhulupirika mochirikiza dzina la Mulungu, kwa zaka makumi ambiri zagwira ntchito yakalavula gaga ndi kwanthaŵi yaitali pansi pa ziletso zoperekedwa ndi maboma amene anali a Soviet Union. Yehova akukumbukira ntchito zawo zabwino ndipo akuwatsanulira madalitso Aufumu. Mwachitsanzo, tiyeni tipende lipoti la chaka chatha chautumiki kuchokera ku maiko atatu okha a zigawo zimenezo.
Maiko Amene Kale Anali Soviet Union
Maiko a imene kale inali Soviet Union akuchitira lipoti kuti mkati mwa chaka chautumiki cha 1992, chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa Ufumu chinawonjezereka ndi 35 peresenti—kuchokera pa 49,171 kufika pa 66,211! Komatu sizokhazo, popeza kuti ofalitsa amenewo akhala okangalika kwambiri, monga momwe kukuwonekera ndi ziwonjezeko zabwino kwambiri zamabukhu ofotokoza Baibulo ogaŵiridwa, kuphatikizapo magazini. Iwo agwiritsiranso ntchito bwino lomwe mabrosha ndi timabhuku, akumagaŵira 1,654,559. Zimenezo ziri kuposa kuŵirikiza katatu chiŵerengero cha chaka chatha cha 477,235! Kodi kulabadira kwake kwakhala kotani kwa ogaŵiridwa mabukhu onsewa? Kuŵirikiza nthaŵi ziŵiri kwa chiŵerengero cha maphunziro a Baibulo apanyumba. Tsopano maphunziro a Baibulo 38,484 akuchititsidwa.
Ndiponso, kukhala ndi phande mu utumiki waupaniya wothandiza kunawonjezereka ndi 94 peresenti. Mwachiwonekere chimenechi chinathandizira pa chiŵerengero chapamwamba cha ophunzira obatizidwa chatsopano, 26,986, poyerekezeredwa ndi chiŵerengero cha chaka chatha cha 6,570, chiwonjezeko chodabwitsa cha 311-peresenti!
Kodi ena a obatizidwa chatsopano amenewa anayamba bwanji kukondwerera mbiri yabwino? Nthaŵi zina kudera nkhaŵa kwakukulu kochitidwa ndi Mboni yochititsa phunzirolo kunachititsa. Woyang’anira wotsogoza wa ku Moldova akusimba kuti:
“Mkazi wanga ndi ine tinakacheza kwa mkazi wina amene poyamba anasonyeza chikondwerero m’chowonadi cha Baibulo. Phunziro la Baibulo linayambidwa naye. Komabe, mwamuna wake sanasonyeze chikondwerero chirichonse. Tsiku lina pamene tinali panjira yokacheza naye kupitiriza phunzirolo, mkhalidwe wa nyengo unali wozizira kopambanitsa ndipo kunali chipale chofeŵa. Panalibe munthu aliyense pamakwalala, koma tinafika kunyumba kwake panthaŵi yeniyeni imene tinapangana. Iye anauza mwamuna wake kuti: ‘Kodi mwawona mmene anthu awa aliri odera nkhaŵa ndi ife? Iwo amasunga nthaŵi mosasamala kanthu za chipale chofeŵa.’ Chochitika ichi chinachititsa mwamuna wake kuganiza. Iye anasintha malingaliro ake nagwirizana nafe m’phunzirolo, ndipo tsopano mwamunayo ndi mkazi wake ali Mboni zobatizidwa.”
Panthaŵi zina kudekha kwa Mboni kungayambitse chikondwerero m’mbiri yabwino. Mkulu wina, nayenso ngwa ku Moldova, anali ndi chokumana nacho ichi:
“Mwamuna wina amene ndinachezera m’gawo langa lolalikira sanali wokondwerera Mboni za Yehova. Iye ananena kuti anali wa Orthodox, mofanana ndi atate wake ndi agogo ake. Chotero anandipempha kuchoka panyumba pake. Komabe, ndisanachoke, anandipatsa mpata wakumuuza chifukwa chimene ndinadzera. Ndinasonya ku Mateyu 28:19 pamene pamati: ‘Chifukwa chake mukani ndi kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, mukumawabatiza m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera.’ Pamenepo ndinampatsa keyala ya malo athu osonkhanako ndipo ndinachoka. Mondidabwitsa, mlungu umodzi pambuyo pake mwamunayo anafika ku msonkhano! Iye sanachoke kufikira programu yonse itatha. Iye anafotokoza kuti mkati mwa mlungu wonsewo, anamva chisoni chifukwa chakusachita nane mwaubwenzi. Phunziro la Baibulo linayambidwa nthaŵi yomweyo, ndipo tsopano iye ali mmodzi wa abale athu.”
Mbali ina yapadera ya chaka chautumiki chimenecho yakhala kulabadira kwakukulu ku zosoŵa za abale athu m’dera limenelo. Mkati mwa chisanu cha 1991/92, pafupifupi chakudya cholemera matani 400 ndi zovala zambirimbiri za amuna, akazi, ndi ana zinatumizidwa kwa osoŵa. Zinthu zimenezi zinagaŵiridwa pafupifupi mbali zonse za maiko amene kale anali Soviet Union, kufikira ngakhale ku Irkutsk ku Siberia ndi Khabarovsk, kufupi ndi Japan. Ndithudi chisonyezero chochititsa chidwi chakuti Yehova sanaiŵale chikondi chimene abale athu asonyeza dzina lake! Umboni umenewu wakukonda abale wosonkhezeredwa ndi mzimu wa Yehova wakhalanso ndi chotulukapo chakuwagwirizanitsa ndi banja la dziko lonse lapansi. Mwachitsanzo, mlongo wina ku Ukraine analembera ofesi ya nthambi kuti:
“Chithandizo chimene munatipatsa chinatikhudza pansi pa mitima yathu. Tinasonkhezeredwa kulakatitsa misozi ndipo tinayamika Yehova chifukwa chakusatiiŵala. Ndithudi, tiri ndi mavuto akusoŵa zinthu zakuthupi tsopano lino, koma tiyamika chithandizo chimene chafika kuchokera kwa abale athu amaiko Akumadzulo, tachira mwanjira ya zinthu zakuthupi. Tsopano, chifukwa cha chithandizo chanu, banja lathu lidzakhoza kuthera nthaŵi yowonjezereka mu utumiki wa Yehova. Ngati Yehova alola, mwana wanga wamkazi ndi ine tidzachita upainiya wothandiza m’miyezi ya chilimwe.”
Kuwonjezera apa, zoyesayesa za kupereka chithandizo zapereka umboni kwa akunja chifukwa chakuti openyerera akhoza kuwona kuti Mboni zimasonyeza chikondi m’zochita zawo. Banja lamumpingo wina linalemba kuti: “Tinalandira chithandizo cha zinthu zakuthupi chophatikizapo zakudya ndi zovala. Nzambirimbiri! Chichirikizo chanu ndi chilimbikitso chikupereka phunziro kwa ife kuti nafenso tiyenera kuchitira ena zabwino. Mchitidwe wachikondi umenewu sunali wosawonedwa ndi osakhulupirira, kuphatikizapo anthu okondwerera ndi mabanja awo; wakhala umboni waukulu wonena za ubale wowona.”
Misonkhano yachigawo isanu ndi msonkhano wa mitundu yonse umodzi m’June ndi July wapitayu, yokhala ndi mutu wakuti “Onyamula Kuunika,” inali umboni wina wa dalitso la Yehova pa ntchito yamphamvu ya Mboni zake ndi chikondi chimene iwo asonyeza kudziŵitsa dzina lake. Misonkhanoyo inali ndi ofikapo okwanira 91,673, ndipo 8,562 anabatizidwa. Chiŵerengero chachikulu choposa cha ofikapo chinali ku St. Petersburg, malo kumene msonkhano wa mitundu yonse unachitidwira, kumene 46,214—kuphatikizapo nthumwi zochokera ku maiko 30 kuzungulira dziko—zinasonkhana pa sitediyamu ya Kirov Stadium.
Mu Siberia mwamuna wina wa zaka pafupifupi 60 zakubadwa anafika pa malo amsonkhano ku Irkutsk kudzangowona chabe. Iye anati: “Ofikapo onse ngovala bwino, ankhope zomwetulira, ndipo ngachifundo kwa wina ndi mnzake. Anthu awa ali ngati banja limodzi logwirizana. Munthuwe ungathe kuwona kuti iwo ali mabwenzi osati kokha pa sitediyamu komanso mmoyo wa tsiku ndi tsiku. Ndinalandira bukhu labwino kwambiri lofotokoza Baibulo ndipo ndinaphunzira bwino kwambiri kuti gululi nlotani. Ndifuna kupitirizabe kuwonana ndi Mboni za Yehova ndi kuphunzira Baibulo.”
Pamsonkhano waukulu umodzimodziwo mu Irkutsk, kumene 5,051 anasonkhana, mkazi wina wokondwerera wa ku Yakut Republic, Siberia, anati: “Ndimayang’ana anthu, ndipo ndimafuna kulira ndi chisangalalo. Ndiri woyamikira kwambiri kwa Yehova chifukwa chakundithandiza kudziŵa anthu otere. Pano pamsonkhano, ndalandira mabukhu, ndipo ndifuna kulankhula ndi ena za iwo. Ndikufuna kwambiri kukhala mlambiri wa Yehova.”
Woyang’anira Central Stadium mu Alma Ata, Kazakhstan, kumene 6,605 anafika pamsonkhano waukulu, ananena zotsatirazi: “Ndikuchita chidwi ndi mkhalidwe wanu. Tsopano ndakhutira kuti inu nonse, achichepere ndi achikulire omwe, ndinu anthu olemekezeka. Ine sindinganene kuti ndimakhulupirira Mulungu, koma ndimakhulupirira zinthu zopatulika zimene mwasonyeza kupyolera mwa ubale wanu, m’kaimidwe kanu kamaganizo kulinga ku zinthu zopindulitsa zauzimu ndi zakuthupi.”
Ofisala wina wa polisi pamsonkhano wa ku Alma Ata anati: “Ndawonana ndi anthu inu kaŵiri, iriyonse yanthaŵizo panali pamsonkhano waukulu. Kuli kokondweretsa kwambiri kugwira ntchito ndi Mboni za Yehova.”
Romania
Yehova sanaiŵalenso chikondi chimene abale aku Romania nawonso anasonyeza ku dzina lake. Chaka chathachi chautumiki chinali ndi zochitika zambiri zokondweretsa kwa Mboni. Choyamba, ofesi ya nthambi kachiŵirinso inakhazikitsidwa mu Bucharest. Chilolezo cha lamulo cha boma la Romania chinatha mu 1949. Ofesi iri ndi pafupifupi abale ndi alongo 20 ogwira ntchito mu nyumba zatsopano. Ofesi ya nthambi ikutumikira ofalitsa 24,752—chiŵerengero chapamwamba koposa cha nthaŵi zonse chimene chimaimira chiwonjezeko cha 21-peresenti kuposa avareji ya chaka chatha.
Pambuyo pa zaka zambiri zakulalikira mobisa, ofalitsa akupanga masinthidwe abwinopo antchito yochitira umboni poyera kunyumba ndi nyumba. Chokumana nacho cha ku Chigawo cha Mureş chimasonyeza mmene Mboni zina zimagwiritsirira ntchito bwino mpata uliwonse wakulalikira kwa ena, ngakhale pamene ali paulendo. Ofesi yanthambi ikulemba kuti:
“Wofalitsa wina anapanga chosankha cha kulalikira m’matiroko a tireni. Mbali yaikulu ya anthu inalabadira mwachiyanjo, koma m’tiroko yomalizira, mavuto anabuka. Palibe ndi mmodzi yense wa apaulendowo anafuna kulandira kopelo la magazini athu. Pambuyo pake, mwamuna mmodzi, atakwiya kwambiri, anaimirira nalalata kuti: ‘Ndidzatayira magazini anu onsewo pa zenerapo! Kodi mutivutilanji kwambiri choncho ndi chipembedzo chanu?’ Wofalitsayo modekha anayankha kuti ngakhale ngati iye akataya magazini athu, munthu wina akapindula ndi chochita chakecho—awo amene akatola magaziniwo. Atawona kudekha kwa wofalitsayo, mwamunayo anakopeka mtima kwambiri kotero kuti anatenga magaziniwo nayamba kuwagaŵira iye mwini kwa apaulendo ena m’tirokolo. Modabwitsa, onse anatenga magazini. Atatha kuwagaŵira, mwamunayo analibe makope aliwonse a iyemwini. Chotero, wofalitsa anamfunsa kuti: ‘Bwana, kodi inu simufuna makope alionse a inumwini?’ Pamenepo mwamunayo anatsomphola amodzi a magazini kwa wapaulendo wina amene anali ndi makope aŵiri nati: ‘Tsopano inenso ndapeza kope!’”
M’maiko ambiri ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova nthaŵi zina yasonkhezera chitsutso cha atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko. M’Romania, wansembe wa Tchalitchi cha Orthodox kaŵirikaŵiri amakwiyira Mboni. Koma zimenezi sizingaletse Yehova kudalitsa anthu ake chifukwa cha chikondi chimene iwo asonyeza kudzina lake. Woyang’anira dera wina akulemba kuti:
“Limodzi ndi mpingo wa malo ano, tinapita kukalalikira kumidzi. Panali abale zana limodzi. Tinachita hayara basi limene linatiyendetsa pafupifupi makilomita 50 chakumidzi, ku katawuni kakang’ono. Tinaitanira anthu ambiri ku nkhani yapoyera imene inali kudzachitidwira m’Nyumba Yamaseŵero. Mwamsanga msonkhanowo utayamba, wansembe wa Orthodox anafika kudzadodometsa msonkhano wathu. Akuluakulu a polisi anayesa kuletsa wansembeyo. Komabe, iye anakana kukhala chete. Anapeza chipambano m’kuimitsa msonkhanowo pamene anaswa galasi pachitseko chachikulu. Komabe, nzika zambiri za mmalowo sizinavomereze konse mchitidwe wa wansembeyo. Pamenepo kuchitira umboni kosamalitsa kunaperekedwa kwa ofikapo onse, ndipo mabukhu ambirimbiri anagaŵiridwa.”
Momvetsa chisoni, m’mbali zina za dzikoli, muli Mboni zochepekera kwambiri. Pamene mpainiya wokhazikika anafika kwa nthaŵi yoyamba kuchigawo cha Olt, anapeza abale asanu ndi anayi okha m’chigawo chonsecho ndi gawo lalikulu lolalikirako. Pambuyo pa chaka chimodzi chiŵerengero cha Mboni chinawonjezereka kufika 27, amene asanu ake anali ofalitsa oyambiranso kugwira ntchito. Mpainiya anapeza malo okhala mu mzinda wa Corabia, kumene kunalibe Mboni konse. Mboni zitakhala kumeneko kwa masiku 45 okha, wansembe wa malowo ananena mawu otsutsa ntchito yawo pa wailesi ya Craiova. Iye ananena kuti Mbonizo “zinaukira” mzinda wa Corabia ndi ziphunzitso zawo, zikumayesa kuchititsa anthu kusintha chipembedzo chawo. Ziukirozo zinapitirizabe, ncholinga cha kuimitsa ntchito ndi kuwononga mbiri ya Mboni m’chigawocho. Zonsezo zinafika pachimake pamene abale anali ku Bucharest ku msonkhano wachigawo. Wansembe wa Orthodox wa Corabia anapereka chilengezo champhamvu pambuyo pa ulaliki wake m’tchalitchi: “Tonsefe tiyenera kukafola mkhwalala kukasonyeza kusakondwa kuti tisonkhezere apolisi kuchitapo kanthu motsutsana ndi Mboni, zimene zawanditsa dera lonseli ndi mabukhu awo ndipo zaipitsa anthu.” Koma pausiku weniweniwo tsiku limene msonkhanowo unayenera kuchitika, kanthu kachilendo kanachitika. Kagulu ka owononga zinthu dala kanawononga tchalitchi ndi Nyumba Yamzinda Yamaseŵero. Chifukwa chake, msonkhano wosonyeza kusakondwa sunachitike konse!
Madera Amene Anali Yugoslavia
Chaka chautumiki cha 1992 chakhala chovuta koposa kwa abale m’chigawo cha Yugoslavia. Komabe, panthaŵi imodzimodziyo, iwo akhala ndi zokumana nazo zokondweretsa, Tiyamika kuti Yehova samaiŵala ntchito ndi chikondi zosonyezedwa ku dzina lake.
Nkhondo inayambira mu Slovenia, kenako m’Croatia, ndipo pambuyo pake Bosnia ndi Herzegovina. Mkati mwa chaka chimodzi, kuchokera mu lipabuliki limodzi, maiko atsopano asanu anali kufunafuna kuika malire a iwo eni, malamulo awo awo, ndi ndalama zawozawo. Mboni mazana ambiri zinafunikira kuthaŵa nyumba zawo ndi kukapeza pobisala kwa abale awo m’malo ena. Mofanana ndi maiko ena Akummaŵa kwa Yuropu, makomiti osamalira zochitika zamwadzidzidzi anaikidwa m’mizinda yaikulu, kuti apezere malo ogona, chakudya ndi zovala abale athu osoŵa. Mkati mwa chaka chautumiki, pafupifupi matani 55 achakudya anagaŵiridwa kwa abale m’mipingo ya m’zigawo zovutitsidwazo. Makalata ambiri oyamikira alandiridwa.
Abale ku Dubrovnik anasimba mmene analiri oyamikira chithandizo choperekedwa. Pamene mlongo wina anapita kunyumba ndi phukusi lake lachakudya, mnansi wina anafunsa kumene anagula mazira. Mlongoyo anauza mkaziyo kuti abale ake auzimu akuchigawo china anamtumizira mazirawo. Mnansiyo anazizwa. M’chochitika china mwamuna wina wosadziŵika wa ku Slovenia anachitira telefoni mkulu wina nanena kuti: “Ndamva kuti Mboni za Yehova zikugaŵira chakudya chimene zalandira kuchokera kwa abale awo moyeneleradi. Ine ndatumiza mapukusi angapo kwa anthu; komabe, mapukusiwo samafika konse. Kodi ndingatumize katundu wachithandizo wotero kwa inu, ndipo inu mukamgaŵire?” Ndiponso, manyuzipepala ndi mawailesi anasimba moyanja ntchito yathu yopereka chithandizo.
Mbale wina amene anabatizidwa pamsonkhano wa mitundu yonse mu Zagreb mu 1991 anazindikira za mavuto amene analinkudza ndipo anagula sitolo yonse ya zakudya. Iye anatengera chakudyacho kunyumba kwake pafupi ndi chigawo cha nkhondo. Pamene kupereŵera kwa chakudya kunafikira kukhala kwadzawoneni kwambiri, chakudyachi chinatsimikizira kukhala dalitso lenileni kwa abale.
Kunali kotheka kupeza chilolezo chakuti lole yaikulu ipititse zakudya kwa abale otsekerezedwa mu Sarajevo. Tiri okondwera kunena kuti chakudyacho chinatumizidwa mwachipambano.
Nkhondoyo yapha anthu wamba ambiri. Mwachisoni, podzafika mapeto a chaka chautumiki, abale athu ndi alongo asanu ndi mmodzi ndi anthu okondwerera aŵiri anaphedwa, ndipo ena anavulazidwa.
Komabe, zokumana nazo zambiri zikusonyeza kuti kwakukulukulu, kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova ndiko chitetezo. M’chochitika china abale anali paulendo womka kumsonkhano wachigawo ku Belgrade pamene basi linaimikidwa ndi asilikali ankhondo, anafunsa ngati panali ziŵalo zirizonse za chipembedzo chakutichakuti pakati pawo. Abalewo anayankha kuti panalibe. Iwo anafunikira kusonyeza zitupa zawo, ndipo ena a iwo anali ndi maina amene anasonyeza kuti akakhoza kukhala achipembedzo chimenecho. Asilikali ankhondowo anawaimba mlandu wakunama, koma abale anali ndi zikalata zosonyeza kuti anachoka m’tchalitchi chimenecho; ngakhale kuti iwo anabadwira m’chipembedzo chimenecho, abale anafotokoza kuti iwo tsopano anali Mboni za Yehova, ndipo anali kupita ku msonkhano wawo waukulu. Atamva izi asilikaliwo anawalola kupitiriza ulendo wawo.
Apainiya akupitirizabe utumiki wawo ndi changu chosafwifwa, ndipo izi zatsimikizira kukhala chisonkhezero chenicheni ku ntchito. Nsanja ya Olonda, limodzi ndi zikuto zake zokongola m’mawonekedwe ake onse, ikutembenuzidwira pa nthaŵi imodzimodzi m’zinenero zazikulu zonse za chigawochi. Ikupereka mokhazikika kwa okonda chowonadi ndi chilungamo gawo lawo la ‘phoso lauzimu panthaŵi yake.’ (Luka 12:42) Mkati mwa chaka chautumiki cha 1992, abale ndi alongo atsopano 674 anabatizidwa.
Ndithudi, Mulungu sanaiŵale ntchito ya abale a Kummaŵa kwa Yuropu ndi chikondi chimene asonyeza ku dzina lake. Ndiponso, iye ali ndi chikhumbo chakuti alambiri ake onse, mosasamala kanthu za kumene iwo akukhala, atsatire uphungu wabwino kwambiri umene kenako Paulo anapereka pa Ahebri 6:11 umene umati: ‘Koma tikhumba kuti yense wa inu awonetsere changu chomwechi cholinga ku chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro.’