Mafunso OChokera kwa Oŵerenga
Kodi Mkristu angachitenji pamene ali wosakhoza kupeza mnzake wamuukwati woyenerera?
Ngakhale kuti tingakhale Akristu odzipereka, tingathedwebe nzeru pamene tiyembekezera mophanaphana ndi mtima kanthu kena kamene kwenikweni sikamachitika. Malingaliro athu amakhala ofanana ndendende ndi zonenedwa pa Miyambo 13:12, pamene pamati: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” Umu ndimo mmene Akristu ena alingalirira pamene akhala ndi chikhumbo cha kukwatira koma sakhoza kupeza wokwatirana naye woyenerera. Izi ziri makamaka choncho ponena za awo amene mtumwi Paulo anawafotokoza monga “otentha mtima.”—1 Akorinto 7:9.
Yehova anaika mwa anthu chikhumbo cha kupeza wothangatira woyenera mwa mwamuna kapena mkazi. Chifukwa chake, sikuli kodabwitsa kuti Akristu ambiri amene ali mbeta amakhala ndi malingaliro amphamvu otero. (Genesis 2:18) Malingaliro ozoloŵereka amenewa angawonjezeredwe ndi miyambo imene imaika chigogomezero chachikulu pa kukwatira (kapena kukwatiwa pamene ufika msinkhu wakutiwakuti) kapena pamene Akristu mbeta akwetezedwa ndi anthu okwatirana achimwemwe mumpingo. Komabe, sikuli kwabwino kulola kukhala ndi nkhaŵa kwa nyengo yaitali. Chotero kodi ndimotani mmene Akristu owona mtima angalakire mkhalidwewo popanda kuda nkhaŵa mopambanitsa?
Sikuli kokhweka kulaka mkhalidwewo, ndipo ena sayenera kuwona nkhaŵa imeneyi, ngati kuti kunali kukulitsa mbuto ya kalulu ndidzawoneni kapena mkhalidwe wovutitsa waung’onong’ono chabe. Koma kumlingo waukulu, kuthekera kwa kugonjetsa kapena kulaka mkhalidwewo kumadalira pa njira zimene munthu mbetayo angatenge.
Timapeza maziko m’lamulo la Baibulo la makhalidwe abwino lothandiza iri: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Limenelo linanenedwa ndi Yesu Kristu mwamuna amene anali mbeta, ndipo anadziŵa zimene anali kulankhula. Kuchitira anthu ena zinthu ncholinga chopanda dyera ndicho njira yabwino kwambiri yakuthandizira aliyense wa ife kugonjetsa malingaliro a chiyembekezo chozengereza. Kodi zimenezi zimatanthauzanji kwa Akristu mbeta amene akuphatikizidwa?
Kalimirani kuchita ntchito zachifundo kubanja la inu mwini ndi ena mumpingo, ndipo wonjezerani ntchito yanu mu uminisitala. Uphungu umenewu suli kokha njira yonenera kuti, ‘Tanganitsidwani ndipo mudzaiŵala za kufuna kukwatira.’ Ayi. Kutanganitsidwa m’ntchito Zachikristu zimenezi, mungapeze kuti mumafikira kukhala ‘wokhazikika mu mtima mwanu, muli ndi ulamuliro pachifuniro cha inu mwini’ ndipo mungathe kugwiritsira ntchito mikhalidwe yanu yapanthaŵi ino mwanjira yopindulitsa.—1 Akorinto 7:37.
Ena amene akhala ndi chikhumbo chachikulu cha kuloŵa mu ukwati alola chikhumbo chawo kukhala champhamvu kwambiri. Iwo apitirira muyezo kufikira pa kulengeza m’manyuzipepala kuti akufuna mnzawo wa muukwati. Komabe, kukakhala kwabwinopo kwambiri chotani nanga, kuika chigogomezero chokulirapo pa kuyamikira mapindu amene angapezedwe kuchokera m’nthaŵi ya umbeta.—Chonde wonani nkhani zakuti “Wosakwatira koma Wokwanira kaamba ka Utumiki wa Mulungu” ndi “Umbeta—Njira Yamoyo Yofupa” mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1987, ndi “Kodi Ukwati ndiwo Mfungulo Yokha ya Chimwemwe?” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1992.
Pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni kupirira mu mkhalidwe wa umbeta. (Afilipi 4:6, 7, 13) Akristu ambiri mbeta apeza kuti mwakugwiritsira ntchito nthaŵi yawo ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu ndi kufika limodzi ndi kukhala ndi phande pamisonkhano Yachikristu, iwo akhala ndi ‘mpumulo pa moyo wawo,’ wowonjezereka monga momwe Yesu analonjezera kwa omtsatira. (Mateyu 11:28-30) Izi zawathandiza kukulitsa mkhalidwe wauzimu kotero kuti adzakhale amuna kapena akazi abwinopo ngati m’kupita kwanthaŵi angapeze wokwatirana naye woyenerera.
Musaiŵale konse kuti Yehova amazindikira mkhalidwe wa mbeta zonse zimene zikumtumikira. Iye amadziŵa kuti inu mungakhale muli kulingalira kuti mikhalidwe yanu yapanthaŵi ino sindiyo imene mukanakonda. Atate ŵathu wachikondi wakumwamba amazindikiranso zimene ziri zokukomerani koposa pamlingo wokhalitsa, ponse paŵiri mwauzimu ndi mwamaganizo. Inunso mungathe kudziŵa chowonadi ichi: Mwakuyembekezera pa Yehova moleza mtima ndipo mwa kugwiritsira ntchito malamulo a makhalidwe abwino a Mawu ake m’moyo wa tsiku ndi tsiku, mungakhale otsimikizira kuti iye adzakhutiritsa zosoŵa zanu zofunika koposa mwanjira imene iri ndi ubwino wanu wosatha.—Yerekezerani ndi Salmo 145:16.