Chabwino Motsutsana ndi Choipa—Nkhondo Yakalekale
MUAKANEMA akale “munthu wabwino” nthaŵi zonse anagonjetsa magulu a oipa. Koma chowonadi sichinakhale chokhweka motero. Kaŵirikaŵiri kwambiri m’zochitika zenizeni, choipa chimawonekera kupeza chipambano.
Malipoti ochititsa mantha ophatikizapo zochitika zamphulupulu ali zochitika za usiku uliwonse panyuzi. Chakumpoto kwa United States, mwamuna wina ku Milwaukee akupha mwambanda anthu 11 ndipo akusunga zotsala zamitembo yawo yodulidwa nthulinthuli m’friza yake. Chakutaliko kummwera, munthu wosadziŵika akuloŵa mwachiwawa m’kantini ku Texas ndipo ayamba kuwombera volovolo mosasankha kwa mphindi khumi, akumapha anthu 23, kuphatikizapo iye mwini. Wotsutsa wina wosakhutira m’Korea akukoleza moto Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova, akumapha olambira 14.
Sikokha kuti pali zochitika zoopsa zamphulupulu za apa ndi apo koma palinso zoipa zina zochititsa mantha zimene zikuyambukira dziko—kusolotsa fuko kwadala. Kukuyerekezeredwa kuti nzika za Armenia miliyoni imodzi, Ayuda mamiliyoni asanu ndi imodzi, ndi nzika za Cambodia zoposa miliyoni imodzi asolotsedwa m’kupululutsana kwamafuko ndi kwandale zadziko m’zaka za zana lino zokha. Kotchedwa kuyeretsa fuko kwakantha ambirimbiri muimene kale inali Yugoslavia. Palibe munthu amene adziŵa kuchuluka kwa mamiliyoni a anthu osalakwa amene akuzunzidwa mwankhalwe padziko lonse lapansi.
Masoka onga amenewa amatikakamiza kuyang’anizana ndi funso lovutitsa maganizo, Kodi nchifukwa ninji anthu amachita mwanjirayi? Sitingathe kunyalanyaza nkhalwe zimenezi kuti ndizo zochititsidwa ndi maganizo openga. Ukulu wokha wa zoipa zochitidwa m’zaka za zana lathu umalandula malongosoledwe otero.
Chochitika choipa chimafotokozedwa kukhala cholakwa mwamakhalidwe. Ndicho mchitidwe wochitidwa ndi munthu amene angathe kusankha pakati pa kuchita chabwino ndi kuchita choipa. Mwanjira ina yake malangizo ake amakhalidwe amapotoka ndipo choipa chimapambana. Koma kodi nchifukwa ninji ndipo ndimotani mmene izi zimachitikira?
Kaŵirikaŵiri mafotokozedwe achipembedzo onena za choipa ngosakhutiritsa. Wanthanthi Wachikatolika Thomas Aquinas ananena kuti “zinthu zochuluka zabwino sizikanakhalako ngati Mulungu sanalole choipa kukhalako.” Anthanthi Achiprotestante ambiri ali ndi malingaliro ofanana. Mwachitsanzo, monga momwe kwafotokozedwera mu The Encyclopædia Britannica, Gottfried Leibniz analingalira choipa “kukhala kokha chosonyezera chabwino m’dziko, chimene choipacho chimawonjezera mwakusiyana kwake.” Mwa mawu ena, iye anakhulupirira kuti timafunikira choipa kuti tizindikire chabwino. Kulingalira kotero kuli kofanana ndi kuuza wodwala kansa kuti matenda akewo ngofunikiradi kupangitsa munthu wina kudziwona kukhala wamoyo ndi wabwino.
Zolinga zoipa ziyenera kuchokera kwinakwake. Kodi Mulungu ali ndi liwongo losati lachindunji? Baibulo limayankha kuti: “Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” Ngati Mulungu alibe liwongo, kodi ali nalo ndani? Mavesi otsatira akupereka yankho: ‘Koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.’ (Yakobo 1:13-15) Chotero mchitidwe woipa umayamba pamene chilakolako choipa chikulitsidwa mmalo mwakukanidwa. Komabe, sizokhazo.
Malemba amafotokoza kuti zilakolako zoipa zimabuka chifukwa anthu ali ndi mphulupulu yaikulu—kupanda ungwiro kobadwa nako. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Chifukwa chake, monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.’ (Aroma 5:12) Chifukwa cha uchimo wacholoŵa, dyera mothekera lingapambane chifundo m’kuganiza kwathu, ndipo nkhalwe ingapambane kukoma mtima.
Ndithudi, mwachibadwa anthu ambiri amadziŵa kuti mkhalidwe wakutiwakuti ngwolakwa. Chikumbumtima chawo—kapena ‘lamulo lolembedwa m’mitima yawo’ monga momwe Paulo akuchitchulira—chimawaletsa kuchita choipa. (Aroma 2:15) Komabe, mkhalidwe wankhalwe ungathe kutsendereza malingaliro otero, ndipo chikumbumtima chingafikire kukhala chakufa ngati chinyalanyazidwa mobwerezabwereza.a—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 4:2.
Kodi kupanda ungwiro kwaumunthu kokha ndiko chochititsa kuipa kochitidwa m’nthaŵi yathu? Wolemba mbiri Jeffrey Burton Russell anati: “Nzowona kuti aliyense wa ife ali ndi mphulupulu, koma ngakhale kuwonkhetsa pamodzi ziŵerengero zazikulu za zoipa zirizonse sikumasonyeza chochititsa chenicheni cha zoipa zochitidwa ku Auschwitz . . . Zoipa pamlingo umenewu zimawonekera kukhala zosiyana mumkhalidwe ndi m’kukula kwake.” Anali Yesu mwini amene anasonyeza motsimikizirika magwero a choipa amenewa amkhalidwe wosiyana.
Nthaŵi yochepa imfa yake isanachitike, Yesu anafotokoza kuti anthu amene anali kulinganiza kumupha sanali kuchita mogwirizana ndi chikhumbo chawo kotheratu. Mphamvu yosawoneka inali kuwatsogolera. Yesu anawawuza kuti: ‘Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’chowonadi.’ (Yohane 8:44) Mdyerekezi, amene Yesu anamutcha ‘wolamulira wadziko lino,’ alidi ndi mbali yaikulu m’kusonkhezera zoipa.—Yohane 16:11; 1 John 5:19.
Zonse ziŵiri kupanda ungwiro kwaumunthu ndi chisonkhezero cha Satana zadzetsa kuvutika kochuluka kwa zaka zikwi zambiri. Ndipo palibe chizindikiro chakuti chisonkhezero chawo pa anthu chikuchepa. Kodi kuipa sikudzatha? Kapena kodi mphamvu zosonkhezera chabwino potsirizira pake zidzachotsa choipa?
[Mawu a M’munsi]
a Posachedwapa ofufuza awona kugwirizana pakati pa chiwawa choipitsitsa pawailesi yakanema ndi upandu wa achichepere. Malo ofalikira ndi upandu ndi mabanja osweka zirinso nakatande wakudzisungira koipa kwa chitaganya. M’Nazi Jeremani manenanena osalekeza osankhana mtundu anachititsa anthu ena kulungamitsa—ndipo ngakhale kutamanda—kuchitira nkhalwe Ayuda ndi Aslav.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Chikuto: Chithunzithunzi cha U.S. Army
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Chithunzithunzi cha U.S. Army