Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 3/1 tsamba 24-25
  • Kondwerani! Nsupa Zikusefukira ndi Mafuta

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kondwerani! Nsupa Zikusefukira ndi Mafuta
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Mafuta a Golide a ku Mediterranean
    Galamukani!—2008
  • Mtengo Wauŵisi wa Azitona M’nyumba ya Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Mtengo Ukadulidwa Umaphukanso?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Mukudziwa?
    Nsanja ya Olonda—2011
Nsanja ya Olonda—1993
w93 3/1 tsamba 24-25

Zithunzithunzi za Dziko Lolonjezedwa

Kondwerani! Nsupa Zikusefukira ndi Mafuta

MNENERI Yoweli anasonkhezera ‘ana a Ziyoni kukondwera ndi kusekera mwa Yehova.’ Iye anagwiritsira ntchito mafuta a azitona kulongosola chikondwerero chawo ndi kulemerera: “Madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m’zosungiramo zawo.”​—Yoweli 2:23, 24.

Mukanakhala m’Israyeli m’nthaŵi za Baibulo, mukanakondwera kuti pafupi ndi nyumba yanu, kapena minda, pakhale mtengo wa azitona monga uwo wosonyezedwa pamwambapa.a Ukanapangitsa moyo wanu kukhala wosavutirapo, wokondweretsa koposerapo. Kodi nchifukwa ninji mtengo wa azitona ukakhala wofunika kwambiri chotero?​—Yerekezerani ndi Oweruza 9:8, 9.

Choyamba, yang’anitsitsani mtengo wanuwo. Mitengo ya azitona ingakhale ndi moyo kwa zaka mazana angapo, ina ngakhale zaka zikwi zingapo, chotero mwachiwonekere kufufuzako kungasonyeze mawonekedwe ake otumbuluka. Mtengo wanu ungakhale wotalika mamita 6, ndithudi osati wotalika kwambiri mofanana ndi mkungudza kapena wowongoka mofanana ndi kanjedza. Masamba ake obiriŵira nthaŵi zonse, okhala ndi kuyera kong’animira, amapereka mthunzi nthaŵi iriyonse yachaka. Komabe, simungathe kuŵerengera mtengo wanu kwakukulukulu chifukwa cha mawonekedwe ake kapena mthunzi wake. Kutalitali.

Zipatso ndizo chinthu cha mtengo wapatali, zipatso za azitona zikwi zambirimbiri zobiriŵira kapena zakuda! Ndizo zimene zikapangitsa mtengo wa azitona kukhala mbali yofunika m’miyoyo ya anthu ndi ntchito m’Israyeli. Mtengowo umatuŵa maluŵa m’May, kukonzekera kubala zipatso zobulungirazo. (Yobu 15:33) Pamene zimenezi zipsa, zingasinthe kuchokera ku mawonekedwe achikasu obiriŵira kukhala zodera kapena zakuda.

Kututa azitona m’October/​November kunali ntchito yolimba. Mukafunikira kukantha mtengowo ndi ndodo kotero kuti zipatso zakupsa zigwere pa nsalu zoyalidwa pansipo. (Deuteronomo 24:20) Zipatso za azitona zikatsukidwa zisanakonzedwe, monga ngati kunyikidwa m’madzi amchere kuchotsa kuŵawa kwake kozoloŵereka. Kodi chotsatira nchiyani?

Zimenezo zikadalira ndi mmene mukafunira kusangalala kapena kupindula ndi zokolola zanu zolemererazo. Mukadya zipatso za azitona zosaphikidwa, kapena mukakhoza kuziŵiritsa m’vinyo wosasa kotero kuti banja lanu likakhoza kusunga zipatso zokomazo kwa miyezi yambiri. Zipatso za azitona zinakhoza kukhala mbali yaikulu ya chakudya, mwina mwake chakudya chophatikizapo zipatso za azitona zokoleretsedwa limodzi ndi makeke a barele.

Komabe, mwina mwake, mungaike zambiri za zipatso za azitona kuti zikonzedwe mwamadongosolo otsatizanatsatizana ofunika kuti mupeze chinthu chopindulitsa koposa ndi chamtengo wake​—mafuta a azitona. Mukapeza milingo yosiyanasiyana yamafuta, mukumagwiritsira ntchito amenewa m’njira zambiri. Choyamba, mukatha kuwomba pang’ono kapena kuponda zipatso za azitona zakucha mumtondo kapena ngakhale kuziponda ndi mapazi. (Mika 6:15) Kutero kunatulutsa mafuta abwino koposa, amene tsopano akutchedwa oyengeka mwapadera, amene anali oyenerera m’nyali zimene zinaunikira chihema chokomanira. (Eksodo 25:37; 27:20, 21) Tayerekezerani mmene mukanayamikirira kukhala ndi mafuta a mtengo wapatali otero owagwiritsira ntchito pophika m’zochitika zapadera!

Zipatso za azitona, ngakhale zosakhala zabwino kwambiri, zikakhoza kuikidwa mumtondo kutulutsamo mafuta owonjezereka kuchokera ku chipondeponde, ngakhale kuti angakhale osakwera mtengo kwambiri. Chipondeponde chiri pafupifupi 50 peresenti yamafuta. Mungagwiritsire ntchito zoponderamo zamitundumitundu, koma chimodzi chasonyezedwa m’chithunzithunzi panopa. Zipatso za azitona zathunthu kapena zophwanyidwa zinali kuikidwa m’chotengera chonga mtondo. Mphero, yogubuduzidwa ndi bulu kapena munthu, inayendetsedwa pamwamba pake, ikumatulutsa mafuta, amene anatuluka naikidwa m’nsupa.​—Mateyu 18:6.

Mafuta a azitona angayerekezedwe ndi golidi wamadzi​—anali kuŵerengeredwa kwambiri limodzi ndi kugwiritsidwa ntchito kwawo m’mnjira zambiri. Mtengo umodzi unali wokhoza kutulutsira banja la anthu asanu kapena asanu ndi mmodzi mafuta a chaka chathunthu. Akakhala mbali yaikulu ya chakudya chawo, chifukwa chakuti amapukusidwa mosavuta ndipo amapereka nyonga yambiri. (Yerekezerani ndi Yeremiya 41:8; Ezekieli 16:13.) Mukakhoza kutsira zonunkhira m’mafuta ena ndi kuwagwiritsira ntchito monga mafuta odzola kapena kutsanulira ena pamutu wa mlendo monga chisonyezero chakumchereza. (2 Samueli 12:20; Salmo 45:7; Luka 7:46) Mumakhoza kuwagwiritsira ntchito monga mankhwala ochiritsa zilonda.​—Yesaya 1:6; Marko 6:13; Luka 10:34.

Zimenezo sindizo njira zokha zakugwiritsira ntchito kwanu mafuta anu a azitona a mtengo wapataliwo. Mukatha kuwagwiritsiranso ntchito kuunikira m’nyumba mwanu, kukhala mbali yansembe kwa Mulungu, kapena monga chuma chopindulitsa cha kuchigulitsa. Inde, m’nthaŵi za Baibulo mtengo wa azitona unali chomera cha mtengo wapatali koposa, chotero moyenerera Yoweli akanaugwiritsira ntchito kuimira kulemerera ndi chisangalalo.​—Deuteronomo 6:11; Salmo 52:8; Yeremiya 11:16; Mateyu 25:3-8.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti muwone chithunzi chokulirapo cha malo amenewa, wonani Calendar ya Mboni za Yehova ya 1993.

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena