Baibulo—Chitsogozo Chogwira Ntchito cha Munthu Wamakono
“Lemba lililonse adaliuzira Mulungu ndipo lingagwiritsiridwe ntchito mopindulitsa . . . kutsogozera miyoyo ya anthu.”—2 Timoteo 3:16, “The Jerusalem Bible.”
LEMBA limeneli limafotokoza chifukwa chachikulu chimene Baibulo liliri logwira ntchito m’tsiku lathu. Nlouziridwa ndi Mulungu. Popeza kuti Mulungu anatilenga, palibe aliyense amene amadziŵa zambiri ponena za matupi, maganizo, malingaliro, ndi zosoŵa zathu kuposa iye. Nthaŵi ina, Mfumu Davide ya Israyeli inati za Yehova Mulungu: “Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziŵalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu.” (Salmo 139:16) Ngati Mlengi wathu amadziŵa zambiri chotero ponena za ife, moyenerera uphungu ndi chilangizo chake ponena za mmene tingakhalire achimwemwe ndi achipambano m’moyo ziyeneradi kufufuzidwa.
Zochitika zasonyeza kuti malamulo amakhalidwe Abaibulo ali ponse paŵiri ogwira ntchito ndi oyenera m’tsiku lathu. Alinso achindunji. Panopa pali zitsanzo zinayi zosonyeza kugwira ntchito kwamasiku onse kwa Baibulo.
Maunansi a Anthu ndi Khalidwe la Munthu: Baibulo limachilikiza mpambo wabwino wa makhalidwe abwino aumwini amene angachititse maunansi abwino, ndi achipambano ndi ena. Mwachitsanzo, mtundu wa Israyeli unalamulidwa kuti: “Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi . . . koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha.” (Levitiko 19:18) Ngakhale kuti sitili pansi pa lamulo la Aisrayeli, kutsatira malamulo ake amakhalidwe Abaibulo kungatithandize kukhala pamtendere ndi anthu anzathu. Mwachitsanzo, talingalirani kuchuluka kwa mavuto amene angathetsedwe ngati aliyense ayesayesa kukulitsa mikhalidwe yauzimu yopezeka pa Agalatiya 5:22, 23: “Chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.”—Yerekezerani ndi Aroma 8:5, 6.
Mwachisoni, pamene zitsenderezo zichuluka m’moyo, kaŵirikaŵiri mkwiyo ndi nkhwidzi zimakula. M’mikhalidwe yotero, kugwiritsira ntchito mawu achenjezo opezeka pa Miyambo 29:11 kungatipulumutse ku mavuto ochuluka. “Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.”—Yerekezerani ndi Miyambo 15:1; Mateyu 7:12; Akolose 3:12-14.
Uphungu wabwino zedi—koma kodi umagwira ntchito m’moyo? Talingalirani mwamuna wina ku Falansa amene anali ndi vuto lalikulu la kulamulira mkwiyo wake. Nthaŵi zambiri anali kuloŵa m’mavuto, ngakhale kuikidwa m’ndende, chifukwa cha kuchita ndewu. Kukhala kwake katswiri wa nkhonya kunaipitsiratu zinthu. Nthaŵi ina panabuka mkangano pakati pa mwamunayu ndi atate ake. Mwadzidzidzi, nzeru zisanabweremo, anagwetsera pansi atate ake ndi nkhonya imodzi. Panakhala udani waukulu pakati pawo.
M’kupita kwanthaŵi, mwamunayu anakumana ndi Mboni za Yehova nayamba kuphunzira malamulo amakhalidwe Abaibulo. Zimenezi zinamchititsa kupenda mosamalitsa njira imene iye anali kuchitira ndi ena. Mwakuyesayesa kwakukulu khalidwe lake linayamba kusintha, ndipo anakhala wamtendere kwambiri. Ndiyeno tsiku lina mwamunayo anabwerera kwa atate ake kukathetsa chidani. Atate ake anachita chidwi kwambiri ndi masinthidwe amene mwana wawo anachita kotero kuti unansi wawo unabwezeretsedwa.
Chimenechi chili chimodzi cha zitsanzo zambiri zochitira umboni kuwona kwa mawu a mtumwi Paulo akuti: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, . . . nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.”—Ahebri 4:12.
Moyo Wabanja: Kodi banja lanu nlachimwemwe? Mabanja ambiri sali achimwemwe. “Mfundo yakuti moyo wabanja monga kakonzedwe ukuwopsezedwa njotsimikizirika tsopano,” ikutero The Natal Witness, nyuzipepala ya ku South Africa, ikumawonjezera kuti “ana amakono akubadwira m’chipanduko cha kakhalidwe ka anthu.”
Komabe, Baibulo nlodzala ndi uphungu wopindulitsa wolinganizidwa kuthandiza mabanja kupeza chipambano ngakhale pamene mavuto abuka. Mwachitsanzo, ponena za mbali ya amuna, Baibulo limati: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha.” Pamene mwamuna akwaniritsa chofunika chimenechi, mkazi wake amakondwa kumchitiranso mofanana mwakukhala ndi “ulemu wakuya pa mwamuna wake.” (NW) (Aefeso 5:25-29, 33) Unansi pakati pa makolo ndi ana ukunenedwa pa Aefeso 6:4: “Ndipo atate inu, musakwiitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].” Chotero, zimenezi zimapanga mkhalidwe wabanja umene umakuchititsa kukhala kosavuta kwa ana kutsatira lamulo la Baibulo ndi kukhala omvera makolo awo.—Aefeso 6:1.
Zimene zatchulidwazo zangokhala zina za ndemanga zambiri za Baibulo zonena za moyo wabanja. Mwakulabadira chitsogozo cha Mulungu, ambiri apeza chipambano ndipo ali achimwemwe m’banja. Edward, bambo wa ana aŵiri, akulongosola mapindu amene anapeza mwakugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe Abaibulo. “Ukwati wanga unali kusweka,” iye akukumbukira motero. “Ndinalibe nthaŵi yakukhala ndi unansi watanthauzo ndi ana anga. Chinthu chokha chimene chinatigwirizanitsa pamodzi chinali kugwiritsira ntchito kwathu zimene Baibulo limanena pa moyo wabanja.”—Miyambo 13:24; 24:3; Akolose 3:18-21; 1 Petro 3:1-7.
Thanzi Lamaganizo, Lakuthupi, ndi Lamtima: Kufufuza kwasonyeza kuti, kumlingo wakutiwakuti, thanzi lakuthupi la munthu nlogwirizana ndi mkhalidwe wa thanzi lake lamaganizo ndi mtima. “Zizindikiro zofala za kupsinjika,” ikutero The World Book Encyclopedia, “zimaphatikizapo kugunda kofulumira kwa mtima, kuthamanga kwambiri kwa mwazi, kukwinjika kwa minofu, kuchita tondovi, ndi kulephera kusumika maganizo.” Komabe, ena amakhulupirira kuti kuyesera machitachita achiwawa ndiko njira yochepetsera kupsinjika. “Maseŵera a nkhonya angathandize kwambiri kuchepetsa kupsinjika,” ikutero nyuzipepala ya ku South Africa, The Star. Ikugwira mawu a phungu wa maseŵera olimbitsa thupi Jannie Claasens kuti: “Ngati tsiku linali logwiritsa mwala kwambiri kwa mkazi, iye angamasule kupsinjika kwakeko mwakupamantha chithumba cholemera.”
Komabe, kodi sikukakhala kwabwinopo kudziŵa kulamulira magwero enieni a kugwiritsa mwala? M’magazini ya Stress—The Modern Scourge, Dr. Michael Slutzkin akunena kuti “kuzindikira kupsinjika . . . nkofunika, chifukwa zochititsa zambiri zikhoza kuthetsedwa.” Iye akuwonjezera kuti “kulamulira kupsinjika . . . mwina kungathandizirenso kuchira kwa matenda osiyanasiyana.”
Baibulo limafotokoza njira yothandiza kulamulira kupsinjika: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse . . . zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Kulamulira kupsinjika mwanjira imeneyi kuli ndi mapindu ochuluka—ngakhale mwakuthupi. Mwambi wina wa Baibulo umati: “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi.” (Miyambo 14:30) Mwambi winanso umati: “Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.”—Miyambo 17:22.
Poyesa kupeŵa chipsinjo ndi chitsenderezo, ambiri amadalira fodya, zakumwa zoledzeretsa, ndi anamgoneka. Kuvulaza kumene kumwerekera kotero kumachititsa nkodziŵika bwino. Komabe, Baibulo nthaŵi zonse lachilikiza kudzisungira koyera mwakupeŵa “chodetsa chonse cha thupi.” (2 Akorinto 7:1; yerekezerani ndi Miyambo 23:29-35.) Ndithudi, kupeŵa machitachita ovulaza otero kuli njira yachitetezo yogwira ntchito m’dziko lamakono.
Ntchito, Ndalama, ndi Kuwona Mtima: Ulesi supindulitsa. “Wolesi salima chifukwa cha chisanu; adzapemphapempha m’masika osalandira kanthu,” imatero Miyambo 20:4. Komabe, kugwira ntchito zolimba kumapindulitsadi. “Wakubayo asabenso,” amatero Aefeso 4:28. Lembali limawonjezera kuti nkwabwino kwambiri kuti munthu “agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosoŵa.”—Yerekezerani ndi Miyambo 13:4.
Kodi mudziŵa kuti malamulo amakhalidwe Abaibulo angagwirenso ntchito m’maunansi akuntchito? Antchito, mofanana ndi “akapolo” a m’nthaŵi za m’Baibulo, amachita bwino ‘kumvera m’zonse iwo amene ali ambuye [awo] monga mwa thupi.’ Komabe, akulu a ntchito, kapena “ambuye,” ayenera ‘kuchita cholungama ndi cholingana’ kwa antchito awo.—Akolose 3:22-24; 4:1; yerekezerani ndi 1 Petro 2:18-20.
Baibulo limanena zambiri ponena za ntchito zamalonda zowona mtima. Ngakhale nzachisoni kuti kuwona mtima kukusoŵeka lerolino, kumazindikiridwa ndi kuyamikiridwa kaŵirikaŵiri kukhala khalidwe labwino. Kumeneku nkumene Baibulo limagogomezera. Panthaŵi ina Yesu anati: “Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu.”—Luka 16:10; yerekezerani ndi Miyambo 20:10; 22:22, 23; Luka 6:31.
M’dziko lina la m’Afirika, mu indasitale ya diamondi munali kuba kwambiri ndi ziphuphu. Panakhala chigamulo chakuti munthu wina aikidwe kukhala woyang’anira. Nduna za boma zinapemphedwa kupereka maina a awo amene zinalingalira kuti angayenerere malowo. Pamene ndunazo zinachita msonkhano kuti zisankhe munthuyo, maina operekedwawo anafafanizidwa limodzi ndi limodzi, kwakukulukulu chifukwa cha ziphuphu. Potsirizira, anafika pa dzina lothera pandandandayo—losankhidwa ndi prezidenti.
“Koma saali membala wa chipani!” inatsutsa motero nduna ina.
Prezidentiyo anayankha kuti malo amenewo sanali andale.
“Ndimmodzi wa Mboni za Yehova,” wina anatero.
“Nchifukwa chake iye adzatenga ntchito imeneyi,” anatero prezidentiyo. Ndiyeno anawonjezera kuti: “Timadziŵa kuti iwo ali owona mtima, ndipo ndimunthu wamtundu umenewu amene tifuna. Tidziŵa kuti tingamdalire.”
Inde, amene amagwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe Abaibulo kaŵirikaŵiri amawona kuti kuteroko kumawadzetsera mapindu ngakhale m’dziko lamakono.
Sungani Nzeru Yeniyeni
Tangopenda mbali yochepa ya zimene kumatanthauza “kumdziŵadi Mulungu.” (Miyambo 2:1-9) Nkhokwe ya uphungu woyenera, wogwira ntchito ndiyo Baibulo. Malamulo amakhalidwe okhudza ukhondo, kugwira ntchito zolimba, kulankhulana, kugonana, chisudzulo, kulipira msonkho, kuchita ndi kusiyana kwa maumunthu, ndi kuchita ndi umphaŵi zili chabe zina za mbali zochuluka za moyo zofotokozedwa ndi Baibulo. Mamiliyoni ambiri amachitira umboni kuti mlingo wa chipambano ndi kulephera m’moyo umadalira pa mlingo umene iwo amagwiritsirira ntchito malamulo amakhalidwe Abaibulo.
Pamene kugwira ntchito kwa Baibulo kwatsopano lino kuli kotsimikizirika, ilo limapatsanso chiyembekezo cha mapindu ambiri okhalitsa. Mwachitsanzo, Baibulo limalonjeza kuti magwero enieni a zopweteka ndi kuvutika m’dziko lamakono adzachotsedwa posachedwapa mwakuloŵerera kwa Mulungu.—Danieli 2:44; 2 Petro 3:11-13; Chivumbulutso 21:1-5.
Chotero, tikukulimbikitsani kuphunzira zambiri monga momwe mungathere ponena za Baibulo. Ngati mulibe kope lake, yesetsani kupeza limodzi. Ofalitsa magazini ino adzakuthandizani mwachimwemwe. Monga momwedi ambiri apindulira ndi kugwiritsira ntchito malingaliro ogwira ntchito a Baibulo, nanunso mungathandizidwe kuzindikira phindu la Mawu a Mulungu, ponse paŵiri tsopano ndi mtsogolo.
[Chithunzi patsamba 7]
Baibulo lili chitsogozo chogwira ntchito chopangitsa moyo wabanja kukhala wachimwemwe