Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 5/1 tsamba 21-26
  • Chilanditso pa Vumbulutso la Yesu Kristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilanditso pa Vumbulutso la Yesu Kristu
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Kudza” kwa Yesu Kristu
  • Dongosolo la Zochitika
  • Babulo Wamkulu Awonongedwa!
  • Ukwati wa Mwanawankhosa
  • Kuwonongedwa kwa Dziko la Satana
  • Kodi Tsiku la Ambuye Lidzatanthauzanji kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Tamandani Ya Chifukwa cha Ziweruzo Zake
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • “Opani Mulungu Ndipo Mpatseni Ulemerero”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Mmene Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso Akukukhudzirani
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 5/1 tsamba 21-26

Chilanditso pa Vumbulutso la Yesu Kristu

“Kondwerani; kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu.”​—1 PETRO 4:13.

1. Kodi ndimotani mmene Yehova walemeretsera atumiki ake?

YEHOVA walemeretsa Mboni zake ndi mphatso zambiri. Monga Mlangizi wathu Wamkulu, watiunikira ndi chidziŵitso chokwanira ponena za chifuniro ndi cholinga chake. Mwa mzimu wake woyera, wakulitsa mwa ife luso lakuŵalitsa kuunika molimba mtima. Mtumwi Paulo wouziridwayo akutiuza izi pa 1 Akorinto 1:6, 7: “Umboni wa Kristu unakhazikika mwa inu; kotero kuti [siikusoŵani inu mphatso iliyonse, NW]; pakulindira inu vumbulutso la Ambuye wathu Yesu Kristu.”

2. Kodi “vumbulutso la Ambuye wathu Yesu Kristu” limapereka chiyembekezo chosangalatsa chotani?

2 “Vumbulutso la Ambuye wathu Yesu Kristu”​—kodi litanthauza chiyani? Ndiyo nthaŵi pamene Yesu adzavumbulutsidwa monga Mfumu yaulemerero, akuchitapo kanthu kufupa otsatira ake okhulupirika ndi kubwezera chilango anthu osapembedza. Monga momwe 1 Petro 4:13 akusonyezera, idzakhala nthaŵi ya ‘kukondwera ndi kukondwera kwakukulukulu’ kwa Akristu odzozedwa ndi mzimu osunga umphumphu ndi atsamwali awo a khamu lalikulu, pakuti idzasonyeza mapeto a dongosolo la zinthu la Satana.

3. Kodi tiyenera kuchilimika motani, monga momwe anachitira abale athu m’Tesalonika?

3 Pamene nthaŵiyo ikuyandikira, Satana pokhala ndi mkwiyo akukulitsa chitsenderezo pa ife. Monga mkango wobuma, akuyesayesa kutilikwira. Tiyenera kuchilimika zolimba! (1 Petro 5:8-10) Abale athu m’Tesalonika wakale, pamene anali atsopano m’chowonadi, anakumana ndi masautso ofanana ndi amene Mboni za Yehova zambiri zikuyang’anizana nawo lerolino. Chifukwa chake, mawu amene mtumwi Paulo anawalembera ngothandiza kwambiri kwa ife. Iye anati: “Nkolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso, ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu.” (2 Atesalonika 1:6-8) Inde, mpumulo udzafika!

4. Kodi nchifukwa ninji atsogoleri achipembedzo akuyenerera chiweruzo chimene chidzaperekedwa pa vumbulutso la Yesu?

4 M’nthaŵi ya Paulo masautso ambiri anachititsidwa ndi atsogoleri achipembedzo Achiyuda. Mofananamo lerolino, chitsutso kwa Mboni za Yehova zosunga mtendere kaŵirikaŵiri chayambitsidwa ndi awo odzinenera kukhala oimira Mulungu, makamaka atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko. Iwowa amanamizira kuti amamdziŵa Mulungu, koma amakana “Yehova mmodzi” wa Baibulo, akuika m’malo mwake Utatu wachinsinsi. (Marko 12:29, NW) Iwo samalabadira mbiri yabwino yonena za Ambuye wathu Yesu, namayembekezera kupeza mpumulo mu ulamuliro wa munthu ndi kukana mbiri yabwino ya Ufumu wa Kristu wolungama ukudzawo. Otsutsa achipembedzo onseŵa adzawonongedwa panthaŵi ya “vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera kumwamba”!

“Kudza” kwa Yesu Kristu

5. Kodi vumbulutso la Yesu likusonyezedwa bwino lomwe motani pa Mateyu 24:29, 30?

5 Vumbulutso limenelo likusonyezedwa mowonekera bwino ndi Yesu pa Mateyu 24:29, 30. Polongosola mbali zosiyanasiyana za chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha chimaliziro cha dongosolo la zinthu, iye akuti: “Dzuŵa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzawonetsa kuŵala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka.” Panthaŵiyo ‘chizindikiro cha Mwana wa munthu chidzawoneka kumwamba.’ Mitundu ya dziko lapansi “idzadziguguda pachifuŵa, nidzapenya Mwana wa munthu [Mfumu Yaumesiya ya Mulungu] alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” “Kudza” kumeneku, er·khoʹme·non m’Chigiriki, kumasonya ku kuwonekera kwa Yesu monga Wolemekeza Yehova.

6, 7. Kodi “diso lililonse lidzampenya iye” motani, ndipo ndani amene akuloŵetsedwa m’zimenezi?

6 “Kudza” kumeneku kumafotokozedwanso ndi mtumwi Yohane pa Chivumbulutso 1:7, pamene amati: “Tawonani, adza ndi mitambo.” Eya, adani amenewo sadzamuwonadi Yesu ndi maso awo akuthupi, pakuti “mitambo” imatanthauza kuti iye adzadza mosawoneka kudzapereka chiweruzo. Ngati anthu wamba ati amuwone mu ulemerero wake wakumwamba ndi maso awo akuthupi, iwo akachita khungu, mongatu momwe Saulo anachitira, popita ku Damasiko, pamene anakanthidwa ndi khungu pamene Yesu wovekedwa ulemereroyo anawonekera kwa iye ndi cheza chakuŵala kwakukulu.​—Machitidwe 9:3-8; 22:6-11.

7 Cholembedwa cha Chivumbulutso chimanena kuti “diso lililonse lidzampenya iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira iye.” Izi zitanthauza kuti otsutsa apadziko lapansi adzazindikira m’chiwonongeko kuti Yesu wafika pa iwo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu monga Wakupha wa Yehova. Kodi nchifukwa ninji adaniwa akulongosoledwa kuti “amene anampyoza”? Chili chifukwa chakuti mkhalidwe wawo wamaganizo wa chidani kwa atumiki a Yehova lerolino uli ngati wa aja amene anazunza Yesu. Ndithudi, iwo ‘adzadziguguda pachifuŵa ndi chisoni chachikulu chifukwa cha iye.’

8. Kodi ndichenjezo lotani limene onse aŵiri Yesu ndi Paulo akupereka ponena za chiwonongeko chamwadzidzidzi?

8 Kodi tsiku la Yehova lakubwezera limenelo lidzafika motani? Mu ulosi wa Luka chaputala 21, Yesu akufotokoza zochitika zatsoka zimene zatipatsa chizindikiro cha kukhalapo kwake chiyambire 1914. Ndiyeno, m’mavesi 34 ndi 35, Yesu akuchenjeza kuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi.” Inde, tsikulo la kubwezera kwa Yehova lidzafika mwadzidzidzi, mwabalamantha! Mtumwi Paulo akutsimikizira zimenezi pa 1 Atesalonika 5:2, 3, kumati: “Tsiku la [Yehova, NW] lidzadza monga mbala usiku. Pamene angonena, Mtendere ndi [chisungiko!, NW], pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera.” Ngakhale tsopano mitundu ikulankhula za mtendere ndi chisungiko ndi kulingalira zakulimbitsa Mitundu Yogwirizana kuti iyang’anire malo okhalako mavuto mwakugwiritsira ntchito asilikali.

9. Kodi ‘kuunika kukufesekera’ kwa yani ndipo chifukwa ninji?

9 M’mavesi 4 ndi 5, mtumwiyo akupitiriza kutiuza kuti: “Koma inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala; pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitili a usiku, kapena a mdima.” Tikusangalala kukhala ana a kuunika​—oŵalitsira kuunika kwa ena olakalaka mtendere weniweni ndi chisungiko m’dziko latsopano la Mulungu. Pa Salmo 97:10, 11, timaŵerenga kuti: “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m’manja mwa oipa. Kuunika kufesekera wolungama, ndi chikondwerero owongoka mtima.”

Dongosolo la Zochitika

10. Kodi tiyenera kulabadira chenjezo lapasadakhale lotani ponena za tsiku la Mulungu lakuŵerengera mlandu? (Chivumbulutso 16:15)

10 Kodi dongosolo la zochitika lidzakhala lotani pamene chisautso chachikulu chibuka? Tiyeni tiwone Chivumbulutso chaputala 16. Onani kuti, monga momwe kwafotokozedwera m’mavesi 13 mpaka 16, mizimu yonyansa yaziŵanda isonkhanitsa mitundu ya dziko lapansi ku Harmagedo, nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse. Ndiponso, kafikidwe konga mbala ka tsiku la kuŵerengera mlandu kakugogomezeredwa, ndipo tikuchenjezedwa kukhala ogalamuka​—kukhala titavalabe zovala zauzimu zokhala ndi chizindikiro cha chipulumutso chathu. Nthaŵi yafika yakuweruza anthu apadziko lapansi, mitundu, ndi​—wina wake. Ndani ameneyo?

11. Kodi mkazi wa pa Chivumbulutso 17:5 wadzidziŵikitsa motani?

11 Ali mkazi wophiphiritsira amene wayesayesadi kudzipanga kukhala “wina wakeyo” wofunika kwambiri. Iye walongosoledwa pa Chivumbulutso 17:5 monga “Chinsinsi, Babulo Waukulu, amayi wa achigololo ndi wa zonyansitsa za dziko.” Koma iye salinso chinsinsi kwa Mboni za Yehova. Iye wadzidziŵikitsa yekha poyera kukhala ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga, amene magulu achipembedzo a Chikristu Chadziko akupanga mbali yake yaikulu. Kumene kumamnyansadi Yehova ndiko kuloŵerera kwake m’nkhani za ndale, kukhala kwake “woledzera ndi mwazi wa oyera mtima” mwakuzunza Akristu owona, ndi kukhala kwake ndi liŵongo la mwazi wa “onse amene anaphedwa padziko,” kuphatikizapo oposa mamiliyoni zana limodzi la ophedwa m’nkhondo za m’zaka za zana la 20 lino lokha.​—Chivumbulutso 17:2, 6; 18:24.

12. Kodi nchifukwa ninji magulu achipembedzo a Chikristu Chadziko ali otsutsidwa?

12 Choipirapo koposa, magulu achipembedzo a Chikristu Chadziko adzetsa chitonzo pa dzina la Mulungu amene mwachinyengo amanena kuti amamuimira. Iwo aphunzitsa nthanthi Zachibabulo ndi Zachigiriki m’malo mwa Mawu oyera a Mulungu ndipo awonjezera makhalidwe oluluzika a mitundu yonse mwakuvomereza njira za moyo wolekerera zimene zimapeputsa malamulo amkhalidwe a Baibulo. Amalonda aumbombo pakati pawo akutsutsidwa ndi mawu a Yakobo 5:1, 5 kuti: “Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu. Mwadyerera padziko, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m’tsiku lakupha.”

Babulo Wamkulu Awonongedwa!

13. Kodi chisautso chachikulu chidzabuka motani, ndipo nkufulumira kotani kumene kwagogomezeredwa pa Chivumbulutso 18:4, 5?

13 Chisautso chachikulu chikubuka ndi kuperekedwa kwa chiweruzo cha Yehova pa Babulo Wamkulu. Chivumbulutso 17:15-18 chimafotokoza bwino “za m’mtima” wa Mulungu​—zakuchititsa “nyanga khumi,” mphamvu zolimba za mkati mwa “chilombo” cha Mitundu Yogwirizana cha mitundu yambiricho, kuti zimkhadzule. “Ndipo nyanga khumi udaziwona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsereza ndi moto. Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwawo kuchita za m’mtima mwake.” Mposadabwitsa kuti mawu akumwamba akupereka chenjezo lofulumira pa Chivumbulutso 18:4, 5 kuti: “Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake; pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m’mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.” Chilengezocho chikupitiriza kuperekedwa: Lekani kugwirizana kulikonse ndi chipembedzo chonyenga, musanachedwe!

14. Kodi ndani amene adzalira pa chiwonongeko cha Babulo Wamkulu, ndipo chifukwa ninji?

14 Kodi dziko lidzakuwona motani kusakazidwa kwa Babulo Wamkulu? Ataima patali, andale onyenga​—“mafumu a dziko”​—adzalirira iye chifukwa kwa zaka mazana ambiri anasangalala naye m’chigololo chauzimu. Amene adzamliranso ndi kumchitira chisoni ndiwo amuna amalonda aumbombo, ‘ochita malonda a m’dziko . . . , olemezedwa naye.’ Awa nawonso aima patali naye, akumati: “Tsoka, tsoka, mudzi waukulu wovala bafuta ndi chibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golidi ndi mwala wa mtengo wake, ndi ngale! Pakuti m’ola limodzi chasanduka bwinja chuma chachikulu chotere.” Zovala zake zachipembedzo zamtengo wapatali zonsezo ndi ulemerero wa nyumba zake zatchalitchi zazikulu za padziko lonse zidzapita kotheratu! (Chivumbulutso 18:9-17) Koma kodi aliyense adzamlira Babulo Wamkulu?

15, 16. Kodi nchifukwa chotani chimene anthu a Mulungu adzasangalalira?

15 Chivumbulutso 18:20, 21 chimayankha kuti: “Kondwera pa iye, m’mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu. Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala, ngati mphero yaikulu, naiponya m’nyanja, nanena, Chotero Babulo, mudzi waukulu, [wa]pasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.”

16 Nchifukwa chosangalalira chotani nanga! Chivumbulutso 19:1-8 chimatsimikiziritsa zimenezi. Chilengezo chakuti “Aleluya” chikumveka kanayi kuchokera kumwamba. Zitamando zoyamba zitatu zimenezi za Aleluya zimatamanda Yehova chifukwa chakuti wapereka chiweruzo cholungama pa mkazi wachigololo wambiri yoipayo, Babulo Wamkulu. Ulamuliro wadziko wa chipembedzo chonyenga palibenso! Mawu ochokera kumpando wachifumu wa Mulungu, akuti: “Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse, akumuwopa iye, aang’ono ndi aakulu.” Tidzakhala ndi mwaŵi wotani nanga kuimbako nyimbo imeneyi!

Ukwati wa Mwanawankhosa

17. Poyerekezera Chivumbulutso 11:17 ndi 19:6, kodi ndi m’nkhani ziŵiri ziti m’mene Yehova akuyamba kulamulira monga Mfumu?

17 Aleluya wachinayi akuyambitsa mutu wina kuti: “Aleluya; pakuti achita ufumu [Yehova, NW] Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.” Koma kodi kolasi lofanana silinaimbidwe pa Chivumbulutso 11:17? Pamenepo timaŵerenga kuti: “Tikuyamikani, [Yehova, NW] Mulungu, Wamphamvuyonse, . . . popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu.” Inde. Komabe, nkhani ya Chivumbulutso 11:17 ikunena za kubweretsa Ufumu Waumesiya kwa Yehova mu 1914 ‘kudzaŵeta mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo.’ (Chivumbulutso 12:5) Chivumbulutso 19:6 chikunena za nkhani ya kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu. Chipembedzo chonga mkazi wachigololo chitachotsedwa, Umulungu wa Yehova udzalemekezedwa. Kumlambira iye monga Wolamulira Wamkulukulu ndi Mfumu kudzakhalapo tsopano ndi ku umuyaya wonse!

18. Kuchotsedwa kwa Babulo Wamkulu kumalola kuperekedwa kwa chilengezo chotamanda chotani?

18 Chifukwa chake, chilengezo chotamanda chingaperekedwe chakuti: “Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa [Ya]; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera. Ndipo anampatsa iye avale bafuta wonyezimira woti mbu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.” (Chivumbulutso 19:7, 8) Sikunanenedwe kuti nliti kwenikweni pamene odzozedwa okhalapobe padziko lapansi adzalandira chiukiriro chakumwamba. Koma tikutsimikiziridwa m’nkhani ino kuti kutengamo mbali kwawo muukwati wa Mwanawankhosa, Kristu Yesu, kudzakhala nthaŵi yachimwemwe, ndipo idzakhaladi yotero koposa, chifukwa chakuti adzakhala atadziwonera kunyazitsidwa kwa mkazi wachigololo wambiri yoipayo, Babulo Wamkulu.

Kuwonongedwa kwa Dziko la Satana

19. Kodi nchochitika china chotani chofotokozedwa pa Chivumbulutso 19:11-21?

19 Kavalo woyera woyamba kutchulidwa pa Chivumbulutso 6:2 akuwonekeranso. Timaŵerenga motere pa Chivumbulutso 19:11: “Iye wakumkwera [kavalo woyera aku]tchedwa Wokhulupirika ndi Wowona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.” Chotero “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye” akuthira nkhondo ali pakavalo kuukira mitundu ndi kuponda “moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.” Kuli kosaphula kanthu kuti “mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo awo” akusonkhana kuti amenye nkhondo ya Harmagedo. Wokwera kavalo woyera akumaliza kugonjetsa kwake. Palibe chimene chikutsala cha gulu la Satana ladziko lapansi.​—Chivumbulutso 19:12-21.

20. Kodi nchiyani chimene chidzamchitikira Mdyerekezi iye mwiniyo?

20 Koma bwanji za Mdyerekezi iye mwiniyo? Pa Chivumbulutso 20:1-6, Kristu Yesu akulongosoledwa monga ‘mngelo wotsika kumwamba, wokhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake.’ Iye agwira chinjokacho, Njoka yokalambayo, amene ali Mdyerekezi ndi Satana, ammanga, kumponyera m’phompho, ndi kutsekapo naikapo chizindikiro. Pokhala kuti Satana wachokapo wosakhozanso kusocheretsa mitundu, Ulamuliro wa Zaka Chikwi waulemerero wa Mwanawankhosa ndi mkwatibwi wake udzayamba. Sipadzakhalanso misozi yachisoni! Imfa ya kwa Adamu kulibenso! Palibe maliro, palibe kulira, palibe choŵaŵitsa! “Zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4.

21. Pamene tikuyembekezera mwachidwi vumbulutso la Yesu Kristu, kodi tiyenera kukhala otsimikizira kuchitanji?

21 Pamene tikuyembekezera mwachidwi vumbulutso la Ambuye wathu Yesu Kristu, tiyeni tisonyeze changu cha kuuza ena ponena za malonjezo achikondi a Ufumu wa Mulungu. Chilanditso chayandikira! Tipitebe patsogolo, inde nthaŵi zonse, monga ana ounikiridwa a Ambuye Mfumu Yehova!

Kubwereramo

◻ Kodi nchiyani chimasonyeza kuti vumbulutso la Yesu Kristu layandikira?

◻ Kodi tsiku lakubwezera la Yehova lidzafika motani?

◻ Kodi “okonda Yehova” ayenera kuuwona motani mkhalidwe wadziko lerolino?

◻ Kodi dongosolo la zochitika lidzakhala lotani pamene chisautso chachikulu chibuka?

[Chithunzi patsamba 23]

Yesu ‘akudza ndi mitambo,’ mosawoneka, kudzapereka chiweruzo

[Chithunzi patsamba 25]

Posachedwapa, chipembedzo chonyenga, dongosolo loipa la Satana, zidzapita limodzi ndi Satana iye mwiniyo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena