Kodi Nkupenderanji Kulondola kwa Baibulo?
Kodi mumaliwona motani Baibulo? Ena amakhulupirira kwambiri kuti ndivumbulutso la Mulungu kwa anthu. Ena amakhulupirira kuti ndibuku wamba. Komabe ena amakayikakayika. Ngati mumakayikira ponena za kumene Baibulo linachokera, pali zifukwa zamphamvu zimene muyenera kulipendera ndi kuthetsa nkhaniyo.
KUFIKIRA m’zaka za zana la 18, Baibulo linali kulemekezedwa monga Mawu a Mulungu m’maiko a Chikristu Chadziko. Koma kuyambira m’zaka za zana la 19 kumka mtsogolo, chiŵerengero chomawonjezereka cha aphunzitsi, asayansi, ndipo ngakhale akatswiri amaphunziro azaumulungu ndi atsogoleri atchalitchi anayamba kukayikira poyera kulondola kwa Baibulo.
Chotsatirapo nchakuti kusuliza Baibulo kwakhala kofala kwambiri kwakuti ambiri amangonyalanyaza asanawone konse zimene zili mkati mwa Baibulo. Mmalo mwa Baibulo, anthu ambiri m’Chikristu Chadziko tsopano amayang’ana kunthanthi za anthu. Komabe, nthanthi zamakono sizinachititse anthu kukhala achisungiko ndi achimwemwe. Chimenecho nchifukwa chimodzi chabwino chimene muyenera kupendera Baibulo ndi kuwona ngati chitsogozo chake chimatsogolera kuchimwemwe ndi chipambano.
Chifukwa china chopendera kulondola kwa Baibulo ndicho chiyembekezo chabwino koposa chimene limapereka kwa mtundu wa anthu. Mwachitsanzo, lemba la Salmo 37:29 limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Chivumbulutso 21:3-5) Kodi malonjezo amenewo amakuyambukirani motani? Ndithudi, ali zifukwa zokwanira zopendera Baibulo ndi kuwona ngati lingadaliridwe.
Magazini ano achilikiza mosalekeza kuwona kwa Baibulo ndipo kaŵirikaŵiri apereka umboni wa kulondola kwake. Pali mbali zambiri zimene kulondola kwa Baibulo kungapendedwe. Makope osiyanasiyana a Nsanja ya Olonda adzakuthandizani kuyankha mafunso awa: Kodi maumboni a mbiri yamakedzana amagwirizana ndi Baibulo? Kodi maulosi ake ngolondola? Kodi uphungu wake umathandiza, kapena kodi aphunzitsi ndi anthanthi amakono atsimikizira kuti Baibulo nlachikale?
Malo otchulidwamo ali mbali ina imene mungapendere kulondola kwa Baibulo. Kaŵirikaŵiri nthano zachikunja zimasemphana ndi maumboni a malo otchulidwa. Mwachitsanzo, anthu ambiri amakedzana anasimba nthano za maulendo opita kumalo otchedwa dziko la akufa. Buku la A Guide to the Gods likulongosola motere ponena za Agiriki amakedzana: “Dziko lapansi linawonedwa monga lathyathyathya lozingidwa ndi mkwamba waukulu wa madzi wotchedwa Nyanja. Kutsidya kwake kunali Dziko la Akufa, chipululu chokhala ndi zomera zosabala zipatso.” Pamene zimenezi zinatsimikiziridwa kukhala nthano, anthanthi achikunjawo anayenera kupeza malo ena otchedwa dziko la akufa. “Malo oyenerera anapezeka, okhala kunsi kwa dziko, ogwirizanitsidwa ndi dziko lino ndi mapanga osiyanasiyana,” akulongosola motero wolemba nkhani Richard Carlyon. Lerolino, timadziŵa kuti imeneyinso ndinthano. Kulibe dziko la akufa kapena njira yoteroyo.
Mosiyana ndi nthano za anthu amakedzana, Baibulo lilibe lingaliro lolakwika lakuti dziko lapansi nlathyathyathya. Mmalomwake, limanena chowonadi cha sayansi chakuti dziko lapansi ndi chinthu chobulungira cholenjekeka pachabe. (Yobu 26:7; Yesaya 40:22) Bwanji za malo ena otchulidwa m’Baibulo? Kodi ndinthano, kapena kodi nkotheka kuyerekezera molondola zochitika za Baibulo pamene tipita ku Igupto wamakono, kuphatikizapo ndomo ya Sinai, ndi Israyeli wamakono?
[Chithunzi patsamba 3]
“Pali Iye amene akukhala pamwamba pa mbulunga ya dziko lapansi.”—Yesaya 40:22, NW
‘Alenjeka dziko pachabe.’—Yobu 26:7