Kodi Tingawonjezere Motani Ukoma Pachikhulupiriro Chathu?
“Muonjezerapo ukoma pachikhulupiriro chanu.”—2 PETRO 1:5.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuyembekezera anthu a Yehova kuchita chimene chili chokoma?
NTHAŴI zonse Yehova amachita zinthu mwaukoma. Amachita zimene zili zolungama ndi zabwino. Chifukwa chake, mtumwi Petro anafotokoza Mulungu kukhala uyo amene anaitana Akristu odzozedwa “ndi ulemerero ndi ukoma wake wa Iye yekha.” Chidziŵitso cholongosoka cha ukoma wa Atate wawo wakumwamba chinali chitawasonyeza zimene zinali zofunika kuti atsate moyo wa kudzipereka kwaumulungu kowona.—2 Petro 1:2, 3.
2 Mtumwi Paulo amafulumiza Akristu ‘kukhala akutsanza Mulungu, monga ana okondedwa.’ (Aefeso 5:1) Mofanana ndi Atate wawo wakumwamba, olambira a Yehova ayenera kuchita zimene zili zabwino mumkhalidwe uliwonse. Koma kodi ukoma nchiyani?
Chimene Ukoma Uli
3. Kodi ndimotani mmene liwulo “ukoma” lafotokozedwera?
3 Madikishonale amakono amafotokoza liwulo “ukoma” kukhala “ubwino woposa wa mkhalidwe; ubwino.” Uli “kulingalira ndi kachitidwe kolungama.” Munthu waukoma ngwolungama. Ukoma wafotokozedwanso kukhala “kugwirizana ndi muyezo wa chilungamo.” Zowonadi, kwa Akristu, “muyezo wa chilungamo” umaikidwa ndi Mulungu ndi kumveketsedwa bwino m’Mawu ake Opatulika, Baibulo.
4. Kodi ndimikhalidwe yotani yotchulidwa pa 2 Petro 1:5-7 imene Akristu ayenera kuigwirira ntchito zolimba kuti aikulitse?
4 Akristu owona amagwirizana ndi miyezo yolungama ya Yehova Mulungu, ndipo amachita mogwirizana ndi malonjezo ake amtengo wapatali mwa kusonyeza chikhulupiriro. Amamveranso uphungu wa Petro wakuti: “Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pachikhulupiriro chanu, ndi paukoma [chidziŵitso, NW]; ndi [pachidziŵitso, NW] chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro [kudzipereka kwaumulungu, NW]; ndi [pakudzipereka kwaumulungu, NW] chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi.” (2 Petro 1:5-7) Mkristu ayenera kuyesayesa zolimba kuti akulitse mikhalidwe imeneyi. Zimenezi sizimachitidwa m’masiku kapena zaka zoŵerengeka koma zimafuna kuyesayesa kosalekeza kwa moyo wonse. Eya, kuwonjezera ukoma pachikhulupiriro chathu ndiyo ntchito yovuta mwa iko kokha!
5. Kodi ukoma nchiyani m’lingaliro la m’Malemba?
5 Wolemba dikishonale M. R. Vincent akunena kuti lingaliro loyambirira lakale la liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kuti “ukoma” limapereka lingaliro la “ubwino woposa wa mtundu uliwonse.” Petro anagwiritsira ntchito mpangidwe wake wochulukitsa pamene ananena kuti Akristu anafunikira kukalengeza “zoposazo,” kapena zokoma, za Mulungu. (1 Petro 2:9) Kunena mwa lingaliro la Malemba, ukoma ukufotokozedwa osati monga mkhalidwe wamphwayi koma monga “mphamvu ya khalidwe, nyonga ya khalidwe, mphamvu ya moyo.” Potchula za ukoma, Petro anali kunena za ubwino woposa wa mkhalidwe umene atumiki a Mulungu amayenera kusonyeza ndi kusunga. Komabe, popeza kuti ndife opanda ungwiro, kodi tingachitedi zimene zili zokoma pamaso pa Mulungu?
Opanda Ungwiro Koma Aukoma
6. Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, kodi nchifukwa ninji tinganene kuti tingathe kuchita chimene chili chokoma m’maso mwa Mulungu?
6 Tinalandira choloŵa cha kupanda ungwiro ndi uchimo, chotero tingakayikire za mmene tingachitiredi zimene zili zokoma pamaso pa Mulungu. (Aroma 5:12) Ndithudi tifunikira thandizo la Yehova ngati titi tikhale ndi mitima yoyera, mmene mumachokera malingaliro, mawu ndi machitidwe okoma. (Yerekezerani ndi Luka 6:45.) Atachimwa ndi Bateseba, wamasalmo wolapayo Davide anapempha kuti: “Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika mkati mwanga.” (Salmo 51:10) Davide anakhululukiridwa ndi Mulungu ndipo analandira thandizo lofunika kuti alondole njira yaukoma. Chifukwa chake, ngati tachita tchimo lalikulu komabe tivomereza molapa thandizo la Mulungu ndi akulu a mumpingo, tikhoza kubwereranso m’njira yaukoma ndi kupitirizabe kuyendamo.—Salmo 103:1-3, 10-14; Yakobo 5:13-15.
7, 8. (a) Ngati titi tikhalebe aukoma, kodi chikufunika nchiyani? (b) Kodi ndithandizo lotani limene Akristu ali nalo m’kukhala aukoma?
7 Chifukwa cha choloŵa cha uchimo, tiyenera kupitirizabe kumenya nkhondo mkati mwa thupi lathu ya kuchita zimene njira ya ukoma ikufuna kuti tichite. Ngati titi tikhalebe aukoma, sitiyenera kudzilola kukhala akapolo a uchimo. Mmalomwake, tiyenera kukhala “akapolo a chilungamo,” nthaŵi zonse tikumaganiza, kulankhula, ndi kuchita zinthu m’njira yaukoma. (Aroma 6:16-23) Ndithudi, zikhumbo zathu zathupi ndi zikhoterero zauchimo nzamphamvu, ndipo timayang’anizana ndi nkhondo imene ili pakati pa mikhalidwe imeneyi ndi zinthu zaukoma zimene Mulungu amafuna kuti tichite. Chotero, kodi tingachitenji?
8 Choyamba, tifunikira kutsatira chitsogozo cha mzimu woyera wa Yehova, kapena mphamvu yake yogwira ntchito. Chifukwa chake tiyenera kulabadira uphungu wa Paulo wakuti: “Muyendeyende ndi mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi. Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye mzimu, ndi mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.” (Agalatiya 5:16, 17) Inde, tili ndi mzimu wa Mulungu monga nyonga ya chilungamo, ndipo tili ndi Mawu ake monga chitsogozo cha khalidwe labwino. Tilinso ndi thandizo lachikondi m’gulu la Yehova ndi uphungu wa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Motero, tikhoza kumenya nkhondo yachipambano molimbana ndi zikhoterero zauchimo. (Aroma 7:15-25) Ndithudi, ngati malingaliro oipa adza m’maganizo athu, tiyenera kuwachotsa nthaŵi yomweyo ndi kupempherera thandizo la Yehova kuti tikanize chiyeso chilichonse cha kuchita zinthu m’njira ina iliyonse yopanda ukoma.—Mateyu 6:13.
Ukoma ndi Malingaliro Athu
9. Kodi khalidwe la ukoma limafuna kuganiza kwa mtundu wotani?
9 Ukoma umayamba mwanjira imene munthu amaganizira. Kuti tiyanjidwe ndi Mulungu, tiyenera kuganiza za zinthu zolungama, zabwino, ndi zokoma. Paulo anati: “Abale, zinthu zili zonse zowona, zili zonse zolemekezeka, zili zonse zolungama, zili zonse zoyera, zili zonse zokongola, zili zonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.” (Afilipi 4:8) Tifunikira kusumika maganizo athu pazinthu zolungama ndi zoyera, ndipo kanthu kalikonse kamene kalibe ukoma sikayenera kutikopa. Nchifukwa chake Paulo anatha kunena kuti: “Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani.” Ngati tili ofanana ndi Paulo—okoma m’malingaliro, m’zonena, ndi m’machitidwe—tidzakhala mabwenzi abwino ndi opereka chitsanzo chabwino m’moyo Wachikristu, ndipo ‘Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi nafe.’—Afilipi 4:9.
10. Kodi ndimotani mmene kugwiritsira ntchito kwa munthu mwini mawu a pa 1 Akorinto 14:20 kudzatithandizira kukhalabe aukoma?
10 Ngati tikukhumba kukhalabe ndi ukoma m’malingaliro ndipo motero kukondweretsa Atate wathu wakumwamba, nkoyenerera kuti tigwiritsire ntchito uphungu wa Paulo wakuti: “Musakhale ana m’chidziŵitso, koma m’choipa khalani makanda, koma m’chidziŵitso akulu misinkhu.” (1 Akorinto 14:20) Zimenezi zikutanthauza kuti monga Akristu ife sitimafunafuna kudziŵa zoipa kapena kuchita zoipa. Mmalo mwa kulola maganizo athu kuipitsidwa mwanjira imeneyi, ife mwanzeru timasankha kukhala makanda osadziŵa kanthu kumbali imeneyi. Panthaŵi imodzimodziyo, timazindikira mokwanira kuti makhalidwe oipa ndi kuchita zoipa zili uchimo m’maso mwa Yehova. Chikhumbo cha mtima wonse cha kumkondweretsa mwa kusonyeza ukoma chidzatipindulitsa, chidzatisonkhezera kupeŵa mipangidwe yonyansa ya kusanguluka ndi ziyambukiro zina zoipitsa maganizo za dzikoli limene lagona mumphamvu ya Satana.—1 Yohane 5:19.
Ukoma ndi Kalankhulidwe Kathu
11. Kodi kukhala waukoma kumafuna mtundu wanji wa kalankhulidwe, ndipo ponena za nkhani imeneyi, kodi ndizitsanzo zotani zimene tili nazo mwa Yehova ndi Yesu Kristu?
11 Ngati malingaliro athu ali okoma, ameneŵa ayenera kukhala ndi chiyambukiro chachikulu pazimene timanena. Kukhala aukoma kumafuna kalankhulidwe komangirira, koyera, kabwino, ndi kowona. (2 Akorinto 6:3, 4, 7) Yehova ndiye “Mulungu wa chowonadi.” (Salmo 31:5) Ngwokhulupirika m’zochita zake zonse, ndipo malonjezo ake ngotsimikizirika chifukwa chakuti sanganame. (Numeri 23:19; 1 Samueli 15:29; Tito 1:2) Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, ali “wodzala ndi chisomo ndi chowonadi.” Pamene anali padziko lapansi, nthaŵi zonse analankhula chowonadi monga momwe anachilandirira kwa Atate wake. (Yohane 1:14; 8:40) Ndiponso, Yesu “sanachita tchimo, ndipo m’kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo.” (1 Petro 2:22) Ngati tilidi atumiki a Mulungu ndi Kristu, tidzakhala owona m’kalankhulidwe kathu ndi akhalidwe lowongoka, monga ngati kuti ‘tamangirira chowonadi m’chuuno.’—Aefeso 5:9; 6:14.
12. Ngati titi tikhale aukoma, kodi ndimitundu yotani ya kalankhulidwe imene tiyenera kupeŵa?
12 Ngati tili aukoma, pali mitundu ya kalankhulidwe imene tidzapeŵa. Tidzalamulidwa ndi uphungu wa Paulo wakuti: “Chiwawo chonse, ndi kupsya mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.” “Dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.” (Aefeso 4:31; 5:3, 4) Anthu ena adzatsitsimulidwa poyanjana nafe chifukwa chakuti mitima yathu yolungama imatisonkhezera kupeŵa kalankhulidwe kosakhala Kachikristu.
13. Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kulamulira lilime?
13 Kukhumba kutumikira Mulungu ndi kunena zinthu zokoma kudzatithandiza kulamulira lilime lathu. Chifukwa cha zikhoterero zauchimo, nthaŵi zina tonsefe timakhumudwa m’mawu. Komabe, wophunzira Yakobo amanena kuti “ngati tiikira akavalo zogwirira m’kamwa mwawo,” adzalabadira kupita kumene tiwatsogoza. Chifukwa chake, tiyenera kugwira ntchito zolimba kuti tigwire lilime ndi kuyesa kuligwiritsira ntchito m’njira zokoma zokha. Lilime losalamuliridwa ndilo “dziko la chosalungama.” (Yakobo 3:1-7) Mkhalidwe woipa ulionse wa dziko lopanda umulungu limeneli umagwirizanitsidwa ndi lilime losalamuliridwa. Ndilo limene lili ndi mlandu wa zinthu zowononga monga ngati kuchitira umboni wonama, kutonza, ndi kuneneza. (Yesaya 5:20; Mateyu 15:18-20) Ndipo pamene lilime losalamulirika linena mawu otukwana, opweteka, kapena oneneza, limadzadzidwa ndi ululu wakupha.—Salmo 140:3; Aroma 3:13; Yakobo 3:8.
14. Kodi ndimuyezo wapaŵiri wotani wa kalankhulidwe umene Akristu ayenera kupeŵa?
14 Monga momwe Yakobo akusonyezera, ‘kuyamika [Yehova, NW]’ mwa kunena za zinthu zabwino za Mulungu komanso tikumagwiritsira ntchito lilime moipa mwa ‘kutemberera anthu’ kuti zoipa ziwagwere kukakhala kosephana. Nkulakwa kotani nanga kuimba zitamando za Mulungu pamisonkhano ndiyeno kutuluka kukanenera zoipa wokhulupirira mnzathu! Madzi okoma ndi oŵaŵa omwe sangatuluke pakasupe mmodzimodziyo. Ngati tikutumikira Yehova, anthu ayenera kutiyembekezera kunena zinthu zokoma mmalo mwa kulankhula mawu oipa. Chifukwa chake tiyeni tiipidwe ndi kalankhulidwe koipa ndi kufunafuna kunena zinthu zimene zidzapindulitsa mabwenzi athu ndi kuwalimbikitsa mwauzimu.—Yakobo 3:9-12.
Ukoma ndi Machitidwe Athu
15. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kupeŵa kubwereranso kunjira zaukathyali?
15 Popeza kuti lingaliro la Mkristu ndi kalankhulidwe ziyenera kukhala zokoma, bwanji nanga za machitidwe athu? Kukhala aukoma m’makhalidwe ndiko njira yokha yokhalira ndi chiyanjo cha Mulungu. Palibe mtumiki wa Yehova amene angasiye mkhalidwe wa ukoma, nakhala waukathyali ndi wachinyengo, naganiza kuti mikhalidwe imeneyo idzavomerezedwa ndi Mulungu. Lemba la Miyambo 3:32 limati: “Wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi Chake chili ndi owongoka.” Ngati timasamalira bwino unansi wathu ndi Yehova Mulungu, mawu osonkhezera maganizo amenewo ayenera kutiletsa kuchita chiwembu kapena kuchita kanthu kalikonse kaukathyali. Eya, pakati pa zinthu zisanu ndi ziŵiri zimene mtima wa Yehova umanyansidwa nazo pali “mtima woganizira ziwembu zoipa”! (Miyambo 6:16-18) Chifukwa chake, tiyeni tipeŵe machitidwe otero ndi kuchita zimene zili zokoma, kuti tipindulitse anthu anzathu ndi kulemekeza Atate wathu wakumwamba.
16. Kodi nchifukwa ninji Akristu sayenera kuloŵa m’machitachita alionse onyenga?
16 Kusonyeza ukoma kumafunikiritsanso kuti tikhale owona mtima. (Ahebri 13:18) Munthu wachinyengo, amene amachita zinthu mosiyana ndi mawu ake, sali waukoma. Liwu Lachigiriki lakuti “wonyenga” (hy·po·kri·tesʹ) limatanthauza “munthu amene amayankha” ndiponso limapereka lingaliro la munthu woseŵera seŵero. Popeza kuti oseŵera seŵero Achigiriki ndi Achiroma anali kuvala chinyau kumaso, liwu limeneli linafikira pakugwiritsiridwa ntchito mokuluŵika kwa munthu amene amavala mkhalidwe wonyengezera. Anthu onyenga ali “osakhulupirika.” (Yerekezerani ndi Luka 12:46 ndi Mateyu 24:50, 51.) Chinyengo (hy·poʹkri·sis) chingaperekenso lingaliro la kuipa ndi machenjera. (Mateyu 22:18; Marko 12:15; Luka 20:23) Nzomvetsa chisoni chotani nanga pamene munthu wokhulupirika anyengedwa ndi kumwetuliridwa, kubwatikidwa, ndi machitidwe amene ali kokha onyengezera! Komanso kuli kothutsa mtima pamene tidziŵa kuti timachita zinthu ndi Akristu odalirika. Ndipo Mulungu amatidalitsa chifukwa cha kukhala aukoma ndi opanda chinyengo. Chiyanjo chake chili pa awo amene amasonyeza ‘kukonda abale kopanda chinyengo’ ndi kukhala ndi “chikhulupiriro chosanyenga.”—1 Petro 1:22; 1 Timoteo 1:5.
Ukoma Ndiwo Ubwino Wokangalika
17, 18. Pamene tikusonyeza chipatso cha mzimu cha ubwino, kodi tidzachita motani ndi ena?
17 Ngati tiwonjezera ukoma pachikhulupiriro chathu, tidzayesayesa kudziletsa kuganiza, kunena, ndi kuchita zinthu zimene zili zosavomerezedwa ndi Mulungu. Komabe, kusonyeza ukoma Wachikristu kumafunanso kuti tisonyeze ubwino mokangalika. Kwenikweni, ukoma wafotokozedwa kukhala ubwino. Ndipo ubwino ndiwo chipatso cha mzimu woyera wa Yehova, osati chipatso wamba cha kuyesayesa kwa munthu. (Agalatiya 5:22, 23) Pamene tikusonyeza chipatso cha mzimu cha ubwino chimenechi, tidzasonkhezeredwa kuganizira ena m’njira yabwino ndi kuwayamikira kaamba ka mikhalidwe yawo yabwino mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwawo. Kodi iwo atumikira Yehova mokhulupirika kwazaka zambiri? Pamenepo tiyenera kuwapatsa ulemu ndi kuyamikira zimene achita m’kutumikira kwawo Mulungu. Atate wathu wakumwamba amaona chikondi chimene amasonyeza chifukwa cha dzina lake ndi ntchito zawo zaukoma zochitidwa mokhulupirika, ndipo ndimo mmene nafenso tiyenera kuwaonera.—Nehemiya 13:31b; Ahebri 6:10.
18 Ukoma umatichititsa kukhala oleza mtima, omvetsetsa, omvera chisoni. Ngati wolambira Yehova mnzathu akuzunzika kapena apsinjika maganizo, tidzalankhula naye motonthoza ndi kufunafuna kumsangulutsa, monga momwedi Atate wathu wakumwamba amatitonthozera. (2 Akorinto 1:3, 4; 1 Atesalonika 5:14) Timamvera chisoni anthu amene agwidwa chisoni, mwinamwake chifukwa cha kutayikiridwa ndi wokondedwa muimfa. Ngati pali kalikonse kamene tingathe kuchita kuchepetsako mavuto awo, tidzakachita, pakuti mzimu waukoma umasonkhezera mchitidwe wachikondi ndi wokoma mtima.
19. Kodi ndimotani mmene ena adzachitira nafe ngati tili aukoma m’malingaliro, m’mawu, ndi m’zochita?
19 Monga momwe timadalitsira Yehova mwa kunena za ubwino wake, anthu enanso adzatidalitsa ngati tili aukoma mulingaliro, mawu, ndi machitidwe. (Salmo 145:10) Mwambi wanzeru umanena kuti: “Madalitso ali pamtu pa wolungama; koma m’kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.” (Miyambo 10:6) Munthu woipa ndi wachiwawa alibe ukoma umene ungamchititse kukondedwa ndi ena. Amatuta zimene amabzala, pakuti anthu sangampatse madalitso awo mowona mtima mwa kulankhula zabwino ponena za iye. (Agalatiya 6:7) Nkwabwino kwambiri chotani nanga kwa awo amene amaganiza, kulankhula, ndi kuchita m’njira zaukoma monga atumiki a Yehova! Amakondedwa, kudaliridwa ndi kulemekezedwa ndi ena, amene amasonkhezeredwa kuwadalitsa ndi kulankhula za ubwino wawo. Ndiponso, ubwino wawo waumulungu umachititsa madalitso osayerekezereka a Yehova.—Miyambo 10:22.
20. Kodi malingaliro, kalankhulidwe, ndi machitidwe a ukoma angakhale ndi chiyambukiro chotani pampingo wa anthu a Yehova?
20 Malingaliro, kalankhulidwe, ndi machitidwe aukoma adzapindulitsadi mpingo wa anthu a Yehova. Pamene olambira anzawo ali ndi malingaliro achikondi ndi akulemekezana, kukonda abale kumafalikira pakati pawo. (Yohane 13:34, 35) Kalankhulidwe kokoma, kuphatikizapo chiyamikiro chowona mtima ndi chilimbikitso, zimakulitsa mzimu wachikondi wa kumvana ndi umodzi. (Salmo 133:1-3) Ndipo machitidwe othutsa mtima, aukoma amasonkhezera ena kuchita mofanana. Koposa zonse, kusonyezedwa kwa ukoma Wachikristu kumabweretsa chiyanjo ndi madalitso zochokera kwa Atate wathu wakumwamba waukomayo, Yehova. Chotero tipangetu chonulirapo chathu kukhala cha kulabadira malonjezo amtengo wapatali a Mulungu mwa kusonyeza chikhulupiriro. Ndipo ndithudi tiyeni tiyesetse kuchitapo kathu kuwonjezera ukoma pachikhulupiriro chathu.
Kodi Mayankho Anu Ngotani?
◻ Kodi mungafotokoze motani liwulo “ukoma,” ndipo zili motani kuti anthu opanda ungwiro angathe kukhala aukoma?
◻ Kodi ukoma umafuna mtundu wotani wa malingaliro?
◻ Kodi ndimotani mmene ukoma uyenera kuyambukirira kalankhulidwe kathu?
◻ Kodi ukoma uyenera kuyambukira motani machitidwe athu?
◻ Kodi mapindu ena a kukhala waukoma ngotani?
[Chithunzi patsamba 21]
Popeza kuti madzi okoma ndi oŵaŵa sangatuluke pakasupe mmodzimodziyo, moyenerera ena amayembekezera kuti atumiki a Yehova anene zinthu zaukoma zokha