Kuŵeta Nkhosa Zamtengo Wake za Yehova Mokoma Mtima
AKULUWO anamvetsera mwatcheru. Iwo anali atayenda mtunda wa makilomita pafupifupi 50 kuchokera ku Efeso kupita ku Melito kukalandira malangizo kwa mtumwi Paulo. Tsopano iwo anachita chisoni kumva kuti imeneyi ikakhala nthaŵi yomalizira kumuwona. Chotero iwo anadziŵa kuti mawu amene akamva akakhala ofunika koposa: “Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo mzimu woyera [u]nakuikani oyang’anira, kuti muŵete [mpingo, NW] wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa [Mwana, NW] wa iye yekha.”—Machitidwe 20:25, 28, 38.
Kutchula za abusa kwa Paulo mwachiduleko kunaperekadi chidziŵitso chachikulu kwa akulu a ku Efeso amenewo. Iwo anali ozoloŵerana bwino ndi ntchito yoŵeta nkhosa m’midzi yozungulira. Iwo anadziŵanso za mawu ambiri onena za abusa m’Malemba Achihebri. Ndipo anadziŵa kuti Yehova anadziyerekezera mwini kukhala Mbusa wa anthu ake.—Yesaya 40:10, 11.
Paulo analankhula za iwo monga “oyang’anira” pakati pa “gulu,” ndiponso monga “abusa” a “mpingo.” Pamene kuli kwakuti liwu lakuti “oyang’anira” limasonyeza imene ili ntchito yawo, liwulo “mbusa” limafotokoza mmene ayenera kuchitira uyang’aniro umenewo. Inde, oyang’anira anayenera kusamalira chiŵalo chilichonse cha mpingo mumkhalidwe wachikondi umodzimodziwo umene mbusa angayang’anire nawo gulu lake la nkhosa.
Lerolino, ndiakulu oŵerengeka okha amene anaŵetapo nkhosa zenizeni. Koma Baibulo limatchula nthaŵi zambiri ponse paŵiri nkhosa ndi abusa, makamaka m’lingaliro lophiphiritsira, kotero kuti mawu a Paulo ali ndi tanthauzo lamphamvu mosasamala kanthu za nthaŵi yake. Ndipo tingaphunzire zambiri m’nkhani zonena za abusa amene Mulungu anayanja m’nthaŵi zakale. Zitsanzo zawo zabwino zingathandize akulu amakono kuwona mikhalidwe imene ayenera kukulitsa kotero kuti aŵete mpingo wa Mulungu.
Davide Mbusa Wopanda Mantha
Pamene tilingalira za abusa a m’nthaŵi za m’Baibulo, mosakayikira konse tidzakumbukira Davide, popeza kuti anayamba monga woŵeta nkhosa. Limodzi la maphunziro oyamba amene tingaphunzire m’moyo wa Davide nlakuti kukhala mbusa simalo apamwamba. Kwenikweni, pamene mneneri Samueli anafika kudzadzoza mwana wa Jese monga mfumu yamtsogolo ya Israyeli, poyamba Davide wachichepereyo ananyalanyazidwa kotheratu. Kunali kokha pambuyo pakuti Yehova wakana akulu ake asanu ndi aŵiri pamene Davide anatchulidwa, amene anali kumunda ‘kuŵeta nkhosa.’ (1 Samueli 16:10, 11) Komabe, zaka zimene Davide anathera monga mbusa zinamkonzekeretsa kaamba ka ntchito yovuta ya kuŵeta mtundu wa Israyeli. Lemba la Salmo 78:70, 71 limati: “[Yehova] anasankha Davide mtumiki wake, namtenga kumakola a nkhosa . . . aŵete Yakobo, anthu ake.” Moyenerera, Davide analemba Salmo lokongola ndi lodziŵika bwino kwambiri la 23, akumayamba ndi mawu akuti: “Yehova ndiye mbusa wanga.”
Mofanana ndi Davide, akulu mumpingo Wachikristu ayenera kutumikira monga abusa aang’ono odzichepetsa ndipo sayenera kufuna malo apamwamba mosayenera. Monga momwe mtumwi Paulo analembera kwa Timoteo, awo okalimira thayo laubusa limeneli ‘akufuna ntchito yabwino,’ osati kutchuka.—1 Timoteo 3:1.
Ngakhale kuti ntchito ya Davide monga mbusa weniweni inali yotsika, nthaŵi zina inafunikira kulimba mtima kwakukulu. Mwachitsanzo, pamene nkhosa ya m’gulu la atate wake panthaŵi ina inatengedwa ndi mkango ndipo panthaŵi ina ndi chimbalangondo, Davide mopanda mantha analimbana ndi zilombozo ndi kuzipha. (1 Samueli 17:34-36) Chimenechi chinali chisonyezero chapadera cha kulimba mtima pamene mulingalira kuti mkango ukhoza kupha nyama zazikulu kwambiri kuposa iwo. Ndipo chimbalangondo chofiirira cha ku Asuri chimene chinali kupezeka m’Palestina, cholemera pafupifupi makilogalamu 140, chikhoza kupha mbawala mwakuimenya kamodzi kokha ndi phazi lake lamphamvu.
Kulimba mtima chifukwa cha nkhosa za atate wake kwa Davide kuli chitsanzo chabwino kwa abusa mumpingo Wachikristu. Mtumwi Paulo anachenjeza akulu a ku Efeso za “mimbulu yosautsa” imene ‘sikalekerera gulu.’ (Machitidwe 20:29) M’nthaŵi zamakononso, padzabuka nthaŵi zimene abusa Achikristu akayenera kusonyeza kulimba mtima kotero kuti achinjirize ubwino wauzimu wa nkhosa za Yehova.
Pamene kuli kwakuti nkhosa ziyenera kutetezeredwa molimba mtima, ziyeneranso kuchitiridwa mwachifundo kwambiri, motsanzira mbusa wachikondiyo Davide ndi Mbusa Wabwino, Yesu Kristu. (Yohane 10:11) Podziŵa kuti gululo nla Yehova, akulu sayenera konse kukhala okakala kwa nkhosazo, ‘kuchita ufumu pagulu la Mulungu.’—1 Petro 5:2, 3; Mateyu 11:28-30; 20:25-27.
Kuŵerengera Mlandu
Kholo Yakobo anali mbusa wina wodziŵika bwino. Iye anadzilingalira kukhala ndi thayo kaamba ka nkhosa iliyonse yoikizidwa kwa iye kuti aisamalire. Iye anasamalira gulu la mpongozi wake Labani mokhulupirika, kotero kuti atatha zaka 20 muutumiki wake, Yakobo anakhoza kunena kuti: “Nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoŵeta zako sindinadye. Chimene chinazomoledwa ndi chirombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; pa dzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana.”—Genesis 31:38, 39.
Oyang’anira Achikristu amasamaliradi kwambiri nkhosa zimene Mbusa wa miyoyo yathu, Yehova Mulungu, “anaugula ndi mwazi wa Mwana wa iye yekha.” (Machitidwe 20:28; 1 Petro 2:25; 5:4) Paulo anagogomezera kufunika kwa thayoli pamene anakumbutsa Akristu Achihebri kuti amuna otsogolera mumpingo “alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera.”—Ahebri 13:17.
Chitsanzo cha Yakobo chimasonyezanso kuti ntchito ya ubusa ilibe malire a nthaŵi. Ndintchito yatsiku lonse ndipo kaŵirikaŵiri imafunikira kudzimana. Iye anauza Labani kuti: “Chotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku chisanu; tulo tanga tinachoka m’maso mwanga.”—Genesis 31:40.
Zimenezi nzowonadi kwa akulu ambiri achikondi Achikristu lerolino, monga momwe chokumana nacho chotsatirachi chikusonyezera. Mbale anagonekedwa m’chipinda cha odwala mwakayakaya m’chipatala pambuyo pakuti opaleshoni yofufuza chotupa muubongo inayambitsa zovuta zina. Banja lake linapanga makonzedwe akukhala naye pafupi m’chipatalamo usana ndi usiku. Kuti apereke chichilikizo ndi chilimbikitso chofunikira, mkulu wina wampingo anasintha ndandanda yake yotanganitsidwa kotero kuti adzikaona munthu wodwalayo ndi banja lake tsiku lililonse. Komabe, chifukwa cha ndandanda yoperekera mankhwala yosapatsa mpata ya chipatalacho, nthaŵi zonse sikunali kotheka kuti apite kukamuona masana. Zimenezi zinatanthauza kuti kaŵirikaŵiri mkuluyo anayenera kupita kuchipatalako usiku kwambiri. Koma anapitako mosangalala usiku uliwonse. “Ndinazindikira kuti ndinayenera kuona wodwalayo panthaŵi imene inali yomuyenera, osati nthaŵi yoyenera kwa ine,” anatero mkuluyo. Pamene mbaleyo anachira moyenera kusamutsidwira kumalo ena a chipatalacho, mkuluyo anapitirizabe maulendo ake a tsiku ndi tsiku olimbikitsa.
Zimene Mose Anaphunzira Monga Mbusa
Baibulo limafotokoza Mose kukhala “wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi.” (Numeri 12:3) Komabe, cholembedwacho chimasonyeza kuti nthaŵi zonse sizinali zotero. Pamene anali mnyamata, iye anapha Mwaigupto amene anapha Mwiisrayeli. (Eksodo 2:11, 12) Kameneka sikanali konse kachitidwe ka munthu wofatsa! Komabe, pambuyo pake Mulungu anagwiritsira ntchito Mose kutsogolera mtundu wa anthu mamiliyoni ambiri kupyola chipululu kumka ku Dziko Lolonjezedwa. Pamenepo mwachiwonekere, Mose anafunikira kuphunzitsidwa kowonjezereka.
Pamene kuli kwakuti Mose anali atalandira kale maphunziro akudziko mu “nzeru zonse za Aaigupto,” iye anafunikira zowonjezereka kuti aŵete gulu la Yehova. (Machitidwe 7:22) Kodi maphunziro owonjezereka ameneŵa anafunikira kukhala amtundu wanji? Eya, kwa zaka 40 Mulungu analola Mose kutumikira monga mbusa wamba m’dziko la Midyani. Pamene anali kuŵeta nkhosa za apongozi ake a Yetero, Mose anakulitsa mikhalidwe yabwino ya kuleza mtima, chifatso, kudzichepetsa, kupirira, kusakwiya msanga, ndi kudziletsa. Iye anaphunziranso kudikira pa Yehova. Inde, kuŵeta nkhosa zenizeni kunayeneretsa Mose kukhala mbusa waluso wa mtundu wa Israyeli.—Eksodo 2:15–3:1; Machitidwe 7:29, 30.
Kodi imeneyi sindiyo mikhalidwe yeniyeni imene mkulu afunikira kuti asamalire anthu a Mulungu lerolino? Inde, popeza kuti Paulo anakumbutsa Timoteo kuti “kapolo wa Ambuye . . . akhale woyenera, waulere pa onse, wodziŵa kuphunzitsa, woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa.”—2 Timoteo 2:24, 25.
Pangakhale nthaŵi zina pamene mkulu amadzimva kukhala wogwiritsidwa mwala chifukwa chakuti ali ndi vuto kukulitsa mikhalidwe imeneyi mokwanira. Komabe, iye sayenera kuleka. Monga momwe zinaliri ndi Mose, kungatenge nthaŵi yaitali kukulitsa mokwanira mikhalidwe yofunikira kuti munthu akhale mbusa wabwino. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, kuyesayesa kwakhama kumeneko kudzafupidwa.—Yerekezerani ndi 1 Petro 5:10.
Monga mkulu, mwinamwake simukugwiritsiridwa ntchito mokwanira monga ena. Kodi kungakhale kwakuti, mofanana ndi Mose, Yehova akukulolani kukulitsa mikhalidwe ina yofunika mokwanira kwambiri? Musaiŵale konse kuti Yehova ‘amakusamalirani.’ Komabe, tiyeneranso kukumbukira kufunika kwa ‘kuvala kudzichepetsa kuti titumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.’ (1 Petro 5:5-7) Ngati mudzipereka inu eni ndi kulandira maphunziro onse amene Yehova akukupatsani, adzakugwiritsirani ntchito kwambiri, monga momwe analiri Mose.
Nkhosa Zonse za Yehova Nzamtengo Wake
Akulu odalirika, achikondi a m’nthaŵi za m’Baibulo anali kudzimva kukhala athayo kulinga kwa nkhosa iliyonse payokha. Ndimmenenso abusa auzimu ayenera kukhalira. Zimenezi zimamvekera bwino m’mawu a Paulo akuti: “Tadzichenjerani . . . ndi gulu lonse.” (Machitidwe 20:28) Kodi ndani amene angaphatikizidwe mu “gulu lonse”?
Yesu anapereka fanizo la munthu amene anali ndi nkhosa zana limodzi koma anafunafuna mwamsanga imodzi imene inasochera kuti aibwezere kugululo. (Mateyu 18:12-14; Luka 15:3-7) Mofananamo woyang’anira ayenera kuda nkhaŵa ndi chiŵalo chilichonse cha mpingo. Kusakangalika muutumiki kapena kufika pamisonkhano Yachikristu sikumatanthauza kuti nkhosayo siilinso mbali ya gulu. Iye amakhalabe mbali ya “gulu lonse” limene akulu ayenera “kuŵerengera” kwa Yehova.
Bungwe lina la akulu linada nkhaŵa kwambiri kuti ena amene anali kusonkhana ndi mpingo analeka kukhala okangalika. Anapanga ndandanda ya anthu ameneŵa, ndipo anapanga kuyesayesa kwapadera kuwachezera ndi kuwathandiza kubwerera m’khola la Yehova. Akuluwa anayamikira kwambiri Mulungu kuti panyengo ya zaka ziŵiri ndi theka, anali okhoza kuthandiza anthu oposa 30 kukhala okangalika kachiŵirinso muutumiki wa Yehova. Mmodzi wa anthu amene anathandizidwawo anali wosakangalika kwa pafupifupi zaka 17!
Kuwopsa kwa thayo limeneli kukugogomezeredwa mowonjezereka kwa oyang’anira ndi chenicheni chakuti nkhosazo ‘zinagulidwa ndi mwazi wa Mwana wa [Mulungu].’ (Machitidwe 20:28) Palibe mtengo wapamwamba woposa umenewu umene ukanaperekedwa kaamba ka nkhosa zamtengo wake zimenezi. Ndipo talingalirani za nthaŵi yonse ndi kuyesayesa kumene kumatheredwa muutumiki kufunafuna ndi kuthandiza munthu wonga nkhosa aliyense! Kodi kuyesayesa kofananako sikuyenera kupangidwa kuti onse a iwo akhalebe m’khola la Mulungu? Ndithudi, nkhosa iliyonse mumpingo njamtengo wake.
Ngakhale pamene chiŵalo cha gululo chichita tchimo lalikulu, thayo la akulu silimasintha. Iwo amapitirizabe kukhala abusa osamalira, akumayesayesa mokoma mtima ndi mofatsa kupulumutsa wolakwayo ngati kuli kotheka. (Agalatiya 6:1, 2) Momvetsa chisoni, nthaŵi zina kumakhala kowonekeratu kuti chiŵalo cha mpingo cholakwa sichimamva chisoni chaumulungu kaamba ka machimo aakulu amene chawachita. Pamenepo abusa achikondi amakhala ndi thayo la m’Malemba la kutetezera gulu lonse ku chisonkhezero choipitsa chimenechi.—1 Akorinto 5:3-7, 11-13.
Ngakhale zikhale choncho, Yehova Mulungu amakhazikitsa chitsanzo chabwino koposa cha kusonyeza chifundo kwa nkhosa yosochera. Mbusa wathu wachifundo amati: “Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopitikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndi kulimbitsa yodwalayo.” (Ezekieli 34:15, 16; Yeremiya 31:10) Potsanzira chitsanzo chapamwamba koposa chimenechi, kakonzedwe kachikondi kapangidwa tsopano kakuti abusa auzimu amakono adziona anthu ochotsedwa, amene angalandire chithandizo chawo. Kuyesayesa kwachifundo kumeneku kwakulanditsa nkhosa zotayika zimenezo kwatulutsa zipatso zabwino. Mlongo wina amene anabwezeretsedwa anati: “Pamene akuluwo anafika, chinali chilimbikitso chomwe ndinafunikira kuti ndibwerere.”
Mosakayikira mawu a Paulo kwa akulu a ku Efeso pa Melito anali ndi tanthauzo—kwa iwo ndi kwa oyang’anira lerolino. Kutchula kwake abusa kunali chikumbutso cha mikhalidwe yokondweretsa imene iyenera kukhala yowonekera mwa oyang’anira—mikhalidwe yonga ngati kudzichepetsa ndi kulimba mtima, monga kumene kunasonyezedwa ndi mfumu yaubusayo Davide; kudzimva kukhala wathayo ndi chisamaliro chotetezera, zowonekera muutumiki wa usana ndi usiku wa Yakobo; ndi kufunitsitsa kulandira maphunziro owonjezereka moleza mtima, monga kunasonyezedwa ndi Mose. Ndithudi, zitsanzo za m’Baibulo zimenezi zidzathandiza akulu ampingo kukulitsa ndi kusonyeza mikhalidwe yofunikira kotero kuti akhoze ‘kuŵeta [mokoma mtima] mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Mwana wake.’