Kodi Nkukonderanji Mnansi Wanu?
MOYO wosatha umadalira pakukonda kwathu Mulungu ndi mnansi. Mfundoyi inatchulidwa pakukambitsirana kumene kunachitika pafupifupi zaka 2,000 zapitazo.
Mwamuna Wachiyuda wodziŵa bwino Chilamulo cha Mose anafunsa Yesu Kristu kuti: “Ndidzaloŵa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?” Yesu anayankha kuti: “M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uŵerenga bwanji?” Pogwira mawu a Chilamulocho, mwamunayo anati: “Uzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.” “Wayankha bwino,” Yesu anatero. “Chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.”—Luka 10:25-28.
Pakumva zimenezo, wofunsa Yesuyo anafunsa kuti: “Ndipo mnansi wanga ndani?” Mmalo moyankha mwachindunji, Yesu anasimba fanizo la mwamuna Wachiyuda amene anaberedwa, kumenyedwa, ndi kusiyidwa kuti afe. Panjirapo panadzera Ayuda aŵiri—woyamba anali wansembe ndiyeno Mlevi. Onse aŵiri anaona mkhalidwe wa Myuda mnzawo koma sanachite kalikonse kumthandiza. Ndiyeno Msamariya anadzerapo. Pogwidwa ndi chifundo, anamanga mabala a Myuda wovulalayo, namtengera kunyumba ya alendo, napanga makonzedwe akulipirira chithandizo chake chowonjezereka.
Yesu anafunsa amene anamfunsayo kuti: “Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m’manja a achifwamba?” Mwachionekere, anali Msamariya wachifundoyo. Motero Yesu anasonyeza kuti chikondi chowona cha mnansi chilibe kanthu ndi fuko la munthu.—Luka 10:29-37.
Kusoŵeka kwa Chikondi cha pa Mnansi
Lerolino pali udani womakulakula pakati pa anthu a mafuko osiyana. Mwachitsanzo, ochilikiza Chinazi amakono ku Germany posachedwapa anagwetsera mwamuna wina pansi nampondereza ndi nsapato zawo zolemera, akumathyola pafupifupi nthiti zake zonse. Ndiyeno anamthira zakumwa zokhala ndi mankhwala oyaka ochuluka namtentha. Mwamuna yemwe anasiyidwa kuti afe ameneyo anaukiridwa chifukwa chakuti analingaliridwa kukhala Myuda. M’chochitika china chosiyana, nyumba ina pafupi ndi Hamburg inatenthedwa ndi bomba, ikumanyeketsa anthu atatu a ku Turkey kufikira imfa—mmodzi wa iwo anali msungwana wa zaka khumi zakubadwa.
Kumaiko a m’dera la Balkan ndi kummaŵa kwenikweni, nkhondo za ufuko zinali kupha miyoyo zikwi zambiri. Ena anafera m’kulimbana kwa anthu a ziyambi zosiyana ku Bangladesh, India, ndi Pakistan. Ndipo mu Afirika, kulimbana kwa pakati pa mitundu ndi mafuko kunapha miyoyo ina yambiri.
Anthu ochuluka amaipidwa ndi chiwawa chotero ndipo sangachite kanthu kalikonse kuvulaza anansi awo. Kunena zowona, zionetsero zotsutsa zazikulu zochitidwa ku Germany zinatsutsa chiwawa cha ufuko kumeneko. Komabe, The New Encyclopædia Britannica ikuti: “Ziŵalo za pafupifupi zitaganya zonse za dziko zimaona njira yawo ya moyo kukhala yoposa ngakhale ija ya anansi awo apafupi kwambiri.” Malingaliro otero amadodometsa chikondi cha pa mnansi. Kodi pali chilichonse chimene chingachitidwe pankhaniyi, makamaka popeza Yesu anati moyo umadalira pakukonda Mulungu ndi mnansi?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Pachikuto: Jules Pelcog/Die Heilige Schrift
[Mawu a Chithunzi patsamba 3
Msamariya Wachifundo/The Doré Bible Illustrations/Dover Publications, Inc.