Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 9/15 tsamba 7-8
  • Papias Anaona Mawu a Ambuye Kukhala Amtengo Wapatali

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Papias Anaona Mawu a Ambuye Kukhala Amtengo Wapatali
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira Yosamalitsa
  • Zimene Analemba
  • Ndemanga Zake pa Mauthenga Abwino
  • Wozindikira Kusoŵa Kwake Kwauzimu
  • Uthenga wa M’chivumbulutso—Kodi ndi Woopsa Kapena ndi Wotipatsa Chiyembekezo?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Ziphunzitso za Abambo a Atumwi Zimagwirizana ndi za Atumwi a Yesu?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • ‘Kutsutsa—Chotchedwa Chidziŵitso Konama’
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Gawo 2—Kodi Abambo Autumwi anaphunzitsa chiphunzitso cha Utatu?
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 9/15 tsamba 7-8

Papias Anaona Mawu a Ambuye Kukhala Amtengo Wapatali

“SINDINAKONDE kuyanjana ndi anthu amene ali nzonena zochuluka, koma awo amene anaphunzitsa chowonadi.” Analemba motero Papias, wodzinenera kukhala Mkristu wa m’zaka za zana lachiŵiri la Nyengo Ino.

Papias anakhalako m’nyengo yomwe inatsatira imfa ya atumwi a Yesu Kristu. Kwenikweni, iye anali bwenzi la Polycarp, amene zinamveka kuti anaphunzitsidwa ndi mtumwi Yohane. Maumboni ameneŵa, limodzi ndi njira ya Papias yopezera chidziŵitso, zimasonyeza kuti mwachionekere anali munthu wachidziŵitso.

Njira Yosamalitsa

Ludzu la chowonadi la Papias likuonekera bwino m’mabuku asanu opanga zolembedwa zake zonena za mawu a Ambuye. M’zaka zake zoyambirira, Papias mosakayikira anakumbukira mawu ambiri a chowonadi amene anamva. Pambuyo pake, ali kwawo kumzinda wa ku Frugiya wa Herapoli, m’Asia Minor, Papias anafunsa achikulire kuti adziŵe ngati iwo anaonapo kapena kumvapo za atumwi a Yesu. Anawafunsa mwakhama nalemba zimene ananena.

Papias akufotokoza kuti: “Sindidzazengereza kulemba . . . zilizonse zimene ndinaphunzira mosamalitsa panthaŵi iliyonse kwa akulu, ndi kuzikumbukira bwino, kukutsimikizirani za chowonadi chawo. Popeza, mosiyana ndi anthu ochuluka, sindinakonde kuyanjana ndi anthu amene ali nzonena zochuluka, koma awo amene anaphunzitsa chowonadi; ndiponso sindinakonde amene anasimba malamulo a ena, koma awo amene anasimba malamulo operekedwa ndi Ambuye pachikhulupiriro ndi ochokera m’chowonadi chenichenicho. Ndipo ngati aliyense amene anali wotsatira akulu adza kwa ine, ndidzapempha zimene akulu anasimba​—zimene Andreya kapena zimene Petro ananena, kapena zimene Filipo kapena Tomasi kapena Yakobo, kapena zimene Yohane kapena Mateyu ananena, kapena wophunzira aliyense wa Ambuye.”

Zimene Analemba

Mosakayikira Papias anali ndi nkhokwe ya chidziŵitso chauzimu. Tingangoyerekezera mmene anamvetserera mosamalitsa maumboni onena za moyo ndi utumiki wa aliyense wa atumwiwo. Pafupifupi 135 C.E., Papias analemba buku lake la zimene anafuna kusimba. Mwachisoni, buku limeneli linasoŵa. Mawu ake anagwidwa ndi Irenaeus, wodzinenera kukhala Mkristu wa m’zaka za zana lachiŵiri C.E., ndi wolemba mbiri wa m’zaka za zana lachinayi Eusebius. Kwenikweni, linali kuŵerengedwabe m’zaka za zana la 9 C.E. ndipo mwina linaliko kufikira m’zaka za zana la 14 C.E.

Papias anakhulupirira Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu ulinkudza. (Chivumbulutso 20:2-7) Malinga nkunena kwa Irenaeus, iye analemba za nthaŵi “pamene chilengedwe, chokonzedwanso ndi chomasuka, chidzabala mitundu yonse ya chakudya chochuluka, kuchokera kumame a kumwamba ndi chonde cha padziko lapansi, monga momwe akulu, amene anaona Yohane, wophunzira wa Ambuye, ananenera kuti anamva mmene Ambuye ankaphunzitsira za nthaŵi zimenezo.” Papias anaonjezera kulemba kuti: “Kwa okhulupirira zinthu zimenezi nzokhulupirika. Ndipo pamene Yudasi, woperekayo, anakana kukhulupirira nafunsa kuti, ‘Kodi chinthu chotero chidzachitidwa motani ndi Ambuye?’ Ambuye anati, ‘Awo amene adzakhalako panthaŵiyo adzaona.’”

Papias analemba zimenezi panthaŵi imene Kukayikira Kukhalapo kwa Mulungu kunali kofala. Okayikira Kukhalapo kwa Mulungu anagwirizanitsa nthanthi, zopeka, ndi zinsinsi zachikunja ndi Chikristu champatuko. Kwenikweni, kufotokoza kwa Papias maneno, kapena mawu a Ambuye, kunali kuyesayesa kuletsa kufalikira kwa funde la Kukayikira Kukhalapo kwa Mulungu. Iye atafa, Irenaeus anapitiriza kutsutsa mkhalidwe wa uzimu wonama ndi wongoyerekezera wa Okayikira Kukhalapo kwa Mulungu. Mabuku a Okayikira Kukhalapo kwa Mulungu ayenera kukhala anali ochuluka kwambiri, akumachititsa Papias kutchula monyodola “anthu amene ali nzonena zochuluka.” Cholinga chake chinali choonekera bwino​—kutsutsa chinyengo mogwiritsira ntchito chowonadi.​—1 Timoteo 6:4; Afilipi 4:5.

Ndemanga Zake pa Mauthenga Abwino

M’zidutswa za zolembedwa za Papias zimene zilipobe, timapeza mawu onena za nkhani zolembedwa ndi Mateyu ndi Marko. Mwachitsanzo, Papias akunena motero pacholembedwa cha Marko: “Marko, pokhala womasulira wa Petro, analemba molondola zonse zimene anakumbukira.” Akupereka umboni woonjezereka wa kulondola kwa Uthenga Wabwino umenewu, Papias akupitiriza kuti: “Chotero Marko sanaphonye konse, pamene kuli kwakuti analemba zinthu zina monga momwe anazikumbukirira; pakuti nkhaŵa yake yaikulu inali yakusasiya kalikonse kamene anamva, kapena kulembamo mawu alionse onama.”

Papias amapereka umboni wapadera wakuti poyamba Mateyu analemba Uthenga wake Wabwino m’chinenero cha Chihebri. Papias akuti: “Analemba mawuwo m’chinenero cha Chihebri, ndipo aliyense anawamasulira bwino koposa malinga ndi kukhoza kwake.” Nkwachionekere kuti Papias anali kunena za zolembedwa za Uthenga Wabwino za Luka ndi Yohane, limodzinso ndi zolembedwa zina za m’Malemba Achikristu Achigiriki. Ngati anaterodi, angakhale mmodzi wa mboni zoyambirira kutsimikiza kudalirika ndi kuuziridwa kwawo kwaumulungu. Komabe, mwatsoka, zidutswa zoŵerengeka za zolembedwa za Papias ndizo zokha zimene zilipo.

Wozindikira Kusoŵa Kwake Kwauzimu

Pokhala woyang’anira mumpingo wa ku Herapoli, Papias anali wofufuza wosatopa. Kuwonjezera pakukhala wofufuza wakhama, iye anasonyeza chiyamikiro chachikulu cha Malemba. Papias ananena molondola kuti mawu alionse achiphunzitso cha Yesu Kristu kapena atumwi Ake akakhala ofunika kwambiri kuwafotokoza koposa mawu osadalirika opezeka m’mabuku a m’nthaŵi yake.​—Yuda 17.

Kwasimbidwa kuti Papias anaphedwera chikhulupiriro ku Pergamo mu 161 kapena 165 C.E. Ukulu umene ziphunzitso za Yesu Kristu zinayambukirira moyo ndi khalidwe la Papias sunganenedwe motsimikiza. Komabe, iye anali ndi chikhumbo chachikulu cha kuphunzira ndi kukambitsirana Malemba. Ndimmenenso amachitira Akristu owona lerolino, pakuti amazindikira kusoŵa kwawo kwauzimu. (Mateyu 5:3) Ndipo mofanana ndi Papias amaona mawu a Ambuye kukhala amtengo wapatali.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena