Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 10/15 tsamba 3-4
  • Kodi Nchifukwa Ninji Kuba Kukuwonjezerekabe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Kuba Kukuwonjezerekabe?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Anthu Amaberanji?
  • Usabe
  • Kuba—Kulekeranji?
    Galamukani!—1995
  • Kodi Kuba kwa wosauka Nkololeka?
    Galamukani!—1997
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amaba M’masitolo?
    Galamukani!—2005
  • Usakhale Wakuba!
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 10/15 tsamba 3-4

Kodi Nchifukwa Ninji Kuba Kukuwonjezerekabe?

RIO DE JANEIRO​—Sande, October 18, 1992. Magombe otchuka a Copacabana ndi Ipanema ali odzaza ndi anthu. Mwadzidzidzi, magulu a achichepere akuloŵerera magombewo, akumamenyana ndi kuba chinthu chilichonse chamtengo kwa anthu amene ali pagombepo. Apolisi amene ali ochepa m’chiŵerengero angoima chilili​—kusoŵa chochita. Kwa nzika za Rio de Janeiro ndi alendo odzacheza, chochitikacho chili ngati loto lamasana.

Ndithudi, upandu wakuba katundu wakhala wofala. M’mizinda yaikulu, mbala zakhala zikubera achichepere​—ndipo nthaŵi zina ngakhale kuwapha​—kuti zitengeko nsapato zawo za sneaker. Mbala zimaloŵa m’nyumba za anthu kaya anthu akhalepo kapena ayi. Ogwira ntchito za m’nyumba osawona mtima, atadziŵa pamene zinthu zimakhala, amaba ndalama ndi zinthu zina zamtengo wake, ndiyeno nkuthaŵa. Magulu achiwawa amaphwanya ndi kuba m’masitolo. Magulu olinganizidwa bwino amaba ngakhale anthu, monga momwe zikuonekera m’chiŵerengero chomakulakula cha anthu obedwa m’Brazil. Ndipo mwachionekere mukhoza kupereka zitsanzo zina kuchokera m’zokumana nazo zanu kapena kuchokera m’zimene zinachitika m’dera limene mumakhala. Koma kodi nchifukwa ninji kuba kwakhala kowanda motero?

Kodi Anthu Amaberanji?

Ngakhale kuti umphawi womawonjezereka ndi kugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa ndiko zifukwa zazikulu ziŵiri, yankho lake silikudziŵika bwino. The New Encyclopædia Britannica imanena kuti: “Kufufuza kofuna kupeza chifukwa chimodzi chokha chochititsa upandu kwalekedwa chifukwa kwapezedwa kukhala kosaphula kanthu.” Komabe, buku limodzimodzilo limapereka lingaliro lakuti mavuto oterowo onga kuba “amagwirizanitsidwa mwachindunji ndi malingaliro a achichepere akudzimva kukhala opanda pake ndi oipidwa pokhala osakhoza kupeza zipambano zakuthupi ndi mapindu a moyo wozoloŵereka.” Inde, chifukwa cha chitsenderezo chachikulu cha mzimu wa kugula zinthu, ambiri samaona njira iliyonse yopezera zinthu zimene amakhumba kusiyapo kuba.

Komabe, mokondweretsa, The World Book Encyclopedia imanena kuti: “Mlingo wa upandu sumakwera mofulumira m’zitaganya zakumidzi kumene anthu amakhulupirira kuti njira yawo ya moyo idzapitirizabe. Mlingo wa upandu ukuoneka kukhala ukukwera m’zitaganya kumene kuli masinthidwe ofulumira m’malo okhalamo anthu ndi zimene anthuwo amachita kuchilikiza moyo​—ndiponso m’ziyembekezo zawo za moyo wamtsogolo.” Insaikulopediyayo ikupitiriza kuti: “Achichepere ali ndi mwaŵi wochepa wakupeza ntchito. Ntchito wamba zimene zilipo zimaoneka kukhala zosasangalatsa poziyerekezera ndi mapindu okopa opezedwa mofulumira mwa kuba. Achichepere amakhalanso ofunitsitsa kwambiri kukhala paupandu wakumangidwa chifukwa chakuti moyo wawo weniweniwo siwopindulitsa kwenikweni.”

Komabe, ambiri amene sakugwira ntchito kapena amene akugwira ntchito za malipiro ochepa samaba, pamene kuli kwakuti ambiri ogwira ntchito zovala thayi ndi zovala ovolosi amaba pantchito monga ngati kuti zobedwazo zinali mbali ya malipiro awo. Kwenikweni, machitachita ena aukatangale amafunikira kukhala pamalo apamwamba m’chitaganya. Kodi simunamvepo za milandu ya kubedwa kwa ndalama zochuluka kwambiri imene oloŵetsedwamo anali andale zadziko, antchito za boma, ndi abizinesi? Mosakayikira konse, kuba sikuli kwa osauka okha.

Kumbukiraninso kuti, mafilimu ndi maprogramu a pa TV kaŵirikaŵiri amasonyeza kuba kukhala chinthu chosangalatsa (ngwazi ndiyo ingakhale mbala), zimene zimachititsa kuba kukhala kovomerezeka. Nzowona, kupenyerera zinthu zotero kungatchedwe kukhala chosangulutsa, koma panthaŵi imodzimodziyo, openyererawo amasonyezedwa mmene angabere. Kodi sikumakhala kupereka lingaliro mwamachenjera lakuti upandu nthaŵi zina umapindulitsa? Ndithudi, kusirira, ulesi, ndi lingaliro lakuti aliyense amachita zimenezo ndi kusalangidwa zonsezo zimawonjezera mzimu wa kuba. Zowonadi, tikukhala mu “masiku otsiriza” onenedweratu pamene dyera ndi chikondi cha ndalama zakhala zowanda.​—2 Timoteo 3:1-5.

Usabe

Mosasamala kanthu za mikhalidwe yoluluzika ya dziko, nkofunika kwambiri kulabadira lamulo lakuti: “Wakubayo asabenso.” (Aefeso 4:28) Munthu amene amaona chuma kapena zosangulutsa kukhala zofunika mopambanitsa angakhale akudzinyenga m’kukhulupirira kuti kuba kuli bwino mosasamala kanthu za upandu wake. Koma kuba ndimlandu wowopsa pamaso pa Mulungu ndipo kumasonyeza kupanda chikondi kwa munthu mnzanu. Ndiponso, ngakhale kuba kwakung’ono kungakhwimitse mtima wa munthu. Ndipo bwanji za kuonedwa kukhala wosawona mtima? Kodi ndani amene angakhulupirire mbala? Mwanzeru, Mawu a Mulungu amati: “Asamve zoŵaŵa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa.”​—1 Petro 4:15.

Ndithudi, inu mumaipidwa ndi kuwonjezereka kwa kuba, koma kodi anthu okhala m’madera mmene upandu uli wowanda akuchita motani? Kodi ndimotani mmene anthu ena amene kale anali mbala asinthira miyoyo yawo? Kodi kuba kudzatha konse padziko lonse? Tikupemphani kuŵerenga nkhani yotsatirayi yakuti, “Dziko Lopanda Mbala.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena