Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 10/15 tsamba 8-11
  • Vuto Lakuphunzira Kuyembekezera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Vuto Lakuphunzira Kuyembekezera
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nzeru ya Kuphunzira Kuyembekezera
  • Chitokoso Chatsopano kwa Ambiri
  • Kuphunzira kwa Ena
  • Kumenya Nkhondo Yabwino
  • Kuphunzira Kuyembekezera m’Mbali Zonse
  • Gawo 6: Kukhupuka ndi Kugwa kwa Dongosolo Lamalonda
    Galamukani!—1992
  • Kodi Mukhoza Kuyembekezera Moleza Mtima?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Kodi Mayiko Angathe Kuyendetsa Chuma Mokomera Aliyense?
    Nkhani Zina
  • Nchifukwa Ninji Pali Vuto la Mtengo wa Kakhalidwe?
    Galamukani!—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 10/15 tsamba 8-11

Vuto Lakuphunzira Kuyembekezera

KUPHUNZIRA kuyembekezera zinthu zimene timafuna mwinamwake ndiko chinthu chovuta kwambiri chimene anthufe timafunikira kuvomereza. Ana aang’ono mwachibadwa ngosapirira. Chinthu chilichonse chimene chimawakopa, amachifuna, ndipo amachifuna nthaŵi yomweyo! Koma monga momwe mudziŵira, chowonadi nchakuti kanthu kalikonse kamene timafuna sikamapezeka pamene tikafuna. Ngakhale pankhani ya zikhumbo zoyenera, tiyenera kuphunzira kuyembekezera kaamba ka nthaŵi yoyenera kuti tizikhutiritse. Anthu ambiri amaphunzira zimenezi; koma ena samatero.

Anthu amene amafuna kupeza chivomerezo cha Mulungu ali ndi zifukwa zapadera zophunzirira kuyembekezera. Yeremiya, mtumiki wa Yehova amene anakhalako Chikristu chisanadze, anagogomezera zimenezi kuti: “Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.” Pambuyo pake, wophunzira Wachikristu Yakobo anati: “Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye.”​—Maliro 3:26; Yakobo 5:7.

Yehova ali ndi nthaŵi yake yochitira zifuno zaumulungu. Ngati tili osakhoza kuyembekezera kufikira nthaŵi yake yokwanira ya kuchita zinthu zina, tidzakhala osakhutiritsidwa, kumene kudzathetsa chimwemwe. Popanda chimwemwe mtumiki wa Mulungu adzakhala wofooka mwauzimu, monga momwe Nehemiya anauzira anthu akwawo kuti: “Chimwemwe mwa AMBUYE ndicho nyonga yanu.”​—Nehemiya 8:10, The New English Bible.

Nzeru ya Kuphunzira Kuyembekezera

Nkwachibadwa kwa mbeta kukhumba kuloŵa muukwati kapena kwa okwatirana opanda ana kufuna kubala ana. Ndiponso, palibe cholakwika m’kukhumbira zosoŵa zoyenera zakuthupi. Komabe, chifukwa cha kukhulupirira kuti masiku a dongosolo lino la zinthu atsala pang’ono kutha ndi kuti m’dongosolo latsopano limene likudzalo Mulungu ‘adzaolowetsa dzanja lake ndi kukwaniritsa chokhumba cha za moyo zonse,’ Akristu ambiri asankha kuyembekezera kuti adzakwaniritse zina za zikhumbo zimenezi panthaŵi yoyenera kwambiri.​—Salmo 145:16.

Komabe, anthu opanda chiyembekezo chozikika bwino Chachikristu chimenechi sangaone mokwanira chifukwa chake ayenera kuyembekezera. Posoŵa chikhulupiriro mwa Yehova, kwa amene “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro” zimachokerako, amakayikira nzeru ya kuyembekezera zinthu zimene akukayikira kuti zidzachitika. Ali ndi lingaliro lakuti: “Tidye timwe pakuti maŵa timwalira.”​—Yakobo 1:17; 1 Akorinto 15:32; Yesaya 22:13.

M’maiko otukuka anthu osatsa malonda amagwiritsira ntchito mpata umenewu wachionekere wa chikhoterero cha kudzikhutiritsa kwanthaŵi yomweyo. Anthu amalimbikitsidwa kudzikhutiritsa iwo eni. Anthu amalonda angakonde kuti tikhulupirire kuti ziwiya zamakono nzofunika kotheratu. Nkulekeranji kukhala nazo, iwo amasonkhezera motero, makamaka pamene makadi ogulira zinthu pangongole, dongosolo la kulipirira zinthu mwapang’onopang’ono, ndi njira za “kugula tsopano lino​—ndi kulipira pambuyo pake” zimachititsa kukhala kothekera kupeza zonse tsopano lino? Ndiponso, ‘Mumayenerera zabwino koposa; dzikomereni mtima! Sankhani, kaya kusangalala tsopano lino kapena osadzasangalala konse!’ Mawu osatsa malonda ofala amatero.

Izi zidakali choncho, anthu mamiliyoni makumi ambiri m’maiko osatukuka ali ndi zinthu zokwanira kukhala ndi moyo zokha​—kapena zopereŵera. Kodi pali kanthu kena koposa zimenezi kamene kangagogomezere mwamphamvu za kupanda ungwiro ndi chisalungamo za ndale za munthu ndi madongosolo ake azachuma?

Nzeru ya kuphunzira kuyembekezera imaonedwa nchakuti mamiliyoni a anthu amene safuna kuchita motero​—kapena amene samaona kwenikweni chifukwa chochitira motero​—aloŵa m’ngongole zazikulu kwambiri kuti akhutiritse zikhumbo zawo zapanthaŵiyo. Mikhalidwe yosaonedweratu, monga ngati kudwala kapena kutha kwa ntchito, ingatanthauze tsoka. Nyuzipepala ina ya ku Germany yotchedwa Frankfurter Allgemeine Zeitung inafotokoza chifukwa chake anthu miliyoni imodzi a ku Germany akusimbidwa kukhala osoŵa nyumba: “Kwenikweni, kaŵirikaŵiri kusoŵa nyumba kumachitika pambuyo pa kutha kwa ntchito kapena kuloŵa m’ngongole zambiri.”

Polephera kulipira ngongole zawozo, anthu ambiri ogweredwa tsokawo amatayikiridwa ndi nyumba ndi chuma chomwe. Kaŵirikaŵiri, kupsinjika maganizo kowonjezereka kumadzetsa mavuto m’banja. Maukwati ogwedera amayamba kusweka. Nyengo za kupsinjika maganizo ndi mavuto ena athanzi zimakhala zofala. Kwa Akristu, mkhalidwe wawo wauzimu umakhala pamavuto, ukumachititsa kuyamba kulingalira molakwa ndi mayendedwe osayenera. Anthu amene poyamba ankafuna kukhala ndi zinthu zonse mopanda nzeru potsirizira pake amakhala opanda pafupifupi kanthu kalikonse.

Chitokoso Chatsopano kwa Ambiri

Yesu anafotokoza bwino kwambiri kuti tiyenera kusamala ndi “malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, [zoloŵamo, zimene] zitsamwitsa mawu.” (Marko 4:19) Tiyenera kukumbukira kuti palibe dongosolo la ndale limene lachotsa nkhaŵa mwachipambano, kuphatikizapo zachuma, zimene Yesu ananena.

Chikomyunizimu chimene maiko a ku Eastern Europe achikana tsopano chinayesa kupereka zinthu kwa anthu molingana mwanjira ya chuma cholamuliridwa ndi Boma. Mosiyana ndi dongosolo la zamalonda lopikisana, dongosolo loyambalo linapereka chisungiko m’zachuma kwa anthu a m’maiko amenewo zimene kaŵirikaŵiri chikapitolizimu chimalephera kuchita. Komabe, nkhaŵa zimene Yesu ananena mumpangidwe wa kupereŵera kwa katundu wofunika kwa ogula ndi kuchepetsedwa kwa ufulu wa munthu zinakhalapobe.

Pakali pano, ambiri a maiko amenewo akuyambitsa misika yodzetsa chuma, motero akumapereka chitosoko chatsopano kwa nzika zawo. Lipoti lina posachedwapa linati: “Umbuli waphatikizidwa ndi chikhumbo cha kufikira mofulumira njira ya moyo ya maiko akumadzulo ya kugwiritsira ntchito zinthu.” Kuti apeze zimenezi “chiŵerengero cha anthu chomakula mu Länder watsopano kummaŵa kwa Germany chikutengeka kuloŵa m’ngongole yovuta kuwonjokamo.” Lipotilo likuwonjezera kuti: “Pambuyo pa mkhalidwe wakanthaŵi wokondweretsa kwambiriwo paufulu wazachuma mantha ndi kuthedwa nzeru zikuwanda tsopano.” Nkhaŵazo zilipobe, koma tsopano zowonekera mumpangidwe wa chikapitolizimu.

Ufulu wokulirapo wazandale ndi zachuma watsegula mipata ina yowongolerera njira zopezera chuma. Chifukwa chake, anthu ambiri angayesedwe kulingalira mwamphamvu za kuyambitsa bizinesi yawo kapena kusamukira kudziko lina lokhala ndi mipata ya ntchito yabwinopo.

Zosankha zonga zimenezi zili nkhani za munthu mwini. Sikolakwa kwa Mkristu kufuna kuwongolera mkhalidwe wake wazachuma. Iye angasonkhezeredwe ndi chikhumbo cha kufuna kusamalira banja lake, podziŵa kuti “ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.”​—1 Timoteo 5:8.

Chifukwa chake, kuli kosayenera kusuliza chosankha chimene ena amapanga. Panthaŵi imodzimodziyo, Akristu ayenera kukumbukira kuti sikuli kwanzeru kufunafuna thandizo la ndalama mwa kudziloŵetsa m’ngongole yaikulu imene ingawatchere msampha. Kungakhalenso kolakwa kufunafuna thandizo la ndalama mwanjira imene imaphatikizapo kunyalanyaza mathayo auzimu ndi zikondwerero zake.

Kuphunzira kwa Ena

M’zaka za pambuyo pa Nkhondo Yadziko II, nzika za Germany zikwi zambiri zinasamuka mu Ulaya wosakazidwa ndi nkhondoyo kumka kumaiko ena, makamaka ku Australia ndi Canada. Mwakutero ambiri anakhoza kuwongolera mkhalidwe wawo wazachuma, koma panalibe aliyense wa iwo amene anakhoza kupeŵa kotheratu nkhaŵa zachuma zimene Yesu ananena. Nthaŵi zina kuthetsa mavuto azachuma kunachititsa mavuto atsopano​—kulakalaka kumudzi, chinenero chachilendo, kuzoloŵera zakudya zatsopano, miyambo yosiyana, kugwirizana ndi mabwenzi atsopano, kapena kulimbana ndi mikhalidwe ya maganizo ina.

Ena a anthu osamuka ameneŵa anali Mboni za Yehova. Moyamikirika, ambiri a iwo sanalole mavuto amene amachitika chifukwa cha kusamuka kudodometsa mkhalidwe wawo wauzimu. Koma oŵerengeka anatero. Ena anakhala mikhole ya chinyengo cha chuma. Kupita kwawo patsogolo kwateokratiki kunalephera kuyendera pamodzi ndi mkhalidwe wazachuma.

Ndithudi zimenezi zimasonyeza nzeru ya kupenda mosamalitsa mkhalidwe wathu tisanapange zosankha zimene zikhoza kukhala zopusa. Zikhoterero za kukondetsa zinthu zakuthupi zidzatifooketsa muntchito imene sidzabwerezedwanso ya kupanga ophunzira imene Akristu atumidwa kuchita. Zimenezi nzowona mosasamala kanthu za kumene timakhala, popeza kuti palibe dziko limene nzika zake zili zomasuka pankhaŵa zachuma.

Kumenya Nkhondo Yabwino

Paulo analangiza Timoteo kuti: “Utsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso. Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira.” Kwa Akristu a ku Korinto iye anati: “Khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye.”​—1 Timoteo 6:11, 12; 1 Akorinto 15:58.

Kutsatira uphungu wabwino kwambiri umenewu ndiko njira yabwino koposa ya kulimbana ndi kukondetsa zinthu zakuthupi mwachipambano, ndipo palidi zinthu zambiri zoti Mkristu achite! M’maiko ena mmene chiŵerengero cha alaliki Aufumu chili chaching’ono, makamu a anthu adziŵa pang’ono pokha za chowonadi. Yesu ananeneratu molondola kuti: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka.”​—Mateyu 9:37.

Mmalo mwa kulola nkhaŵa zachuma m’maiko ameneŵa kuwapatutsa pantchito yauzimu imene ilipo, Mboni za Yehova zimagwiritsira ntchito bwino mkhalidwewo mwakugwiritsira ntchito mokwanira mipata imene ilipo. Pamene ali osalembedwa ntchito kwakanthaŵi, ambiri a iwo amafutukula ntchito yawo ya kulalikira. Utumiki wawo, kuwonjezera pakukuza mfuu yachitamando kwa Yehova, umawapatsa chisangalalo chofunika kulimbana ndi mavuto azachuma a iwo eni.

Mboni zimenezi zimaika ntchito ya kulalikira pamalo oyamba ndi kuika mavuto azachuma pamalo achiŵiri, zimene zimasonyeza gulu lonse la abale la padziko lapansi kuti iwo amadalira kotheratu mwa Yehova kuwasamalira. Lonjezo lake nlakuti: “Muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”​—Mateyu 6:33.

Chiyambire pakubwezeretsedwa kwa kulambira kowona mu 1919, Yehova sanalole anthu ake kugonja. Iye wawatetezera m’chizunzo chachikulu ndipo m’malo ena kwazaka makumi ambiri za kuchita ntchito mobisa. Mboni za Yehova zimadziŵa bwino kwambiri kuti zimene Mdyerekezi analephera kukwaniritsa mwa chizunzo, sadzazikwaniritsa ndi msampha wamachenjera koposa wa kukondetsa zinthu zakuthupi!

Kuphunzira Kuyembekezera m’Mbali Zonse

Nyumba Zaufumu zazikulu, ziwiya zokuzira mawu zokwera mtengo, Nyumba za Misonkhano, ndi nyumba zokongola za Beteli zimadzetsa ulemerero kwa Mulungu ndi kupereka umboni popanda mawu wakuti iye akudalitsa anthu ake. Mboni za Yehova m’maiko amene kalelo ntchito yawo inali yoletsedwa zingalingalire kuti pankhaniyi ziyenera kuchita zambiri kuti zigwirizane ndi maiko ena. Koma chofunika kwambiri nchakuti ziyenera kupita patsogolo mwauzimu. Zisonyezero zakuthupi za dalitso la Mulungu zidzatsatira m’nthaŵi yake.

Atumiki a Yehova odzipatulira afunikira kukhala maso, kuti mwina pofunafuna zikondwerero zawo, angayambe kulingalira kuti amanidwa zinthu zina zakuthupi kwanthaŵi yaitali. Kulakalaka kupeza mpumulo pakupereŵera m’zachuma ndi kusiyana kwa kakhalidwe ka anthu m’zitaganya nkomvekera bwino, koma anthu a Yehova samanyalanyaza kuti atumiki onse a Mulungu amakhumba mpumulo. Akhungu amakhumba kudzaonanso, odwala matenda osachiritsika amakhumba kudzachiritsidwa, opsinjika mtima amakhumba mkhalidwe wa zinthu wabwino, ndipo oferedwa amakhumba kudzaonananso ndi okondedwa awo amene anafa.

Chifukwa cha mikhalidwe, Mkristu aliyense amaumirizika mwanjira ina kuyembekezera dziko latsopano la Yehova kudzathetsa mavuto ake. Zimenezi ziyenera kutichititsa kudzifunsa kuti, ‘Ngati ndili ndi zakudya ndi zofunda, kodi sindiyenera kukhutiritsidwa ndi zinthu zimenezi ndi kukhala wofunitsitsa kuyembekezera mpumulo pamavuto azachuma?’​—1 Timoteo 6:8.

Akristu amene amadalira kotheratu mwa Yehova angatsimikiziridwe kuti ngati alidi ofunitsitsa kuyembekezera, zikhumbo zawo zonse zoyenerazo ndi zosoŵa zidzakhutiritsidwa posachedwapa. Palibe aliyense amene adzakhala atayembekezera pachabe. Tikubwerezanso kunena mawu a Paulo akuti: “Khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka muntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.”​—1 Akorinto 15:58.

Chotero, kodi kuphunzira kuyembekezera kuyeneradi kukhala vuto lalikulu?

[Chithunzi patsamba 10]

Kuphunzira kuyembekezera kungapulumutse moyo wanu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena