Yendani Molimba Mtima M’njira za Yehova
“Wodala yense wakuwopa Yehova, wakuyenda m’njira zake.”—SALMO 128:1.
1, 2. Kodi cholembedwa cha Baibulo chili ndi thandizo lotani la mawu ndi ntchito za mboni zoyambirira za Yehova?
MAWU Opatulika a Yehova ngodzala ndi zochitika za mayesero ndi zisangalalo za atumiki ake okhulupirika. Zokumana nazo za Nowa, Abrahamu, Sara, Yoswa, Debora, Baraki, Davide, ndi ena nzofotokozedwa bwino m’masamba ake. Onsewo anali anthu enieni okhala ndi chinthu chimodzi chapadera chofanana. Anali ndi chikhulupiriro mwa Mulungu ndipo anayenda molimba mtima m’njira zake.
2 Mawu ndi zochita za mboni zoyambirira za Yehova zingakhale zotilimbikitsa pamene tikuyesayesa kuyenda m’njira za Mulungu. Ndiponso, tidzadala pamene tisonyeza Mulungu ulemu ndi mantha oyenera kuwopera kusamkondweretsa. Zimenezi zili choncho ngakhale pamene tiyang’anizana ndi mayesero m’moyo, pakuti wamasalmo wouziridwa anaimba kuti: “Wodala yense wakuwopa Yehova, wakuyenda m’njira zake.”—Salmo 128:1.
Chimene Kulimba Mtima Kuli
3. Kodi kulimba mtima nchiyani?
3 Kuti tiyende m’njira za Yehova, tiyenera kukhala olimba mtima. Kwenikweni, Malemba amalamula anthu a Mulungu kusonyeza mkhalidwe umenewu. Mwachitsanzo, wamasalmo Davide anaimba kuti: “Limbikani, ndipo iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekeza Yehova.” (Salmo 31:24) Kulimba mtima ndiko “nyonga yamaganizo kapena makhalidwe ya kukhala pachiswe, kulimbikira, ndi kupirira ngozi, mantha, kapena chovuta.” (Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary) Munthu wolimba mtima ngwamphamvu, wolimba, wanyonga. Kuti Yehova amapatsa atumiki ake kulimba mtima nkwachionekere m’mawu awa a mtumwi Paulo kwa wantchito mnzake Timoteo akuti: “Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.”—2 Timoteo 1:7.
4. Kodi ndiiti imene ili njira imodzi ya kupezera kulimba mtima?
4 Njira imodzi yopezera kulimba mtima koperekedwa ndi Mulungu kumeneku ndiyo mwa kulingalira mwapemphero Mawu a Yehova, Baibulo. Zochitika zambiri zimene zili m’Malemba zingatithandize kukhala olimba mtima kwambiri. Chifukwa chake, choyamba tiyeni tione zimene tingaphunzire m’zolembedwa za m’Malemba Achihebri za ena amene anayenda molimba mtima m’njira za Yehova.
Kulimba Mtima Kuti Alengeze Uthenga wa Mulungu
5. Kodi ndimotani mmene kulimba mtima kwa Enoke kungapindulitsire atumiki a Yehova amakono?
5 Kulimba mtima kwa Enoke kungathandize atumiki amakono a Yehova kunena za uthenga wa Mulungu molimba mtima. Enoke asanabadwe, “anthu anayamba kutchula dzina la Yehova.” Ophunzira ena amanena kuti anthu “anayamba mwamwano” kutchula dzina la Yehova. (Genesis 4:25, 26; 5:3, 6) Dzina laumulungulo lingakhale litapatsidwa kwa anthu kapena kwa mafano. Chifukwa chake, chipembedzo chonyenga chinali chofala pamene Enoke anabadwa mu 3404 B.C.E. Kwenikweni, akuonekera kukhala anali yekha ‘m’kuyenda ndi Mulungu,’ akumalondola njira ya chilungamo mogwirizana ndi chowonadi cha Yehova chovumbulidwa.—Genesis 5:18, 24.
6. (a) Kodi ndiuthenga wamphamvu wotani umene Enoke analengeza? (b) Kodi nchidaliro chotani chimene tingakhale nacho?
6 Enoke anapereka uthenga wa Mulungu molimba mtima, mwinamwake mwa kulalikira. (Ahebri 11:5; yerekezerani ndi 2 Petro 2:5.) Mboni yokhayokha imeneyi inalengeza kuti: “Taona, wadza [Yehova, NW] ndi oyera ake zikwi makumi, kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zawo zonse zosapembedza, zimene anazichita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa iye.” (Yuda 14, 15) Enoke anasonyeza kulimba mtima kwa kugwiritsira ntchito dzina la Yehova pamene anali kupereka uthenga wotsutsa anthu osapembedza. Ndipo monga momwe Mulungu anapatsira Enoke kulimba mtima kuti alengeze uthenga wamphamvu umenewo, Yehova waperekanso mphamvu kwa Mboni Zake zamakono kulankhula mawu Ake molimba mtima muutumiki, kusukulu, ndi kwina kulikonse.—Yerekezerani ndi Machitidwe 4:29-31.
Kulimba Mtima Poyesedwa
7. Kodi Nowa amapereka chitsanzo chotani cha kulimba mtima?
7 Chitsanzo cha Nowa chingatithandize kukhala olimba mtima pochita ntchito zolungama pamene tikuyesedwa. Pokhala ndi kulimba mtima ndi chikhulupiriro, iye anachitapo kanthu pa chenjezo la Mulungu la chigumula cha padziko lonse ndipo “anamanga chingalaŵa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake.” Mwa machitidwe omvera ndi olungama, Nowa anatsutsa dziko losakhulupirira chifukwa cha ntchito zake zoipa nalitsimikizira kukhala loyenerera chiwonongeko. (Ahebri 11:7; Genesis 6:13-22; 7:16) Kusinkhasinkha za njira ya Nowa kumathandiza atumiki amakono a Mulungu kuchita molimba mtima ntchito zolungama zotero monga utumiki Wachikristu.
8. (a) Kodi Nowa anayang’anizana ndi chiyani monga “mlaliki wa chilungamo” wolimba mtima? (b) Kodi Yehova adzatichitiranji ngati tikhala alaliki a chilungamo olimba mtima?
8 Ngati tikulondola njira yachilungamo komano sitikudziŵa mmene tingalimbanirane ndi chiyeso chakutichakuti, tiyeni tipempherere nzeru yolimbanirana nacho. (Yakobo 1:5-8) Kukhulupirika kwa Nowa kwa Mulungu poyesedwa kumasonyeza kuti nkotheka kuyang’anizana ndi chiyeso molimba mtima ndi mokhulupirika. Iye analimbana ndi zitsenderezo za dziko loipa ndi za angelo ovala matupi aumunthu ndi za ana awo zimphonazo. Inde, Nowa anali “mlaliki wa chilungamo” wolimba mtima ku “dziko lapansi lakale” limene linayembekezera kuwonongedwa. (2 Petro 2:4, 5; Genesis 6:1-9) Ngakhale kuti ananena molimba mtima polengeza za chenjezo la Mulungu kwa anthu okhalako chisanachitike chigumula, “iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.” (Mateyu 24:36-39) Koma tiyeni tikumbukire kuti mosasamala kanthu za chizunzo ndi kukanidwa kwa uthenga wathu wa m’Baibulo ndi anthu ochuluka lerolino, Yehova adzatichirikiza monga momwe anachirikizira Nowa ngati tisonyeza chikhulupiriro chofananacho ndi kulimba mtima monga alaliki a chilungamo.
Kulimba Mtima kwa Kumvera Mulungu
9, 10. Kodi ndim’njira zotani zimene Abrahamu, Sara, ndi Isake anasonyezera kumvera kolimba mtima?
9 Abrahamu “bwenzi la [Yehova, NW]” ndiye chitsanzo chabwino kwambiri cha kulimba mtima kwa kumvera Mulungu. (Yakobo 2:23) Abrahamu anafunikira chikhulupiriro ndi kulimba mtima kuti amvere Yehova ndi kuchoka mu Uri wa Akaldayo, mzinda wokhala ndi mapindu ambiri a chuma chakuthupi. Iye anakhulupirira lonjezo la Mulungu lakuti “mabanja onse a dziko lapansi” adzadzidalitsa kupyolera mwa iye ndi kuti mbewu yake ikapatsidwa dziko. (Genesis 12:1-9; 15:18, 19) Ndi chikhulupiriro Abrahamu “anakhala mlendo ku dziko la lonjezano” nayembekezera mwachidwi “mudzi wokhala nawo maziko [enieni, NW]”—Ufumu wakumwamba wa Mulungu, mu umene akaukitsidwira kumoyo padziko lapansi.—Ahebri 11:8-16.
10 Mkazi wa Abrahamu, Sara, anali ndi chikhulupiriro ndi kulimba mtima kofunikira kuchoka mu Uri, kutsagana ndi mwamuna wake kudziko lachilendo, ndi kupirira zovuta zilizonse zimene akakumana nazo kumeneko. Ndipo ndimfupo yabwino chotani nanga imene anakhala nayo chifukwa cha kumvera kwake Mulungu molimba mtima! Ngakhale kuti anali chumba kufikira pafupifupi zaka 90 ndipo “patapita nthaŵi yake,” Sara anapatsidwa mphamvu ‘ya kukhala ndi pakati pa mbewu, popeza anaŵerengera Mulungu amene analonjezayo kukhala wokhulupirika.’ M’kupita kwa nthaŵi, iye anabala Isake. (Ahebri 11:11, 12; Genesis 17:15-17; 18:11; 21:1-7) Zaka zingapo pambuyo pake, Abrahamu molimba mtima anamvera Mulungu ndipo “anapereka nsembe Isake.” Ataletsedwa ndi mngelo, khololo linalandiranso mwana wake wolimba mtima ndi womverayo kuimfa “pachiphiphiritso.” Motero iye ndi Isake molosera anachitira chitsanzo kuti Yehova Mulungu akapereka Mwana wake, Yesu Kristu, monga dipo kotero kuti awo osonyeza chikhulupiriro mwa iye akakhale nawo moyo wosatha. (Ahebri 11:17-19; Genesis 22:1-19; Yohane 3:16) Ndithudi, kumvera kolimba mtima kwa Abrahamu, Sara, ndi Isake kuyenera kutisonkhezera kumvera Yehova ndi kuchita chifuniro chake nthaŵi zonse.
Kulimba Mtima kwa Kuima ndi Anthu a Mulungu
11, 12. (a) Kodi ndimotani mmene Mose anasonyezera kulimba mtima ponena za anthu a Yehova? (b) Polingalira za kulimba mtima kwa Mose, kodi ndifunso lotani limene lingafunsidwe?
11 Molimba mtima Mose anaima limodzi ndi anthu otsenderezedwa a Mulungu. M’zaka za zana la 16 B.C.E., makolo a Mose eniwo anasonyeza kulimba mtima. Posawopa lamulo la mfumu la kupha ana aamuna Achihebri obadwa chatsopano, anabisa Mose namuika m’kabokosi ka gumbwa pakati pa mabango m’mbali mwa mtsinje wa Nile. Atapezedwa ndi mwana wamkazi wa Farao, analeredwa monga mwana wake, ngakhale kuti poyamba anaphunzitsidwa zinthu zauzimu kunyumba kwa makolo ake. Monga wa m’banja la Farao, Mose “anaphunzira nzeru zonse za Aaigupto” nakhala “wamphamvu m’mawu ake ndi m’ntchito zake,” wamphamvu m’luso la kuganiza ndi la kuthupi.—Machitidwe 7:20-22; Eksodo 2:1-10; 6:20.
12 Mosasamala kanthu za mapindu a chuma chakuthupi a m’nyumba yachifumu, Mose molimba mtima anasankha kuima ndi olambira Yehova, amene panthaŵiyo anali muukapolo kwa Aigupto. Potetezera Mwisrayeli, iye anapha Mwaigupto nathaŵira ku Midyani. (Eksodo 2:11-15) Pafupifupi zaka 40 pambuyo pake, Mulungu anamgwiritsira ntchito kutsogolera Aisrayeli kutuluka muukapolo. Pamenepo Mose “anasiya Aigupto, wosawopa mkwiyo wa mfumu,” imene inafuna kumupha chifukwa cha kuimira Yehova kaamba ka Israyeli. Mose anayenda monga ngati kuti anali kuona “Wosaonekayo,” Yehova Mulungu. (Ahebri 11:23-29; Eksodo 10:28) Kodi muli ndi chikhulupiriro ndi kulimba mtima koteroko kwakuti mudzamamatirabe kwa Yehova ndi anthu ake mosasamala kanthu za zovuta ndi chizunzo?
Kulimba Mtima kwa ‘Kutsata Yehova ndi Mtima Wonse’
13. Kodi ndimotani mmene Yoswa ndi Kalebi anaperekera zitsanzo za kulimba mtima?
13 Yoswa ndi Kalebi olimba mtimawo anapereka umboni wakuti tikhoza kuyenda m’njira za Mulungu. Iwo “anatsata Yehova ndi mtima wonse.” (Numeri 32:12) Yoswa ndi Kalebi anali pakati pa amuna 12 amene anatumizidwa kukazonda Dziko Lolonjezedwa. Powopa nzika zake, azondi khumi anayesa kuwopseza Israyeli kusaloŵa m’Kanani. Komabe, Yoswa ndi Kalebi molimba mtima anati: “Yehova akakondwera nafe, adzatiloŵetsa m’dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Chokhachi musamapikisana naye Yehova; musamawopa anthu a m’dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wawo wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawawopa.” (Numeri 14:8, 9) Posoŵa chikhulupiriro ndi kulimba mtima, mbadwo wa Aisrayeli umenewo sunafike kudziko la lonjezo. Koma Yoswa ndi Kalebi, limodzi ndi mbadwo wina watsopano, analoŵamodi.
14, 15. (a) Pamene Yoswa anagwiritsira ntchito mawu a pa Yoswa 1:7, 8, kodi nchiyani chimene iye ndi Aisrayeli anapeza? (b) Kodi ndiphunziro lanji loloŵetsamo kulimba mtima limene tikuphunzira kwa Yoswa ndi Kalebi?
14 Mulungu anauza Yoswa kuti: “Khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipambukire kudzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako. Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.”—Yoswa 1:7, 8.
15 Pamene Yoswa anagwiritsira ntchito mawu amenewo, Yeriko ndi mizinda ina inagonjetsedwa ndi Aisrayeli. Mulungu anachititsa ngakhale dzuŵa kuima kotero kuti linapitirizabe kuunikira kufikira Israyeli anapambana ku Gibeoni. (Yoswa 10:6-14) Pamene anali patsoka la kuukiridwa ndi mdani wa magulu a nkhondo ogwirizana “kuchuluka kwawo ngati mchenga uli m’mphepete mwa nyanja,” Yoswa anachitapo kanthu molimba mtima, ndipo Mulungu anachititsa Israyeli kupambana. (Yoswa 11:1-9) Ngakhale kuti ndife anthu opanda ungwiro, mofanana ndi Yoswa ndi Kalebi, tingathe kutsata Yehova ndi mtima wonse, ndipo Mulungu akhoza kutipatsa mphamvu ya kuyenda m’njira zake molimba mtima.
Kulimba Mtima kwa Kudalira Mulungu
16. Kodi Debora, Baraki, ndi Yaeli anasonyeza kulimba mtima m’njira zotani?
16 Chidaliro cholimba mtima mwa Mulungu chimafupidwa, monga momwe kwasonyezedwera m’zochitika pamene oweruza anapereka chiweruzo cholungama mu Israyeli. (Rute 1:1) Mwachitsanzo, Woweruza Baraki ndi mneneri wachikazi Debora anadalira Mulungu molimba mtima. Mfumu Yachikanani Yabini inali itatsendereza Israyeli kwa zaka 20 pamene Yehova anachititsa Debora kusonkhezera Baraki kuti asonkhanitse amuna 10,000 pa phiri la Tabori. Mkulu wankhondo wa Yabini, Sisera, anafika mwamsanga kuchigwa cha mtsinje wa Kisoni, akumatsimikizira kuti pabwalo limeneli amuna a Israyeli sangakhale kanthu pagulu lake lankhondo ndi magaleta ake 900 ankhondo okhala ndi mazenga achitsulo pa magudumu awo. Pamene Aisrayeli anatuluka kutsikira m’chigwacho, Mulungu anawamenyera nkhondo, ndipo chigumula chamadzi chinachititsa malowo kukhala athope limene linachititsa magaleta a Sisera kutitimira. Amuna a Baraki analakika, kotero kuti “gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa.” Sisera anathaŵira kuhema wa Yaeli, koma pamene anali mtulo, mkaziyo analimba mtima namupha mwa kukhomera chichiri m’litsipa mwake. Zinachitikadi monga mwa mawu aulosi a Debora kwa Baraki, motero “ulemu” wa chipambanochi unamka kwa mkazi. Chifukwa chakuti Debora, Baraki, ndi Yaeli anadalira Mulungu molimba mtima, dziko la Israyeli “linapumula zaka makumi anayi.”—Oweruza 4:1-22; 5:31.
17. Kodi nchitsanzo chotani cha kulimba mtima kodalira Yehova chimene chinaperekedwa ndi Woweruza Gideoni?
17 Woweruza Gideoni anadalira Yehova Mulungu molimba mtima pamene Amidyani ndi ena anaukira Israyeli. Ngakhale kuti anaposedwa ndi chiŵerengero cha oukira 135,000, amuna ankhondo 32,000 a Israyeli akanaonabe chipambano choperekedwa ndi Mulungu kukhala chochititsidwa ndi mphamvu za iwo eni. Chifukwa chake, atalamulidwa ndi Yehova, Gideoni anachepetsa gulu lake lankhondo kukhala timagulu titatu ta amuna 100 kalilonse. (Oweruza 7:1-7, 16; 8:10) Pamene 300 amenewo anazinga msasa wa Amidyani usiku, aliyense wa iwo anali ndi lipenga ndi mbiya ndi miyuni mkati mwa mbiyazo. Pamene chizindikiro chinaperekedwa, iwo anawomba malipengawo, naphwanya mbiyazo, nanyamulira miyuni m’mwamba, ndipo anafuula kuti: “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.” (Oweruza 7:20) Amidyani owopsedwawo anayamba kuthaŵa ndipo anagonjetsedwa. Zochitika zotero ziyenera kutikhutiritsa maganizo kuti kudalira Mulungu molimba mtima kumafupidwanso lerolino.
Kulimba Mtima kwa Kulemekeza Yehova ndi Kuchirikiza Kulambira Koyera
18. Kodi nchiyani chimene Davide anachita molimba mtima pamene anapha Goliati?
18 Zitsanzo zina za Baibulo zimalimbitsa mtima kuti tilemekeze Yehova ndi kuchirikiza kulambira koyera. Davide wachichepere, amene analanditsa nkhosa za atate wake molimba mtima, anasonyezanso kukhala wolimba mtima pamaso pa chimphona cha Afilisti Goliati. “Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo,” anatero Davide, “koma ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli amene iwe unawanyoza. Lerolino Yehova adzakupereka iwe m’dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. . . . Kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israyeli kuli Mulungu. Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo.” (1 Samueli 17:32-37, 45-47) Mothandizidwa ndi Mulungu, Davide analemekeza Yehova molimba mtima, anapha Goliati, ndipo motero anachita mbali yaikulu pochotsa chiwopsezo cha Afilisti pakulambira koyera.
19. Kodi ndintchito yotani imene Solomo anafunikira kukhala wolimba mtima, ndipo kodi ndimotani mmene mchitidwe wake ungagwiritsiridwire ntchito m’tsiku lathu?
19 Pamene Solomo mwana wa Mfumu Davide anali pafupi kumanga kachisi wa Mulungu, atate ake okalambawo anamlimbikitsa kuti: “Limbika, nulimbe mtima, nuchichite; usawopa, kapena kutenga nkhaŵa; pakuti Yehova Mulungu, ndiye Mulungu wanga, ali nawe; sadzakusoŵa kapena kukutaya mpaka zitatha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova.” (1 Mbiri 28:20) Pochitapo kanthu molimba mtima, Solomo anamaliza kachisiyo mwachipambano. Pamene programu ya kumanga kwateokratiki idzetsa zovuta lerolino, tiyeni tikumbukire mawu a Davide akuti: “Limbika, nulimbe mtima, nuchichite.” Ha, imeneyi ndinjira yabwino kwambiri chotani nanga ya kulemekeza Yehova ndi kuchirikiza kulambira koyera!
20. Kodi ndim’mbali iti imene Mfumu Asa anachita molimba mtima?
20 Chifukwa cha chikhumbo cha Mfumu Asa cha kulemekeza Mulungu ndi kuchirikiza kulambira koyera, anachotsa m’Yuda mafano ndi anyamata adama a pakachisi. Iye anachotsanso agogo ake aakazi ampatuko pamalo awo aulemu ndi kutentha ‘fano lawo lonyansitsa.’ (1 Mafumu 15:11-13) Inde, Asa “analimbika mtima, nachotsa zonyansazo m’dziko lonse la Yuda ndi Benjamini, ndi m’midzi adailanda ku mapiri a Efraimu; nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pa likole la Yehova.” (2 Mbiri 15:8) Kodi nanunso mumakana mpatuko molimba mtima ndi kuchirikiza kulambira koyera? Kodi mukugwiritsira ntchito chuma chanu chakuthupi kupititsira patsogolo zinthu Zaufumu? Ndipo kodi mukufunafuna kulemekeza Yehova mwa kukhala ndi phande lokhazikika m’kulengeza mbiri yabwino monga mmodzi wa Mboni zake?
21. (a) Kodi ndimotani mmene zochitika za anthu osunga umphumphu okhalako Chikristu chisanadze zingatithandizire? (b) Kodi nchiyani chimene chidzapendedwa m’nkhani yotsatira?
21 Ndife othokoza chotani nanga kuti Mulungu wasunga zochitika zimenezi za m’Malemba zonena za osunga umphumphu amene analiko Chikristu chisanadze! Ndithudi, zitsanzo zawo zabwino zingatithandize kupereka utumiki wopatulika kwa Yehova molimba mtima, mwamantha aumulungu, ndi ulemu. (Ahebri 12:28) Koma Malemba Achigiriki Achikristu alinso ndi zitsanzo za anthu ochitapo kanthu okhala ndi kulimba mtima kwaumulungu. Kodi ndimotani mmene zina za zochitika zimenezi zingatithandizire kuyenda m’njira za Yehova molimba mtima?
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi kulimba mtima nchiyani?
◻ Kodi ndimotani mmene Enoke ndi Nowa anasonyezera kulimba mtima?
◻ Kodi ndim’mbali zotani zimene Abrahamu, Sara, ndi Isake anachitirapo kanthu molimba mtima?
◻ Kodi nzitsanzo za kulimba mtima zotani zimene zinaperekedwa ndi Mose, Yoswa, ndi Kalebi?
◻ Kodi ndimotani mmene ena anasonyezera kuti anali olimba mtima kudalira Mulungu?
[Chithunzi patsamba 15]
Gideoni ndi gulu lake la ankhondo laling’ono anadalira Yehova molimba mtima