Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 11/15 tsamba 28-30
  • Kodi Nkuvomereranji Cholakwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nkuvomereranji Cholakwa?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sitiyenera Kutaya Mtima
  • Kudzichepetsa, Mkhalidwe Wofunika Kwambiri
  • Anavomereza Zolakwa
  • Kuchitapo Kanthu pa Zolakwa Zathu
  • Pamene Mkulu Alakwa
  • Khalani Wofulumira Kuvomereza Cholakwa
  • Kukondwera ndi Kuvomereza Zolakwa
  • Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?
    Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa
  • Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Tizitani Tikalakwitsa Zinthu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Kupepesa—Njira Yothandiza Yopezera Mtendere
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 11/15 tsamba 28-30

Kodi Nkuvomereranji Cholakwa?

CHINALI chimodzi cha zochitika zachilendo kwambiri m’mbiri ya zankhondo. Nthumwi yosanyamula chida inabweza asilikali ouma mitima okwanira 400 amene anafuna kubwezera kunyozedwa. Atamva kuchonderera kwa mkazi mmodzi yekha wolimba mtima, mtsogoleri wa amunawo analeka zimene anafuna kuchita.

Mtsogoleri ameneyo anali Davide, amene pambuyo pake anadzakhala mfumu ya Israyeli. Iye amamvetsera mkaziyo Abigayeli chifukwa chakuti anafuna kukondweretsa Mulungu. Pamene mkaziyo mochenjera anamsonyeza kuti kubwezera mwamuna wake, Nabala, kukamchititsa kukhala ndi liŵongo la mwazi, Davide anafuula kuti: “Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, amene anakutumiza lero kudzandichingamira ine; ndipo, kudalitsike kuchenjera kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi, ndi kusabwezera chilango ndi dzanja la ine ndekha.” Davide anayamikira kuti Mulungu anagwiritsira ntchito Abigayeli kumletsa kuchita cholakwa chowopsa.​—1 Samueli 25:9-35.

M’salmo lina, Davide anafunsa kuti: “Zolakwa​—ndani angazizindikire?” (Salmo 19:12, NW) Mofanana naye, nafenso tingakhale tisakudziŵa zolakwa zathu kufikira wina atatitchulira zimenezo. Nthaŵi zina, zotulukapo zosakondweretsa zimatikakamiza kuzindikira kuti talakwa, tachita mopanda nzeru, kapena mosakoma mtima.

Sitiyenera Kutaya Mtima

Ngakhale kuti tonsefe timalakwa, zimenezi siziyenera kutitayitsa mtima. Katswiri wa nkhani zokambirana Edward John Phelps ananena kuti: “Munthu amene samalakwa kaŵirikaŵiri samachita chinthu chilichonse.” Ndipo wophunzira Wachikristu Yakobo anati: “Timakhumudwa tonse pazinthu zambiri.” (Yakobo 3:2) Kodi mwana angaphunzire kuyenda popanda kukhumudwa? Ayi, pakuti mwana amaphunzira mwa zolakwa ndipo amapitirizabe kuyesayesa kufikira atadziŵa kudzichirikiza.

Kuti tikhale ndi miyoyo yokhazikika, nafenso tifunikira kuphunzirira pazolakwa zathu ndi za ena. Popeza kuti Baibulo limasimba zokumana nazo za ambiri amene mikhalidwe yawo ingakhale yofanana ndi yathu, tingathandizidwe kupeŵa kuchita zolakwa zofananazo zimene iwo anachita. Pamenepo, kodi tingaphunzirenji pazolakwa zawo?

Kudzichepetsa, Mkhalidwe Wofunika Kwambiri

Phunziro lina nlakuti Mulungu samatsutsa onse amene amalakwa koma amaweruza awo okha amene amakana kuziwongolera ngati kuli kotheka. Sauli Mfumu ya Israyeli sanamvere malangizo a Yehova onena za kuwonongedwa kwa Amaleki. Pamene anauzidwa za cholakwacho ndi mneneri Samueli, Sauli choyamba anachepetsa nkhaniyo ndiyeno anayesa kukankhira ena mlanduwo. Iye anali wodera nkhaŵa kwambiri za kuchititsidwa manyazi pamaso pa anyamata ake m’malo mwa kuwongolera cholakwacho. Chifukwa chake, ‘Yehova anamkana iye kukhala mfumu.’​—1 Samueli 15:20-23, 30.

Ngakhale kuti Davide, amene analoŵa m’malo Sauli, anachita zolakwa zazikulu, iye anakhululukiridwa chifukwa chakuti modzichepetsa analandira uphungu ndi chilango. Kudzichepetsa kwa Davide kunamsonkhezera kulabadira mawu a Abigayeli. Asilikali ake anali okonzekera kumenya nkhondo. Komabe, pamaso pa asilikali ake, Davide anavomereza kuti anapanga chosankha chansontho. M’moyo wake wonse, kudzichepetsa koteroko kunathandiza Davide kufunafuna chikhululukiro ndi kuwongolera njira zake.

Kudzichepetsa kumasonkhezeranso atumiki a Yehova kuwongolera ndemanga zosalingalira. Mkati mwa kuweruza mlandu m’Bwalo la Akulu, mkulu wansembe analamula kuti Paulo aombedwe pama. Mtumwi Paulo anayankha kuti: “Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe.” (Machitidwe 23:3) Mwinamwake chifukwa cha maso osaona bwino, Paulo sanazindikire amene iye anali kuuza mawuwo kufikira pamene opezekapo ena anafunsa kuti: “Ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu?” Pamenepo, Paulo anavomereza mwamsanga cholakwa chake, akumati: “Sindinadziŵa, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako.” (Machitidwe 23:4, 5; Eksodo 22:28) Inde, Paulo anavomereza cholakwa chake modzichepetsa.

Anavomereza Zolakwa

Baibulo limasonyezanso kuti anthu ena anasintha kalingaliridwe kawo kolakwika. Mwachitsanzo, talingalirani za wamasalmo Asafu. Chifukwa chakuti anthu oipa anaonekera kuti zinthu zinali kuwayendera bwino, iye anati: “Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe.” Koma Asafu anadzazindikira kulakwa kwake pamene anapita kunyumba ya Yehova ndi kusinkhasinkha za mapindu a kulambira koyera. Ndiponso, iye anavomereza kulakwa kwake m’Salmo 73.

Yona nayenso analola malingaliro olakwa kuphimba maganizo ake. Atalalikira mu Nineve, iye anasamalira kwambiri za ulemerero wake m’malo mwa kupulumutsidwa kwa anthu a mzindawo. Yona anakwiya pamene Yehova sanalange anthu a Nineve mosasamala kanthu za kulapa kwawo, koma Mulungu anamuwongolera. Yona anadzazindikira kuti lingaliro lake linali lolakwa, chifukwa chakuti buku la Baibulo lotchedwa ndi dzina lake limavomereza zolakwa zake mosabisa.​—Yona 3:10–4:11.

Atalingalira molakwa kuti Yehova Mulungu, osati Satana Mdyerekezi, ndiye anali kumsautsa, munthuyo Yobu anayesa kutsimikizira kuti sanafunikire kuvutika motero. Iye sanadziŵe za nkhani yaikuluyo yakuti: Kodi atumiki a Mulungu akakhalabe okhulupirika kwa iye poyesedwa? (Yobu 1:9-12) Pambuyo pakuti Elihu ndiyeno kenako Yehova anathandiza Yobu kuona kulakwa kwake, iye anavomereza kuti: “Chifukwa chake ndinafotokozera zimene sindinazizindikira . . . Chifukwa chake ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m’fumbi ndi mapulusa.”​—Yobu 42:3, 6.

Kuvomereza zolakwa kumatithandiza kusunga unansi wathu wabwino ndi Mulungu. Monga momwe zitsanzo zapapitapozi zikusonyezera, iye sadzatikana chifukwa cha zolakwa zathu ngati tizivomereza ndi kuchita zimene tingathe kuti tiwongolere malingaliro athu, mawu osalingalira, kapena machitidwe aliuma lopanda pake. Kodi tingagwiritsire ntchito motani chidziŵitso chimenechi?

Kuchitapo Kanthu pa Zolakwa Zathu

Kuvomereza cholakwa modzichepetsa ndi kuchitapo kanthu kuchiwongolera kungalimbitse maunansi a banja. Mwachitsanzo, mwinamwake chifukwa cha kutopa kapena mkwiyo, kholo lingakhale linali lankhanza pang’ono polanga mwana. Kukana kuwongolera cholakwa chimenechi kungakhale ndi ziyambukiro zoipa. Moyenerera, mtumwi Paulo analemba kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].”​—Aefeso 6:4.

Mkristu wachichepere wotchedwa Paul akukumbukira mwachimwemwe kuti: “Atate anapepesa nthaŵi zonse pamene anaona kuti anachita mopambanitsa. Zimenezo zinandithandiza kuwalemekeza.” Kuti kaya kupepesa kuli kofunika mumkhalidwe wakutiwakuti ndiko chosankha chaumwini. Komabe, kupepesa kuyenera kutsatiridwa ndi zoyesayesa zowona mtima za kupeŵa zolakwa zofananazo mtsogolo.

Bwanji ngati mwamuna kapena mkazi achita cholakwa chovutitsa maganizo? Kuvomereza kosabisa kanthu, kupepesa kochokera mumtima, ndi mzimu wa kukhululukira zidzathandiza kusungitsa unansi wawo wachikondi. (Aefeso 5:33; Akolose 3:13) Jesús, mwamuna wa ku Spain wamtima wapachala wa zaka za m’ma 50, sali wonyada kosati nkupepesa kwa mkazi wake, Albina. “Tili ndi chizoloŵezi cha kupepesa pamene tilakwirana,” akutero mkaziyo. “Zimenezi zimatithandiza kupirirana mwachikondi.”

Pamene Mkulu Alakwa

Kuvomereza zolakwa ndi kupepesa mowona mtima kudzathandizanso akulu Achikristu kugwirira ntchito pamodzi mogwirizana ndi ‘kulemekezana.’ (Aroma 12:10) Mkulu angazengereze kuvomereza cholakwa chifukwa cha kuopa kunyozetsa ulamuliro wake mumpingo. Komabe, kuyesa kulungamitsa molakwa, kunyalanyaza, kapena kupeputsa cholakwacho nkothekera kwambiri kuchititsa ena kuleka kudalira uyang’aniro wake. Mbale wachidziŵitso amene amapepesa modzichepetsa, mwinamwake chifukwa cha mawu osalingalira, amalemekezedwa ndi ena.

Fernando, mkulu m’Spain, akukumbukira nthaŵi ina pamene woyang’anira dera amene anali kuchititsa msonkhano waukulu wa akulu anapereka ndemanga yolakwa ponena za mmene msonkhano uyenera kuchitidwira. Pamene mbale wina mwaulemu anawongolera zimene iye ananena, woyang’anira derayo mwamsanga anavomereza kuti anali ataphonya. Fernando akukumbukira kuti: “Pamene ndinamuona akuvomereza cholakwa chake pamaso pa akulu onsewo, ndinachita chidwi kwambiri. Ndinamlemekeza mokulirapo pambuyo pa kupepesa kumeneko. Chitsanzo chake chinandiphunzitsa mmene kuliri kofunika kuzindikira zophophonya zanga.”

Khalani Wofulumira Kuvomereza Cholakwa

Kaŵirikaŵiri kupepesa kumayamikiridwa, makamaka ngati kuchitidwa mwamsanga. Kwenikweni, pamene tivomereza cholakwa msanga kwambiri mpamenenso zimakhala bwino kwambiri. Mwachitsanzo: Pa October 31, 1992, Papa John Paul II anavomereza kuti bwalo lamilandu la Inquisition linachita “molakwa” zaka 360 zapitazo polanga Galileo chifukwa chonena motsimikiza kuti dziko lapansi sindilo pakati pa chilengedwe chonse. Komabe, kuchedwetsa kupepesa kwa nthaŵi yaitali motero kumachepetsa phindu lake.

Nzofanananso ndi m’maunansi a anthu. Kupepesa kwamsanga kungapoletse chilonda chochititsidwa ndi mawu kapena mchitidwe wopanda chifundo. Yesu anatifulumiza kusachedwa kubwezeretsa mtendere, akumati: “Ngati ulikupereka mtulo wako paguwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.” (Mateyu 5:23, 24) Kaŵirikaŵiri, kubwezeretsa maunansi amtendere kumangofuna kokha kuvomereza kuti talakwitsa zinthu ndi kupempha chikhululukiro. Tikayembekezera kwambiri tisanachite zimenezi, kumakhalanso kovuta kwambiri kutero.

Kukondwera ndi Kuvomereza Zolakwa

Monga momwe zitsanzo za Sauli ndi Davide zimasonyezera, njira imene timachitira ndi zolakwa zathu ingayambukire miyoyo yathu. Sauli mouma khosi anakana uphungu, ndipo zolakwa zake zinachuluka, potsirizira pake zikumamfikitsa kuimfa ali wopanda chiyanjo cha Mulungu. Komabe, mosasamala kanthu za zolakwa zake ndi machimo, Davide molapa anavomereza kuwongoleredwa ndipo anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova. (Yerekezerani ndi Salmo 32:3-5.) Kodi chimenecho sindicho chikhumbo chathu?

Mphotho yaikulu koposa ya kuvomereza ndi kuwongolera cholakwa kapena kulapa tchimo ndiyo kudziŵa kuti takhululukiridwa ndi Mulungu. “Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake,” anatero Davide. “Wodala munthuyo Yehova samuŵerengera mphulupulu zake.” (Salmo 32:1, 2) Motero, nkwanzeru chotani nanga kuvomereza cholakwa!

[Chithunzi patsamba 29]

Kodi mwana angaphunzire kuyenda popanda kukhumudwa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena