Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 4/1 tsamba 20-24
  • Moyo Wolemeretsa, Wofupa mu Utumiki wa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo Wolemeretsa, Wofupa mu Utumiki wa Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Madzulo Amene Anasintha Moyo Wanga
  • Utumiki Wathu m’Zaka Zoyambirira
  • Kusintha Koyesa Chikhulupiriro Chathu
  • Kupulumuka Tsoka Lili Nenene
  • Kuthandiza Pozenga Mlandu
  • Nkhondo Itha​—Utumiki Wathu Upitiriza
  • Njira ya Yehova Ndiyo Yabwino Koposa Yokhalira ndi Moyo
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Ndife Otsimikiza Kutumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kutumikira Pansi pa Dzanja la Yehova Lachikondi
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Zaka Zoposa 50 za ‘Kuwolokerako’
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 4/1 tsamba 20-24

Moyo Wolemeretsa, Wofupa mu Utumiki wa Yehova

YOSIMBIDWA NDI LEO KALLIO

Munali m’chaka cha 1914, ndipo tsiku lakumapeto kwa chilimwe linalinkutha m’mlaga wathu wa Turku, mzinda wa m’Finland. Mwadzidzidzi, mkhalidwe wabatawo unadukizidwa ndi mbiri ya nkhondo yaikulu imene inali itabuka. Posapita nthaŵi, makwalala anadzala ndi piringupiringu wa anthu ozizwa ofuna kudziŵa zimene zinali kuchitika. Nkhope za akulu zodera nkhaŵazo zinachititsa anafe kuzizwa kuti chikachitika nchiyani. Ndinali wazaka zisanu ndi zinayi, ndipo ndikukumbukira kuti kuseŵera kwamtendere kwa ana kunasanduka maseŵera ankhondo.

NGAKHALE kuti Finland sanadziloŵetse m’Nkhondo Yadziko ya I (1914-18), dzikolo linasakazidwa ndi nkhondo yachiŵeniweni mu 1918. Achibale ndi mabwenzi akale ananyamula zida ndi kumenyana okhaokha chifukwa cha maganizo andale otsutsana. Banja lathu la anthu asanu ndi aŵiri linakumana ndi chidani chimenechi. Atate wanga, omwe ankalankhula malingaliro awo mosabisa, anamangidwa naweruzidwa zaka zisanu ndi ziŵiri m’ndende. Pambuyo pake anamasulidwa, koma panthaŵiyo thanzi lawo linali litawonongeka.

Banja lathu linali litavutika ndi njala ndi matenda mkati mwa nyengo yosautsa imeneyi. Atatu a alongo anga aang’ono anamwalira. Akulu awo a atate, omwe ankakhala mumzinda wa Tampere, adamva za nsautso yathu ndipo adaitana atate wanga ndi amayi ndi ana aŵiri otsalafe kukakhala nawo kumeneko.

Pambuyo pa zaka zambiri, pamene ndinkakhalabe mu Tampere, ndinakumana ndi mtsikana yemwe anali chiphadzuŵa wotchedwa Sylvi. Anali ndi makulidwe ofanana ndi anga. Atate wake adaphedwa m’nkhondo yachiŵeniŵeni, ndiyeno pambuyo pake bwenzi lapamtima la banja lawo, a Kaarlo (Kalle) Vesanto a ku tauni la Pori, adatenga iye, mkulu wake, ndi amayi ake nakakhala nawo kwawoko. Iwo anapanga makonzedwe akuti amake Sylvi apeze ntchito ndi kuti atsikanawo aloŵe sukulu. M’kupita kwanthaŵi Sylvi anasamukira ku Tampere kukaloŵa ntchito, ndipo nkumene tinakumana kumeneko.

Madzulo Amene Anasintha Moyo Wanga

Mu 1928, tinatomerana ndi Sylvi, ndipo tsiku lina tinatenga ulendo wopita ku Pori kukachezera a Kalle Vesanto ndi banja lawo. Palibe chochitika china chimene chinayambukira moyo wanga motsimikizirika kwambiri koposa chimenechi. A Kalle anali ndi akavalo ampikisano waliŵiro ndipo ankachititsa mpikisanowo koma anali ataleka bizinesiyo. Iwo ndi akazi awo anali atakhala ofalitsa achangu a mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Buku la 1990 Yearbook of Jehovah’s Witnesses limasimba mmene iwo analembera anthu ganyu ya kulemba mawu akuti “Mamiliyoni Okhala ndi Moyo Tsopano Sadzafa Konse” pachipupa chakunja cha nyumba yawo yosanja zipinda ziŵiri. Mawu olembedwawo anali aakulu moti nkukhoza kuŵerengedwa mosavuta ndi anthu oyenda m’sitima yodutsa yothamanga kwambiri.

Usiku womwewo a Kalle ndi ine tinalankhula kupyola pakati pausiku. “Nchifukwa ninji? Nchifukwa ninji? Nchifukwa ninji?” ndinkafunsa motero, ndipo a Kalle ankafotokoza. Kwenikweni ndinaphunzira ziphunzitso zoyambirira za Baibulo usiku umodzi. Ndinalemba malemba omwe analongosola ziphunzitso zosiyanasiyana. Pambuyo pake, nditabwerera kunyumba, ndinatenga notibuku ndi kulembamo malemba onsewo liwu ndi liwu. Popeza kuti ndinali ndisanazoloŵere Baibulo, ndinagwiritsira ntchito notibuku imeneyi kulalikira kwa amene ndinagwira nawo ntchito pamalo omangira. Pamene ndinavumbula ziphunzitso za chipembedzo chonyenga, kaŵirikaŵiri ndinali kupeza kuti ndikubwereza mawu a a Kalle akuti: “Mwanyengedwaditu anzanganu!”

A Kalle anandipatsa keyala ya nyumba ina yaing’ono mu Tampere kumene Ophunzira Baibulo okwanira 30 ankachitira misonkhano yawo. Kumeneko ndinkaloŵa ndi kukhala pangodya chakukhomo pafupi ndi Mbale Andersson, mwini nyumbayo. Kufikapo kwanga kunali kwa kamodzikamodzi, koma pemphero linakhala lothandiza kwambiri. Nditakhala ndi mavuto aakulu kuntchito, nthaŵi ina ndinapemphera kuti: “Chonde, Mulungu, ngati mundithandiza kuthetsa mavuto angaŵa, ndilonjeza kuti ndidzafika pamsonkhano uliwonse.” Koma zinthu zinangoipiraipira. Ndiyeno ndinazindikira kuti ndinali kulamulira Yehova, motero ndinasintha pemphero langa ndi kumati: “Mosasamala kanthu ndi zimene zingachitike, ndilonjeza kuti ndidzafika pamsonkhano uliwonse.” Pamene ndinatero zovuta zanga zinachepekera, ndipo ndinayamba kufika pamisonkhano mokhazikika.​—1 Yohane 5:14.

Utumiki Wathu m’Zaka Zoyambirira

Mu 1929, Sylvi ndi ine tinakwatirana, ndipo mu 1934 tonse aŵiri tinasonyeza kudzipatulira kwathu kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi. M’masikuwo utumiki wathu unaloŵetsamo kunyamula galamafoni ndi malekodi kumka nazo kunyumba za anthu ndi kupempha mwaulemu kuti tipereke nkhani ya Baibulo kwaulere. Kaŵirikaŵiri anthuwo mofunitsitsa anatilola kuloŵa, ndipo pambuyo pake atamvetsera nkhani yojambulidwayo, tinakambitsirana nawo ndipo analandira ena a mabuku athu.

Mwa chilolezo cha akuluakulu aboma, tinaseŵera nkhani za Baibulo zimodzimodzizi mwa kugwiritsira ntchito mikuza mawu m’mapaki. Ndipo m’milaga tinkalumikiza chokuzira mawu patsindwi kapena kuchumuni. Nthaŵi zina tinapereka nkhanizo pagombe la nyanja kumene anthu a mumzinda ankasonkhana m’makamu aakulu. Tinkangonyamula mikuza mawu yathuyo m’bwato ndi kuyenda pang’onopang’ono m’mphepete mwagombe. Pa Masande, tinkapita pamkupiti wokalalikira kumadera akumidzi, titanyamula mikuza mawu yathu yabwinoyo ndi mabuku ochuluka.

Kusintha Koyesa Chikhulupiriro Chathu

Mu 1938, ndinaloŵa utumiki wanthaŵi yonse monga mpainiya, koma ndinapitiriza kugwira ntchito monga womanga. M’ngululu yotsatira ndinalandira chiitano chochokera ku ofesi yanthambi ya Sosaite kuti ndikhale mtumiki woyendayenda, tsopano wotchedwa woyang’anira dera. Chosankha cha kulandira chiitanocho chinali chovuta chifukwa chakuti ndinasangalala kwambiri ndi kugwira ntchito ndi mpingo wathu mu Tampere. Ndiponso, tinali ndi nyumba yathu; tinalinso ndi mwana wamwamuna wazaka zisanu ndi chimodzi, Arto, yemwe anali pafupi kuyamba sukulu; ndipo Sylvi anasangalala ndi ntchito yake monga kalaliki wa m’sitolo. Komabe, titakambitsirana pamodzi, ndinavomereza kutenga mwaŵi wowonjezereka umenewu wa utumiki wa Ufumu.​—Mateyu 6:33.

Ndiyeno nyengo ina yovuta inayamba. Nkhondo inaulika pa November 30, 1939, pamene asilikali a ku Soviet Union analoŵa m’Finland. Nkhondoyo, yotchedwa Nkhondo ya m’Chisanu, inapitiriza mpaka m’March 1940, pamene Finland anakakamizika kuvomereza pangano la mtendere. Zinaoneka ngati kuti nyengo nayonso inali pankhondo, popeza kuti nyengo imeneyi inali chisanu chozizira koposa chilichonse chimene ndingakumbukire. Ndinatchova njinga kupita kumpingo ndi mpingo ngakhale kuti thermometer inasonyeza -30 digiri Celcius!

Mu 1940 ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa m’Finland. Kenako Mboni zachinyamata zochuluka Zachifinishi zinaponyedwa m’ndende ndi kukakamizidwa kukhala mmenemo m’mikhalidwe yauchinyama. Mwamwaŵi, ndinakhoza kutumikirabe mipingo m’nthaŵi yonseyo ya nkhondo yadziko yachiŵiri, kuyambira 1939 mpaka 1945. Zimenezi kaŵirikaŵiri zinandichititsa kukhala kutali ndi Sylvi ndi Arto kwa miyezi nthaŵi zina. Ndiponso, panali chiwopsezo chanthaŵi zonse chakuti ndikamangidwa chifukwa cha kuchita ntchito yoletsedwa.

Ndiyenera kukhala ndinali munthu wonyumwitsadi, ndikumatchova njinga yolemera ndi sutukesi, chola cha mabuku, ndi galamafoni ndi malekodi. Chifukwa china chimene ndinanyamulira galamafoni chinali cha kupereka umboni nditamangidwa, wakuti sindinali mzondi waparachuti wa ku Russia. Mwaona nanga, ndikanatsutsa kuti ngati ndikadakhala mzondi waparachuti, malekodiwo akadasweka polumpha.

Komabe, panthaŵi ina pochezera mudzi wapafupi umene unachenjezedwa za mzondi, banja la Mboni linandiyesa mzondi. Ndinagogoda pakhomo lawo usiku m’chisanu, ndipo anachita mantha kwambiri kuti anditsegulire. Motero usikuwo ndinagona m’khola, nditadziloŵetsa muudzu wodya ziŵeto kuti ndifunditsidwe. Mmaŵa mwake ndinazindikiridwa bwino, ndipo kunena zowona, m’kucheza kwanga konseko, ziŵalo za banjalo zinandikomera mtima mwapadera kwambiri!

Mkati mwa zaka zankhondo, Mbale Johannes Koskinen yekha ndi ine ndife tinatumikira mipingo m’chigawo chapakati ndi chakumpoto kwa Finland. Aliyense wa ife anali ndi madera aakulu owasamalira, pafupifupi makilomita 600 utali wake. Tinali ndi mipingo yochuluka kwambiri yoichezera kwakuti tinali okhoza kukhala kwa masiku aŵiri kapena atatu okha pampingo uliwonse. Sitima kaŵirikaŵiri sizinali kusunga nthaŵi, ndipo mabasi anali oŵerengeka ndi odzala anthu kwambiri kwakuti zinali zozizwitsa mmene tinafikira kumene tinkapita.

Kupulumuka Tsoka Lili Nenene

Tsiku lina, kuchiyambi kwa Nkhondo ya m’Chisanuyo, ndinapita ku ofesi yanthambi mu Helsinki ndi kutenga mabokosi olemera anayi amabuku oletsedwa kuti ndipite nawo pasitima kukagaŵira mipingo. Pamene ndinali pasiteshoni ya sitima ya Riihimäki, tinamva kulira kwa belu lochenjeza za kuukira kwa ndege zankhondo. Asilikali omwe anali m’sitima anavala malaya awo a m’chisanu, ndipo apaulendo anauzidwa kutuluka m’sitima ndi kuthaŵira m’munda wopanda kanthu pandunji pa siteshoniyo.

Ndinapempha asilikaliwo kunyamula mabokosi angawo, nditawauza kuti anali ofunika kwambiri. Anayi ananyamula mabokosiwo limodzilimodzi, ndipo tinathamanga kwa mamita 200 m’mundawo wokutidwa ndi chipale. Ndiyeno tinadzigwetsera pansi, ndipo munthu wina anafuula kwa ine nati: “Iwe apo, usasunthe pamenepo! Oponya mabombawo akaona kusuntha kulikonse, adzatiponyera mabomba.” Ndinachita chidwi kwambiri moti ndinalimba mtima ndi kutembenuka mosamalitsa kupenya kumwamba, kumene ndinaŵerenga ndege zokwanira 28!

Mwadzidzidzi nthaka inagwedezeka ndi kuphulika kwa mabomba. Ngakhale kuti siteshoniyo sinaphulitsidwe, sitima imene tinafika nayo inaphulitsidwa. Ndipo anali maonekedwe owopsa chotani nanga kuona sitima yopasulidwayo ndi njanje zopotokapotoka! Mmaŵa mwake ndinakhoza kupitiriza ndi ulendo wanga ndi mabokosi angawo, ndipo asilikaliwo anapitirizanso ndi ulendo wawo pasitima ina. Mmodzi wa iwo anakhala Mboni pambuyo pankhondoyo, ndipo anandiuza kuti asilikali aja adakambitsirana pambuyo pake za munthu wodabwitsa uja ndi mabokosi ake.

Nthaŵi ina pambuyo pake Mbale Koskinen, ali paulendo wokachezera mpingo wina waung’ono mu Rovaniemi kumpoto kwa Finland, anamangidwa asanatsike m’sitima. Anatengeredwa kundende, kumene anachitidwa nkhanza moipitsitsa. Pamene nthaŵi yanga inafika yakutumikira mpingo umodzimodziwo, ndinalinganiza kuchoka m’sitimayo pakasiteshoni kakang’ono ka Koivu. Kumeneko Mlongo Helmi Pallari anapanga makonzedwe akuti ndipitirize ndi ulendo wotsalawo m’ngolo yonyamula mkaka. Kuchezera kwanga Mpingo wa Rovaniemi kunali kwachipambano. Komabe, pochoka ndinaloŵa m’mavuto.

Tili paulendo womka ku siteshoni ya sitima, ine ndi mnzanga woyenda naye tinakumana ndi maofesala ankhondo aŵiri omwe anali kuona zipepala za odutsa onse. “Usawayang’ane kumaso. Ingopenya kutsogolo,” ndinatero. Tinadutsa pakati pawo monga kuti sanalipo. Ndiyeno anayamba kutilondola. Potsirizira pake, pasiteshoni yasitima, ndinakhoza kuwazemba mkati mwa anthu ndi kulumphira m’sitima yoyenda. Eya, panali zosangalatsa zambiri m’ntchito yoyendayenda m’masiku amenewo!

Panthaŵi ina ndinamangidwa ndi kutengeredwa ku bungwe losankha ankhondo. Cholinga chinali chonditumiza kubwalo lankhondo. Koma lamya inalira, ndipo ofesala wankhondo yemwe anayenera kundifunsa mafunso anayankha. Ndinakhoza kumva liwu lake palamyapo likufuula kuti: “Kodi mwatani kumangotitumizira amuna odwala ndi opanda pakeŵa? Sitimachita nawo kanthu koma kumangowabweza chabe. Tikufuna amuna amphamvu okhoza kugwira ntchito!” Mwamwaŵi, ndinali ndi chikalata chakuchipatala cha matenda anga. Pamene ndinachisonyeza, ndinaloledwa kupita, motero ndinapitiriza ntchito yanga mosadodometsedwa pakati pa mipingoyo!

Kuthandiza Pozenga Mlandu

Mantha ankhondo anapitirizabe kukula, ndipo bwenzi langa Ahti Laeste anamangidwa. Mkazi wake anandiitana. Pamene ndinapita kunyumba kwawo, ndinapeza pakati pazikalata zake chikalata chochokera ku polisi yakumakolo chololeza Ahti kupereka nkhani zojambulidwa m’mapaki a anthu onse a mzindawo. Tinafika ku bwalo la milandu ndi chikalatacho. Mlanduwo utaŵerengedwa, ndinapatsa Mbale Laeste chikalatacho. Woweruzayo anauza msilikali kubweretsa galamafoni ndi malekodi angapo a nkhani za Baibulo zojambulidwa kuti bwalo la milandu limvetsere. Atamvetsera nkhani iliyonse, woweruzayo anati sanaone cholakwa chilichonse ndi zimene zinanenedwa.

Ndiyeno Ahti, mkazi wake, ndi ine tinauzidwa kutuluka ndi kukayembekeza chigamulo cha bwalo la milandu m’likole. Tinadikirira mmenemo mitima ili m’mwamba osadziŵa chotulukapo chake. Pomalizira pake tinamva liwu likumati: “Wamlanduwe, chonde loŵa m’bwalo la milandu.” Mbale Laeste anamasulidwa! Mitima yathu inasefukira ndi chiyamikiro kwa Yehova pamene tinapitiriza ndi ntchito yathu, Mbale ndi Mlongo Laeste ndi ntchito yawo m’mipingo yakumaloko, ndipo nanenso ndi ntchito yanga yoyendayenda.

Nkhondo Itha​—Utumiki Wathu Upitiriza

Chiletso pantchito yathu yolalikira chinachotsedwa pamene nkhondo inatha, ndipo abale anamasulidwa m’ndende. Mkati mwa zaka zanga zambiri za utumiki, ndakondweretsedwa kwambiri ndi mbali imene alongo athu Achikristu aichita m’ntchito ya Ufumu ndi m’kuchirikiza amuna awo. Makamaka ndakhala woyamikira kaamba ka zolepa ndi chichirikizo cha Sylvi. Monga chotulukapo, ndinali wokhoza kupitiriza m’ntchito yoyendayenda kwa zaka 33 mosadodometsedwa ndipo pambuyo pake ndinakatumikira monga mpainiya wapadera.

Tonse aŵiri ineyo ndi Sylvi tinalimbikitsa Arto kuyamba upainiya pamene anamaliza sukulu, kuphunzira Chingelezi, ndi kupita ku Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower mu United States. Iye anamaliza maphunziro a Gileadi mu 1953. Pambuyo pake anakwatira Eeva, ndipo aŵiriwo achitira pamodzi mitundu yosiyanasiyana ya utumiki wanthaŵi yonse, kuphatikizapo ntchito ya m’dera, utumiki wa pa Beteli, ndi upainiya wapadera. Mu 1988 anasamukira ku Tampere, mzinda womwe tikukhalamo, kudzathandiza kusamalira Sylvi ndi ine pamene akupitiriza kutumikira monga apainiya apadera.

Sylvi ndi ine tasangalala ndi moyo wolemeretsa ndi wodalitsidwa limodzi ndi zikumbukiro zambirimbiri zotilimbikitsa, ngakhale kuti nyonga yathu tsopano ikutha kwambiri. Kuli kolimbikitsa kulingalira za chiwonjezeko chimene taona. Pamene ndinayamba kuchezera mipingo mu 1939, munali ofalitsa a Ufumu okwanira 865 m’Finland, koma tsopano alimo oposa 18,000!

Sindinazindikire konse pamene ndinayamba utumiki wanthaŵi yonse kalelo mu 1938 kuti pambuyo pa zaka 55 ndikakhalabe ndikusangalala ndi ntchitoyi. Chinkana kuti takalamba, tikupitirizabe mwa mphamvu ya Yehova, tikumapenya kutsogolo pamphotho yathu yolonjezedwa. Tikukhulupirira mawu a wamasalmo akuti: “Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimamka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.”​—Salmo 100:5.

[Chithunzi patsamba 21]

Leo ndi Sylvi Kallio anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova mu 1934

[Chithunzi patsamba 23]

Chithunzithunzi chaposachedwa cha Leo ndi Sylvi pamene akufikira zaka 60 za utumiki wopatuliridwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena