Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 5/15 tsamba 26-27
  • Sanali Wokalamba Kwambiri Kosakhoza Kutumikira Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sanali Wokalamba Kwambiri Kosakhoza Kutumikira Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Sanachoka ku Kachisi”
  • Dalitso la Mwadzidzidzi
  • Chitsanzo Chabwino cha Anna
  • Mphunzitsi Anasintha Maganizo Ake
    Galamukani!—2009
  • Latvia Alabadira Uthenga Wabwino
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Iwo Ndi Okalamba Koma Akubalabe Zipatso Zauzimu
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Tumikirani Yehova Masiku Oipa Asanafike
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 5/15 tsamba 26-27

Sanali Wokalamba Kwambiri Kosakhoza Kutumikira Yehova

ANTHU ambiri okalamba amalingalira kuti zaka zawo zotsalazo nzopanda chimwemwe. Mkazi wina wokalamba wochita maseŵero ananenadi kuti: “Ndawononga kale moyo wanga, ndipo sindingathenso kuusintha . . . Pamene ndimka kokayenda ndili ndekha, ndimaganiza za moyo wanga kumbuyoko, ndipo sindikukondwera ndi zimene ndinachita nawo . . . Ndili wosakhazikika maganizo ndi wosakhoza kukhazikika pamalo amodzi.”

Mkazi wina wokalamba amene anakhalako zoposa zaka 2,000 zapitazo analibe vuto la mtundu umenewo. Iye anali mkazi wamasiye wa zaka zakubadwa 84, koma anali wokangalika, wachimwemwe, ndi woyanjidwa kwambiri ndi Mulungu. Dzina lake anali Anna, ndipo iye anali ndi chifukwa chapadera chokhalira wosangalala. Kodi icho chinali chiyani?

“Sanachoka ku Kachisi”

Wolemba Uthenga Wabwino Luka amatidziŵitsa za Anna. “Ndipo,” iye amatero, “panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanueli, wa fuko la Aseri” mu Israyeli. Monga mneneri wamkazi, iye anali ndi mphatso ya mzimu wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, m’lingaliro lapadera. Ndipo Anna anali ndi mwaŵi waukulu wa kulosera pachochitika china chapadera.

Luka akufotokoza kuti: “Anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake, zaka zisanu ndi ziŵiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinayi.” (Luka 2:36, 37) Mwinamwake Anna anakhala mkazi wamasiye pamene anali wachichepere ndithu. Akazi Achikristu amene ali amasiye ausinkhu uliwonse amadziŵa mmene kuferedwa ndi mwamuna wokondedwa kulili koswetsa mtima. Komabe, mofanana ndi akazi ambiri aumulungu a m’tsiku lathu, Anna sanalole chokumana nacho chomvetsa chisoni chimenechi kuletsa utumiki wake kwa Mulungu.

Luka akutiuza kuti Anna “sanachoka ku kachisi” mu Yerusalemu. (Luka 2:37) Iye anazindikira mwamphamvu madalitso amene amadza muutumiki wa panyumba ya Mulungu. Zochita zake zinasonyeza kuti iye, mofanana ndi mfumu ya Israyeli ya masalmo Davide, anali ndi chinthu chimodzi chopempha kwa Yehova. Ndipo kodi chimenecho chinali chiyani? Davide anaimba kuti: “Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi: kuti ndikhalitse m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m’kachisi wake.” (Salmo 27:4) Kumbali imeneyinso, Anna n’ngwofanana ndi akazi Achikristu lerolino amene amapeza chisangalalo m’kukhala pamalo olambirira Yehova nthaŵi zonse.

Anna anapereka utumiki wopatulika kwa Yehova usiku ndi usana. Iye anachita zimenezi “ndi kusala kudya ndi kupemphera,” kusonyeza kulira ndi chikhumbo champhamvu. (Luka 2:37) Kulamuliridwa kwa Ayuda ndi Akunja kwa zaka mazana ambiri, limodzi ndi kunyonyotsoka kwa mikhalidwe ya chipembedzo kumene kunayambukira kachisi ndi ansembe ake, kungakhalenso zina zochititsa Anna kusala kudya ndi kupembedzera Yehova Mulungu. Koma iye analinso ndi chifukwa chokhalira wachimwemwe, makamaka chifukwa cha kanthu kena kachilendo kamene kanachitika patsiku losaiŵalikalo m’chaka cha 2 B.C.E.

Dalitso la Mwadzidzidzi

Patsiku lofunika kwambiri limeneli, khandalo Yesu linabweretsedwa ku kachisi wa ku Yerusalemu ndi amake, Mariya, ndi atate wake womlera, Yosefe. Simeoni wokalambayo anaona khandalo nalankhula mawu olosera pachochitikacho. (Luka 2:25-35) Anna anali pa kachisipo monga mwa nthaŵi zonse. “Ndipo iye,” akusimba motero Luka, “anafikako pa nthaŵi yomweyo.” (Luka 2:38) Anna ayenera kukhala wokondwera chotani nanga pamene maso ake aukalambawo anaona Mesiya wamtsogolo!

Masiku 40 pambuyo pake, mngelo wa Mulungu anachititsa abusa omwe anali pafupi ndi Betelehemu kudabwa ndi mawu akuti: “Onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse; pakuti wakubadwirani inu lero, m’mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.” Gulu la kumwamba linatamanda Yehova ndi kuwonjezera kuti: “Ulemerero ukhale kwa Mulungu kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.” (Luka 2:8-14) Mofananamo, Anna tsopano anasonkhezereka kuchitira umboni wonena za Uyo amene akakhala Mesiya!

Ataona Yesu khandalo, Anna “[anayamba kuthokoza, NW] Mulungu, nalankhula za [mwanayo, NW] kwa anthu onse akuyembekeza chiwombolo cha Yerusalemu.” (Luka 2:38) Mofanana ndi Simeoni wokalambayo, amenenso anali ndi mwaŵi wa kuona khandalo Yesu pakachisi, mosakayikira Anna anali kulakalaka, kupemphera, ndi kuyembekezera Mombolo wolonjezedwayo. Mbiri yabwino yakuti Yesu anali Munthuyo inali yabwino kwambiri kwa iye kwakuti sakanatha kuibisa.

Ngakhale kuti mwina Anna sanayembekezere kuti adzakhala wa moyo pamene Yesu akakula, kodi iye anachitanji? Anachitira umboni mwachisangalalo kwa ena wonena za kumasulidwa koyandikira koti kuchitike kupyolera mwa Mesiya wakudza ameneyu.

Chitsanzo Chabwino cha Anna

Kodi ndi anthu angati achipembedzo a dziko amene angapereke umboni wotero kapena amene angalambirebe usiku ndi usana pausinkhu za zaka 84? Mwachionekere, iwo angafune kupatsidwa ndalama zolandira atapuma pantchito pambuyo pake. Anna ndi Simeoni sanali otero. Iwo anaika zitsanzo zabwino kwa atumiki onse okalamba a Yehova. Ndithudi, iwowa anakonda nyumba ya Yehova yolambiriramo ndi kumtamanda ndi mtima wawo wonse.

Mwa Anna tili ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha mkazi wamasiye waumulungu. Kwenikweni, mafotokozedwe a Luka ponena za mkazi wokalamba ameneyu wodzichepetsa amagwirizana bwino lomwe ndi ziyeneretso za mkazi wamasiye woyenerera zofotokozedwa pa 1 Timoteo 5:3-16. Pamenepo mtumwi Paulo amanena kuti mkazi wamasiye wotero “[ama]khalabe m’mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana,” ali “mkazi wa mwamuna mmodzi,” ndipo ‘wotsatadi ntchito zonse zabwino.’ Anna anali mkazi wotero.

Lerolino, timapeza akazi amasiye okalamba opereka utumiki wopatulika kwa Mulungu usiku ndi usana m’mipingo mazana ambiri ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi. Timayamikira chotani nanga kukhala ndi “Aanna” amakono ameneŵa pakati pathu!

Ngakhale pausinkhu waukalamba, amuna ndi akazi akhoza kudzipatulira kwa Mulungu ndi kukusonyeza mwa ubatizo wa m’madzi. Okalamba sali achikulire kwakuti sangakhoze kutumikira Yehova ndi kuchitira umboni za Ufumu Waumesiya umene tsopano ukulamulira kumwamba ndi umene posachedwapa udzadzetsa madalitso aakulu kwa anthu omvera. Anthu okalamba amene tsopano akupereka utumiki wopatulika kwa Mulungu akhoza kulandira dalitso la Yehova, monga momwedi Anna anadalitsidwira zaka mazana zapitazo. Iye sanali wokalamba kwambiri kosakhoza kutumikira Yehova ndi kutamanda dzina lake loyera​—ndipo nawonso sali otero.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena