Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 6/1 tsamba 3-4
  • Kodi Nkukhaliranji Okondweretsedwa ndi Chipembedzo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nkukhaliranji Okondweretsedwa ndi Chipembedzo?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chipembedzo Chingakhutiritse Zosowa Zathu?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Nkuchitengeranji Mosamalitsa Chipembedzo?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mmene Mungapezere Zinthu Zauzimu Zimene Mumafunikira
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 6/1 tsamba 3-4

Kodi Nkukhaliranji Okondweretsedwa ndi Chipembedzo?

M’DZIKO lililonse pankhope ya dziko lapansi, pali kukondwera ndi chipembedzo. Kumbali ina, palinso ambiri amene amanena mosabisa mawu kuti samakondwera ndi chipembedzo. Koma kodi nthaŵi zonse akhala akulingalira motero?

Chibadwa cha anthu nchakuti munthu samakhutira kwenikweni ndi zinthu zakuthupi zokha. Anthu amafunikira zinthu zauzimu. Kukhalapo kwa tsiku ndi tsiku kumene kuli kozikidwa pa kupeza chabe zinthu zakuthupi, limodzi ndi nyengo za kusanguluka za kamodzikamodzi, sikumakhutiritsa mokwanira chosoŵa chamkati cha munthu. Mosiyana ndi zinyama, anthu amafuna kudziŵa kuti, ‘Kodi chifuno cha moyo nchiyani?’ ‘Moyo waufupiwu, umene umaphatikizapo zambiri zimene zili zokongola ndiponso zambiri zimene zili zoipa, kodi ndiwo wokha umene ulipo?’ Kodi simunafunsepo mafunso onga ameneŵa?

Komabe, mamiliyoni ambiri a anthu amene ali ndi moyo lerolino anakulira m’malo amene kukondwerera kulikonse kwatanthauzo m’chipembedzo kunafooledwa. Chisonkhezero chimenecho chingakhale chinachokera kwa makolo awo, kwa aphunzitsi, kwa ausinkhu wawo, kapena ngakhale ku boma.

Skalabrino, mwamuna wachichepere wa ku Albania, analongosola kuti pansi pa ulamuliro wa Chikomyunizimu anthu anaphunzitsidwa kuti kulibe Mulungu. Ndiponso, kunali kwaupandu kwa iwo kulankhula za chipembedzo; kuchita zimenezo kukanatsogolera ku kuikidwa m’ndende. Komabe, mu 1991, pamene anali ku Switzerland monga wothaŵa kwawo, anapatsidwa mwaŵi wa kuphunzira Baibulo. Iye anavomera. Chifukwa ninji?

Eya, mu Albania iye anali atamva kuti kuli buku lotchedwa Baibulo, koma sanadziŵe kwenikweni kalikonse ponena za ilo. Motero, poyamba sichinali kwakukulukulu chikhumbo cha kumvetsetsa Baibulo chimene chinamsonkhezera. Pamene kuli kwakuti anauzidwa kuti akaphunzira ponena za chifuno cha Mulungu kwa mtundu wa anthu ndi dziko lapansi, iye anauwonanso kukhala mwaŵi wakuwongolera kalankhulidwe kake ka chinenero chakumaloko. Komabe, mofulumira, anapeza kuti zimene anali kuphunzira zinakhutiritsa chilakolako chake chakuya chauzimu. Mtima wake unakondwera ndi lonjezo la Mulungu la dziko latsopano mmene mudzakhala mtendere wochuluka, m’dziko limene anthu adzakhala ndi moyo kosatha ndi kusangalala ndi unyinji wa zinthu zonse zofunika za moyo. Chikondwerero chake chinawonjezereka pamene anaphunzira kuti iye ndi banja lake angakhale mbali ya dziko latsopano limeneli. Atalephera kusunga mbiri yabwino imeneyi kwa iye yekha, anaimbira foni banja lake mu Albania kuwauza mbiriyo.

Aleksei, amene amakhala m’Russia, anadabwanso ndi chiyambukiro chimene chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chingakhale nacho pa moyo wa munthu. Atathedwa nzeru ndi mavuto ndi kulephera kupeza yankho lokhutiritsa la chifuno cha moyo, iye analingalira za kudzipha. Komabe, poyamba, anapita ku Finland kukachezera mnzake. Ali paulendowo m’sitima, anauza apaulendo ena za mavuto akewo. Pakati pawo panali mmodzi wa Mboni za Yehova, amene anamsonkhezera kuphunzira Baibulo chifukwa chakuti limapereka mayankho a mavuto oterowo. Iye anali kukayikira. Ali paulendo wake wobwerera, anakumana ndi zofananazo. Panthaŵiyi inali Mboni ina imene inalankhula momvekera bwino ndi kumuuza kuti nayonso inakhalapo kale ndi mavuto ofananawo koma Baibulo linaithandiza kuwalaka. Mkazi ameneyunso anamlimbikitsa kuphunzira Baibulo. Pamene anafika kunyumba, foni inalira. Linali bwenzi lina, lomwe linali kuphunzira ndi Mboni ndipo linali lachimwemwe kwambiri. Mwamunayu anayamba kuzindikira kuti mwinamwake Baibulo lingaperekedi zimene anafuna, koma anadziŵa kuti popanda chithandizo sangalimvetsetse. Anavomera kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba lokhazikika ndi Mboni za Yehova, ndipo anayamba kufika pamisonkhano yawo. Sizinamtengere nthaŵi yaitali kuzindikira chifukwa chake awo amene amaumba miyoyo yawo mogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa ali achimwemwe kwambiri, ngakhale kuti nawonso amayang’anizana ndi mavuto ofala kwa anthu.

Akumazindikira chibadwa cha anthu, Yesu Kristu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi mkate wokha.” (Mateyu 4:4, The New English Bible) Iye anatinso: “Odala ali osauka mumzimu.” (Mateyu 5:3) Amakhala achimwemwe chifukwa chakuti amazindikira mwachidwi kusoŵa kwawo, kutenga njira zofunikira kuchikhutiritsa, ndi kulandira dalitso la Mulungu. Komabe, kusoŵa kwathu kwauzimu sikumakhutiritsidwa mwa kungogwirizana ndi tchalitchi kapena kufika pa misonkhano ina yachipembedzo. Chipembedzo chimene kwakukulukulu chili cha mwambo chingakope maganizo, koma kodi chimapereka mayankho enieni a mavuto a moyo? Ngakhale ngati chipembedzo chimachirikiza malingaliro ena ake amene ali abwino, ngati chilephera kupereka chidziŵitso chenicheni cha chifuno cha moyo, kodi chidzakhutiritsa chosoŵa chanu chauzimu? Chodetsa nkhaŵa kwambiri nchakuti, kodi kulondola chipembedzo choterocho kudzatsogolera ku unansi wabwino ndi Mulungu? Popanda zimenezo, chikhutiro chenicheni sichidzakhalapo.

Pa chifukwa chimenechi anthu ambiri akufunafuna chinachake chimene sanachipezebe.

[Chithunzi patsamba 3]

Kodi zosoŵa zanu zauzimu zidzakhutiritsidwadi mwa kugwirizana ndi tchalitchi?

[Chithunzi patsamba 4]

Ambiri apeza kuti pamene amvetsetsa Baibulo, moyo umakhala ndi tanthauzo latsopano

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena