Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 6/15 tsamba 8-11
  • Kodi Mumakondwera ndi Phunziro Laumwini?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumakondwera ndi Phunziro Laumwini?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anawonjezeranso Nyonga Yawo Kupyolera m’Phunziro Laumwini
  • Lolani Utumiki Ukhale Chisonkhezero
  • Nthaŵi Zonse Idyani Mawu a Mulungu
  • Malingaliro Ena Anzeru
  • Khalani Ofunitsitsa Kuphunzira
  • Tsanzirani Chitsanzo cha Mfumu
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Muziyesetsa Kuti Kuphunzira Kuzikuthandizani!
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kupindula ndi Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Phunziro Limapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 6/15 tsamba 8-11

Kodi Mumakondwera ndi Phunziro Laumwini?

MTUMIKI aliyense woona mtima wa Mulungu angasangalale kuthera nthaŵi yaikulu pa phunziro laumwini la Baibulo. (Salmo 1:1, 2) Komabe, pokhala ndi zambiri zofuna nthaŵi ndi nyonga yawo, ambiri amakupeza kukhala kovuta kuthera nthaŵi ndi nyonga zochuluka pa phunziro laumwini monga momwe angafunire.

Komabe, kuti apitirize monga atumiki okangalika a Mulungu, onse afunikira kupangitsa chisangalalo chawo ndi nyonga kukhalanso zatsopano tsiku ndi tsiku mwa kupeza mbali zatsopano kapena zakuya za choonadi cha Mawu a Mulungu. Choonadi cha Baibulo chimene chinakusonkhezerani mwakuya zaka zimene zapitazo chingakhale chisakukusonkhezerani kwambiri tsopano. Chifukwa chake, nkwabwino, nkofunika ndithu, kuti tipange kuyesayesa kwenikweni ndi kosalekeza kwa kupeza chidziŵitso chatsopano cha choonadi kotero kuti tipitirize kudzisonkhezera mwauzimu.

Kodi amuna a chikhulupiriro akale anadzilimbitsa motani mwauzimu kupyolera m’phunziro laumwini la Mawu a Mulungu? Kodi ena a atumiki amakono a Yehova amapanga motani phunziro lawo kukhala lokondweretsa ndi lobala zipatso? Kodi afupidwa motani chifukwa cha zoyesayesa zawo?

Anawonjezeranso Nyonga Yawo Kupyolera m’Phunziro Laumwini

Mfumu Yosiya ya Yuda inayamba mkupiti wake wolimbana ndi kulambira mafano ndi changu chachikulu kwambiri pambuyo pa kuŵerengeredwa ‘buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.’ Mosakayikira imeneyo sinali nthaŵi yoyamba imene anaŵerenga mbali imeneyi ya Mawu a Mulungu; koma kumva uthengawo mwachindunji kuchokera m’malembo apamanja oyambirira kunamsonkhezera m’nkhondo yake yomenyera kulambira koyera.​—2 Mbiri 34:14-19.

Mneneri Danieli anazindikira ‘chiŵerengero cha zaka za kukwaniritsa kupasulidwa kwa Yerusalemu’ ndi kutsimikizirika kwake osati m’buku la Yeremiya lokha komanso “mwa mabuku.” Mothekera kwenikweni ameneŵa anaphatikizapo mabuku onga Levitiko (26:34, 35), Yesaya (44:26-28), Hoseya (14:4-7), ndi Amosi (9:13-15). Zimene anatsimikizira mwa kuphunzira kwake mwakhama mabuku a Baibulo zinatsogolera munthu wopembedza ameneyu kufunafuna Mulungu mwa pemphero laphamphu. Pembedzero lake loona mtima linayankhidwa ndi vumbulutso ndi chitsimikiziro chowonjezereka ponena za mzinda wa Yerusalemu limodzi ndi anthu ake.​—Danieli, chaputala 9.

Yosiya, amene anachita “zoongoka pamaso pa Yehova,” ndi Danieli, amene anali ‘wokondedwa kwambiri’ pamaso pa Mulungu, sanali osiyana kwenikweni ndi ife lerolino. (2 Mafumu 22:2; Danieli 9:23) Zoyesayesa zawo zaumwini m’phunziro laphamphu la Malemba amene analipo panthaŵiyo zinawatsogolera ku uzimu waukulu kwambiri ndi kuwathandiza kukhala ndi zomangira zolimba kwambiri ndi Mulungu. Zofananazo zinganenedwe kwa atumiki ena akale ambiri a Yehova, monga ngati Yefita, wamasalmo wa nyumba ya Asafu, Nehemiya, ndi Stefano. Onsewa anapereka umboni wa phunziro laumwini losamalitsa la mbali ya Baibulo imene inalipo m’nthaŵi yawo.​—Oweruza 11:14-27; Masalmo 79, 80; Nehemiya 1:8-10; 8:9-12; 13:29-31; Machitidwe 6:15–7:53.

Lolani Utumiki Ukhale Chisonkhezero

Atumiki ochuluka a Yehova lerolino amene amtumikira kwa zaka zambiri ali ndi ndandanda ya phunziro laumwini la Baibulo. Iwo apeza zimenezi kukhala zofunika kuti akhalebe ogalamuka ndi kukwaniritsa kotheratu mathayo awo Achikristu. Ngakhale zili choncho, ambiri a iwo amavomereza kuti nthaŵi zonse sizimakhala zokhweka kulinganiza nthaŵi ndi nyonga yogwiritsiridwa ntchito pakati pa kuphunzira ndi zinthu zina zimene siziyenera kunyalanyazidwa.

Chikhalirechobe, kukhala maso mwauzimu mwa phunziro laumwini lakhama kuli kofunika pochita ndi zosoŵa mu utumiki Wachikristu pa nthaŵi ino ya mkhalidwe wopita patsogolo wa ntchito yolalikira Ufumu ya padziko lonse. Awo amene amakondwera ndi chidziŵitso chatsopano ndi chakuya kwambiri cha Mawu a Mulungu angakwaniritse chitokoso cha kukhudza mitima ya njala. Zimenezi zili choncho kaya wina wagaŵiridwa kumene angayembekezere kugwira zambiri posodza mwauzimu kapena kumene wina akulimbikira m’magawo amene amafoledwa bwino kumene anthu ambiri amakhala amphwayi.

Nthaŵi Zonse Idyani Mawu a Mulungu

Zimene ena akuchita zingakupatseni malingaliro a mmene mungasangalalire ndi njira yanu ya kuphunzira mowonjezereka kapena mmene inuyo ndi banja lanu mungagwiritsire ntchito mopindulitsa kwambiri nthaŵi yophunzira. Pakati pa zinthu zimene mtumiki wa Mulungu sadzafuna kuphonya ndiko kuŵerenga Mawu a Mulungu enieniwo pa maziko okhazikika. Ambiri apanga chonulirapo cha kuŵerenga pafupifupi machaputala atatu mpaka anayi a Baibulo mlungu uliwonse. Kodi mukufuna kuŵerenga Baibulo lonse m’chaka chimodzi? Pamenepo mudzakhala wachimwemwe kuthera nthaŵi yochuluka mukuliŵerenga, mwinamwake theka la ola pa tsiku.

Kodi munaŵerenga Baibulo lonse koposa kamodzi? Bwanji osadziikira chonulirapo chatsopano nthaŵi yotsatira? Pofuna kusintha, mkazi wina Wachikristu anaŵerenga mabuku a Baibulo mogwirizana ndi dongosolo limene analembedwa. Iye anapeza tsatanetsatane wochuluka, wozikidwa pa kuŵerenga nthaŵi, kumene anaphonya kalelo. Mkazi wina Wachikristu waŵerenga Baibulo kuchokera kuchikuto mpaka chikuto nthaŵi zisanu m’zaka zisanu zapita, nthaŵi iliyonse ali ndi lingaliro losiyana. Nthaŵi yoyamba, anangoliŵerenga lonse. Pamene anali kuŵerenga kachiŵiri, analemba mwachidule za mkati mwa chaputala chilichonse pa mzera umodzi kapena iŵiri m’kope lolembamo manotsi. Kuyambira chaka chachitatu kumka mtsogolo, anayamba kuŵerenga Baibulo lalikulu la zilozero, poyamba akumapenda apa ndi apa zilozero za m’mphepete ndiyeno kupereka chisamaliro chachikulu ku mawu amtsinde limodzinso ndi mawu a zoonjezera. Nthaŵi yachisanu, anagwiritsira ntchito mapu a Baibulo kuonjezera kumvetsetsa kwake mbali za malo. Iye akuti: “Kwa ine, kuŵerenga Baibulo kwakhala kokondweretsa mofanana ndi chakudya.”

Ophunzira Baibulo ena akhama akupeza kukhala kwaphindu kukhala ndi kope la Baibulo logwiritsira ntchito kaamba ka phunziro laumwini lokha, akumalemba mwachidule m’mphepete mwake ndemanga zokondweretsa, mafanizo osonkhezera maganizo, kapena manambala a masamba a zofalitsidwa zina zimene angatembenukireko pambuyo pake. Mtumiki wina wanthaŵi yonse amakuona kukhala kosangalatsa pamapeto a mwezi uliwonse kulemba m’kope lake la phunziro mfundo zatsopano zimene waphunzira mkati mwa mweziwo. “Kuyembekezera maola anga amtengo wake ameneŵa,” iye akutero, “kumandithandiza kufikira zonulirapo zina za mwezi mofulumira kwambiri.”

Malingaliro Ena Anzeru

Kodi mukuganiza kuti ndandanda yanu yadzaza ndi zoyenera kuchitidwa za tsiku ndi tsiku ndi za mlungu ndi mlungu ndi kuti mukufuna chithandizo china pa kugwiritsira ntchito bwino kwambiri nthaŵi yanu yochepa? Eya, nyamulani zimene mukufuna kuŵerenga, ndipo gwiritsirani ntchito mphindi zanu za kupumula. Pa nyumba kapena kumene mumaphunzirira nthaŵi zonse, ku ukulu wothekera linganizani mabuku ndi ziŵiya zina zophunzirira kotero kuti zikhale zosavuta kuzipeza. Pangani malo anu ophunzirira kukhala abwino koma osati abwino kopambanitsa kwakuti mudziwodzera. Kodi muli ndi nkhani yoti mukambe? Ŵerengani nkhaniyo mwamsanga monga momwe kungathekere, ndiyeno lolani malingaliro kubwera pamene mukupumula kapena kuchita ntchito zina.

Ena angagwirizane nanu m’kugwiritsira bwino ntchito nthaŵi kaamba phindu la onse. Mwachitsanzo, mungapemphe wina kukuŵerengerani mofuula zinthu zokhweka pamene mukuchita ntchito yanthaŵi zonse kapena kupatsa tii woŵerenga wanu wokoma mtimayo. Bwanji ngati onse m’nyumba avomereza kukhala ndi nthaŵi yabata ya phunziro laumwini? “Kodi nchiyani chimene mwakondwera kuŵerenga posachedwapa?” Nthaŵi zina mungakhale okhoza kudziŵa zimene mabwenzi anu aŵerenga mwa kuyamba kukambitsirana mwa njira imeneyi.

Kodi mumakondwera ndi kuyambitsa malingaliro atsopano m’programu yanu ya phunziro? Mungaike chonulirapo cha nthaŵi ya kuphunzira mofanana ndi mmene ambiri amaikira chonulirapo cha nthaŵi ya kulankhula ndi ena za Baibulo. Wofalitsa wa nthaŵi yonse (mpainiya) amaika chonulirapo cha mwezi ndi mwezi cha maola a kuphunzira ndipo amakondwera pamene aona tchati cha chonulirapo chake chikukwera. Ena amachepetsa nthaŵi yoonerera wailesi yakanema ndipo mwa njira imeneyo amapeza nthaŵi ya kuphunzira. Ambiri amasankha mutu wophunzira umene amautsatira kwa kanthaŵi, monga ngati zipatso za mzimu, mbiri ya mabuku a Baibulo, kapena luso la kuphunzitsa. Ena amasangalala ndi kupanga matchati a kuŵerengera nthaŵi, monga ngati amene amasonyeza kugwirizana kwa pakati pa mafumu ndi aneneri a Israyeli kapena Machitidwe a Atumwi ndi makalata a Paulo.

Achichepere, kodi mukufuna chikhulupiriro cholimba kwambiri? Bwanji osasankha chofalitsidwa kuti muchiphunzire mosamalitsa mkati mwa tchuthi chanu chotsatira cha sukulu? Wophunzira wobatizidwa wa pa sukulu yasekondale anasankha Mankind’s Search for God, buku lofalitsidwa ndi Watch Tower Society. Iye analemba ndemanga zachidule za zimene anaphunzira mutu ndi mutu. Zinali zovuta ndipo zinatenga nthaŵi yochuluka kuposa mmene analingalira. Komabe, pamene anamaliza buku lonse, anachita chidwi kwambiri ndi kunena zoona kwa uthenga wa Baibulo.

Khalani Ofunitsitsa Kuphunzira

Atumiki a Yehova ochuluka kwambiri amakono ali kale “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akorinto 15:58) Ngakhale mutakhala ndi ndandanda yosinthidwa ndi zoyesayesa zoona mtima, dongosolo limene mumatsatira mkati mwa mlungu silingasinthe kwakukulu. Komabe, kufunitsitsa kwanu kosalephera kwa kumvetsetsa kwambiri choonadi ndi kukhala kwanu mogwirizana ndi zifuno zovumbulidwa za Yehova zidzakhala zothandiza.

Nkolimbikitsa kumva mphotho za awo amene awongolera dongosolo lawo la kuphunzira. Mwamuna wina Wachikristu, atazindikira kuti anali kutaya kaimidwe kabwino kamaganizo kulinga ku kufuna kumvetsetsa kwambiri choonadi, analinganiza moyo wake kotero kuti athere ochuluka a maola ake a kupumula pa phunziro laumwini. “Zandidzetsera chisangalalo chomwe ndinalibe ndi kale lonse,” iye akutero. “Pokhala ndi chidaliro chomakulakula chakuti Baibulo linalembedwa ndi Mulungu, ndimapeza kuti ndingalankhule ndi ena ponena za chikhulupiriro changa motenthedwa maganizo kwenikweni. Ndimadzimva kukhala wodyetsedwa bwino, wolama maganizo mwauzimu, ndi wokhutira pamapeto a tsiku lililonse.”

Woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova, amene amachezera mipingo yambiri, analongosola mapindu ena mwa njira iyi: “Awo amene ali akhama m’phunziro laumwini kaŵirikaŵiri amakhala osangalala ndi olondola m’kalankhulidwe kawo. Iwo amakhala bwino ndi ena, ndipo samapambutsidwa mosavuta ndi ndemanga zosalimbikitsa za ena. Pamene ali muutumiki wakumunda, amakhala okhoza kusintha ndiponso amaso pa zosoŵa za anthu amene akumana nawo.”

Iye akuwonjezera mfundo imene ena angafune kuikumbukira pamene apenda njira yawo ya kuphunzira. “Pa misonkhano yokambitsirana Malemba, ambiri amakonda kuŵerenga ndemanga zawo pa tsamba losindikizidwa. Iwo angapindule kwambiri ngati asinkhasinkha pa mmene nkhaniyo ikugwirizanirana ndi zimene anaphunzira kale kapena ndi miyoyo yawo.” Kodi muganiza kuti mungawongolere m’mbali imeneyi?

Mneneri Danieli, pambuyo pokhala ndi moyo kwa zaka zoposa 90, sanalingalire kuti anamvetsetsa mokwanira njira za Yehova. M’zaka zake zomalizira, iye anafunsa ponena za nkhani imene sanamvetsetse kwambiri kuti: “Nditani Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi nchiyani?” (Danieli 12:8) Mosakayikira kufunitsitsa kosasintha kumeneku kwa kuphunzira choonadi cha Mulungu chowonjezereka kunali mfungulo ya umphumphu wake wopambana mkati mwa njira ya moyo wake yokhala ndi zochitika zambiri.​—Danieli 7:8, 16, 19, 20.

Mtumiki aliyense wa Yehova ali ndi thayo lofananalo la kuchirimika monga mmodzi wa Mboni Zake. Khalani ofunitsitsa nthaŵi zonse kuphunzira kukhala olimba mwauzimu. Yesani kuwonjezera mbali imodzi kapena ziŵiri zatsopano pa ndandanda yanu ya phunziro laumwini ya mlungu ndi mlungu, mwezi ndi mwezi, kapena chaka ndi chaka. Onani mmene Mulungu adzadalitsira kuyesayesa kulikonse kwakung’ono kumene mupanga. Inde, sangalalani ndi phunziro lanu laumwini la Baibulo ndi zotulukapo zimene limabweretsa.​—Salmo 107:43.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena