Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 7/1 tsamba 23-28
  • Kugonjera Mwachimwemwe ku Ulamuliro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugonjera Mwachimwemwe ku Ulamuliro
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugonjera Mofunitsitsa ku Uchifumu wa Yehova
  • Kugonjera Mwachimwemwe kwa Mfumu Yathu
  • Oyang’anira Amamvera Mwachimwemwe
  • Kugonjera Kwateokratiki
  • Kutumikira ndi Chimwemwe
  • Mtendere Umene Umadza ndi Kugonjera Mwachimwemwe
  • Tizigonjera Abusa Achikondi Modzichepetsa
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Abusa ndi Nkhosa M’teokrase
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulemekeza Ulamuliro?
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kristu Amatsogolera Mpingo Wake
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 7/1 tsamba 23-28

Kugonjera Mwachimwemwe ku Ulamuliro

“Mwamvera ndi mtima.”​—AROMA 6:17.

1, 2. (a) Kodi ndi mzimu wotani umene ukuonekera m’dziko lerolino, ndipo kodi nchiyani chimene chili magwero ake ndi ziyambukiro zake? (b) Kodi atumiki odzipatulira a Yehova amasonyeza motani kuti ali osiyana?

“MZIMU wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera” uli woonekera kwambiri lerolino. Ndi mzimu wa kudziimira kosadziletsa, wochokera kwa Satana, “mkulu wa ulamuliro wa [mpweya, NW].” Mzimu umenewu, kapena “mpweya,” kapena mkhalidwe wolamulira wa dyera ndi kusamvera, uli ndi “ulamuliro,” kapena mphamvu, pa anthu ochuluka. Ichi nchimodzi cha zifukwa zimene dziko likuyang’anizirana ndi chimene chatchedwa tsoka la ulamuliro.​—Aefeso 2:2.

2 Mwamwaŵi, atumiki odzipatulira a Yehova lerolino samadzaza mapapu awo auzimu ndi “mpweya” woipa umenewu, kapena mzimu wachipanduko. Iwo amadziŵa kuti “umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.” Mtumwi Paulo akuwonjezera kuti: “Chifukwa chake musakhale olandirana nawo.” (Aefeso 5:6, 7) Mmalomwake, Akristu oona amayesayesa ‘kudzala naye Mzimu [wa Yehova],’ ndipo amamwa “nzeru yochokera kumwamba,” imene ili “yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino.”​—Aefeso 5:17, 18; Yakobo 3:17.

Kugonjera Mofunitsitsa ku Uchifumu wa Yehova

3. Kodi mfungulo ya kugonjera mofunitsitsa n’njotani, ndipo ndi phunziro lalikulu lotani limene mbiri imatiphunzitsa?

3 Mfungulo ya kugonjera mofunitsitsa ndiyo kuzindikira ulamuliro woyenera mwalamulo. Mbiri ya anthu imasonyeza kuti kukana uchifumu wa Yehova sikumadzetsa chimwemwe. Kukana kotero sikunadzetse chimwemwe kwa Adamu ndi Hava, ngakhale kwa wosonkhezera chipanduko chawo, Satana Mdyerekezi. (Genesis 3:16-19) Mumkhalidwe wake wotsika umene alimo tsopano, Satana ali ndi “udani waukulu” chifukwa chakuti akudziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi. (Chivumbulutso 12:12) Mtendere ndi chimwemwe cha anthu, inde, cha chilengedwe chonse, zimadalira pa kuzindikira kwa m’chilengedwe chonse uchifumu wolungama wa Yehova.​—Salmo 103:19-22.

4. (a) Kodi ndi mtundu wotani wa kugonjera ndi kumvera umene Yehova amafuna atumiki ake kusonyeza? (b) Kodi tiyenera kutsimikizira za chiyani, ndipo kodi ndimotani mmene wamasalmo akusonyezera chimenechi?

4 Komabe, chifukwa cha mikhalidwe yake yolinganizika bwino koposa, Yehova samakhutira ndi kumvera kwamphwayi. O, inde, iye n’ngwamphamvu! Koma sali wankhalwe. Iye ndi Mulungu wa chikondi, ndipo amafuna zolengedwa zake zaluntha kumumvera mofunitsitsa, chifukwa cha chikondi. Amafuna kuti izo zigonjere ku uchifumu wake chifukwa chakuti zimasankha ndi mtima wonse kukhala pansi pa ulamuliro wake wolungama ndi woyenera mwalamulo, zili zotsimikizira kuti palibe kanthu kamene kangazikomere kuposa kumumvera kosatha. Mtundu wa munthu amene Yehova amafuna m’chilengedwe chake amagwirizana ndi malingaliro a wamasalmo amene analemba kuti: “Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru; malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima: malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso. Kuwopa Yehova kuli mbe, kwakukhalabe nthaŵi zonse: maweruzo a Yehova ali oona, alungama konsekonse.” (Salmo 19:7-9) Chidaliro chotheratu m’kuyenera ndi kulungama kwa uchifumu wa Yehova​—ndicho chiyenera kukhala mkhalidwe wathu wamaganizo ngati tifuna kukhala m’dziko latsopano la Yehova.

Kugonjera Mwachimwemwe kwa Mfumu Yathu

5. Kodi Yesu anafupidwa motani kaamba ka kumvera kwake, ndipo kodi nchiyani chimene timavomereza mofunitsitsa?

5 Kristu Yesu mwiniyo ali chitsanzo chabwino koposa cha kugonjera kwa Atate wake wakumwamba. Timaŵerenga kuti “anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya [pamtengo wozunzirapo, NW].” Paulo akuwonjezera kuti: “Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse, kuti m’dzina la Yesu, bondo lililonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.” (Afilipi 2:8-11) Inde, timapinda maondo athu mwachimwemwe pamaso pa Mtsogoleri ndi Mfumu yathu yolamulira, Kristu Yesu.​—Mateyu 23:10.

6. Kodi ndimotani mmene Yesu wakhalira mboni ndi mtsogoleri kwa mitundu, ndipo kodi ndimotani mmene “ulamuliro” wake udzapitirizira pambuyo pa chisautso chachikulu?

6 Ponena za Kristu monga Mtsogoleri wathu, Yehova analosera kuti: “Taonani, ndampereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.” (Yesaya 55:4) Mwa utumiki wake wapadziko lapansi ndi mwa kuyang’anira ntchito yolalikira ali kumwamba pambuyo pa imfa ndi kuuka kwake, Yesu wadzisonyeza kukhala “mboni yokhulupirika ndi yoona” ya Atate wake kulinga kwa anthu a mitundu yonse. (Chivumbulutso 3:14; Mateyu 28:18-20) Magulu a mitundu imeneyo akuimiridwa tsopano m’ziŵerengero zomawonjezereka ndi “khamu lalikulu,” limene lidzapulumuka “chisautso chachikulu” pansi pa utsogoleri wa Kristu. (Chivumbulutso 7:9, 14) Koma utsogoleri wa Yesu suthera pamenepo. “Ulamuliro” wake udzakhala wa zaka chikwi. Kwa anthu omvera, adzachita mogwirizana ndi dzina lake lakuti “Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.”​—Yesaya 9:6, 7; Chivumbulutso 20:6.

7. Ngati tifuna kuti Kristu Yesu atitsogolere ku “akasupe a madzi a moyo,” kodi tiyenera kuchitanji mosazengereza, ndipo kodi nchiyani chimene chidzatichititsa kukondedwa ndi Yesu ndi Yehova?

7 Ngati tifuna kupindula ndi “akasupe a madzi a moyo” kumene Mwanawankhosa, Kristu Yesu, akutsogolera anthu olungama, tiyenera mosazengereza kusonyeza ndi machitidwe athu kuti tikugonjera mwachimwemwe ku ulamuliro wake monga Mfumu. (Chivumbulutso 7:17; 22:1, 2; yerekezerani ndi Salmo 2:12.) Yesu ananena kuti: “Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga. Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda.” (Yohane 14:15, 21) Kodi mukufuna kukondedwa ndi Yesu ndi Atate wake? Pamenepo gonjerani ku ulamuliro wawo.

Oyang’anira Amamvera Mwachimwemwe

8, 9. (a) Kodi nchiyani chimene Kristu wapereka kuti mpingo umangiriridwe, ndipo kodi ndi m’mbali ziti zimene amuna ameneŵa ayenera kukhalira zitsanzo za gululo? (b) Kodi kugonjera kwa oyang’anira Achikristu kumaphiphiritsiridwa motani m’buku la Chivumbulutso, ndipo kodi ndimotani mmene ayenera kufunira “mtima womvera” pamene akusamalira nkhani zachiweruzo?

8 “Mpingo umagonjera kwa Kristu.” (NW) Monga Woyang’anira wake, iye wapereka “mphatso mwa amuna” (NW) kuti ‘amangirire’ mpingo. (Aefeso 4:8, 11, 12; 5:24) Amuna akulu ameneŵa amauzidwa ‘kuŵeta gulu la nkhosa lili mwa iwo,’ “osati monga ochita ufumu pa iwo [amene ali choloŵa cha Mulungu, NW], koma okhala zitsanzo za gululo.” (1 Petro 5:1-3) Gululo nla Yehova, ndipo Kristu ndiye “mbusa [wake] wabwino.” (Yohane 10:14) Popeza kuti oyang’anira amayembekezera moyenerera kugwirizanika kofunitsitsa kwa nkhosazo zimene Yehova ndi Kristu awaikizira, iwo eniwo ayenera kukhala zitsanzo zabwino za kugonjera.​—Machitidwe 20:28.

9 M’zaka za zana loyamba, oyang’anira odzozedwa anasonyezedwa mophiphiritsira kukhala ali “m’dzanja,” kapena “pa dzanja” lamanja la Kristu, kusonyeza kugonjera kwawo kwa iye monga Mutu wa mpingo. (Chivumbulutso 1:16, 20; 2:1) Ngakhale lerolino, oyang’anira m’mipingo ya Mboni za Yehova ayenera kugonjera ku chitsogozo cha Kristu ndi ‘kudzichepetsa pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu.’ (1 Petro 5:6) Pamene apemphedwa kusamalira nkhani zachiweruzo, mofanana ndi Solomo m’zaka zake za kukhulupirika, ayenera kupemphera kwa Yehova kuti: “Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa.” (1 Mafumu 3:9) Mtima womvera udzasonkhezera mkulu kufunitsitsa kuona zinthu mmene Yehova ndi Kristu Yesu akuzionera kotero kuti chosankha chopangidwa pa dziko lapansi chifanane kwambiri ndi chija chopangidwa kumwamba.​—Mateyu 18:18-20.

10. Kodi oyang’anira onse ayenera kuyesayesa motani kutsanzira Yesu m’njira imene iye anachitira ndi nkhosa?

10 Mofananamo oyang’anira oyendayenda ndi akulu ampingo amayesayesa kutsanzira Kristu m’njira imene anachitira ndi nkhosa. Mosiyana ndi Afarisi, Yesu sanaumirize malamulo ochuluka amene anali ovuta kutsatira. (Mateyu 23:2-11) Iye anati kwa onga nkhosawo: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:28-30) Pamene zili zoona kuti Mkristu aliyense “adzasenza katundu wake wa iye mwini,” oyang’anira ayenera kukumbukira chitsanzo cha Yesu ndi kuthandiza abale awo kumva kuti katundu wawo wa thayo Lachikristu ali ‘wofeŵa,’ “wopepuka,” ndi wosangalatsa kunyamula.​—Agalatiya 6:5.

Kugonjera Kwateokratiki

11. (a) Kodi ndimotani mmene munthu angalemekezere umutu komano nkusakhala wateokratiki? Perekani chitsanzo. (b) Kodi kukhaladi wateokratiki kumatanthauzanji?

11 Teokrase ndi ulamuliro wa Mulungu. Umaphatikizapo lamulo la mkhalidwe la umutu losonyezedwa pa 1 Akorinto 11:3. Koma umatanthauza zoposa zimenezo. Munthu angaonekere kukhala akusonyeza ulemu kaamba ka umutu komano nkusakhala wateokratiki m’lingaliro lenileni la liwulo. Kodi zimenezi zingakhale choncho motani? Mwachitsanzo, demokrase ndi boma losankhidwa ndi anthu, ndipo wademokrase walongosoledwa kukhala “munthu amene amakhulupirira miyezo ya demokrase.” Munthu anganene kuti ali wademokrase, kutenga mbali m’chisankho, ndipo ngakhale kukhala wandale wachangu. Koma ngati, m’kakhalidwe kake konse, amanyalanyaza mzimu wa demokrase ndi malamulo onse a mkhalidwe ophatikizidwamo, kodi kunganenedwedi kuti ali wademokrase? Mofananamo, kuti akhaledi wateokratiki, munthu ayenera kuchita zoposa kungogonjera ku umutu mwamwambo. Ayenera kutsanzira njira ndi mikhalidwe ya Yehova. Ayeneradi kulamuliridwa ndi Yehova m’njira iliyonse. Ndipo popeza kuti Yehova wapatsa Mwana wake ulamuliro wonse, kukhala wateokratiki kumatanthauzanso kutsanzira Yesu.

12, 13. (a) Kodi nchiyani, makamaka, chimene kukhala wateokratiki kumaphatikizapo? (b) Kodi kugonjera kwateokratiki kumaphatikizapo kumvera malamulo ochuluka? Perekani chitsanzo.

12 Kumbukirani, Yehova amafuna kugonjera kofunitsitsa kosonkhezeredwa ndi chikondi. Imeneyo ndiyo njira yolamulirira chilengedwe. Iye ndiye chitsanzo chenicheni cha chikondi. (1 Yohane 4:8) Kristu Yesu ali “chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake.” (Ahebri 1:3) Amafuna ophunzira ake oona kukondana wina ndi mnzake. (Yohane 15:17) Choncho kukhala wateokratiki kumaphatikizapo osati kungokhala wogonjera komanso kukhala wachikondi. Nkhaniyi ingafotokozedwe mwachidule motere: Teokrase ndi ulamuliro wa Mulungu; Mulungu ndiye chikondi; chotero teokrase ndi ulamuliro wa chikondi.

13 Mkulu wina angaganize kuti, kuti akhale ateokratiki, abale ayenera kumvera malamulo amtundu uliwonse. Akulu ena asandutsa malingaliro operekedwa nthaŵi ndi nthaŵi ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kukhala malamulo. (Mateyu 24:45) Mwachitsanzo, kunalingaliridwa kuti, kuti pakhale kudziŵana mofulumira kwambiri ndi abale mu mpingo, kungakhale bwino nthaŵi zina kusakhala pa mpando umodzimodzi m’Nyumba Yaufumu. Limeneli linali chabe lingaliro lothandiza, osati lamulo lokhwima. Koma akulu ena angakhale ndi chikhoterero cha kulitembenuza kukhala lamulo ndi kuganiza kuti awo amene samalitsatira saali ateokratiki. Komabe, pangakhale zifukwa zabwino zambiri zimene zimachititsa mbale kapena mlongo kusankha kukhala kumbali yakutiyakuti. Ngati mkulu mopanda chikondi salingalira zimenezo, kodi iye mwiniyo akukhaladi wateokratiki? Kuti mukhale ateokratiki, “zanu zonse zichitike m’chikondi.”​—1 Akorinto 16:14.

Kutumikira ndi Chimwemwe

14, 15. (a) Kodi ndimotani mmene akulu angachotsere abale ndi alongo ena chimwemwe chawo potumikira Yehova, ndipo nchifukwa ninji zimenezi sizingakhale zateokratiki? (b) Kodi Yesu anasonyeza motani kuti amayamikira chikondi chosonyezedwa ndi utumiki wathu, koposa unyinji? (c) Kodi nchiyani chimene akulu ayenera kulingalira?

14 Kukhala wateokratiki kumatanthauzanso kutumikira Yehova ndi chimwemwe. Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Amafuna olambira ake kumtumikira mwachimwemwe. Awo amene amaumirira pa malamulo ayenera kukumbukira kuti pakati pa malemba amene Aisrayeli anafunikira ‘kuwasamalira kuwachita’ panali lotsatirali: “Nimukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu m’zonse mudazigwira ndi dzanja lanu.” (Deuteronomo 12:1, 18) Zonse zimene timachita muutumiki wa Yehova ziyenera kukhala zosangalatsa, osati mtolo. Oyang’anira angachite zochuluka kuchititsa abale kukhala okondwera kuchita zimene angathe muutumiki wa Yehova. Mosiyana ndi zimenezo, ngati akulu sasamala, angachotsere abale ena chimwemwe chawo. Mwachitsanzo, ngati akuyerekezera, akumayamikira awo amene afika kapena kupyola pa avareji ya mpingo ya maola otheredwa muumboni ndipo mwanjira ina nkumasuliza awo amene sanafikepo, kodi awo amene angakhale anali ndi chifukwa chabwino choperekera lipoti lotsika kwambiri angamve motani? Kodi zimenezi sizingawachititse kudzimva aliwongo mosafunikira ndi kuwachotsera chimwemwe chawo?

15 Maola oŵerengeka amene ena angapereke kuchitira umboni poyera angakhale kuyesayesa kokulirapo kuposa maola ambiri amene ena amathera muulaliki, polingalira za usinkhu waung’ono, thanzi labwinopo, ndi mikhalidwe ina. Pambali imeneyi, akulu sayenera kuwaweruza. Ndithudi, Atate apereka “mphamvu ya kuchita mlandu” kwa Yesu. (Yohane 5:27) Kodi Yesu anasuliza mkazi wamasiye wosauka chifukwa chakuti chopereka chake chinali chosafika pa avareji? Ayi, anazindikira zimene timakobiri tiŵiri timeneto tinatayitsa mkaziyo. Tinali “moyo wake wonse.” Timeneto tinasonyeza chikondi chakuya chotani nanga pa Yehova! (Marko 12:41-44) Kodi akulu ayenera kukhala osazindikira mpang’ono pomwe zoyesayesa zachikondi za awo amene zawo zonse sizifika pa “avareji” m’chiŵerengero? Malinga ndi chikondi pa Yehova, zoyesayesa zimenezo zingakhaledi zoposa pa avareji!

16. (a) Ngati akulu agwiritsira ntchito ziŵerengero m’nkhani zawo, nchifukwa ninji afunikira kuzindikira ndi kukhala achikatikati? (b) Kodi abale angathandizidwe bwino motani kuwonjezera utumiki wawo?

16 Tsono kodi ndemanga zimenezi ziyenera kutembenuzidwa kukhala “lamulo” latsopano lakuti ziŵerengero​—ngakhale maavareji​—siziyenera kutchulidwa nkomwe? Kutalitali! Mfundo n’njakuti oyang’anira ayenera kukhala achikatikati ponena za kulimbikitsa abale kufutukula utumiki wawo ndi kuwathandiza kuchita zimene angathe ndi chimwemwe. (Agalatiya 6:4) M’fanizo la Yesu la matalente, mbuyeyo anapereka zinthu zake kwa akapolo ake “kwa iwo onse monga nzeru zawo.” (Mateyu 25:14, 15) Mofananamo akulu ayenera kulingalira za zimene zili zotheka kwa wofalitsa Ufumu aliyense. Zimenezi zimafuna kuzindikira. Zingachitikedi kuti ena akufunikiradi chilimbikitso kuti achite zambiri. Iwo angayamikire chithandizo chokhudza kulinganiza bwino lomwe zochita zawo. Koma mulimonse mmene zingakhalire, ngati angathandizidwe kuchita zimene angathe ndi chimwemwe, mwina chimwemwe chimenecho chidzawalimbitsa kufutukula zochita zawo Zachikristu ngati kutheka.​—Nehemiya 8:10; Salmo 59:16; Yeremiya 20:9.

Mtendere Umene Umadza ndi Kugonjera Mwachimwemwe

17, 18. (a) Kodi ndimotani mmene kugonjera mwachimwemwe kungatidzetsere mtendere ndi chilungamo? (b) Kodi nchiyani chimene chingakhale chathu ngati timveradi malamulo a Mulungu?

17 Kugonjera mwachimwemwe ku uchifumu woyenera mwalamulo wa Yehova kumatidzetsera mtendere wochuluka. Wamasalmo anati m’pemphero kwa Yehova: “Akukonda chilamulo chanu ali nawo mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.” (Salmo 119:165) Mwa kumvera chilamulo cha Mulungu, timapindula. Yehova anauza Aisrayeli kuti: “Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israyeli, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”​—Yesaya 48:17, 18.

18 Nsembe yadipo ya Kristu imatichititsa kukhala pamtendere ndi Mulungu. (2 Akorinto 5:18, 19) Ngati tili ndi chikhulupiriro m’mwazi woombola wa Kristu ndipo timayesayesa mwamphamvu kulimbana ndi zifooko zathu ndi kuchita chifuniro cha Mulungu, timamasuka ku malingaliro aliwongo. (1 Yohane 3:19-23) Chikhulupiriro chotero, chochirikizidwa ndi ntchito, chimatipatsa kaimidwe kolungama pamaso pa Yehova ndi chiyembekezo chabwino koposa cha kupulumuka “chisautso chachikulu” ndi kukhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano la Yehova. (Chivumbulutso 7:14-17; Yohane 3:36; Yakobo 2:22, 23) Zonsezi zikhoza kukhala zathu ‘titangomvera malamulo a Mulungu.’

19. Kodi chimwemwe chathu tsopano ndi chiyembekezo chathu cha moyo wosatha zimadalira pa chiyani, ndipo kodi ndimotani mmene Davide anasonyezera chikhutiro chochokera mumtima?

19 Inde, chimwemwe chathu tsopano ndi chiyembekezo chathu cha moyo wosatha pa dziko lapansi laparadaiso chazikidwa pa kugonjera kwathu mwachimwemwe ku ulamuliro wa Yehova monga Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse. Nthaŵi zonse tiyeni tisonyeze malingaliro a Davide, amene anati: “Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam’mwamba ndi za pa dziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse. Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.”​—1 Mbiri 29:11, 13.

Mfundo Zoyenera Kukumbukira

◻ Kodi ndi mtundu wotani wa kugonjera ndi kumvera umene Yehova amafuna atumiki ake kusonyeza?

◻ Kodi Yesu anafupidwa motani kaamba ka kumvera kwake, ndipo kodi tiyenera kusonyezanji ndi kachitidwe kathu?

◻ Kodi oyang’anira onse ayenera kuyesayesa motani kutsanzira Yesu m’njira imene iye anachitira ndi nkhosa?

◻ Kodi kukhala wateokratiki kumaphatikizapo chiyani?

◻ Kodi kugonjera mwachimwemwe kumatidzetsera madalitso otani?

[Chithunzi patsamba 24]

Akulu amalimbikitsa gulu la nkhosa kuchita zimene angathe mwachimwemwe

[Chithunzi patsamba 26]

Yehova amakondwera ndi awo amene amamumvera ndi mtima wonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena