“Ndasunga Chikhulupiriro”
MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI MABWENZI A BRUNELLA INCONDITI
“LOŴERUKA linali tsiku lochedwa kutha ndi la kusukidwa. Ndinali ndekhandekha m’chipinda, ndili wopanda chiyembekezo. Linali lotayitsa mtima. Zinthu zonse zinali kuyenda bwino, ndipo mwadzidzidzi, monga ngati kuti wina wamenyetsa chitseko ndili pakhomo, ndinasoŵa kotulukira, mosasamala kanthu ndi kuyesayesa kwanga zolimba.”
Kugwiritsidwa mwala kwakukulu kunalefula mtima wa Brunella Inconditi wa zaka 15. Tsiku lofunika koposa m’moyo wake wachichepere linali kutha. Kuchiyambiyambi kwa chaka chimenecho chikondi chake chomakula pa Yehova ndi Baibulo chinamsonkhezera kupatulira moyo wake kwa iye. M’July 1990 anafunikira kubatizidwa pa Msonkhano Wachigawo wa “Chinenero Choyera” wa Mboni za Yehova ku Montreal, Canada. M’malo mwake, Brunella anali pafupi kuyang’anizana ndi chiyeso cha chikhulupiriro chake chimene chikakhalapo moyo wake wonse.
Patatsala masiku aŵiri poyembekezera kusonyeza kudzipatulira kwake mwa ubatizo wa m’madzi, Brunella anadziŵa kuti anali ndi leukemia. Madokotala a ku chipatala cha ana chakumaloko anafuna kuyamba kupereka mankhwala nthaŵi yomweyo, chotero Brunella anakhalabe m’chipatala.
Kudzinenera Kwake Kuchititsa Chidwi Madokotala
Brunella anadziŵa kuti mwazi n’ngwopatulika kwa Yehova Mulungu. (Levitiko 17:11) Makolo ake, Edmondo ndi Nicoletta, anali atafotokoza kuti palibe mwazi uliwonse umene unayenera kugwiritsiridwa ntchito m’mankhwala a mwana wawo. “Brunella anafuna kuti madokotala amve zimenezi kwa iyenso, ngakhale kuti anali mwana,” akukumbukira motero atate wake. “Iye anawauza mwamphamvu kuti sanafune mankhwala amene akaswa lamulo la Baibulo la ‘kusala mwazi.’”—Machitidwe 15:20.
Pa July 10, 1990, madokotala atatu ndi wantchito yothandiza osauka anakumana ndi makolo a Brunella ndi atumiki ena aŵiri a mpingo wa Mboni za Yehova wakumaloko. Kupima kunasonyeza kuti Brunella anali ndi lymphoblastic leukemia yaikulu. Madokotala anafotokoza zimene akachita kulimbana ndi nthendayo. Iwo anafotokoza mwaluso kuti inali yovuta kwambiri kuchiritsa. “Khalidwe la Brunella ndi chitsimikizo chake cha kumvera Mulungu zinakhudza mtima wa madokotala ndi wantchito yothandiza osauka. Anachita chidwi ndi chikondi cha makolo ake ndi chichirikizo cha mabwenzi a mu mpingo Wachikristu. Anayamikiranso mmene tinazindikirira ndi kulemekeza ntchito yawo,” mkulu wina wa mu mpingo akukumbukira motero.
Madokotalawo analinganiza za kupeŵa kuthira mwazi. Brunella akapatsidwa chemotherapy yambiri, koma ikakhala yosapweteka kwambiri monga ya nthaŵi yonse. Zimenezi zikachepetsa kuwonongedwa kwa maselo ake a mwazi kochitidwa ndi mankhwalawo. “Madokotala analingalira zofunika za kuthupi, za malingaliro, ndi zauzimu za Brunella,” akufotokoza motero Nicoletta. “Pamene tinawapempha kukaonana ndi katswiri wodziŵa kuchiritsa leukemia ya ana popanda mwazi, iwo anavomereza.” Brunella ndi ogwira ntchito m’chipatalamo anaumba ubwenzi wamphamvu.
Zonulirapo Zauzimu
Ngakhale kuti mankhwala oyambirira anali ndi zotulukapo zabwino, vuto la Brunella linali chiyambi chabe. Podzafika November wa 1990 nthenda yake inali itachepera, chotero popanda kuchedwa iye anabatizidwa. Polingalira za miyezi ingapo ya kumbuyoko, Brunella anavomereza kuti: “Inali yovuta. Umafunikira nyonga yaikulu, ndipo umafunikira kuganiza bwino. . . . Chikhulupiriro changa chinaikidwa pachiyeso, koma ndinachirimikabe, ndipo ndikulinganizabe kugwira ntchito monga mpainiya wokhazikika [mtumiki wanthaŵi yonse].”
Kuchiyambiyambi kwa 1991, Brunella anadwalanso nthendayo. Anatsala pafupi kufa pamene anali kupatsidwa chemotherapy, koma modabwitsa ndi mosangalatsa onse, iye anachira. Podzafika August anali bwino ndithu kwakuti anathera mweziwo mu utumiki wapoyera monga mpainiya wothandiza. Nthenda yakeyo inafika poipa kachiŵirinso, ndipo podzafika November 1991 thupi lake linakanthidwa ndi kansa m’malo angapo. Gulu lina la madokotala pa chipatala china linayamba kumpatsa mankhwala a radiation.
Ngakhale pansi pa mikhalidwe yovuta yoteroyo, Brunella analimbabe ndi kudziikira zonulirapo zauzimu. Pamene anadziŵa nthaŵi yoyamba za leukemia, anauzidwa kuti mwina akakhala ndi moyo kwa miyezi isanu ndi umodzi yokha. Tsopano, pafupifupi chaka ndi theka pambuyo pake, Brunella anali kulinganizabe makonzedwe amtsogolo. “Sanataye nthaŵi m’kumenyera nkhondo zonulirapo zake,” mkulu wina wa mu mpingo anasimba motero. “Chikhulupiriro cha Brunella mu Paradaiso wa Mulungu wolonjezedwa chinamchirikiza mu vuto lake lonse. Anafikira pa uchikulire Wachikristu ngakhale kuti anali wamng’ono m’zaka. Khalidwe lake ndi mkhalidwe wamaganizo zinasonkhezera mpingo ndi kukopa mitima ya awo amene anamudziŵa, kuphatikizapo antchito a pa chipatala.” Amake akukumbukira kuti: “Sanadandaulepo. Pamene wina anamfunsa mmene anali kupezera, ankayankha kuti, ‘Ndili bwino’ kapena, ‘Ndilipo bwino, nanga inu muli bwanji?’”
Mtsogolo Motetezereka
Brunella analinganiza kukapezeka pa Msonkhano Wachigawo wa “Onyamula Kuunika” wa Mboni za Yehova mu July 1992. Komabe, podzafika nthaŵi ya msonkhanoyo, Brunella anagonekedwa m’chipatala, ndipo moyo wake unali kutha. Chikhalirechobe, iye anafika pamsonkhano panjinga ya opunduka, ali ndi cholinga cha kuona seŵero lakuti Kuchita Chimene Chiri Chabwino Pamaso pa Yehova.
Anabwerera kubanja la kwawo pamasiku oŵerengeka a moyo wake. “Kufikira mapeto, iye anadera nkhaŵa za ena koposa za iyemwini,” akutero Nicoletta. “Ankawalimbikitsa kuphunzira Baibulo, akumawauza kuti, ‘Tidzakhala tonse m’Paradaiso.’”
Brunella anamwalira pa July 27, 1992, ali wochirimika m’chiyembekezo chake cha kuukitsidwira kumoyo m’Paradaiso wa padziko lapansi. Iye anali atangoyamba kulondola zonulirapo zake, koma analinganiza kupitiriza njira yake yodzipatulirayo pambuyo pa chiukiriro chake. Patatsala masiku oŵerengeka imfa yake isanachitike, Brunella analemba kalata yotsatirayi, imene inaŵerengedwa pa nkhani yake ya maliro.
“Mabwenzi Okondedwa:
“Zikomo chifukwa cha kudza kwanu. Kukhalapo kwanu kukutanthauza zambiri ku banja langa.
“Kwa anthu amene anali oyandikana nane—tapyola zambiri. Tinali ndi nthaŵi zambiri zoipa, komanso panali nthaŵi zina zoseketsa. Inali nkhondo yovuta ndi yotenga nthaŵi yaitali, koma sindiganiza kuti ndalephera. Monga momwe Malemba amanenera kuti, ‘Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro.’—2 Timoteo 4:7.
“Ndaphunziranso zambiri, ndipo ndakhaladi wachikulire, ndipo mabwenzi anga ndi awo amene anandizinga anaona kusintha. Ndikufuna kuthokoza anthu onsewo amene anandichirikiza.
“Inu amene mumakhulupira za dongosolo latsopano ndi Yehova mudziŵa kuti kudzakhala chiukiriro, monga momwe pa Yohane 5:28, 29 pamanenera. Chotero khalanibe olimba m’choonadi, ndipo tidzakhoza kuonananso wina ndi mnzake.
“Ndikufuna kuthokoza anthu amene akudziŵa zimene ndakumana nazo. Nonsenu ndikukumbatirani ndi kukupsompsonani. Nonsenu ndimakukondani.”
Brunella sanalole uchichepere wake kapena matenda ake kumchititsa kuzengereza kudzipatulira kwake kwa Mulungu. Chitsanzo chake cha chikhulupiriro ndi kutsimikiza mtima zimalimbikitsa achichepere ndi achikulire mofanana kuchotsa chilichonse chimene chingawadodometse kuthamanga m’makani a moyo.—Ahebri 12:1.