Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 7/15 tsamba 21-24
  • Kodi Mumathetsa Motani Mikangano?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumathetsa Motani Mikangano?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mikangano Yaing’ono
  • Kuthetsa Mikangano Yaikulu
  • Kodi Mungangokhululukira Basi?
  • Kodi Mumathetsa Nkhani Mwachikondi Mukasemphana Maganizo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Mungabweze Mbale Wanu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • ‘Pitirizani Kukhululukirana Eni Okha’
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Khululukani Kuchokera Mumtima
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 7/15 tsamba 21-24

Kodi Mumathetsa Motani Mikangano?

Mwayenda mosasamala​—yachitatu pamzera wa njovu zisanu zadothi yagwa pashelufu yake. Njovuyo idzafunikira kukonzedwanso. Popanda kutero, mgwirizano wa seti yonseyo udzatayika. Komabe, kukonzanso kumeneko nkovuta kwambiri, ndipo simukudzimva kukhala wokhoza kutero. Mudzafunikira kufunafuna malangizo kapena ngakhale kupempha katswiri wodziŵa kuchita ntchitoyo.

MGWIRIZANO pakati pa abale ndi alongo auzimu n’ngwamtengo wapatali koposa zokometsera wamba. Wamasalmo moyenerera anaimba kuti: “Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!” (Salmo 133:1) Kuthetsa mkangano ndi Mkristu mnzathu nthaŵi zina kungakhale nkhani yofuna kusamala kwambiri. Ndiponso, ena amachita zimenezi m’njira yosayenera. Kaŵirikaŵiri “kukonza” kumeneko kumakhala koŵaŵa mosafunikira kapena sikumakhala kwabwino kwambiri, kukumasiya zizindikiro zoipa zoonekera.

Akristu ena mosafunikira amafuna kuloŵetsa akulu oikidwa m’nkhani zimene angasamalire okha. Zimenezi zingakhale motero chifukwa cha kusadziŵa zimene ayenera kuchita. “Ambiri a abale athu sadziŵa mmene angagwiritsirire ntchito uphungu wa Baibulo kuthetsera mikangano yawo,” anatero mbale wina wodziŵa kupereka uphungu wa Baibulo. “Nthaŵi zambiri,” anapitiriza motero, “samatsatira njira ya Yesu yochitira zinthu.” Chotero, kodi nchiyani chimene Yesu kwenikweni ananena ponena za mmene Mkristu ayenera kuthetsera mikangano ndi mbale wake? Kodi nchifukwa ninji kukhala wozoloŵerana bwino lomwe ndi uphungu umenewu ndi kudziŵa mougwiritsirira ntchito kuli kofunika?

Mikangano Yaing’ono

“Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.”​—Mateyu 5:23, 24.

Pamene Yesu analankhula mawu amenewo, Ayuda mwamwambo ankapereka nsembe, kapena kupereka mitulo, paguwa la nsembe m’kachisi ku Yerusalemu. Ngati Myuda anali atachimwira Mwisrayeli mnzake, wochimwayo ankapereka nsembe yopsereza yathunthu kapena nsembe yauchimo. Chitsanzo chosimbidwa ndi Yesu chikuchitikira panthaŵi yofunika kwambiri. Pamene munthuyo ali kuguwa lansembe ndipo ali pafupi kupereka mtulo wake kwa Mulungu, akukumbukira kuti mbale wake ali ndi kanthu pa iye. Inde, Mwisrayeliyo anafunikira kuzindikira kuti kuyanjananso ndi mbale wake kunayenera kukhala koyamba mmalo mwa kuchita ntchito yachipembedzo imeneyo.

Ngakhale kuti nsembe zotero zinali zofunidwa ndi Chilamulo cha Mose, mwa izo zokha sizinali ndi mtengo waukulu koposa m’maso mwa Mulungu. Mneneri Samueli anati kwa Mfumu Sauli yosakhulupirika: “Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mawu a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.”​—1 Samueli 15:22.

Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anabwereza tsatanetsatane ameneyu wa zinthu zofunika nasonyeza ophunzira ake kuti anayenera kuthetsa mikangano yawo asanapereke nsembe zawo. Lerolino, nsembe zimene zimafunidwa kwa Akristu nzauzimu​—“nsembe yakuyamika . . . , ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” (Ahebri 13:15) Komatu, lamulo la mkhalidwelo lidakagwirabe ntchito. Mofananamo mtumwi Yohane akusonyeza kuti kungakhale kwachabe kwa wina kunena kuti amakonda Mulungu ngati amada mbale wake.​—1 Yohane 4:20, 21.

Mokondweretsa, munthu amene akumbukira kuti mbale wake ali ndi kanthu pa iye ndiye ayenera kutenga sitepe loyamba. Motero kudzichepetsa kumene amasonyeza mwina kudzatulutsa zotsatirapo zabwino. Mothekera, munthu amene wachimwiridwa sadzakana kugwirizana ndi wina amene wamfikira kudzavomereza zolakwa zake. Chilamulo cha Mose chinalangiza kuti chinthu chilichonse chotengedwa mosayenera chinayenera kubwezeredwa chonse ndi kuwonjezerapo limodzi la magawo ake asanu. (Levitiko 6:5) Mofananamo, kubwezeretsa maunansi ogwirizana ndi amtendere kudzakhala kosavuta ngati wochimwayo asonyeza chikhumbo chake cha kuchita zoposa zimene zikufunikira, molingana ndendende ndi lingaliro la liwulo, kukonza chivulazo chilichonse chimene angakhale atachititsa.

Komabe, si nthaŵi zonse pamene zoyesayesa za kubwezeretsa maunansi amtendere zimakhala zachipambano. Buku la Miyambo limatikumbutsa kuti nkovuta kuthetsa mikangano ndi wina amene amaona kuvomereza kukhala kovuta. Pa Miyambo 18:19 pamati: “Kupembedza mbale utamchimwira nkovuta, kulanda mudzi nkosavuta; makangano akunga mipiringidzo ya linga.” Matembenuzidwe ena amati: “Mbale wochimwiridwa avuta kumgonjetsa koposa mudzi wolimba: Ndipo mikangano yawo ikunga mipiringidzo ya linga.” (The Englishman’s Bible) Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, zoyesayesa zoona mtima ndi zodzichepetsa zidzapambana kwa okhulupirira anzanu amene amakhumba kukondweretsa Mulungu. Koma pamene kulingaliridwa kuti uchimo waukulu wachitidwa, uphungu wa Yesu wolembedwa m’Mateyu chaputala 18 ufunikira kugwiritsiridwa ntchito.

Kuthetsa Mikangano Yaikulu

“Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako. Koma ngati samvera, wonjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena aŵiri, kuti atsimikizidwe mawu onse pakamwa pa mboni ziŵiri kapena zitatu. Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.”​—Mateyu 18:15-17.

Bwanji ngati Myuda (kapena pambuyo pake, Mkristu) analoŵa m’mavuto aakulu ndi wolambira Yehova mnzake? Uyo amene anaganiza kuti anachimwiridwa anayenera kutenga sitepe loyamba. Anayenera kukambitsirana nkhaniyo mtseri ndi wochimwayo. Mwa kusayesa kuchirikiza mbali yake ya nkhaniyo, ndithudi iye mothekera kwambiri akabweza mbale wake, makamaka ngati panangokhala chabe kusamvana kumene kukanathetsedwa msanga. Zonse zikathetsedwa mosavuta ngati awo oloŵetsedwamo mwachindunji ndiwo okha amene anadziŵa nkhaniyo.

Komabe, mwinamwake sitepe loyamba silingaphule kanthu. Pochita ndi mkhalidwewo, Yesu anati: “Wonjeza kutenga . . . mmodzi kapena aŵiri.” Ameneŵa akanayenera kukhala mboni zoona ndi maso zimene zinalipo. Mwinamwake anali atamva mmodzi wa anthuwo akunamizira winayo, kapena awo otengedwa anali mboni za pangano lolembedwa limene anthu aŵiriwo tsopano sakugwirizanapo. Kumbali inayo, otengedwawo angakhale mboni pamene mbali zilizonse, zonga maumboni olembedwa kapena apakamwa, zifotokozedwa kudziŵikitsa chochititsa vutolo. Panonso, chiŵerengero chaching’ono chokha chothekera​—“mmodzi kapena aŵiri”​—chiyenera kudziŵa za nkhaniyo. Zimenezi zingaletse zinthu kuipirapo ngati nkhaniyo inali kusamvana chabe.

Kodi ndi malingaliro otani amene munthu wochimwiridwayo ayenera kukhala nawo? Kodi ayenera kuyesa kunyazitsa Mkristu mnzake ndi kufuna kuti iye adziluluze? Polingalira za uphungu wa Yesu, Akristu sayenera kufulumira kutsutsa abale awo. Ngati wochimwayo azindikira cholakwa chake, apepesa, nayesa kuwongolera zinthu, wochimwiridwayo adzakhala ‘atabweza mbale wake.’​—Mateyu 18:15.

Ngati nkhaniyo siinathetsedwe, inafunikira kuperekedwa ku mpingo. Poyamba, zimenezi zinatanthauza kwa akulu a Ayuda koma pambuyo pake, kwa akulu a mpingo Wachikristu. Wochimwa wosalapayo angafunikire kuchotsedwa mumpingo. Zimenezo ndizo zikutanthauzidwa ndi kumuona “monga wakunja ndi wamsonkho,” anthu amene Ayuda anatalikirana nawo. Sitepe lalikulu limeneli silinatengedwe ndi Mkristu aliyense payekha. Akulu oikidwa, amene amaimira mpingo, ndiwo okha amene ali ndi ukumu wa kuchitapo kanthu motero.​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 5:13.

Kuthekera kwakuti wochimwa wosalapayo angachotsedwe kumasonyeza kuti Mateyu 18:15-17 samakhudza mikangano yaing’ono. Yesu anali kunena za zolakwa zazikulu, komabe zokhoza kuthetsedwa pakati pa anthu aŵiri oloŵetsedwamo. Mwachitsanzo, cholakwacho chingakhale kunamizira, kumene kungayambukire moipa mbiri ya wochimwiridwayo. Kapena chingakhudze nkhani zandalama, pakuti mavesi otsatira ali ndi fanizo la Yesu lonena za kapolo wopanda chifundo amene anakhululukidwa mangawa aakulu. (Mateyu 18:23-35) Ngongole yosalipiriridwa panthaŵi yoikika ingangokhala vuto lakanthaŵi limene lingathetsedwe mosavuta ndi anthu aŵiriwo. Koma lingakhale tchimo lalikulu, kutanthauza, kuba, ngati wokongolayo mouma khosi akana kulipirira zimene anakongolazo.

Machimo ena sangathe kuthetsedwa ndi Akristu aŵiri okha. Pansi pa Chilamulo cha Mose, machimo aakulu anafunikira kuululidwa. (Levitiko 5:1; Miyambo 29:24) Mofananamo, machimo aakulu oloŵetsamo chiyero cha mpingo ayenera kuululidwa kwa akulu ampingo.

Komabe, nkhani zochuluka za kusamvana pakati pa Akristu siziyenera kutsatira njira imeneyi.

Kodi Mungangokhululukira Basi?

Yesu atangofotokoza mmene mikangano yaikulu ingathetsedwere, anaphunzitsa phunziro lina lofunika. Timaŵerenga kuti: “Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? kufikira kasanu ndi kaŵiri kodi? Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kaŵiri, koma kufikira makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri.” (Mateyu 18:21, 22) Panthaŵi ina Yesu anauza ophunzira ake kukhululukira “kasanu ndi kaŵiri patsiku.” (Luka 17:3, 4) Pamenepo, mwachionekere, otsatira a Kristu amayembekezeredwa kuthetsa mikangano mwa kukhululukirana mwaufulu.

Imeneyi ndi mbali imene ifunikira kuyesayesa kokulirapo. “Abale ena sadziŵa kukhululukira,” anatero munthuyo wogwidwa mawu poyamba. Anawonjezera kuti: “Amaoneka kukhala odabwa pamene wina afotokoza kuti iwo angasankhe kukhululukira, kwakukulukulu kuti asungitse mtendere mumpingo Wachikristu.”

Mtumwi Paulo analemba kuti: “[Pitirizanibe, NW] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso.” (Akolose 3:13) Chotero, tisanapite kwa mbale amene angakhale atatichimwira, kungakhale bwino kulingalira mafunso otsatirawa: Kodi ndiyeneradi kulankhula naye za cholakwacho? Kodi kulidi kosatheka kwa ine kuiŵala zakale mumzimu weniweni wa Chikristu? Ngati ndinali ine, kodi sindikanafuna kukhululukiridwa? Ndipo ndikasankha kusamkhululukira, kodi ndingayembekezere Mulungu kuyankha mapemphero anga ndi kundikhululukira? (Mateyu 6:12, 14, 15) Mafunso otero angatithandize kwambiri kukhala okhululukira.

Monga Akristu, limodzi la mathayo athu ofunika ndilo kusungitsa mtendere mumpingo wa anthu a Yehova. Chotero, tiyeni tigwiritsire ntchito uphungu wa Yesu. Umenewu udzatithandiza kukhululukira mwaufulu. Mzimu wotero wa kukhululukira udzachirikiza chikondi cha pa abale chimene chili chizindikiro chodziŵira ophunzira a Yesu.​—Yohane 13:34, 35.

[Chithunzi patsamba 23]

Akristu angathetse mikangano yawo mwa kutsatira uphungu wa Yesu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena