Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 9/1 tsamba 26
  • “Kanizani Mdyerekezi, Ndipo Adzakuthaŵani Inu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kanizani Mdyerekezi, Ndipo Adzakuthaŵani Inu”
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Amayankha Mapemphero
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Ndinasiya Zinthu Zambiri Kuti Nditsatire Ambuye
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1994
w94 9/1 tsamba 26

Olengeza Ufumu Akusimba

“Kanizani Mdyerekezi, Ndipo Adzakuthaŵani Inu”

M’ZAKA za zana loyamba, gulu la “akuchita zamatsenga” odzipereka a mu Efeso linalabadira uthenga Wachikristu mwa kutentha poyera mabuku awo a zamatsenga. (Machitidwe 19:19) Mtengo woŵerengedwa wa mabuku ameneŵa unali ndalama za siliva zokwanira 50,000. Ngati cholembedwa cha Baibulochi chikunena za denari, kobiri lasiliva Lachiroma, zikanakwana pafupifupi $37,000!

Lerolino pali anthu ambiri amene panthaŵi ina anali ndi mabuku onena za malaulo koma anasonyeza kutsimikiza mtima kofanana ndi kwa Aefeso akalewo. Talingalirani chochitika chotsatirachi cha ku Canada.

Pafupifupi zaka zisanu zapitazo, mmodzi wa Mboni za Yehova anali kulalikira kunyumba ndi nyumba pamene pakhomo lina mkazi wotchedwa Nora anamkokera m’nyumba. Kwa zaka zambiri za kufufuza kwauzimu, Nora anali atasonkhanitsa mazana a mabuku achipembedzo ndi a mizimu, koma anafuna kudziŵa zimene Baibulo limanena pankhani ya chiyembekezo cha akufa. Mboniyo inamgaŵira trakiti lakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Akufa Okondedwa? Mafunso a Nora anayankhidwa, ndipo analandira masabusikripishoni a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

Pambuyo pake iye anasamuka naleka kuonana ndi Mboni za Yehova. Komabe, anapitiriza kulandira magazini papositi kudzera m’keyala yake yatsopano. Anaodanso zofalitsidwa zina zozikidwa pa Baibulo zotchulidwa m’magaziniwo. Patapita nthaŵi, mmodzi wa Mboni za Yehova anafika pakhomo pake. Atakondwera poona kuti Mboniyo inangopita mwachindunji m’Baibulo poyankha mafunso, Nora analandira mkaziyo ndi kumpempha kubweranso kudzakambitsirana zowonjezereka.

Komabe, kunakhala kovuta kwa Mboniyo kuonananso ndi Nora. Maulendo obwerezabwereza anapangidwa panthaŵi zosiyanasiyana za tsiku ndi pamasiku osiyanasiyana mkati mwa mlungu mosaphula kanthu. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, kuumirira kwake kunaphula kanthu. Phunziro la Baibulo lokhazikika linayambidwa, limene kaŵirikaŵiri linachitidwa katatu pamlungu chifukwa cha kuumirira kwa Nora. Zinthu zimene ankaphunzira zinamsonkhezera kulankhula kwa mabwenzi ndi ziŵalo za banja, zikumachititsa atatu a iwo kupempha maphunziro a Baibulo ndi Mboni za Yehova.

Kupyolera m’phunziro lake Nora anazindikira kuti pali zipembedzo zonyenga ndi aneneri onyenga koma njira imodzi yokha yopita ku moyo. Kwa zaka zambiri iye anali kufunafuna m’zipembedzo zonyenga mayankho a mafunso ake, koma ataphunzira zimene Baibulo limanena ponena za ziŵanda, anachita mofanana ndi Aefeso akale otchulidwa pa Machitidwe 19:19. Iye anachotsa zonse za m’laibulale yake, ndipo m’kupita kwa masiku angapo, anawononga mabuku oposa chikwi chimodzi onena za malaulo ndi ziphunzitso za chipembedzo chonyenga. Pakati pa zofalitsidwa zowonongedwazo, mpambo wa mabuku anayi unali wa mtengo woposa $800!

Mwachionekere, pokwiyitsidwa ndi kachitidwe ka Nora, ziŵandazo zinamvutitsa kwa pafupifupi milungu iŵiri. Komabe, mizimu yoipa imeneyi sinali yokhoza kumleketsa kupitiriza phunziro lake la Baibulo ndi mayanjano ake ndi gulu la Yehova lamakono.

Zochitika zoterozo zimasonyeza bwino lomwe choonadi cha mawu a Baibulo akuti: “Mverani Mulungu; koma kanizani mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.”​—Yakobo 4:7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena