Tengani Chitsanzo cha Aneneri a Mulungu
“Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zoŵaŵa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m’dzina la Ambuye.”—YAKOBO 5:10.
1. Kodi nchiyani chimene chimathandiza atumiki a Yehova kukhala osangalala ngakhale pamene azunzidwa?
ATUMIKI a Yehova amasonyeza chisangalalo mosasamala kanthu za mkhalidwe wosakondweretsa wofala padziko lonse m’masiku ano otsiriza. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti iwo amadziŵa kuti akukondweretsa Mulungu. Mboni za Yehova zimapiriranso chizunzo ndi chitsutso pa utumiki wawo wapoyera chifukwa chakuti zimadziŵa kuti zikuvutika chifukwa cha chilungamo. Yesu Kristu anauza otsatira ake kuti: “Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu m’Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.” (Mateyu 5:10-12) Ndithudi, nthaŵi iliyonse pamene atumiki a Mulungu ayang’anizana ndi mayesero a chikhulupiriro, iwo amawayesa chimwemwe.—Yakobo 1:2, 3.
2. Malinga ndi kunena kwa Yakobo 5:10, kodi nchiyani chimene chingatithandize kusonyeza kuleza mtima?
2 Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zoŵaŵa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m’dzina la Ambuye.” (Yakobo 5:10) W. F. Arndt ndi F. W. Gingrich amafotokoza liwu Lachigiriki lotembenuzidwa pano kuti “chitsanzo” (hy·poʹdeig·ma) kukhala “chotsanzirira, chifanizo, chitsanzo, m’lingaliro labwino monga chinthu china[chake] chimene chimasonkhezera kapena chimene chiyenera kusonkhezera munthu kuchitsanzira.” Monga momwe kwasonyezedwera pa Yohane 13:15, “chimenechi sichili chitsanzo wamba. Icho chili chifaniziro chenicheni.” (Theological Dictionary of the New Testament) Chotero, pamenepo, atumiki amakono a Yehova angatenge aneneri ake okhulupirika kukhala chitsanzo ponena za “kumva zoŵaŵa” ndi “kuleza mtima.” Kodi tingazindikirenso chiyani pamene tipenda miyoyo yawo? Ndipo kodi zimenezi zingatithandize motani mu ntchito yathu yolalikira?
Anamva Zoŵaŵa
3, 4. Kodi ndimotani mmene mneneri Amosi anachitira ndi chitsutso cha Amaziya?
3 Kaŵirikaŵiri aneneri a Yehova anamva zoŵaŵa kapena kuchitiridwa zoipa. Mwachitsanzo, m’zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E., Amaziya wansembe wolambira mwana wang’ombe anatsutsa moipa mneneri Amosi. Monama Amaziya ananena kuti Amosi anapangira chiwembu Yerobiamu II mwa kunenera kuti mfumuyo idzafa ndi lupanga ndi kuti Israyeli adzatengedwa undende. Mwachipongwe, Amaziya anauza Amosi kuti: “Mlauli iwe, choka, thaŵira ku dziko la Yuda, nudye, nunenere komweko; koma usaneneranso ku Beteli; pakuti pamenepo mpamalo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu.” Mosalefulidwa ndi chiukiro cha mawu chimenechi, Amosi anayankha kuti: “Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woŵeta ng’ombe, ndi wakutchera nkhuyu; ndipo Yehova ananditenga ndilikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israyeli.”—Amosi 7:10-15.
4 Mzimu wa Yehova unapatsa Amosi mphamvu ya kunenera molimba mtima. Tangoganizani kachitidwe ka Amaziya pamene Amosi anati: “Tamvera mawu a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera chotsutsana ndi Israyeli, usadonthetsa mawu akutsutsana ndi nyumba ya Isake; chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m’mudzi, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagaŵanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m’dziko lodetsedwa; ndipo Israyeli adzatengedwadi ndende kuchoka m’dziko lake.” Ulosiwo unakwaniritsidwa. (Amosi 7:16, 17) Ha, ayenera kukhala atadabwa chotani nanga Amaziya wampatukoyo!
5. Kodi ndi kufanana kotani kumene kungaonedwe pakati pa mkhalidwe wa atumiki amakono a Yehova ndi uja wa mneneri Amosi?
5 Zimenezi nzofanana ndi mkhalidwe wa anthu a Yehova lerolino. Timamva zoŵaŵa monga awo amene amalengeza mauthenga a Mulungu, ndipo anthu ambiri amanena mwachipongwe za ntchito yathu yolalikira. Zoonadi, ulamuliro wathu wa kulalikira sukuchokera kumaseminale azaumulungu. Mmalomwake, mzimu woyera wa Yehova umatisonkhezera kulengeza mbiri yabwino ya Ufumu. Ife sitimasintha kapenanso kuchepetsa mphamvu ya uthenga wa Mulungu. Mmalomwake, mofanana ndi Amosi, ife momvera timaulengeza mosasamala kanthu za mmene udzayambukirira omvetsera athu.—2 Akorinto 2:15-17.
Anasonyeza Kuleza Mtima
6, 7. (a) Kodi nchiyani chimene chinali chapadera m’kulosera kwa Yesaya? (b) Kodi ndimotani mmene atumiki a Yehova amakono amachitira monga Yesaya?
6 Aneneri a Mulungu anasonyeza kuleza mtima. Mwachitsanzo, kuleza mtima kunasonyezedwa ndi Yesaya, amene anatumikira monga mneneri wa Yehova m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E. Mulungu anamuuza kuti: “Kauze anthu awa, Imvani inu [mobwerezabwereza, NW], koma osazindikira; yang’anani inu [mobwerezabwereza, NW], koma osadziŵitsa. Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu awo, nutseke maso awo; angaone ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angazindikire ndi mtima wawo, nakabwerenso, nachiritsidwe.” (Yesaya 6:9, 10) Anthuwo anachitadi motero. Koma kodi zimenezi zinachititsa Yesaya kuleka? Ayi. Mmalomwake, moleza mtima ndi mwachangu iye analengeza mauthenga achenjezo a Yehova. Kalembedwe Kachihebri ka mawu a Mulungu amene angogwidwa kumenewo kamachirikiza lingaliro la “kupitirizabe kwanthaŵi yaitali” kwa zilengezo za mneneriyo, zimene anthu anamva “mobwerezabwereza.”—Gesenius’ Hebrew Grammar.
7 Lerolino ambiri amachita ndi mbiri yabwino monga momwe anthu anachitira ndi mawu a Yehova operekedwa ndi Yesaya. Komabe, mofanana ndi mneneri wokhulupirika ameneyo, timanena uthenga wa Ufumu “mobwerezabwereza.” Timatero ndi changu ndi khama loleza mtima chifukwa chimenechi ndicho chifuniro cha Yehova.
“Momwemo Anachita”
8, 9. Kodi ndi m’njira ziti zimene mneneri wa Yehova Mose alili chitsanzo chabwino?
8 Mneneri Mose anali chitsanzo chabwino cha kuleza mtima ndi kumvera. Anasankha kuima limodzi ndi Aisrayeli ogwidwa ukapolo, koma anafunikira kuyembekezera mopirira kaamba ka nthaŵi ya chiwomboledwe chawo. Kwa zaka 40 iye anakhala ku Midyani kufikira pamene Mulungu anamgwiritsira ntchito kutsogolera mtundu wa Israyeli kutuluka mu ukapolo. Pamene Mose ndi mkulu wake Aroni anali pamaso pa wolamulira wa Igupto, iwo momvera ananena ndi kuchita zimene Mulungu analamula. Kwenikweni, “momwemo anachita.”—Eksodo 7:1-6; Ahebri 11:24-29.
9 Mose anapirira moleza mtima ndi Israyeli zaka 40 zovuta kwambiri m’chipululu. Iye anatsatiranso chitsogozo chaumulungu momvera pomanga chihema cha Israyeli ndi popanga zinthu zina zogwiritsiridwa ntchito m’kulambira kwa Yehova. Mneneriyo anatsatira mosamalitsa kwambiri malangizo a Mulungu kwakuti timaŵerenga kuti: “Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.” (Eksodo 40:16) Pochita utumiki wathu mogwirizana ndi gulu la Yehova, tiyeni tikumbukire kumvera kwa Mose ndi kugwiritsira ntchito uphungu wa mtumwi Paulo wa kukhala ‘omvera atsogoleri athu.’—Ahebri 13:17.
Anali ndi Mkhalidwe Wamaganizo Wotsimikiza
10, 11. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti mneneri Hoseya anali ndi mkhalidwe wamaganizo wotsimikiza? (b) Kodi ndimotani mmene tingasungire mkhalidwe wamaganizo wotsimikiza pamene tifikira anthu m’magawo athu?
10 Aneneri anafunikira kukhala ndi mkhalidwe wamaganizo wotsimikiza pamene anali kupereka mauthenga achiweruzo ndiponso maulosi osonyeza nkhaŵa yachikondi ya Mulungu pa okhulupirika omwazikana mu Israyeli. Zimenezi zinali choncho kwa Hoseya, amene anali mneneri kwa zaka zosachepera pa 59. Iye anapitirizabe motsimikiza kupereka mauthenga a Yehova ndi kumaliza buku lake la ulosi ndi mawu akuti: “Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? waluntha, kuti adziŵe izi? pakuti njira za Yehova zili zowongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.” (Hoseya 14:9) Malinga ngati Yehova atilola kupereka umboni, tiyeni tikhale ndi mkhalidwe wamaganizo wotsimikiza ndi kupitirizabe kufunafuna awo amene mwanzeru adzalandira chisomo cha Mulungu.
11 Kuti ‘tifunefune amene ali oyenerera,’ tifunikira kuchita khama ndi kuona zinthu motsimikiza. (Mateyu 10:11) Mwachitsanzo, ngati titaya mfungulo zathu, tingabwerere mmene tinadzera ndi kufunafuna m’malo osiyanasiyana amene tinafikamo. Tingazipeze kokha pambuyo pa kuchita zimenezi mobwerezabwereza. Mofananamo tiyeni tichite khama pofunafuna anthu onga nkhosa. Timakhala ndi chisangalalo chotani nanga pamene alabadira mbiri yabwino m’gawo lofoledwa kaŵirikaŵiri! Ndipo tikukondwera chotani nanga kuti Mulungu akudalitsa ntchito yathu m’maiko mmene kalelo ziletso zinachepetsa utumiki wathu wapoyera!—Agalatiya 6:10.
Magwero a Chilimbikitso
12. Kodi ndi ulosi wotani wa Yoweli umene ukukwaniritsidwa m’zaka za zana la 20, ndipo motani?
12 Mawu a aneneri a Yehova angathe kukhala chilimbikitso chachikulu kwa ife mu utumiki wathu. Mwachitsanzo, lingalirani za ulosi wa Yoweli. Uli ndi mauthenga achiweruzo amene analunjikitsidwa kwa Aisrayeli ampatuko ndi ena m’zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E. Komabe, Yoweli anauziridwanso kulosera kuti: “Kudzachitika mtsogolo mwake, [ine Yehova] ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya; ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo.” (Yoweli 2:28, 29) Zimenezi zinakhaladi choncho kwa otsatira a Yesu kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E. kumka mtsogolo. Ndipo ndi kukwaniritsidwa kwakukulu kotani nanga kwa ulosi umenewu kumene tikuona m’zaka za zana la 20 zino! Lerolino tili ndi mamiliyoni amene ‘amanenera,’ kapena kulengeza uthenga wa Yehova—pakati pawo pali oposa 600,000 okhala mu utumiki waupainiya wanthaŵi yonse.
13, 14. Kodi nchiyani chimene chingathandize Akristu achichepere kupeza chisangalalo mu utumiki wakumunda?
13 Olengeza Ufumu ambiri ngachichepere. Nthaŵi zina nkovuta kwa iwo kulankhula kwa anthu achikulire za Baibulo. Nthaŵi zina atumiki achichepere a Yehova amauzidwa kuti: ‘Ukungotaya nthaŵi yako ndi kulalikira,’ ndi kuti ‘bwenzi ukuchita kanthu kena.’ Mboni zachichepere za Yehova zingayankhe mwaluso kuti zili ndi chisoni kuti munthuyo akulingalira motero. Mlaliki wina wa mbiri yabwino wachichepere amakupeza kukhala kothandiza kuwonjezera kuti: “Ndiganiza kuti ndimapinduladi kulankhula ndi anthu achikulire monga inu, ndipo kumandisangalatsa.” Ndithudi, kulalikira mbiri yabwino sikuli kutaya nthaŵi konse. Miyoyo ili pachiswe. Kupyolera mwa Yoweli, Mulungu analengezanso kuti: “Kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.”—Yoweli 2:32.
14 Ana amene amatsagana ndi makolo awo mu ntchito yolalikira Ufumu amalandira thandizo la makolo m’kuika zonulirapo zaumwini. Pang’ono ndi pang’ono achichepere otero amapita patsogolo kuyambira pakuŵerenga lemba ndi kufotokoza chiyembekezo chawo chozikidwa pa Baibulo ndi kugaŵira buku loyenera kwa anthu okondwerera. Pamene aona kupita patsogolo kwawo ndi dalitso la Yehova, ofalitsa achicheperewo amapeza chisangalalo chachikulu m’kulalikira mbiri yabwino.—Salmo 110:3; 148:12, 13.
Changu ndi Mkhalidwe wa Kuyembekezera
15. Kodi ndimotani mmene chitsanzo cha Ezekieli chingathandizire kuyambitsanso changu chathu cha ntchito yolalikira Ufumu?
15 Aneneri a Mulungu analinso achitsanzo chabwino m’kusonyeza changu ndi mkhalidwe woyembekezera womwe—mikhalidwe imene tifunikira mu utumiki wathu lerolino. Panthaŵi yoyamba pamene tinaphunzira choonadi m’Mawu a Mulungu, mwachionekere tinali kuyaka moto ndi changu chimene chinatisonkhezera kulankhula molimbika. Komano pangakhale patapita zaka chiyambire pamenepo, ndipo tingakhale titafola mobwerezabwereza gawo lathu lochitiramo umboni. Tsopano anthu ochepa angakhale akulandira uthenga wa Ufumu. Kodi zimenezi zaziralitsa changu chathu? Ngati ndi choncho, lingalirani za mneneri Ezekieli, amene dzina lake limatanthauza kuti “Mulungu Alimbitsa.” Ngakhale kuti Ezekieli anayang’anizana ndi anthu ouma mtima mu Israyeli wakale, Mulungu anamlimbitsa ndipo mophiphiritsira analimbitsa mutu wake kuposa mwala wolimbitsitsa. Motero, Ezekieli anali wokhoza kuchita utumiki wake kwa zaka zambirimbiri mosasamala kanthu kuti anthuwo anamvetsera kapena ayi. Chitsanzo chake chimasonyeza kuti tingathe kuchita zofananazo, ndipo chingatithandize kuyambitsanso changu chathu kaamba ka ntchito ya kulalikira.—Ezekieli 3:8, 9; 2 Timoteo 4:5.
16. Kodi ndi mkhalidwe wamaganizo wotani wa Mika umene tiyenera kukulitsa?
16 Wodziŵika ndi kuleza mtima kwake anali Mika, amene analosera m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E. “Ine,” iye analemba motero, “ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.” (Mika 7:7) Chidaliro cha Mika chinazikidwa pa chikhulupiriro champhamvu. Mofanana ndi mneneri Yesaya, Mika anadziŵa kuti zimene Yehova analinganiza Iye adzazichitadi. Nafenso timadziŵa zimenezi. (Yesaya 55:11) Chotero tiyenitu tikulitse mkhalidwe wa kuyembekezera kulinga ku kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu. Ndipo tiyenitu tilalikire mbiri yabwino ndi changu, ngakhale m’madera amene anthu samakondwerera kwambiri uthenga wa Ufumu.—Tito 2:14; Yakobo 5:7-10.
Kusonyeza Kuleza Mtima Lerolino
17, 18. Kodi ndi zitsanzo zakale ndi zatsopano zotani zimene zingatithandize kusonyeza kuleza mtima?
17 Ena a aneneri a Yehova anachita khama moleza mtima m’magawo awo kwazaka zambiri koma sanaone kukwaniritsidwa kwa maulosi awo. Komabe, khama lawo loleza mtimalo, kaŵirikaŵiri pamene anali kuvutika ndi kuchitidwa zoipa, limatithandiza kuzindikira kuti tingathe kukwaniritsa utumiki wathu. Tingapindulenso ndi chitsanzo cha odzozedwa okhulupirika m’zaka makumi angapo zoyambirira za m’zaka za zana la 20. Ngakhale kuti ziyembekezo zawo zakumwamba sizinalandiridwe mwamsanga monga momwe anayembekezera, iwo sanalole kugwiritsidwa mwala kochititsidwa ndi kuchedwa kongoganizirako kuchepetsa changu chawo cha kuchita chifuniro cha Mulungu monga momwe anachivumbulira kwa iwo.
18 Kwa zaka zambiri, ambiri a Akristu ameneŵa anagaŵira mokhazikika Nsanja ya Olonda ndi magazini anzakewo, Galamukani!, (amene kale anatchedwa kuti The Golden Age ndipo pambuyo pake Consolation). Iwo mwachangu anachititsa magazini amtengo wapatali ameneŵa kukhala opezeka kwa anthu pamakwalala ndiponso kunyumba zawo mwa zimene lerolino timatcha kuti njira za magazini. Mlongo wina wokalamba amene anamaliza njira yake ya padziko lapansi anasoŵedwa mwamsanga ndi anthu odutsa amene anazoloŵera kumuona akuchitira umboni pakhwalala. Ha, ndi umboni waukulu chotani nanga umene iye anapereka mkati mwa zaka zake zambiri za utumiki wokhulupirika, monga momwe kwasonyezedwera ndi mawu oyamikira a awo amene anaona utumiki wake wapoyera! Monga wolengeza Ufumu, kodi inu mumagaŵira mokhazikika Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa awo amene mumakumana nawo mu utumiki wanu?
19. Kodi ndi chilimbikitso chotani chimene Ahebri 6:10-12 amatipatsa?
19 Lingaliraninso za kuleza mtima ndi utumiki wokhulupirika wa abale amene amatumikira monga ziŵalo za Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Angapo a iwo tsopano ali m’zaka zawo za moyo za makumi asanu ndi anayi kapena makumi khumi, koma iwo adakali olengeza Ufumu amene amasamalira mwachangu mathayo awo. (Ahebri 13:7) Ndipo bwanji za okalamba ena okhala ndi chiyembekezo cha kumwamba ndipo ngakhale ena pakati pa “nkhosa zina” amene akukalamba? (Yohane 10:16) Iwo angathe kukhala otsimikizira kuti Mulungu sali wosalungama kuti aiŵale ntchito yawo ndi chikondi chimene amasonyeza ku dzina lake. Pamodzi ndi okhulupirira anzawo achichepere, Mboni za Yehova zokalamba zipitebetu patsogolo m’kuchita zimene zingathe, zikumasonyeza chikhulupiriro ndi kusonyeza kuleza mtima mu utumiki wa Mulungu. (Ahebri 6:10-12) Pamenepo, kaya ndi mwa chiukiriro, monga aneneri akale, kapena mwa kupulumuka kupyola “chisautso chachikulu” chimene chikudzacho, iwo adzalandira mfupo ya moyo wosatha.—Mateyu 24:21, NW.
20. (a) Kodi mwaphunziranji kuchokera mu “chitsanzo” cha aneneri? (b) Kodi ndimotani mmene kuleza mtima konga kwa aneneri kungatithandizire?
20 Ha, ndi chitsanzo chabwino chotani nanga chimene aneneri a Mulungu atisiyira! Chifukwa chakuti anapirira mavuto, anasonyeza kuleza mtima, ndipo anasonyeza mikhalidwe ina yaumulungu, anali ndi mwaŵi wa kulankhula m’dzina la Yehova. Monga Mboni zake zamakono, tiyenitu tikhale ngati iwo ndi kukhala otsimikiza mtima monga mneneri Habakuku, amene analengeza kuti: “Ndidzaima pa dindiro langa ndi kudziika palinga, ndipo ndidzayang’anira ndione ngati [Mulungu] adzanenanji mwa ine.” (Habakuku 2:1) Tiyeni tikhale ndi kutsimikiza mtima kofananako pamene tikusonyeza kuleza mtima ndipo mwachisangalalo tikumapitiriza kupereka chilengezo chapoyera cha dzina lokwezeka la Mlengi wathu Wamkulu, Yehova!—Nehemiya 8:10; Aroma 10:10.
Kodi Mwagwira Mfundo Izi?
◻ Kodi ndi chitsanzo cha kulimba mtima chotani chimene mneneri Amosi anasonyeza?
◻ Kodi ndi m’njira zotani zimene mneneri Mose analili chitsanzo chabwino?
◻ Kodi ndimotani mmene Mboni zamakono za Yehova zingachitire monga Amosi ndi Yesaya?
◻ Kodi nchiyani chimene atumiki Achikristu angaphunzire pa khalidwe la Hoseya ndi Yoweli?
◻ Kodi tingapindule motani ndi zitsanzo za Ezekieli ndi Mika?
[Chithunzi patsamba 16]
Mosasamala kanthu za chitsutso chaukali cha Amaziya, mzimu wa Yehova unapatsa Amosi mphamvu ya kunenera molimba mtima
[Chithunzi patsamba 18]
Odzozedwa okhulupirika aika chitsanzo chabwino kwambiri mwa kusonyeza kuleza mtima mu utumiki wa Yehova