Baibulo—Buku Lomwe Linalembedwa Kuti Limvetsetsedwe
ANTHU ambiri amakhulupirira kuti Baibulo lilidi Mawu a Mulungu amene ayenera kutsatiridwa monga momwedi alili. Kwa ena, “uthenga wa Baibulo uli wosamveka bwino kwambiri.” Inatero komiti ya ziŵalo 12 ya chikhulupiriro ndi zaumulungu ya chipembedzo chachikulu koposa cha Chiprotestanti ku Canada. Mtsogoleri wachipembedzo Clifford Elliott, wa United Church, akulingalira kuti kwa ena “Baibulo limakhala lovuta kumva, losasangalatsa ndi losafunikira.”
Malingaliro otero akubutsa mafunso oyenerera amene afunikira mayankho. Ofunika kwambiri mwa ameneŵa ndiwo akuti, Kodi nchifukwa ninji Baibulo linalembedwa? Kodi nlosokoneza maganizo ndi lovuta kumvetsetsa? Kodi munthu wamba angalimve? Kodi ndi thandizo lotani limene lifunikira kuti wina azindikire tanthauzo la Malemba? Ndipo kodi nchifukwa ninji chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chili chofunika m’nthaŵi zino zovuta?
Kodi Nchifukwa Ninji Baibulo Linalembedwa?
Nthaŵi zonse kuphunzira Mawu a Mulungu kwakhala kofunika kwa awo amene akapeza chiyanjo ndi chivomerezo cha Mulungu Wam’mwambamwamba, Yehova. Mafumu, ansembe, makolo, amuna, akazi, ndi ana—olemera ndi osauka omwe—analangizidwa kupatula nthaŵi pa zochita za moyo zatsiku ndi tsiku kuti apende mosamalitsa ndi mwapemphero Mawu a Mulungu olembedwa.—Deuteronomo 6:6, 7; 17:18-20; 31:9-12; Nehemiya 8:8; Salmo 1:1, 2; 119:7-11, 72, 98-100, 104, 142; Miyambo 3:13-18.
Mwachitsanzo, Yoswa anauzidwa kuti: “Tsimikizira kuti buku la Chilamulo likuŵerengedwa nthaŵi zonse m’kulambira kwako. Uliphunzire usana ndi usiku, ndipo tsimikizira kuti ukumvera zonse zolembedwamo. Pamenepo udzalemera ndi kupambana.” (Yoswa 1:8, Today’s English Version) Kuphunzira kosamalitsa kotero ndi kugwiritsira ntchito Chilamulo cha Mulungu kukadzetsa chipambano ndi chimwemwe. Yehova sanangofuna kuti “anthu amtundu uliwonse” akamve Mawu ake, Baibulo, komanso kulimvera, ndi chiyembekezo cha kulandira mphatso ya moyo.—1 Timoteo 2:3, 4, NW; Yohane 17:3.
Kodi Nlovuta Kwambiri Kumvetsetsa?
Yesu asanakwere kumwamba, anamveketsa bwino lomwe kuti anafuna mkupiti waukulu wa maphunziro a Baibulo kuti upitirizebe padziko lonse lapansi. (Machitidwe 1:8) Iye anadziŵa kuti Baibulo linalembedwa kuti limvetsetsedwe. Atafotokoza kuti Yehova anali atampatsa ulamuliro wonse kumwamba ndi pa dziko lapansi, iye anapereka lamulo lachindunji ili: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”—Mateyu 28:19, 20.
Asanabatizidwe, ophunzira atsopano anafunikira kuphunzitsidwa za Yehova, Mwana wake, ndi kugwira ntchito kwa mzimu woyera. Ndiponso, anafunikira kuphunzitsidwa lamulo la dongosolo la zinthu Lachikristu. (1 Akorinto 9:21; Agalatiya 6:2) Kuti zimenezi zichitike, oyenererawo choyamba anafunikira kukhulupirira kuti Baibulo linachokera kwa Yehova ndipo chachiŵiri kuti linalembedwa kuti limvetsetsedwe.—Mateyu 10:11-13.
Kodi nchiyani chimene chifunikira kwa inu kuti mumvetsetse Baibulo? Mwana wa Mulungu anayesayesa kwambiri kufotokoza Malemba. Iye anadziŵa kuti Malemba Opatulika ali oona ndi kuti ali ndi chifuniro chotsimikizirika cha Yehova. (Yohane 17:17) Ponena za gawo lake la ntchito limeneli, Yesu Kristu anati: “Ndinabadwa ndi kudza m’dziko kaamba ka chifuno chimodzi ichi, kudzalankhula za choonadi. Aliyense amene ali wa choonadi amvera ine.” (Yohane 18:37, TEV; Luka 4:43) Yesu sanaleke kuphunzitsa awo amene anali ndi mitima ndi makutu omvera. Pa Luka 24:45, timauzidwa kuti: “Ndipo [Kristu Yesu] anawatsegulira mitima yawo, kuti adziŵitse malembo.”
Mu utumiki wa Yesu iye mwaufulu anagwira Mawu olembedwa, akumalongosola ndi kulozera ku malemba “m’chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi masalmo.” (Luka 24:27, 44) Awo amene anamvetsera kulongosola kwake Malemba anachita chidwi kwambiri ndi kumveketsa kwake zinthu, limodzinso ndi luso lake la kuphunzitsa. (Mateyu 7:28, 29; Marko 1:22; Luka 4:32; 24:32) Kwa iye, Malemba anali buku losavuta kumva.
Baibulo ndi Otsatira a Yesu
Mtumwi Paulo, wotsanza Yesu Kristu, anaona kufunika kwa kuphunzitsa ena zimene Malemba ali nazo. Nayenso anadziŵa kuti analembedwa kuti amvetsetsedwe. Nchifukwa chake anaphunzitsa poyera ndipo mosakayikira anamasulira Malemba m’nyumba za awo amene anafuna kuwamvetsetsa. Paulo anadziŵikitsa lingaliro lake pamene anati: “Mudziŵa kuti sindinakubisirani kanthu kamene kakakhala kothandiza kwa inu pamene ndinalalikira ndi kuphunzitsa poyera ndi m’nyumba zanu.” (Machitidwe 20:20, TEV) M’makambitsirano ake anakambitsirana za m’Malemba, akumafotokoza ndi kutsimikizira mfundo zake ndi maumboni. (Machitidwe 17:2, 3) Anali wofunitsitsa kuthandiza ena kumvetsetsa tanthauzo la Malemba.
Kodi muli ndi chilakolako cha kumvetsetsa zinthu zimene Yesu ndi ophunzira ake anaphunzitsa? (1 Petro 2:2) Nzika za Bereya wakale zinali ndi chikhumbo chotero, ndipo zinali zofunitsitsa kukhulupirira zimene mtumwi Paulo anali kuziphunzitsa ponena za Kristu. Chotero zinalimbikitsidwa kuphunzira Malemba tsiku ndi tsiku ndipo motero zinatsimikizira kuti mbiri yabwino imene zinamva inalidi choonadi. Chifukwa chakuti maganizo awo anali omvera, “ambiri a iwo anakhulupira.”—Machitidwe 17:11, 12.
Kuti amvetsetse Baibulo, munthu afunikira kukhala ndi mkhalidwe wabwino wa mtima, chikhumbo choona cha kuphunzira, ndi ‘wozindikira kusoŵa kwake kwauzimu.’ (Mateyu 5:3, NW) Pamene Yesu anafunsidwa kuti: “Chifukwa chanji muphiphiritsira iwo m’mafanizo?” iye anayankha nati: “Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziŵa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo.” Kunanenedweratu kuti iye ‘akatsegula pakamwa pake ndi mafanizo; ndi kuulula zinthu zobisika.’ (Mateyu 13:10, 11, 35) Chotero Yesu analankhula mwa mafanizo kuti apatule awo ongomvetsera chabe ndi omvetsera ongofunsafunsa kwa awo amene moona mtima anafuna kudziŵa. Ophunzira a Yesu anasonyeza kuona mtima kwawo panthaŵi ina pamene analoŵa naye m’nyumba nati: “Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m’munda.”—Mateyu 13:36.
Nkwachionekere kuti tifunikira thandizo ngati titi timvetsetse Baibulo. Mtsogoleri wachipembedzo Hal Llewellyn, mlembi wa United Church wa zaumulungu, chikhulupiriro, ndi chiyanjano, anati: “Nkofunika kwambiri kumveketsa bwino lomwe zimene Baibulo limatanthauza kwa ife ndi mmene limaŵerengedwera ndi kumasuliridwa.” Koma ngakhale kuti si onse amene adziŵa zimenezo, choonadi nchakuti sitingamvetsetse Baibulo mwa ife tokha. Tifunikira thandizo.
Kodi Pali Thandizo Lotani?
M’Baibulo muli miyambi youma, mafunso ovuta, ndi mawu akuya amene amafuna kumasulira. Angakhale atalinganizidwa kuti akavute kumva, akumagwiritsira ntchito mafanizo amene sanayenera kumveka panthaŵi imene analembedwa. Koma ananenadi za zifuno za Yehova. Mwachitsanzo, Chivumbulutso 13:18 chimati “chiŵerengero cha chilombocho” ndicho “mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi.” Pamene vesilo limanena kuti “pano pali nzeru,” silimafotokoza tanthauzo la chiŵerengerocho. Komabe, Yehova, kupyolera mwa gulu lake, walola atumiki ake okhulupirika kuzindikira tanthauzo lake lerolino. (Onani bokosi lakuti, “Njira Yomvetsetsera Baibulo.”) Nanunso mungapeze kuzindikira kumeneku mothandizidwa ndi awo amene ali ozoloŵera ‘kulunjika nawo bwino mawu a choonadi.’—2 Timoteo 2:2, 15, 23-25; 4:2-5; Miyambo 2:1-5.
Nthaŵi zina Yesu anagwiritsira ntchito mafanizo kusonyeza kulabadira kapena kusalabadira kwa anthu uthenga wa Ufumu. Anasonyeza kuti ena sakapita patsogolo chifukwa cha kulefulidwa ndi zitsutso zochokera kwa mabwenzi ndi achibale. Ena akalola “nsautso kapena zunzo” kuwononga chiyamikiro chawo cha uthenga wa Ufumu. Ndiponso ena akalola zochitika zatsiku ndi tsiku za moyo, “kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma,” kutsamwitsa chikondi chilichonse chimene angakhale nacho pa mbiri yabwino. Komanso, pali awo amene mokondwera amalabadira ndipo ali ofunitsitsa kumva mawu amtengo wakewo ndi kupeza lingaliro lake. Iwo “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa” m’Dziko Lachikristu, zonenedwa kukhala zikuchitidwa m’dzina la Yesu Kristu. Oterowo amalakalaka kuphunzitsidwa m’njira ya Yehova ndipo motero kumvetsetsa zimene aŵerenga m’Baibulo.—Mateyu 13:3-9, 18-23; Ezekieli 9:4; Yesaya 2:2-4.
Kwa awo amene afuna kupeza chidziŵitso cha zifuno za Yehova mwaumwini, Yehova angaone kuti thandizo lofunikiralo likuperekedwa. Mwachitsanzo, Baibulo limasimba kuti mzimu wa Yehova unatsogolera mlaliki Filipo kuthandiza mwamuna wa ku Aitiopiya amene anali kupenda buku la Baibulo la Yesaya pamene anali paulendo kuchokera ku Yerusalemu. Paulendo wake wakwawo, iye anali kuliŵerengera m’galeta lake. Pomvera chitsogozo cha mzimu woyera wa Yehova, Filipo anathamangira kugaletalo nafunsa kuti: “Kodi muzindikira chimene muŵerenga?” Mwamunayo anali wodzichepetsa ndi woona mtima ndithu povomereza kuti anafunikiradi thandizo. Filipo mokondwera anaphunzitsa munthu wanjala yauzimu ndi wophunzitsika ameneyu. Malangizowo anamthandiza kumvetsetsa Malemba. Tsopano anadziŵa zimene anafunikira kuchita kuti akhale ndi unansi wabwino ndi Yehova kotero kuti akapeze moyo wosatha. Anakhala mtumiki wachimwemwe, wobatizidwa wa Yehova, amene analondola moyo umene unakondweretsa Mulungu.—Machitidwe 8:26-39.
Inu mungakhale ndi Baibulo m’nyumba mwanu, ndipo mungakhale mutaliŵerenga nthaŵi zambiri. Mwinamwake mwakumana ndi vuto limodzimodzi longa la munthu wa ku Aitiopiya wodzichepetsa ndi woona mtimayo. Iye sanali kumvetsetsa zimene anali kuŵerenga. Anafunikira thandizo ndipo sanazengereze kulandira thandizo limene Yehova Mulungu anakonda kumpatsa. Mofanana ndi Filipo, Mboni za Yehova zili zofunitsitsa kukuthandizani kumvetsetsa zinthu za Mulungu zolembedwa m’Mawu ake, Baibulo. Zimadziŵa kuti Yehova anapereka Baibulo ndipo anafuna kuti limvetsetsedwe.—1 Akorinto 2:10; Aefeso 3:18; 2 Petro 3:16.
Nchifukwa Ninji Baibulo Lili Lofunika?
Tikukhala m’nthaŵi yovuta koposa m’mbiri ya anthu. Baibulo limaitcha “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 24:3) Zochitika zambiri zimene zikuchitika kukwaniritsa ulosi wa Baibulo chiyambire 1914 zikusonyeza kuti tsopano posachedwapa Ufumu wakumwamba wa Mulungu ‘udzaphwanya ndi kutha maboma ena onse.’—Danieli 2:44.
Dziŵerengereni nokha, zimene zinanenedweratu m’Baibulo m’Mateyu chaputala 24, Marko chaputala 13, ndi Luka chaputala 21. Mudzapeza kuti zochitika zofotokozedwazo zimayambukira dziko lonse. Zimaphatikizapo nkhondo za dziko—zosiyana ndi nkhondo zina zilizonse. Kuyambira pa Nkhondo Yadziko I, taona njala, zivomezi, ndi nthaŵi ya kusayeruzika kwakukulu zimene zinanenedweratu. Ndipo tsopano mitundu ikuoneka kukhala ili pafupi kupereka chilengezo chimene chidzapereka chizindikiro chotsimikizirika chakuti chiwonongeko cha dziko chayandikira. Ponena za chimenechi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. Pamene angonena, Mtendere ndi [chisungiko, NW], pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, . . . ndipo sadzapulumuka konse.” (1 Atesalonika 5:2, 3) Kodi ndani amene sadzapulumuka? Paulo akufotokoza kuti: “Iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu.” (2 Atesalonika 1:7-9) Mbali ya chizindikiro chachiungwecho inali kudzakwaniritsidwa ndi awo amene amamvera lamulo loperekedwa pa Mateyu 24:14 la kulalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu pa dziko lonse lapansi.’
Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri zikutsatira lamulo limeneli m’maiko ndi zisumbu za m’nyanja 231. Zimafika panyumba za anthu ndi kuwapempha mwachindunji kuphunzira za boma la Ufumu wa Yehova. Zimasonyeza mokoma mtima njira imene aliyense ayenera kutenga kuti akhale pakati pa opulumuka dongosolo ili la zinthu ndi kukhala pa dziko lapansi laparadaiso pamene sipadzakhala kulira, kuusa moyo, zoŵaŵa, kapena imfa.—Chivumbulutso 21:3, 4.
Nthaŵi ya dziko loipali ikutha mofulumira, ndipo nkofunika kuti onse amene akufuna kupulumuka mapeto a dzikoli aphunzire zimene ‘kumvera uthenga wabwino’ kumaphatikizapo ndipo motero kupulumuka chiwonongekocho. Nthaŵi yotsatira imene Mboni za Yehova zidzafika panyumba panu, bwanji osavomereza pempholo la kukhala ndi phunziro la Baibulo la mlungu ndi mlungu? Chabwinonso, bwanji osazipempha kuphunzira nanu Baibulo chifukwa chakuti mukufuna kulimvetsetsa?
[Bokosi patsamba 8]
NJIRA YOMVETSETSERA BAIBULO
YESU anatitsimikizira kuti pambuyo pa imfa ndi kuuka kwake, akapereka “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene akatumikira monga njira yake yolankhulirana. (Mateyu 24:45-47) Mtumwi Paulo anadziŵikitsa njira imeneyi kwa Akristu a ku Efeso pamene analemba kuti, “kuti mu [mpingo, NW] azindikiritse . . . nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu, monga mwa [chifuno, NW] cha nthaŵi za nthaŵi, chimene anachita mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aefeso 3:10, 11) Unali mpingo wa Akristu odzozedwa, wobadwa pa Pentekoste wa 33 C.E., umene unaikiziridwa “zovumbuluka.” (Deuteronomo 29:29) Monga gulu, Akristu odzozedwa amatumikira monga kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. (Luka 12:42-44) Gawo lawo lopatsidwa ndi Mulungu ndilo kupereka chidziŵitso chauzimu cha “zovumbuluka.”
Monga momwedi ulosi wa Baibulo unasonyera kwa Mesiya, umatilunjikitsanso ku gulu logwirizana la Mboni Zachikristu zodzozedwa limene tsopano likutumikira monga kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.a Limatithandiza kumvetsetsa Mawu a Mulungu. Onse amene afuna kumvetsetsa Baibulo ayenera kuzindikira kuti “nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu” ingadziŵike kokha mwa njira yolankhulirana ya Yehova, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.—Yohane 6:68.
[Mawu a M’munsi]
a Onani The Watchtower ya March 1, 1981, pamasamba 24-30.