Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 11/1 tsamba 4-8
  • Kuvutika kwa Anthu Kodi nchifukwa ninji Mulungu amakulola?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuvutika kwa Anthu Kodi nchifukwa ninji Mulungu amakulola?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyamba kwa Kuvutika kwa Anthu
  • Yankho Lanzeru la Mulungu
  • Kodi Nchiyaninso Chimene Chatsimikiziridwa?
  • N’chifukwa Chiyani Zoipa Zikupitirirabe?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Nkhani Imene Ikulowetsamo Inu
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amavutika?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Chilimbikitso kwa Anthu Amene Akuvutika
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 11/1 tsamba 4-8

Kuvutika kwa Anthu Kodi nchifukwa ninji Mulungu amakulola?

PACHIYAMBI pa mbiri ya munthu, panalibiretu misozi ya chisoni kapena ya zoŵaŵa. Panalibe kuvutika kwa anthu. Mtundu wa anthu unali ndi chiyambi changwiro. “Anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.”​—Genesis 1:31.

Koma ena amatsutsa kuti, ‘Nkhani ya Adamu ndi Hava m’munda wa Edene yangokhala yopeka chabe.’ Mwachisoni, atsogoleri ambiri achipembedzo a Dziko Lachikristu amanena zimenezi. Komabe, munthu wokhala ndi ulamuliro wapamwamba Yesu Kristu mwiniyo anachitira umboni zochitika za mu Edene kukhala za mu mbiri. (Mateyu 19:4-6) Ndiponso, njira yokha yozindikirira chifukwa chimene Mulungu walolera anthu kuvutika ndiyo kupenda zochitika zimenezi za mbiri yoyambirira ya munthu.

Munthu woyamba, Adamu, anapatsidwa ntchito yokhutiritsa ya kusamalira munda wa Edene. Ndiponso, Mulungu anamuikira chonulirapo cha kufutukula malo ake a Edenewo kukhala munda wachisangalalo wapadziko lonse. (Genesis 1:28; 2:15) Kuti athandize Adamu kukwaniritsa ntchito yaikulu imeneyi, Mulungu anampatsa mnzake wa muukwati, Hava, nawauza kuti abalane ndi kuchuluka ndi kugonjetsa dziko lapansi. Komabe panali kufunikira kanthu kena kuti chifuno cha Mulungu cha dziko lapansi ndi mtundu wa anthu chipambane. Pokhala wopangidwa m’chifanizo cha Mulungu, munthu anali ndi ufulu wa kusankha; chifukwa chake, ufulu wa kusankha wa munthu sunafunikire kuwombana konse ndi wa Mulungu. Apo phuluzi, pakakhala chisokonezeko m’chilengedwe, ndipo chifuno cha Mulungu cha kudzaza dziko lapansi ndi banja la anthu lamtendere sichikakwaniritsidwa.

Kugonjera ulamuliro wa Mulungu sikunali kongochitika kokha. Kunafunikira kukhala chisonyezero chachikondi cha ufulu wa kusankha wa munthu. Mwachitsanzo, timaŵerenga kuti pamene Yesu Kristu anayang’anizana ndi chiyeso chachikulu, anapemphera kuti: “Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine; koma sikufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike.”​—Luka 22:42.

Mofananamo, zinadalira kwa Adamu ndi Hava kusonyeza kuti kaya iwo anafuna kugonjera ulamuliro wa Mulungu. Kaamba ka chifuno chimenechi, Yehova Mulungu analinganiza chiyeso chaching’ono. Umodzi wa mitengo imene inali m’munda unatchedwa “mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa.” Unaimira kuyenera kwa Mulungu kwa kupereka miyezo ya khalidwe lolondola. Mosabisa mawu, Mulungu analetsa kudyedwa kwa chipatso cha mtengo umenewu. Ngati Adamu ndi Hava sakamvera, zimenezi zikachititsa imfa yawo.​—Genesis 2:9, 16, 17.

Kuyamba kwa Kuvutika kwa Anthu

Tsiku lina mwana wauzimu wa Mulungu anapereka chikayikiro pa njira ya kulamulira ya Mulungu. Pogwiritsira ntchito njoka monga cholankhulira, iye anafunsa Hava kuti: “Eya! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” (Genesis 3:1) Motero mbewu ya chikayikiro inabzalidwa m’maganizo mwa Hava ponena za kuti kaya njira ya kulamulira ya Mulungu inali yabwino.a Poyankha, Hava anapereka yankho lolondola, limene anauzidwa ndi mwamuna wake. Komabe, pamenepo cholengedwa chauzimucho chinatsutsa Mulungu ndi kunama ponena za zotulukapo za kusamvera, chikumati: “Kufa simudzafayi; chifukwa adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.”​—Genesis 3:4, 5.

Mwachisoni, Hava ananyengedwa nayamba kuganiza kuti kusamvera kukadzetsa moyo wabwino kwambiri osati kuvutika kwa anthu. Pamene anayang’ana kwambiri chipatsocho, mpamenenso chinaonekera kukhala chokhumbika kwambiri, ndipo anayamba kuchidya. Pambuyo pake, iye ananyengerera Adamu kuti nayenso adye. Mwatsoka, Adamu anasankha chiyanjo cha mkazi wake mmalo mwa chiyanjo cha Mulungu.​—Genesis 3:6; 1 Timoteo 2:13, 14.

Mwa kusonkhezera chipanduko chimenechi, cholengedwa chauzimucho chinadzisandutsa wotsutsa Mulungu. Motero iye anatchedwa kuti Satana, kuchokera ku liwu Lachihebri lotanthauza “wotsutsa.” Iye anali atanamiziranso Mulungu, akumadzipanga kukhala woneneza. Chifukwa chake, iye amatchedwanso Mdyerekezi, kuchokera ku liwu Lachigiriki lotanthauza “woneneza.”​—Chivumbulutso 12:9.

Motero, kuvutika kwa anthu kunayamba. Zolengedwa zitatu za Mulungu zinagwiritsira ntchito molakwa mphatso yawo ya ufulu wa kusankha, zikumasankha moyo wadyera wotsutsana ndi Mlengi wawo. Tsopano panabuka funso lakuti, Kodi ndimotani mmene Mulungu akasamalirira nkhani yachipanduko imeneyi m’njira yolungama imene ikakhutiritsa zolengedwa zake zonse, kuphatikizapo angelo okhulupirika kumwamba ndi mbadwa za Adamu ndi Hava zamtsogolo?

Yankho Lanzeru la Mulungu

Ena angatsutse kuti kukanakhala bwino koposa ngati Mulungu akanawononga nthaŵi yomweyo Satana, Adamu, ndi Hava. Koma zimenezo sizikanathetsa nkhani zimene zinadzutsidwa ndi chipandukocho. Satana anali atatsutsa njira ya kulamulira ya Mulungu, akumapereka lingaliro lakuti anthu akakhala bwino kwambiri popanda ulamuliro wa Mulungu. Ndiponso, chipambano chake m’kuchotsa anthu aŵiri oyamba mu ulamuliro wa Mulungu chinadzutsa mafunso ena. Popeza kuti Adamu ndi Hava anachimwa, kodi zimenezi zinatanthauza kuti panali kanthu kena kolakwika ndi njira imene Mulungu analengera munthu? Kodi Mulungu angakhale ndi winawake padziko lapansi amene angakhalebe wokhulupirika kwa iye? Ndipo bwanji za ana aungelo a Yehova amene anaona chipanduko cha Satana? Kodi iwo akachirikiza chilungamo cha ulamuliro Wake? Mwachionekere, panafunika nthaŵi yokwanira yothetsera nkhani zonsezi. Ndicho chifukwa chake Mulungu walola Satana kukhalapobe kufikira tsiku lathu.

Ponena za Adamu ndi Hava, Mulungu anapereka chilango cha imfa kwa iwo patsiku la kusamvera kwawoko. Chotero kufa kunayambika. Mbadwa zawo, zimene zinabadwa Adamu ndi Hava atachimwa, zinalandira choloŵa cha uchimo ndi imfa kwa makolo awo opanda ungwirowo.​—Aroma 5:14.

Satana anayamba ntchito yake ndi anthu aŵiri oyamba kumbali yake pankhaniyo. Iye wagwiritsira ntchito nthaŵi imene waloledwa kuyesa kulamulira mbadwa zonse za Adamu. Iye wakhozanso kunyenga angelo ambiri kugwirizana naye m’chipanduko chake. Komabe, unyinji wa ana aungelo a Mulungu achirikiza mokhulupirika chilungamo cha ulamuliro wa Yehova.​—Genesis 6:1, 2; Yuda 6; Chivumbulutso 12:3, 9.

Mkanganowo unali wonena za ulamuliro wa Mulungu ndi wa Satana, nkhani imene inalidi yamphamvu m’masiku a Yobu. Munthu wokhulupirika ameneyu anasonyeza mwa khalidwe lake kuti anasankha ulamuliro wolungama wa Mulungu mmalo mwa kudziimira kwausatana, mofanana ndi anthu owopa Mulungu onga Abele, Enoke, Nowa, Abrahamu, Isake, Yakobo, ndi Yosefe. Yobu anakhala mumakambitsirano amene anachitika kumwamba pamaso pa angelo okhulupirika a Mulungu. Pochirikiza ulamuliro Wake wolungama, Mulungu anati kwa Satana: “Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuwopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.”​—Yobu 1:6-8.

Pokana kugonja, Satana ananena kuti Yobu anatumikira Mulungu kaamba ka zifukwa za dyera chabe, popeza kuti Mulungu anadalitsa kwambiri Yobu ndi chuma chakuthupi. Chotero Satana anati: “Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pankhope panu.” (Yobu 1:11) Satana anachitadi zowonjezereka, akumatsutsa umphumphu wa zolengedwa zonse za Mulungu. “Munthu adzapereka zonse ali nazo kuwombola moyo wake,” iye anatero. (Yobu 2:4) Kuukira koneneza kumeneku kunaphatikizapo osati Yobu yekha komanso olambira onse okhulupirika a Mulungu, kumwamba ndi padziko lapansi. Satana anapereka lingaliro lakuti iwo akaleka kukhala paunansi wawo ndi Yehova ngati miyoyo yawo inali pachiswe.

Yehova Mulungu anakhulupirira kotheratu kuti Yobu akasunga umphumphu. Popereka umboni wa zimenezo, iye analola Satana kuvutitsa munthuyo Yobu. Mwa kukhulupirika kwake Yobu sanangodzichotsera liwongo pa dzina lake, komanso, chofunika kwambiri, anachirikiza chilungamo cha ulamuliro wa Yehova. Mdyerekezi anasonyezedwa kukhala wonama.​—Yobu 2:10; 42:7.

Komabe, Yesu Kristu ndiye chitsanzo chabwino koposa cha kukhulupirika pansi pa chiyeso. Mulungu anasamutsa moyo wa Mwana waungelo ameneyu kuchokera kumwamba kuuloŵetsa m’mimba ya namwali wina. Chifukwa chake Yesu sanalandire choloŵa cha uchimo ndi kupanda ungwiro. Mmalomwake iye anakula nakhala munthu wangwiro, wolingana ndendende ndi munthu woyamba asanataye ungwiro wake. Yesu anapangidwa kukhala chandamale chapadera ndi Satana, akumabweretsa ziyeso ndi mayesero ambiri pa iye, zikumathera mu imfa yochititsa manyazi. Koma Satana analephera kuswa umphumphu wa Yesu. M’njira yachikwanekwane, Yesu anachirikiza chilungamo cha ulamuliro wa Atate wake. Iye anasonyezanso kuti munthu wangwiroyo Adamu analibe chifukwa chogwirizanirana ndi Satana m’chipanduko chake. Adamu akanatha kukhala wokhulupirika pansi pa chiyeso chake chochepa kwambiricho.

Kodi Nchiyaninso Chimene Chatsimikiziridwa?

Pafupifupi zaka 6,000 za kuvutika kwa anthu zapita chiyambire chipanduko cha Adamu ndi Hava. Mkati mwa nthaŵi imeneyi Mulungu walola mtundu wa anthu kuyesa mipangidwe yambiri yosiyanasiyana ya maboma. Mbiri yonyansa ya kuvutika kwa anthu imatsimikizira kuti munthu sangakhoze kudzilamulira. Kwenikweni, kusalamulirika tsopano kukufala m’madera ambiri a dziko lapansi. Kupandukira Mulungu, kumene kunachirikizidwa ndi Satana, nkwatsoka.

Yehova sanafunikire kutsimikizira kalikonse. Iye amadziŵa kuti njira yake yolamulira njachilungamo ndipo njopindulitsa kwa zolengedwa zake. Komabe, kuti ayankhe mokhutiritsa mafunso onse odzutsidwa ndi chipanduko cha Satana, iye wapatsa mpata zolengedwa zake zanzeru kuti zisankhe ulamuliro wake wolungama.

Mphotho za kukonda Mulungu ndi kukhala wokhulupirika kwa iye zimaposa nyengo yaifupi ya kuvutika pa dzanja la Mdyerekezi. Nkhani ya Yobu imasonyeza zimenezi. Yehova Mulungu anachiritsa Yobu nthenda imene Mdyerekezi anali atambweretsera. Ndiponso, Mulungu “anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake.” Potsirizira pake, pambuyo pa kuwonjezeredwa zaka za moyo 140, ‘anamwalira Yobu, wokalamba ndi wamasiku ochuluka.’​—Yobu 42:10-17.

Wolemba Baibulo Wachikristu Yakobo amatchula zimenezi akumati: “Mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.”​—Yakobo 5:11.

Tsopano nthaŵi ya Satana ndi dziko lake yatha. Posachedwapa, Mulungu adzathetsa kuvutika konse kumene chipanduko cha Satana chadzetsa pa mtundu wa anthu. Ngakhale akufa adzaukitsidwa. (Yohane 11:25) Ndiyeno, amuna okhulupirika onga Yobu adzakhala ndi mwaŵi wa kupeza moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. Madalitso amtsogolo ameneŵa amene Mulungu adzatsanulira pa atumiki ake adzamchirikiza kunthaŵi zanthaŵi kukhala Mfumu imene ilidi ‘yodzala ndi chikondi ndi yachifundo.’

[Mawu a M’munsi]

a Loya ndi wolemba mabuku wina wa m’zaka za zana la 20, Philip Mauro, amene anapenda za nkhani imeneyi pofotokoza “Magwero a Kuipa,” ananena kuti zimenezi zinali “zochititsa mavuto onse a mtundu wa anthu.”

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 8]

MILUNGU YA ANTHU YANKHANZA

MILUNGU yamakedzana kaŵirikaŵiri inasonyezedwa kukhala ya mbanda ndi ya chilakolako choipa. Kuti aikondweretse, makolo anawotcha ngakhale ana awo amoyo pamoto. (Deuteronomo 12:31) Kumbali ina yonkitsa, afilosofi achikunja anaphunzitsa kuti Mulungu anali wopanda mikhalidwe yonga mkwiyo kapena chifundo.

Malingaliro ouziridwa ndi ziŵanda a afilosofi ameneŵa anasonkhezera anthu okhulupirira Mulungu, Ayuda. Wafilosofi Wachiyuda, Philo, yemwe anakhalako m’nthaŵi ya Yesu, ananena kuti Mulungu “sakhoza kukhudzidwa mtima mwa njira iliyonse.”

Ngakhale kagulu Kachiyuda kokhwimitsa zinthu ka Afarisi sikanathe kuleŵa chisonkhezero cha filosofi Yachigiriki. Iwo anatengera ziphunzitso za Plato zakuti munthu anapangidwa ndi moyo wosafa wotsekeredwa m’thupi mwake. Ndiponso, malinga ndi kunena kwa wolemba mbiri wa m’zaka za zana loyamba Josephus, Afarisi anakhulupirira kuti miyoyo ya anthu oipa “imazunzika ndi chilango chosatha.” Komabe, Baibulo silimapereka maziko a lingaliro loterolo.​—Genesis 2:7; 3:19; Mlaliki 9:5; Ezekieli 18:4.

Bwanji ponena za atsatiri a Yesu? Kodi iwo analola kusonkhezeredwa ndi filosofi yachikunja? Pozindikira ngozi imeneyi, mtumwi Paulo anachenjeza Akristu anzake kuti: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.”​—Akolose 2:8; onaninso 1 Timoteo 6:20.

Mwachisoni, odzinenera kukhala oyang’anira Achikristu ambiri a m’zaka za zana lachiŵiri ndi lachitatu ananyalanyaza chenjezo limenelo ndipo anaphunzitsa kuti Mulungu samakhudzidwa mtima. The Encyclopedia of Religion imati: “Kwenikweni, mikhalidwe ya Mulungu inalingaliridwa monga momwe inatsimikiziridwa ndi malingaliro Achiyuda ndi a filosofi a panthaŵiyo . . . Lingaliro lakuti Mulungu Atate angakhale anali ndi mikhalidwe yonga chifundo . . . laonedwa ndi ochuluka monga losalandirika kufikira chakumapeto kwa zaka za zana la makumi aŵiri.”

Motero, Dziko Lachikristu linatengera chiphunzitso chonyenga cha mulungu wankhanza amene amalanga ochimwa mwa kuwazunza amoyo kwamuyaya. Kumbali ina, Yehova Mulungu amanena poyera m’Mawu ake, Baibulo, kuti “mphotho yake ya uchimo ndi imfa,” osati kuzunzika wamoyo kosatha.​—Aroma 6:23.

[Mawu a Chithunzi]

Pamwambapo: Acropolis Museum, Greece

Chilolezo cha The British Museum

[Chithunzi patsamba 7]

Chifuno cha Mulungu cha kusanduliza dziko lapansi kukhala paradaiso wonga Edene chidzakwaniritsidwa!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena