Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 11/15 tsamba 4-7
  • Kodi Akufa Ali Kuti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Akufa Ali Kuti?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ndani Amene Amapita Kumwamba?
  • Amene Samapita Kumwamba
  • Kugona mu Imfa
  • Moyo Watsopano wa Makolo Athu Akufa
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Ndani Amene Amapita Kumwanba, ndipo Nchifukwa Ninji?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Akufa Anu Okondedwa—Kodi Mudzaŵaonanso?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Njira Yokhayo Yothetsera Imfa
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 11/15 tsamba 4-7

Kodi Akufa Ali Kuti?

“DZIKO lapansi ndi pamsika; kumwamba ndiko kwathu,” umatero mwambi wa Ayoruba a ku West Africa. Lingaliro limeneli lili m’zipembedzo zambiri. Limapereka ganizo lakuti dziko lapansi lili monga msika umene timafikapo kwa nthaŵi yochepa ndi kuchoka. Malinga ndi chikhulupiriro chimenechi, pa imfa timapita kumwamba, kumalo athu enieni.

Baibulo limaphunzitsa kuti ena amapita kumwamba. Yesu Kristu anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. . . . Ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.”​—Yohane 14:2, 3.

Mawu a Yesu samatanthauza kuti anthu abwino onse amapita kumwamba kapena kuti kumwamba ndiko kwawo kwa anthu. Enawo amatengeredwa kumwamba kukalamulira dziko lapansi. Yehova Mulungu anadziŵa kuti maboma a munthu sakakhoza konse kuyendetsa zinthu mwachipambano padziko lapansi. Chifukwa chake, iye analinganiza boma lakumwamba, kapena Ufumu, umene potsirizira pake ukatenga ulamuliro wonse wa dziko lapansi ndi kulisintha kukhala Paradaiso amene analinganiza poyambirira. (Mateyu 6:9, 10) Yesu ndiye akakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Danieli 7:13, 14) Ena akasankhidwa mwa mtundu wa anthu kukalamulira naye. Baibulo linaneneratu pasadakhale kuti amene akatengeredwa kumwamba akakhala “ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu” ndipo akachita “ufumu padziko.”​—Chivumbulutso 5:10.

Ndani Amene Amapita Kumwamba?

Polingalira thayo lalikulu limene olamulira akumwamba ameneŵa akakhala nalo, sikodabwitsa kuti iwo akafunikira kufitsa ziyeneretso zokhwima. Opita kumwambawo afunikira kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Yehova ndipo ayenera kummvera iye. (Yohane 17:3; Aroma 6:17, 18) Iwo afunikira kusonyeza chikhulupiriro pa nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. (Yohane 3:16) Komabe, palinso zina zoloŵetsedwamo. Ayenera kuitanidwa ndi kusankhidwa ndi Mulungu kudzera mwa Mwana wake. (2 Timoteo 1:9, 10; 1 Petro 2:9) Ndiponso, iwo ayenera kukhala Akristu obatizidwa ndi ‘obadwa chatsopano,’ obadwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Yohane 1:12, 13; 3:3-6) Afunikiranso kusunga umphumphu kwa Mulungu kufikira imfa.​—2 Timoteo 2:11-13; Chivumbulutso 2:10.

Mamiliyoni osaŵerengeka a anthu omwe akhalapo ndi moyo ndi kufa sanafitse ziyeneretso zimenezi. Ambiri sanakhale ndi mpata waukulu wakuti aphunzire za Mulungu woona. Ena sanaliŵerengepo konse Baibulo ndipo amadziŵa zochepa kwambiri kapena samadziŵa kalikonse ponena za Yesu Kristu. Ngakhale pakati pa Akristu oona padziko lapansi lerolino, ndi oŵerengeka okha omwe asankhidwa ndi Mulungu kukakhala ndi moyo wakumwamba.

Motero, chiŵerengero cha opita kumwambawo chikakhala chochepa. Yesu anatcha oterowo “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Pambuyo pake, zinadzavumbulidwa kwa mtumwi Yohane kuti “ogulidwa kuchokera ku dziko” amenewo odzalamulira ndi Kristu kumwamba akakhala 144,000 chabe. (Chivumbulutso 14:1, 3; 20:6) Pamene ayerekezeredwa ndi mamiliyoni zikwizikwi za anthu omwe akhalapo padziko lapansi, chimenechi nchiŵerengero chaching’ono kwenikweni.

Amene Samapita Kumwamba

Kodi nchiyani chimachitika kwa amene samapita kumwamba? Kodi akuvutika m’malo achizunzo chosatha, monga momwe zipembedzo zina zimaphunzitsira? Kutalitali, pakuti Yehova ali Mulungu wa chikondi. Makolo achikondi samaponya ana awo pamoto, ndipo Yehova samazunza anthu mwa njira imeneyo.​—1 Yohane 4:8.

Chiyembekezo cha ochuluka omwe amwalira ndicho chiukiriro cha padziko lapansi laparadaiso. Baibulo limanena kuti Yehova analenga dziko lapansi kuti “akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Wamasalmo analengeza kuti: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” (Salmo 115:16) Dziko lapansi ndilo limene lidzakhala mudzi wachikhalire wa mtundu wa anthu, osati kumwamba.

Yesu ananeneratu kuti: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [achikumbukiro, NW] adzamva mawu ake [a Yesu, “Mwana wa munthu”], nadzatulukira.” (Yohane 5:27-29) Mtumwi Wachikristu Paulo anatsimikizira kuti: “Ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Ali pamtengo wozunzirapo, Yesu analonjeza wochimwa wolapayo moyo mwa chiukiriro cha padziko lapansi laparadaiso.​—Luka 23:43.

Komabe, kodi mkhalidwe wa pakali pano wa akufa omwe adzaukitsidwa ku moyo padziko lapansi ngwotani? Chochitika china mu utumiki wa Yesu chimayankha funso limeneli. Bwenzi lake Lazaro anali atamwalira. Yesu asanapite kukamuukitsa, Iye anauza ophunzira Ake kuti: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.” (Yohane 11:11) Motero Yesu anayerekezera imfa ndi tulo, tulo tofa nato osalota.

Kugona mu Imfa

Malemba ena amagwirizana ndi lingaliro limeneli la kugona mu imfa. Iwo samaphunzitsa kuti anthu ali ndi mzimu wosafa umene umasamukira ku malo a mizimu pa imfa. M’malo mwake, Baibulo limati: “Akufa sadziwa kanthu bi . . . Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” (Mlaliki 9:5, 6, 10) Ndiponso, wamasalmo analengeza kuti munthu “abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”​—Salmo 146:4.

Malemba ameneŵa amasonyeza bwino lomwe kuti akugona mu imfawo satha kutiona kapena kutimva. Sakhoza kutidzetsera kaya dalitso kapena tsoka. Sali kumwamba, ndipo sakukhala m’chitaganya cha makolo akufa. Iwo ali opanda moyo, saliko.

Panthaŵi yake ya Mulungu, amene akugona mu imfa tsopano amene alinso m’chikumbukiro chake adzagalamutsidwira ku moyo m’dziko lapansi laparadaiso. Lidzakhala dziko lochotsedwapo kuipitsa, zovutitsa, ndi mavuto amene mtundu wa anthu ukuyang’anizana nawo tsopano. Idzakhala nthaŵi ya chisangalalo chotani nanga! M’Paradaiso ameneyo iwo adzakhala ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha, pakuti Salmo 37:29 limatitsimikizira kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”

[Bokosi pamasamba 6, 7]

NDINALEKA KULAMBIRA AKUFA

“Pamene ndinali mnyamata, ndinkathandiza atate popereka nsembe zawo za nthaŵi zonse kwa atate awo akufa. Nthaŵi ina atate atachira nthenda yowopsa, mwamuna wobwebweta anawauza kuti poyamikira kuchira kwawoko anayenera kupereka nsembe ya mbuzi, chilazi, kola nuts, ndi moŵa kwa atate awo akufawo. Atate anauzidwanso kuchonderera kwa makolo akufa kuti awatetezere ku matenda ena ndi masoka.

“Amayi anagula zofunikira za nsembeyo, imene inafunika kuperekedwera pamanda a agogo aamuna. Mandawo anali pambali penipeni pa nyumba yathu, malinga ndi mwambo wathu.

“Mabwenzi, achibale, ndi anansi anaitanidwa kudzaonerera nsembeyo. Atate, atavalira bwino chochitikacho, anakhala pampando atapenya kakachisi kumene zigaza zochulukirapo za mbuzi zimene zinaperekedwa nsembe papitapo zinali zitandandalikidwa. Ntchito yanga inali ya kutsanulira vinyo m’tambula yaing’ono kuchokera m’botolo, imene ndinkapatsa atate. Nawonso ankamutsanulira panthaka monga nsembe. Atate anaitana dzina la atate awo katatu napempherera chitetezo ku tsoka lamtsogolo kwa iwo.

“Anapereka kola nuts, ndipo nkhosa yamphongo inaphedwa, kuphikidwa, ndi kudyedwa ndi onse okhalapo. Nanenso ndinadyako ndi kuvina nawo nyimbo ndi ng’oma zoimbidwa. Atate anavina bwino kwambiri ndipo mwamphamvu, ngakhale kuti ukalamba wawo unali kuonekeratu. Panthaŵi ndi nthaŵi anapemphera kwa makolo awo akufa kuti adalitse tonsefe okhalapo, ndipo anthuwo, kuphatikizapo ine, tinkayankha kuti Ise, kutanthauza kuti ‘Zikhale motero.’ Ndinapenyerera atate ndi chidwi chachikulu ndi kukhumbira ndipo ndinalakalaka tsiku limene ndikakhala wamkulu wokhoza kupereka nsembe kwa makolo akufa.

“Ngakhale kuti panaperekedwa nsembe zochuluka, mtendere unasoŵekabe pabanjapo. Pamene kuli kwakuti panali ana aamuna atatu amoyo a amayi, palibe aliyense wa ana aakazi atatu obadwa kwa iwo yemwe anakhalitsa ndi moyo; onsewo anamwalira paubwana wawo. Pamene amayi anakhalanso ndi pathupi, atate anapereka nsembe zochuluka kuti mwanayo abadwe bwino.

“Amayi anabala mwana wina wamkazi. Patapita zaka ziŵiri mwanayo anadwala namwalira. Atate anakafunsira kwa wobwebweta, yemwe anati imfayo inachititsidwa ndi mdani. Wobwebwetayo anati kuti ‘mzimu’ wa mwanayo ulipsire, pakafunikira nkhuni yoyaka, botolo la moŵa, ndi mwana wa galu za nsembe. Nkhuni yoyakayo inafunikira kuikidwa pamandapo, moŵa unafunikira kuŵazidwa pamanda, ndipo mwana wa galu anafunikira kukwiriridwa wamoyo pafupi ndi mandawo. Zimenezi zinalingaliridwa kuti zikagalamutsa mzimu wa mtsikana wakufayo kuti ulipsire imfa yake.

“Ndinanyamula botolo la moŵalo ndi nkhuni yoyakayo popita kumanda, ndipo atate ananyamula kagaluko, komwe anakwirira malinga ndi malangizo a wobwebwetayo. Tonsefe tinakhulupirira kuti m’masiku asanu ndi aŵiri okha mzimu wa mtsikana wakufayo ukawononga munthu amene anachititsa imfa yake yamsangayo. Miyezi iŵiri inapita, ndipo sikunamveke imfa iliyonse chapafupi. Ndinakhala wogwiritsidwa mwala.

“Ndinali ndi zaka 18 zakubadwa panthaŵiyo. Posapita nthaŵi ndinakumana ndi Mboni za Yehova, zomwe zinandisonyeza m’Malemba kuti akufa sakhoza kuchita chabwino ngakhale choipa kwa amoyo. Pamene chidziŵitso cha Mawu a Mulungu chinazama mumtima mwanga, ndinauza atate kuti sindikatsagana nawonso kukapereka nsembe kwa akufa. Poyamba adakwiya nane chifukwa chakuwasiya, monga momwe iwo ananenera. Koma ataona kuti sindikanakana konse chikhulupiriro changa chatsopano, sanatsutse kulambira kwanga Yehova.

“Pa April 18, 1948, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga mwa ubatizo wa m’madzi. Chiyambire pamenepo, ndapitiriza kutumikira Yehova ndi chisangalalo chachikulu ndi chikhutiro, ndikumathandiza ena kumasuka pa kulambira makolo akufa, omwe sangakhoze kutithandiza ngakhale kutivulaza.”​—Yoperekedwa ndi J. B. Omiegbe, Benin City, mu Nigeria.

[Chithunzi patsamba 7]

Padzakhala chisangalalo chachikulu pamene akufa adzaukitsidwa padziko lapansi laparadaiso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena