“Ngati Muli ndi Mangawa a Misonkho, Perekani Misonkho”
“M’DZIKO lino lapansi palibe chinthu chotsimikizirika kusiyapo imfa ndi misonkho.” Anatero Benjamin Franklin nduna ya boma la America ndi woyamba kupanga zinthu wa m’zaka za zana la 18. Mawu ake, amene amagwidwa kaŵirikaŵiri, samasonyeza kusapeŵeka kwa misonkho kokha komanso mantha amene imadzetsa. Kwa anthu ambiri, kupereka misonkho sikumakondweretsa mofanana ndi imfa.
Ngakhale kuti kupereka misonkho kungakhale kosakondweretsa, kuli thayo limene Akristu oona amaliona mwamphamvu. Mtumwi Paulo analembera mpingo Wachikristu ku Roma kuti: “Patsani aliyense mangawa anu kwa iye: Ngati muli ndi mangawa a misonkho, perekani misonkho, ngati ndi ndalama, ndalamazo; ngati ndi kuwopa; kuwopako; ngati ndi ulemu; ulemuwo.” (Aroma 13:7, New International Version) Ndipo Yesu Kristu anali kunena za misonkho pamene anati: “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.”—Marko 12:14, 17.
Yehova walola “maulamuliro aakulu” a maboma kukhalako ndipo amafuna kuti atumiki ake aziwagonjera mokhala ndi polekezera. Pamenepa, kodi nchifukwa ninji Mulungu amafunitsitsa kuti olambira ake azipereka misonkho? Paulo akutchula zifukwa zazikulu zitatu: (1) “mkwiyo” wa “maulamuliro aakulu” polanga oswa malamulo; (2) chikumbumtima cha Mkristu, chimene sichidzakhala choyera ngati anama pa misonkho yake; (3) kufunikira kwa kulipira ‘atumiki’ ameneŵa kaamba ka ntchito zimene amachita ndi kusungitsa bata pamlingo wakutiwakuti. (Aroma 13:1-7) Ambiri angakhale osafuna kupereka misonkho. Komabe, iwo mosakayikira angaipidwe kwambiri kukhala m’dziko lopanda apolisi kapena ozima moto, okonza misewu, sukulu za boma, ndi zamtengatenga ndi mtokoma. Woweruza Wachimereka Oliver Wendell Holmes panthaŵi ina ananena kuti: “Misonkho ndiyo malipiro athu pokhala ndi chitaganya chotsungula.”
Kupereka misonkho sikuli kwachilendo kwa atumiki a Mulungu. Nzika za Israyeli wakale zinapereka misonkho kuchirikiza mafumu awo, ndipo ena a olamulirawo anaika mtolo wolemera kwambiri pa anthu mwa kukhometsa misonkho yopambanitsa. Ayuda anaperekanso mitulo ndi misonkho kwa maulamuliro akutali amene anawalamulira, onga Igupto, Peresiya, ndi Roma. Chotero Akristu m’tsiku la Paulo anadziŵa bwino zimene iye anali kulankhula pamene anatchula za kupereka misonkho. Iwo anadziŵa kuti ngakhale kuti misonkhoyo inali yabwino kapena yopambanitsa, ndipo mosasamala kanthu za mmene boma likanagwiritsirira ntchito ndalama zimenezo, anafunikira kupereka mangawa onse a msonkho amene anali nawo. Ndi mmenenso zilili kwa Akristu lerolino. Komabe, kodi ndi makhalidwe ati amene angatipatse chitsogozo popereka misonkho m’nthaŵi zino zovuta?
Makhalidwe Asanu Otsogolera
Khalani wadongosolo. Timatumikira ndi kutsanzira Yehova, amene “sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere.” (1 Akorinto 14:33; Aefeso 5:1) Kukhala wadongosolo nkofunika kwambiri pa nkhani ya kupereka misonkho. Kodi zolembedwa zanu zili zokwanira, zolongosoka, ndi zolinganizidwa bwino? Kaŵirikaŵiri, sipamafunikira mafaelo okwera mtengo. Mungaike lebulo pa faelo imodzi ya zolembedwa zamtundu umodzi (zonga malisiti zosonyeza ndalama zosiyanasiyana zolipiridwa). Kungakhale bwino kuika zimenezi m’mafaelo okulirapo a chaka chilichonse. M’maiko ambiri mafaelo amtundu umenewu afunikira kusungidwa kwa zaka zingapo popeza kuti boma lingafune kupenda zolembedwa zakale. Chotero musataye chilichonse kufikira mutatsimikizira kuti sichidzafunikiranso.
Khalani oona mtima. Paulo analemba kuti: “Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala [oona mtima m’zinthu zonse, NW].” (Ahebri 13:18) Kufunitsitsa kwathu kukhala oona mtima kuyenera kulamulira chosankha chilichonse chimene tipanga popereka misonkho yathu. Choyamba, talingalirani misonkho yofunikira kuperekedwa pa malipiro amene ayenera kudziŵitsidwa ku boma. M’maiko ambiri, malipiro owonjezereka—ochokera pa ziwongola dzanja, ntchito zina, malonda—ayenera kutengedwapo msonkho atangopyola pamlingo woikika. Mkristu amene ali ndi “chikumbumtima chokoma” adzafuna kudziŵa kuti ndi malipiro ati amene ayenerera msonkho kwawoko ndipo adzapereka msonkho wofunikawo.
Chachiŵiri, pali nkhani ya kubwezeredwa ndalama zina. Kaŵirikaŵiri maboma amalola opereka msonkho kubwezeredwa ndalama zina zowonongedwa pa malipiro awo otengedwapo msonkho. M’dziko lino losaona mtima, ambiri samaona choipa ndi kukhala “ochenjera” kapena “oyerekezera zinthu” popempha ndalama zoyenera kubwezeredwa. Zinamveka kuti mwamuna wina ku United States anagulira mkazi wake jekete laubweya lokwera mtengo, nalikoloŵeka pamalo ake antchito tsiku limodzi kuti abwezeredwe ndalama zake monga “za chokometsera” malo antchito! Mwamuna wina anapempha kubwezeredwa ndalama zowonongedwera pa ukwati wa mwana wake wamkazi monga zowonongedwera pantchito. Winanso anayesa kupempha kubwezeredwa ndalama zimene analipirira mkazi wake paulendo umene anapita naye ku Far East, ngakhale kuti mkaziyo anapita kumeneko kukangocheza ndi kusanguluka. Nkhani zotero zikuoneka kukhala zosatha. Kunena mwachidule, kutcha kanthu kena kukhala ndalama zowonongedwera pantchito pamene sizili tero ndiko kunama—chinthu chimene Mulungu wathu, Yehova, amanyansidwa nacho kwambiri.—Miyambo 6:16-19.
Khalani ochenjera. Yesu analimbikitsa otsatira ake kukhala “ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.” (Mateyu 10:16) Uphungu umenewu ungagwirebe ntchito pa kupereka kwathu misonkho. Makamaka m’maiko otukuka, anthu ambirimbiri masiku ano amalipirira kampani ya akaunti kapena katswiri wina kuwakonzera misonkho. Ndiyeno iwo amangosaina mafomuwo ndi kutumiza cheke. Imeneyi ingakhale nthaŵi yabwino yosonyezera kuchenjera kolembedwa pa Miyambo 14:15: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”
Opereka msonkho ambiri akumana ndi mavuto ku boma chifukwa chakuti ‘anakhulupirira mawu onse’ a akauntanti wosaona mtima kapena wokonza za misonkho wosadziŵa ntchitoyo. Nkwabwino chotani nanga kukhala wochenjera! Khalani wochenjera mwa kuŵerenga mosamalitsa pepala lililonse musanalisaine. Ngati zolembedwapo zina, zosiyidwa, kapena ndalama zochotsedwapo zikudabwitsani, pemphani kuti zilongosoledwe—mobwerezabwereza ngati nkofunikira—kufikira mutakhutiritsidwa kuti nkhaniyo ili yoona mtima ndi yogwirizana ndi malamulo. Zoona, m’maiko ambiri malamulo a misonkho akhala ocholoŵana kwambiri, koma malinga ndi kukhoza kwanu, kuli kwanzeru kumvetsetsa zonse zimene musaina. Nthaŵi zina, mungapeze kuti Mkristu mnzanu amene adziŵa malamulo a msonkho angakupatseni chidziŵitso china. Mkulu wina Wachikristu amene amasamalira nkhani za msonkho monga loya anati mwachidule: “Ngati akauntanti wanu akuuzani zinthu zabwino koposa, mwinamwake sizoona!”
Khalani wathayo. “Yense adzasenza katundu wake wa iye mwini,” analemba motero mtumwi Paulo. (Agalatiya 6:5) Ponena za kupereka misonkho, Mkristu aliyense ayenera kusenza thayo la kukhala woona mtima ndi wosunga malamulo. Imeneyi si nkhani yakuti akulu a mpingo angalangizirepo gulu la nkhosa limene amalisamalira. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 1:24.) Iwo samadziloŵetsa m’nkhani za msonkho kusiyapo ngati pachitika cholakwa chachikulu, mwinamwake amva mbiri yoipa m’chitaganya. Kaŵirikaŵiri, Mkristu mwiniyo ndiye ali ndi thayo pankhaniyi la kugwiritsira ntchito chikumbumtima chophunzitsidwa bwino kugwiritsira ntchito miyezo ya Malemba. (Ahebri 5:14) Zimenezi zikuphatikizapo kudziŵa kuti kusaina pepala la msonkho—mosasamala kanthu za amene analikonza—kungakhaledi umboni walamulo wakuti mwaŵerenga pepalalo ndipo mukhulupirira kuti zimene zalembedwapo nzoona.a
Khalani wopanda chilema. Oyang’anira Achikristu ayenera kukhala “opanda chilema” kuti ayenerere udindo wawo. Mofananamo, mpingo wonse uyenera kukhala wopanda chilema pamaso pa Mulungu. (1 Timoteo 3:2; yerekezerani ndi Aefeso 5:27.) Chotero amalimbikira kusunga mbiri yabwino m’chitaganya, ngakhale ponena za kupereka misonkho. Yesu Kristu mwiniyo anapereka chitsanzo pankhaniyi. Petro wophunzira wake anafunsidwa ngati Yesu anapereka msonkho wa pakachisi, nkhani yaing’ono ya malupiya aŵiri. Kwenikweni, Yesu sanayenera kupereka msonkho umenewu, chifukwa chakuti kachisi anali nyumba ya Atate wake ndipo palibe mfumu imene imafuna msonkho kwa mwana wake. Yesu ananenanso zimenezo; komabe anapereka msonkhowo. Ndipo iye anachita chozizwitsa kuti apeze ndalama yofunikirayo! Chifukwa ninji anapereka msonkho umene sanafunikira kutero? Yesu mwiniyo anati, “kuti ife tisawakhumudwitse.”—Mateyu 17:24-27.b
Sunganibe Mbiri Yolemekeza Mulungu
Mofananamo, Mboni za Yehova lerolino zimasamala kuti zisakhumudwitse ena. Nchifukwa chake kuli kosadabwitsa kuti monga gulu, zili ndi mbiri yabwino padziko lonse ya kukhala nzika zoona mtima ndi zopereka msonkho. Mwachitsanzo, nyuzipepala Yachispanishi ya El Diario Vasco inanena za kuzemba msonkho kofala m’Spain, koma inati: “Amene samachita zimenezi [ndi] Mboni za Yehova. Pamene akugula kapena kugulitsa, mtengo wa [katunduyo] umene amatchula umakhala woona zedi.” Mofananamo, nyuzipepala ya ku United States ya San Francisco Examiner zaka zingapo zapitazo inati: “Mungathe kuziona [Mboni za Yehova] kukhala nzika zopereka chitsanzo chabwino. Izo zimakhoma misonkho mwakhama, kusamalira odwala, kumenya nkhondo ya kuthetsa kusadziŵa kuŵerenga ndi kulemba.”
Palibe Mkristu woona amene angafune kuchita chinthu chimene chingawononge mbiri imeneyi imene inapezeka mwa kuyesayesa kwakhama. Ngati mwayang’anizana ndi chosankha, kodi mungafune kudziŵika monga wonama pamsonkho kuti musunge ndalama zina? Ayi. Ndithudi mungakonde kutaya ndalamazo m’malo mwa kuipitsa dzina lanu labwino ndi kukayikitsa makhalidwe anu ndipo ngakhale kulambira kwanu Yehova.
Kunena zoona, kusunga mbiri yabwino monga munthu woona mtima ndi wolungama kungakutayitseni ndalama zanu nthaŵi zina. Monga momwe Plato wafilosofi Wachigiriki wakale ananenera zaka mazana 24 zapitazo: “Pamene pali msonkho wa malipiro, munthu wolungama amasonkha zambiri ndipo wosalungama zochepa pa malipiro ofanana.” Iye angakhale atawonjezera kuti munthu wolungama samachita chisoni konse ndi kulipirira kukhala wolungama. Ngakhale kukhala ndi mbiri yabwino yotero kuli koyenerera malipirowo. Zimenezi zili choncho kwa Akristu. Mbiri yawo yabwino ili yamtengo wapatali kwa iwo chifukwa chakuti imalemekeza Atate wawo wakumwamba ndipo ingathandizire kukopera ena ku khalidwe lawo ndi kwa Mulungu wawo, Yehova.—Miyambo 11:30; 1 Petro 3:1.
Komabe koposa zonse, Akristu oona amalemekeza unansi wawo ndi Yehova. Mulungu amaona zonse zimene iwo amachita, ndipo amafuna kumkondweretsa. (Ahebri 4:13) Chotero, iwo amakaniza chiyeso cha kunamiza boma. Iwo amazindikira kuti Mulungu amakondwera ndi khalidwe la kuona mtima ndi lolungama. (Salmo 15:1-3) Ndipo popeza kuti amafuna kukondweretsa mtima wa Yehova, amapereka mangawa onse a misonkho omwe ali nawo.—Miyambo 27:11; Aroma 13:7.
[Mawu a M’munsi]
a Zimenezi zingakhale zovuta kwa Akristu amene amalemba pepala la msonkho limodzi ndi mnzawo wa muukwati wosakhulupirira. Mkazi Wachikristu adzayesayesa kwambiri kukhala wachikatikati pa kusunga lamulo la umutu ndi kumvera malamulo a msonkho a Kaisara. Komabe, ayenera kuzindikira zotulukapo za lamulo za kusaina pepala limene akudziŵa kuti nlonama.—Yerekezerani ndi Aroma 13:1; 1 Akorinto 11:3.
b Chokondweretsa nchakuti, Uthenga Wabwino wa Mateyu ndiwo wokha umene umasimba za chochitika chimenechi m’moyo wa Yesu padziko lapansi. Pokhala wokhometsa msonkho wakale, mosakayikira Mateyu anachita chidwi kwambiri ndi mzimu wa Yesu pankhani imeneyi.