Anachitidwa Chisomo ndi Yehova
“TIKUONENI, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe.” Ameneyo ndi moni wabwino chotani nanga! Amene akulankhulayo ndi mngelo Gabrieli. Akulankhula kwa mtsikana wodzichepetsa mtima—Mariya, mwana wamkazi wa mwamuna wotchedwa Heli. Chakacho ndi 3 B.C.E., ndipo malowo ndi mzinda wa Nazarete.—Luka 1:26-28.
Mariya ali wotomeredwa ndi Yosefe wopala matabwa. Malinga ndi lamulo ndi mwambo Wachiyuda, iye akuonedwa monga mkazi wake. (Mateyu 1:18) Monga mkaziyo, mwamunayo ngosatchuka. Nanga, nchifukwa ninji mngeloyo akupatsa moni mkaziyo monga wochitidwa chisomo?
Mwaŵi Wake Wosaneneka
Gabrieli akuwonjezera kuti: “Usawope, Mariya; pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu. Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo ku nthaŵi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.”—Luka 1:29-33.
Atakondwa ndiponso ndi kudabwa, Mariya akufunsa kuti: “Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziŵa mwamuna?” Gabrieli ayankha, nati: “Mzimu Woyera [u]dzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.” Kuti achotse zikayikiro zilizonse, mngeloyo akuwonjezera nati: “Ndipo taona, Elisabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna m[u] ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma. Chifukwa palibe mawu amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.”—Luka 1:34-37.
Nthaŵi yomweyo Mariya akulandira mwaŵi wosaneneka umenewu wa utumiki. Mwa ufulu, koma modzichepetsa, iye ayankha nati: “Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mawu anu.” Pamenepo, Gabrieli achoka. Mariya mwamsanga apita kumzinda wa kumapiri a Yuda. Atafika panyumba ya Zekariya wansembe ndi mkazi wake, Elisabeti, akupeza kuti mikhalidwe ili mongadi mwa mawu a mngelo. Mtima wa Mariya ukudzala ndi chimwemwe chachikulu chotani nanga! Pakamwa pake patuluka mawu otamanda Yehova.—Luka 1:38-55.
Akhala Mkazi wa Yosefe
Thupi laumunthu la Yesu linayenera kuchokera kwa namwali, pakuti kubadwa kotero kunanenedweratu. (Yesaya 7:14; Mateyu 1:22, 23) Koma kodi nchifukwa ninji pakufunikira namwali wotomeredwa? Kuti pakhale atate wolera amene angalangize mwanayo za choloŵa chalamulo cha mpando wachifumu wa Mfumu Davide. Onse aŵiri Yosefe ndi Mariya ali a fuko la Yuda ndipo ali mbadwa za Mfumu Davide. Motero choloŵa cha Yesu chidzatsimikiziridwa paŵiri. (Mateyu 1:2-16; Luka 3:23-33) Nchifukwa chake mngeloyo pambuyo pake akulimbikitsa Yosefe kuti sayenera kuwopa kutenga Mariya kukhala mkazi wake walamulo, ngakhale kuti ali ndi pakati.—Mateyu 1:19-25.a
Lamulo la kukhoma msonkho loperekedwa ndi Kaisara Augusto likakamiza Yosefe ndi Mariya kukalembetsa ku Betelehemu. Ali kumeneko, abala mwana wake woyamba wamwamuna. Abusa afika kudzaona khandalo, ndipo atamanda Atate wake, Yehova. Atatha masiku 40 a kuyeretsa malinga ndi Chilamulo cha Mose, Mariya apita kukachisi ku Yerusalemu kukapereka nsembe yotetezera machimo ake. (Levitiko 12:1-8; Luka 2:22-24) Inde, popeza kuti mkaziyo anabadwa ndi chilema, motero wosamasuka ku chitonzo cha uchimo, kupanda kwake ungwiro kwa choloŵa kuyenera kukwiriridwa mwa nsembe zotetezera.—Salmo 51:5.
Pamene Mariya ndi Yosefe ali pakachisi, Simeoni wokalambayo ndi Anna mneneri wamkazi wokalamba akhala ndi mwaŵi wa kuona Mwana wa Mulungu. Mariya sindiye akukhala nkhani yaikulu pano. (Luka 2:25-38) Pambuyo pake, anzeru akummaŵa agwadira Yesu osati mkaziyo.—Mateyu 2:1-12.
Atathaŵira ku Igupto ndi kukhala konko kufikira Herode woipayo atamwalira, makolo a Yesu abwerera nakakhala m’mudzi waung’ono wa Nazarete. (Mateyu 2:13-23; Luka 2:39) Yosefe ndi Mariya alerera Yesu komweko m’banja lopembedza.
Mariya Anali ndi Ana Ena
M’kupita kwa nthaŵi, Mariya ndi Yosefe abala abale ndi alongo akuthupi a Yesu. Pamene utumiki wa Yesu umfikitsa kwawo ku Nazarete, mabwenzi ake a kuubwana amzindikira. “Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo?” iwo akufunsa. “Kodi dzina lake la amake si Mariya? ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda? Ndipo alongo ake sali ndife onsewa?” (Mateyu 13:55, 56) Anazaretewo akunena za banja lakuthupi la Yosefe ndi Mariya, kuphatikizapo ana ake aamuna ndi aakazi amene akuwadziŵa monga abale ndi alongo akuthupi a Yesu.
Abale ndi alongo a Yesu ameneŵa sali asuwani ake. Ndipo sali ophunzira ake, kapena abale ndi alongo ake auzimu, pakuti Yohane 2:12 amasiyanitsa bwino lomwe magulu aŵiriwo mwa kunena kuti: “Anatsikira ku Kapernao, Iye [Yesu] ndi amake, ndi abale ake, ndi ophunzira ake.” Zaka zambiri pambuyo pake mu Yerusalemu, mtumwi Paulo anaonana ndi Kefa, kapena Petro, nawonjezera kuti: “Sindinaone aliyense wa atumwi enawo; ndinangoona Yakobo, mbale wa Ambuye.” (Agalatiya 1:19, The Jerusalem Bible) Ndiponso, mawu akuti Yosefe “sanamdziŵa [Mariya] kufikira atabala mwana wake” amasonyeza kuti atate a Yesu omlera anagonana ndi Mariya pambuyo pake nampatsa ana ena. (Mateyu 1:25) Nchifukwa chake, Luka 2:7 imatcha Yesu mwana wake wamwamuna “woyamba.”
Mayi Wowopa Mulungu
Monga mayi wowopa Mulungu, Mariya agwirizana ndi Yosefe pa kulangiza ana ake m’chilungamo. (Miyambo 22:6) Kukhala kwake wophunzira Malemba wakhama kukuonekera m’mawu ake odzala ndi zauzimu pamene apatsidwa moni ndi Elisabeti. Panthaŵiyo mayi wake wa Yesu abwereza mawu a m’nyimbo ya Hana nasonyeza chidziŵitso chake cha masalmo, maulosi ndi mbiri zolembedwa, ndi mabuku a Mose. (Genesis 30:13; 1 Samueli 2:1-10; Miyambo 31:28; Malaki 3:12; Luka 1:46-55) Mariya waloŵeza pamtima zochitika ndi mawu aulosi, kuzisunga mumtima mwake, ndi kuzisinkhasinkha. Chotero ali wokonzeka kutenga mbali pa kupereka malangizo aukholo kwa mnyamatayo Yesu.—Luka 2:19, 33.
Yesu wazaka 12 wophunzitsidwa bwino asonyeza chidziŵitso cha Malemba chimene chidabwitsa amuna ophunzira pakachisi. Popeza kuti walekana ndi makolo ake panyengo ya Paskha imeneyo, amayi ake akuti: “Mwanawe, wachitiranji ife chotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhaŵa.” Yesu ayankha nati: “Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna Ine? Simunadziŵa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale [m’nyumba ya, NW] Atate wanga?” Pokhala wosakhoza kumvetsetsa tanthauzo la yankho limeneli, Mariya alisunga mumtima mwake. Atabwerera ku Nazarete, Yesu apitiriza ‘kukula m’nzeru ndi mumsinkhu, ndi m’chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.’—Luka 2:42-52.
Mariya Monga Wophunzira wa Yesu
Nkoyenera chotani nanga kuti m’kupita kwa nthaŵi Mariya akhala wophunzira wodzipereka wa Yesu! Iye ngwofatsa ndipo alibe cholinga cha kudzionetsera mosasamala kanthu za ntchito yake yapadera yopatsidwa ndi Mulungu. Mariya amadziŵa Malemba. Ngati muwafufuza inu mwini, simudzapeza kuti akulongosoledwa kuti ali ndi nkhokwe ya kuunika, atakhala pampando wachifumu monga “mayi ndi mfumukazi” ndi wokhala m’kuŵala kwa ulemerero wa Kristu. M’malo mwake, mudzapeza kuti sakutchulidwa kwambiri.—Mateyu 13:53-56; Yohane 2:12.
Yesu analetsa Kulambira Mariya pakati pa otsatira ake. Pamene anali kulankhula panthaŵi ina, “mkazi wina mwa khamu la anthu anakweza mawu, nati kwa Iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi maŵere amene munayamwa. Koma Iye anati, . . . koma odala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.” (Luka 11:27, 28) Paphwando la ukwati, Yesu anauza Mariya kuti: “Mkazi, ndili ndi chiyani ndi inu? nthaŵi yanga siinafike.” (Yohane 2:4) Matembenuzidwe ena amati: “Siyani nkhaniyi m’manja mwanga.” (Weymouth) “Musayese kunditsogolera.” (An American Translation) Inde, Yesu analemekeza amayi ake, koma sanawalambire.
Mwaŵi wa Mathayo Amuyaya
Ha, Mariya anali ndi mathayo abwino chotani nanga! Anabala Yesu. Ndiyeno analera ndi kuphunzitsa mwanayo. Pomalizira, anasonyeza chikhulupiriro, akumakhala wophunzira wa Kristu ndi mlongo wake wauzimu. Pamene tiyang’ana Mariya m’Malemba kwa nthaŵi yotsiriza, timuona ali m’chipinda chapamwamba m’Yerusalemu. Ali mmenemo ndi atumwi a Yesu, ana ake ena, ndi akazi ena okhulupirika—onsewo olambira Yehova.—Machitidwe 1:13, 14.
M’kupita kwa nthaŵi, Mariya anamwalira ndipo thupi lake linabwerera kufumbi. Monga otsatira ena odzozedwa oyambirira a mwana wake wokondedwa, iye anagona mu imfa kufikira nthaŵi yoyenera ya Mulungu ya kumuukitsa monga cholengedwa chauzimu chokhala ndi moyo wosafa kumwamba. (1 Akorinto 15:44, 50; 2 Timoteo 4:8) Ha, “wochitidwa chisomo” ameneyu ayenera kukhala wokondwera chotani nanga tsopano kukhala pamaso pa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu!
[Mawu a M’munsi]
a Ngati Mariya sanali namwali, kodi ndani akanafuna kumkwatira? Ayuda anali kufuna kwambiri mtsikana amene anali namwali.—Deuteronomo 22:13-19; yerekezerani ndi Genesis 38:24-26.
[Chithunzi patsamba 31]
Mariya anachitidwa chisomo kukhala mayi wa Yesu