Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 12/15 tsamba 13-18
  • Ogwirizana M’chomangira Champhumphu cha Chikondi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ogwirizana M’chomangira Champhumphu cha Chikondi
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Umodzi Umayenderana ndi Chidziŵitso
  • Kucheutsidwa Kungawononge Umodzi
  • Tiyenera Kukhala Maso ndi Mawu Okopakopa
  • Yehova Akhoza Kukulimbikitsani
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Fufuzani Chuma Chimene ‘Chinabisidwa Mosamala mwa Iye’
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Thandizani Ena Kuyenda Moyenera Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Anthu Afunikira Chidziŵitso Chonena za Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 12/15 tsamba 13-18

Ogwirizana M’chomangira Champhumphu cha Chikondi

‘Khalani ogwirizana pamodzi m’chikondi.’​—AKOLOSE 2:2, NW.

1, 2. Kodi nchisonkhezero chogaŵanitsa chotani chimene chilipo makamaka lerolino?

TAMVERANI! Mawu aakulu akumveka kumwamba konse akumati: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa [M]dyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:12) Pamene chaka chilichonse chikupita, uthenga umenewo umakhala wowopsa kwambiri kwa okhala padziko lapansi.

2 Mdani wamkulu wa Yehova wadziŵika nthaŵi yaitali monga wotsutsa (Satana) ndi woneneza (Mdyerekezi). Koma tsopano wonyenga ameneyu watenga njira ina yoipitsitsa​—wakhala mulungu wokwiya! Chifukwa? Chifukwa chakuti anathamangitsidwa kumwamba ndi Mikayeli ndi angelo ake m’nkhondo imene inayamba kumwamba mu 1914. (Chivumbulutso 12:7-9) Mdyerekezi akudziŵa kuti wangotsala ndi kanthaŵi kuti atsimikizire chinenezo chake chakuti akhoza kuchotsa anthu onse pa kulambira Mulungu. (Yobu 1:11; 2:4, 5) Pokhala opanda malo othaŵirako, iye ndi ziŵanda zake ali ngati nthenje ya njuchi zokwiya zimene zimatsanulira mkwiyo wawo pa makamu osakhazikika a anthu.​—Yesaya 57:20.

3. Kodi kutsitsidwa kwa Satana kwakhala ndi chiyambukiro chotani m’nthaŵi yathu?

3 Zochitika zimenezi, zosaoneka ndi maso aumunthu, zimasonyeza chifukwa chake tsopano pali kunyonyotsoka kwa makhalidwe abwino pakati pa mtundu wa anthu. Zimasonyezanso chifukwa chake anthu akuyesayesa mothedwa nzeru kugwirizanitsa mitundu yomagaŵanikana imene singagwirizane konse. Mafuko amaukirana mwankhalwe, akumachititsa anthu mamiliyoni ambiri kukhala opanda nyumba ndi othaŵa kwawo. Nchifukwa chake kusayeruzika kukuwonjezereka pamlingo umene sunachitikepo ndi kale lonse! Monga momwe Yesu analoserera, ‘chikondano cha anthu aunyinji chikuzirala.’ Kulikonse kumene mungayang’ane, kusagwirizana ndi kupanda chikondi kukusonyeza mkhalidwe wosakhazikika wa anthu lerolino.​—Mateyu 24:12.

4. Kodi nchifukwa ninji anthu a Mulungu ali pangozi kwambiri?

4 Polingalira za mkhalidwe wa dziko, pemphero la Yesu m’malo mwa otsatira ake likukhala ndi tanthauzo lalikulu: “Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:15, 16) Lerolino, “woipayo” amatsanulira mkwiyo wake makamaka pa amene “asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.” (Chivumbulutso 12:17) Pakadapanda chiyang’aniro ndi chisamaliro chachikondi cha Yehova, Mboni zake zokhulupirika zikanafafanizidwa. Miyoyo yathu imadalira pa kugwiritsira ntchito bwino zogaŵira zonse zimene Mulungu amapereka kaamba ka chitetezo ndi ubwino wathu wauzimu. Zimenezo zimafuna kuyesetsa kwathu monga mwa machitidwe a mphamvu Yake mwa Kristu, monga momwe mtumwiyo analimbikitsira pa Akolose 1:29.

5, 6. Kodi Paulo anamva motani ponena za Akristu a ku Kolose, ndipo kodi nchifukwa ninji lemba la chaka cha 1995 lili loyenera?

5 Ngakhale kuti mwina Paulo anali asanawaonepo maso ndi maso abale ake m’Kolose, iye anawakonda. Anawauza kuti: “Ndikanakonda kuti mudziŵe kukula kwa nkhaŵa yanga pa inu.” (Akolose 2:1, The New Testament in Modern English, ya J. B. Phillips) Popeza kuti otsatira a Yesu sali a dziko, “woipayo” akayesayesabe kuswa umodzi wa abalewo mwa kufesa mwa iwo mzimu wa dziko. Mbiri imene Epafra anabweretsa kuchokera ku Kolose inasonyeza kuti zimenezi zinakhala zikuchitika kumlingo wakutiwakuti.

6 Ina ya nkhaŵa yaikulu ya Paulo kaamba ka abale ake Achikristu ingafotokozedwe mwachidule ndi mawu akuti: ‘Khalani ogwirizana pamodzi m’chikondi.’ Mawu ake ali ndi tanthauzo lapadera lerolino, m’dziko lodzala ndi kusagwirizana ndi kupanda chikondi. Ngati tilabadira uphungu wa Paulo, Yehova adzatisamalira. Tidzakhalanso ndi mphamvu ya mzimu wake m’moyo wathu, ikumatithandiza kukaniza zitsenderezo za dziko. Uphungu umenewu ngwanzeru chotani nanga! Ndicho chifukwa chake Akolose 2:2 adzakhala lemba lathu lalikulu la 1995.

7. Kodi ndi umodzi wotani umene uyenera kupezeka pakati pa Akristu?

7 M’kalata yoyamba kwa Akorinto, mtumwiyo anagwiritsira ntchito thupi la munthu monga fanizo. Iye analemba kuti “kusakhale chisiyano” mumpingo wa Akristu odzozedwa koma kuti “ziŵalo zifanane ndi kusamalana china ndi chinzake.” (1 Akorinto 12:12, 24, 25) Ha, limenelo ndi fanizo labwino chotani nanga! Ziŵalo zathu zimadalirana, ndipo chilichonse ncholumikizana ndi thupi lathu. Zimenezi zilinso choncho m’gulu lathu la abale la padziko lonse, lopangidwa ndi odzozedwa ndi mamiliyoni oyembekezera kukhala padziko lapansi laparadaiso. Sitiyenera kudzilekanitsa ndi thupi la Akristu anzathu ndi kukhala patokha! Mzimu wa Mulungu wochuluka, wogwira ntchito kupyolera mwa Kristu Yesu, umadza kwa ife kudzera m’kuyanjana kwathu ndi abale athu.

Umodzi Umayenderana ndi Chidziŵitso

8, 9. (a) Kodi chofunika nchiyani pa kuchirikiza kwathu umodzi mumpingo? (b) Kodi mwapeza motani chidziŵitso cha Kristu?

8 Ina ya mfundo zazikulu za Paulo inali yakuti umodzi Wachikristu umayenderana ndi chidziŵitso, makamaka cha Kristu. Paulo analemba kuti Akristu ayenera “[kukhala ogwirizana pamodzi m’chikondi], kufikira chuma chonse cha chidzalo cha chidziŵitso, kuti akazindikire iwo chinsinsi [chopatulika, NW] cha Mulungu, ndiye Kristu.” (Akolose 2:2) Ifeyo tapeza chidziŵitso​—choonadi​—kuyambira pamene tinayamba kuphunzira Mawu a Mulungu. Monga mbali ya kupeza chidziŵitso cha mmene chochuluka cha choonadi chimenechi chimaloŵera m’chifuno cha Mulungu, timaona ntchito yofunika kwambiri ya Yesu. “Zolemera zonse za nzeru ndi chidziŵitso zibisika mwa Iye.”​—Akolose 2:3.

9 Kodi ndimmene mumaonera Yesu ndi ntchito yake m’chifuno cha Mulungu? Anthu ambiri m’Dziko Lachikristu amafulumira kutchula Yesu, akumanena kuti anamlandira ndi kuti ali opulumutsidwa. Koma kodi amamdziŵadi? Kutalitali, pakuti ochuluka amakhulupirira chiphunzitso cha Utatu chosakhala cha m’malemba. Si choonadi chokha pa nkhaniyi chimene mukudziŵa komanso mwachionekere muli ndi chidziŵitso chochuluka cha zimene Yesu ananena ndi kuchita. Anthu mamiliyoni ambiri athandizidwa pa zimenezi ndi phunziro lopatsa chidziŵitso akumagwiritsira ntchito buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Komabe, tifunikirabe kuzamitsa chidziŵitso chathu cha Yesu ndi njira zake.

10. Kodi tingapeze motani chidziŵitso chobisika?

10 Mawu akuti “zolemera zonse za nzeru ndi chidziŵitso zibisika” mwa Yesu samatanthauza kuti ife sitingapeze chidziŵitso chimenecho. M’malo mwake, chili chofanana kwambiri ndi mgodi wokhala pambalambanda. Sitifunikira kuyenda cha uku ndi cha uku kufunafuna poyambira kukumba. Tikudziŵa kuti chidziŵitso chenicheni chimayamba ndi zimene Baibulo limavumbula ponena za Yesu Kristu. Pamene tizindikira kwambiri ntchito ya Yesu m’kukwaniritsa chifuno cha Yehova, timapeza chuma cha nzeru yeniyeni ndi chidziŵitso cholongosoka. Chotero chimene tifunikira kuchita ndicho kupitiriza kukumba mwakuya, tikumatulutsa ngale zambiri kapena zinthu zamtengo wapatali zopezeka m’magwero ameneŵa amene takumba kale.​—Miyambo 2:1-5.

11. Kodi tingawonjezere motani chidziŵitso ndi nzeru zathu mwa kusinkhasinkha za Yesu? (Gwiritsirani ntchito kusambitsa kwa Yesu mapazi a ophunzira ake monga fanizo, kapena gwiritsirani ntchito zitsanzo zina.)

11 Mwachitsanzo, tingakhale tikudziŵa kuti Yesu anasambitsa mapazi a atumwi ake. (Yohane 13:1-20) Komabe, kodi tinayamba taganizapo za phunziro limene anali kuphunzitsa ndi mkhalidwe wa maganizo umene anasonyeza? Mwakutero, tingakumbe chuma cha nzeru chimene chimatitheketsa​—inde, kutisonkhezera​—kusintha mmene timachitira ndi mbale kapena mlongo amene umunthu wake wakhala ukutikwiyitsa kwa nthaŵi yaitali. Kapena pamene tipatsidwa gawo limene sitimakonda kwambiri, tingalione mosiyana titapeza lingaliro lonse la Yohane 13:14, 15. Umo ndimmene chidziŵitso ndi nzeruyo zimatiyambukirira. Kodi ena angayambukiridwe motani pamene titsanzira kwambiri chitsanzo cha Kristu mogwirizana ndi chidziŵitso chowonjezerekacho? Mwachionekere gulu la nkhosa ‘lidzakhala logwirizana pamodzi kwambiri m’chikondi.’a

Kucheutsidwa Kungawononge Umodzi

12. Kodi tifunikira kuchenjera ndi chidziŵitso chiti?

12 Ngati chidziŵitso cholongosoka chimalimbitsa ‘kukhala kwathu ogwirizana pamodzi m’chikondi,’ nanga “chotchedwa chizindikiritso konama” chimadzetsa chiyani? Zosiyana kwenikweni ndi zimenezo​—mkangano, zotetana, ndi kutaya chikhulupiriro. Chotero tifunikira kuchenjera ndi chizindikiritso chonama chotero, monga momwe Paulo anachenjezera Timoteo. (1 Timoteo 6:20, 21) Paulo analembanso kuti: “Ichi ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mawu okopakopa. Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.”​—Akolose 2:4, 8.

13, 14. (a) Kodi nchifukwa ninji abale a ku Kolose anali pangozi ponena za chidziŵitso? (b) Kodi nchifukwa ninji ena lerolino angalingalire kuti sali pangozi yofananayo?

13 Akristu a ku Kolose anazingidwa ndi chisonkhezero chonyenga cha zimene zinalidi chotchedwa chizindikiritso konama. Anthu ambiri a m’Kolose ndi apafupi naye analemekeza kwambiri nzeru za Agiriki. Panalinso Ayuda Osunga Mwambo amene anafuna kuti Akristu azisunga Chilamulo cha Mose, pa zinthu zonga masiku ake a mapwando ndi m’zakudya. (Akolose 2:11, 16, 17) Paulo sanali kuletsa abale ake kupeza chidziŵitso choona, koma kuti iwo anafunikira kusamala kuti pasakhale wina wowalanda ngati chuma, akumagwiritsira ntchito zigomeko zokopa kuwakhutiritsa kuti akhale ndi kapenyedwe kaumunthu ka moyo ndi ntchito. Mukhoza kumvetsetsa kuti ngati ena mumpingo alola kalingaliridwe kawo ndi zosankha zawo kutsogozedwa ndi malingaliro ndi kapenyedwe kotero ka moyo kosakhala ka malemba, umodzi ndi chikondi pakati pa ziŵalo za mpingo zidzawonongeka.

14 ‘Inde,’ mungaganize motero, ‘ndaona ngozi imene Akolose anayang’anizana nayo, koma sindikhoza kuyambukiridwa ndi malingaliro Achigiriki, onga a moyo wosafa kapena mulungu wa utatu; ndipo sindikuona kuti pali ngozi iliyonse yakuti ndingakopedwe ndi maholide achikunja a chipembedzo chonyenga chimene ndinachokamo.’ Zimenezo nzabwino. Kuli bwino kukhala wotsimikiza mtima ponena za kupambana kwa choonadi choyambirira chovumbulidwa mwa Yesu chimenenso chikupezeka m’Malemba. Komabe, kodi zingachitike kuti tingayambukiridwe ndi nzeru zina za anthu kapena malingaliro awo ofala lerolino?

15, 16. Kodi ndi kapenyedwe kotani ka moyo kamene kangayambukire kalingaliridwe ka Mkristu?

15 Mkhalidwe wina wa maganizo wotero wakhalako nthaŵi yaitali wakuti: “Kodi tsopano lili kuti lonjezo la kudza kwake? Makolo athu amwalira, komabe zinthu zonse zikupitiriza monga momwedi zakhalira nthaŵi zonse.” (2 Petro 3:4, The New English Bible) Lingaliro limenelo lingatchulidwe mwa mawu ena, koma kapenyedwe kake nkamodzimodzi. Mwachitsanzo, wina angalingalire kuti, ‘Pamene ndinangodziŵa choonadi zaka makumi angapo zapitazo, mapeto anali “pafupi kwambiri.” Koma sanafikebe, ndipo adziŵa ndani pamene adzadza?’ Zoona, palibe munthu amene adziŵa pamene mapeto adzafika. Komabe, taonani lingaliro limene Yesu analimbikitsa kuti: “Yang’anirani, dikirani, . . . pakuti simudziŵa nthaŵi yake.”​—Marko 13:32, 33.

16 Ha, kungakhale kowopsa chotani nanga kukhala ndi lingaliro lakuti, popeza sitidziŵa pamene mapeto adzadza, tiyenera kulinganiza kukhala ndi moyo wodzala ndi “wabwino”! Kapenyedwe kameneko kangasonyezedwe ndi lingaliro lakuti, ‘Palibe cholakwika chilichonse ngati ndingatsatire njira imene idzandilola (kapena idzalola ana anga) kupeza ntchito yapamwamba yamalipiro abwino imene idzanditheketsa kukhala ndi moyo wapamwamba. Ndidzafikabe pamisonkhano Yachikristu ndi kukhalako ndi phande m’ntchito yolalikira, koma palibe chifukwa chakuti ndidziyesetsa kapena kudzimana kwambiri.’​—Mateyu 24:38-42.

17, 18. Kodi Yesu ndi atumwi ake anatilimbikitsa kukhala ndi kapenyedwe kotani?

17 Komabe, sitingakane kuti Yesu ndi atumwi ake ananena kuti tiyenera kuchita mofulumira kuti mbiri yabwino ilalikidwe, tikumayesetsa ndi kukhala ofunitsitsa kudzimana. Paulo analemba kuti: “Ichi nditi, abale, yafupika nthaŵi, kuti tsopano iwo akukhala nawo akazi akhalebe monga ngati alibe; . . . ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu; ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.”​—1 Akorinto 7:29-31; Luka 13:23, 24; Afilipi 3:13-15; Akolose 1:29; 1 Timoteo 4:10; 2 Timoteo 2:4; Chivumbulutso 22:20.

18 M’malo mopereka lingaliro lakuti tipange moyo wapamwamba kukhala chonulirapo chathu, Paulo mouziridwa analemba kuti: “Sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire. . . . Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.”​—1 Timoteo 6:7-12.

19. Kodi mpingo umayambukiridwa motani pamene ziŵalo zake zilandira kapenyedwe ka moyo kamene Yesu analimbikitsa?

19 Pamene mpingo uli wopangidwa ndi Akristu achangu amene amayesetsa ‘kuvomereza chivomerezo chabwino,’ umodzi umangodza wokha. Iwo samalola mkhalidwe wa maganizo wakuti, ‘Uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.’ (Luka 12:19) M’malo mwake, ali ogwirizana pa kuyesayesa kumodzimodzi, akumakhala ofunitsitsa kudzimana kuti akhale ndi phande lalikulu lotheka m’ntchitoyi imene sidzachitidwanso konse.​—Yerekezerani ndi Afilipi 1:27, 28.

Tiyenera Kukhala Maso ndi Mawu Okopakopa

20. Kodi ndi mbali ina iti imene Akristu angasokeretsedwe nayo?

20 Ndithudi, pali njira zina zimene Akristu ‘angasokeretsedwere ndi mawu okopakopa’ kapena chinyengo chopanda pake chimene chimadodometsa ‘kukhala kwawo ogwirizana pamodzi m’chikondi.’ Ofesi ya Watch Tower Society ku Germany inalemba kuti: “Chochitika china chinabutsa mkangano, ofalitsa ndipo ngakhale akulu akumakhala kumbali ina ya mkangano wonena za mitundu ya kuchiritsa kochitidwa ndi mbale wina.” Iwo anawonjezera kuti: “Chifukwa cha njira zochuluka zogwiritsiridwa ntchito limodzinso ndi kuchuluka kwa odwala, imeneyi ili nkhani yodzetsa mkangano ndipo, ngati kuchiritsako kuphatikizapo zamizimu, kungakhale kwangozi.”​—Aefeso 6:12.

21. Kodi Mkristu angataye motani kapenyedwe kabwino lerolino?

21 Akristu amafuna kukhalabe amoyo ndi athanzi kuti akhoze kulambira Mulungu. Komabe, m’dongosolo ili timakalamba ndi kudwala chifukwa cha kupanda ungwiro. M’malo mogogomezera zaumoyo, tifunikira kusumika maganizo pa mankhwala enieni, athu ndi a ena. (1 Timoteo 4:16) Kristu ndiye maziko a mankhwala amenewo, monga momwenso analili maziko a uphungu wa Paulo kwa Akolose. Koma kumbukirani, Paulo anasonyeza kuti ena angadze ndi “mawu okopakopa” akumachotsa maganizo athu pa Kristu, ndipo mwinamwake kuwasumika pa njira zopimira matenda, machiritso, kapena zakudya.​—Akolose 2:2-4.

22. Kodi ndi mkhalidwe wa maganizo wachikatikati wotani umene tiyenera kukhala nawo ponena za zimene ambiri anena pa njira zopimira matenda ndi kuchiritsa?

22 Anthu kuzungulira dziko lonse amamva zilengezo zambiri ndi mawu ochuluka ochitira umboni machiritso osiyanasiyana ndi njira zopimira matenda. Ena a machiritsowo kapena njira zimenezo zimagwiritsiridwa ntchito ndipo anthu ambiri amazivomereza; zina anthu ambiri amazisuliza kapena kuzikayikira.b Munthu aliyense ali ndi thayo la kuona zimene adzachita ndi thanzi lake. Koma amene amalandira uphungu wa Paulo wopezeka pa Akolose 2:4, 8 sadzasokeretsedwa ndi “mawu okopakopa” kapena “chinyengo chopanda pake” chimene chimasokeretsa ambiri amene, posoŵa chiyembekezo cha Ufumu, akufunitsitsa mpumulo. Ngakhale ngati Mkristu ali wotsimikizira kuti kuchiritsa kwinakwake nkwabwino kwa iye, sayenera kukuchirikiza mu ubale Wachikristu, chifukwa chakuti kukhoza kukhala nkhani yaikulu ndipo yodzetsa mkangano. Mwakutero angasonyeze kuti amalemekeza kwambiri kufunika kwa umodzi mumpingo.

23. Kodi nchifukwa ninji ifeyo makamaka tili ndi chifukwa chokhalira achimwemwe?

23 Paulo anagogomezera kuti umodzi Wachikristu ndiwo maziko a chimwemwe chenicheni. M’tsiku lake chiŵerengero cha mipingo chinalidi chochepa kuposa lerolino. Komabe anakhoza kulembera Akolose kuti: “Pakuti ndingakhale ndili kwina m’thupi, komatu mumzimu ndili pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu cha kwa Kristu.” (Akolose 2:5; onaninso Akolose 3:14.) Tili ndi chifukwa chachikulu chotani nanga chokhalira achimwemwe! Tikuona umboni weniweni wa mgwirizano, makonzedwe abwino, ndi chilimbiko cha chikhulupiriro mumpingo wathu, umene umasonyeza mkhalidwe wofala wa anthu a Mulungu padziko lonse lapansi. Chotero m’nthaŵi yaifupi yotsala ya dongosolo lilipoli, aliyense wa ife atsimikizetu mtima ‘kukhala ogwirizana pamodzi m’chikondi.’

[Mawu a M’munsi]

a Pamene kuli kwakuti pali zambiri zimene tingaphunzire, onani zimene inu panokha mungaphunzire ponena za Yesu m’zitsanzo zotsatira zimene zingathandizire umodzi mumpingo wanu: Mateyu 12:1-8; Luka 2:51, 52; 9:51-55; 10:20; Ahebri 10:5-9.

b Onani Nsanja ya Olonda ya December 15, 1982, masamba 22-31.

Kodi Mwazindikira?

◻ Kodi lemba la chaka cha 1995 la Mboni za Yehova ndi liti?

◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu a ku Kolose anafunikira kugwirizana pamodzi m’chikondi, ndipo nchifukwa ninji tifunikira kutero lerolino?

◻ Kodi ndi kapenyedwe konyenga kotani ka moyo kamene Akristu afunikira makamaka kuchenjera nako lerolino?

◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kusamala kuti asasokeretsedwe ndi mawu okopakopa onena za thanzi ndi njira zopimira matenda?

[Zithunzi patsamba 17]

Kodi makonzedwe anu a mtsogolo amazikidwa pa kukhalapo kwa Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena