Mboni za Yehova Padziko Lonse—Puerto Rico
PAKATI pa Caribbean Sea ndi Atlantic Ocean pali chisumbu chobiriŵira, chotentha cha Puerto Rico. Christopher Columbus ananena kuti chinali cha Spain mu 1493 ndipo anachitcha San Juan Bautista pokumbukira Yohane Mbatizi. Mzinda wake waukulu unatchedwa Puerto Rico kwanthaŵi yaitali, kapena “Doko Lolemera.” M’kupita kwa nthaŵi, dzinali linagwiritsiridwa ntchito kutchula chisumbu chonsecho, pamene kuli kwakuti mzindawo unadzatchedwa San Juan.
Puerto Rico wakhaladi doko lolemera m’njira zambiri. Golidi wambiri anatumizidwa panyanja kumka kwina kuchokera kunoko m’zaka zoyambirira za ulamuliro wa Aspanya. Tsopano chisumbucho chimatumiza kunja nzimbe, khofi, nthochi, ndi zipatso, ngakhale kuti maindasitale ake opanga zinthu ndi a ntchito zina ndiwo amene amadzetsa chuma chake chambiri lerolino. Komabe, Puerto Rico wakhaladi doko lolemera m’lingaliro linanso lofunika koposa.
Mbiri yabwino yonena za Ufumu wa Mulungu inayamba kulalikidwa kunoko m’ma 1930. Lerolino, mu Puerto Rico muli ofalitsa mbiri yabwino oposa 25,000. Mu 1993 antchito a panthambiyi ya Watch Tower Society anawonjezereka kuchokera pa 23 kufikira pa oposa 100. Chiwonjezeko chimenechi chinali chofunika kotero kuti nthambiyo iyang’anire kutembenuzidwa kwa mabuku ofotokoza Baibulo m’Chispanya, ikumachititsa zofalitsidwazo kukhala zopezeka kwa anthu pafupifupi 350,000,000 olankhula Chispanya padziko lonse.
Munda Watsopano
Ofesi yanthambi ikusimbanso kuti: “Munda watsopano watseguka mu Puerto Rico chifukwa chakuti takhala tikupanga zoyesayesa kutengera uthenga wa Ufumu kwa anthu ogontha. Mlongo wina akusimba za chokumana nacho chotsatirachi: ‘Ndinali kugwira ntchito pakati pa anthu ogontha ndipo ndinafikira mkazi wina wokhala ndi ana aŵiri aang’ono. Pamene anazindikira kuti ndinali Mboni, anakana kulankhula nane nthaŵi yomweyo chifukwa chakuti mwamuna wake, amenenso anali wogontha, sanakonde Mboni za Yehova.
“‘Miyezi ingapo pambuyo pake mkazi mmodzimodziyu anachezera bwenzi lake lina limene linali kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Iye anagwirizana nawo m’phunzirolo ndipo anasangalala nalo kwambiri. Ndinapita kwa mkaziyo kachiŵirinso, ndipo iye anabwereza kunena kuti mwamuna wake samakonda Mboni. Komabe, iye anafuna kumvetsetsa Baibulo ndipo anali atatopa ndi tchalitchi chake chifukwa chakuti sankaphunzira chilichonse. Tinayamba kuphunzira, tikumagwiritsira ntchito trakiti. Tsiku lina iye anandiuza kuti ndibwerenso pa Loŵeruka chifukwa chakuti mwamuna wake adzakhalapo. “Komatu paja samatikonda, kodi sichoncho?” ndinafunsa motero. Iye anayankha kuti: “Akufuna kudziŵa za nkhani yake yonse.”
“‘Aŵiri onsewo anali kugogoda pa khomo panga tsiku lotsatira! Popeza kuti mwamunayo anali ndi mafunso ambiri, ndinawaitanira ku misonkhano yathu ya anthu ogontha. Iye anafika kumeneko ine ndisanafike ndipo kuyambira pamenepo sanaphonyepo msonkhano. Akulalikira kwa anthu ena ogontha, wafika pamsonkhano wadera, ndipo akuyembekezera ubatizo.’”
Lipoti la nthambiyo likupitirizabe kuti: “Pamsonkhano wathu wachigawo chaka chino, programu yonseyo inaperekedwa m’chinenero chamanja, anthu ambirimbiri ogontha analipo ndi mabanja awo. Nthaŵi yotenga mtima inafika mkati mwa nkhani yotsiriza pamene wolankhula wake anatchula za ntchito imene ikuchitidwa pakati pa anthu ogontha ndi kuti pafupifupi 70 analipo. Panali chikondwerero chachikulu, koma, monga momwe wolankhulayo anaonera, anthu ogonthawo sanachione. Chotero akumapempha anthu ogonthawo kuyang’ana omvetsera onse, wolankhulayo anabwerezanso funso lake kuti, ‘Kodi muli achimwemwe kukhala ndi abale anu ogontha pano?’ ndipo anapempha omvetserawo kusonyeza chikondwerero mwa kugwedeza m’mwamba mikono yonse. Kunali kokondweretsa kwambiri kuona abale ndi alongo 11,000 akumakondwera mwa kugwedeza manja awo. Abale ndi alongo athu ogonthawo anali okondwa kwambiri ndipo anadziona kukhala ali mbali ya ubale waukulu. Ambiri anakhetsa misozi yachisangalalo.”
Pamene Mboni za Yehova zikukhala ndi phande m’ntchito ya kututa ku Puerto Rico, mosakayikira dzikolo lidzapitirizabe kukhala doko lolemera. “Nkhosa” za Mulungu zimene iye amatcha kuti “zofunika za amitundu onse,” zidzapitirizabe kufika kotero kuti nyumba ya Yehova idzazidwe ndi ulemerero.—Yohane 10:16; Hagai 2:7.
[Bokosi patsamba 9]
ZIŴERENGERO ZA DZIKOLO
Chaka Chautumiki cha 1994
CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 25,428
KUGAŴA: Mboni 1 pa anthu 139
OFIKA PA CHIKUMBUTSO: 60,252
AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 2,329
AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 19,012
CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 919
CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 312
OFESI YA NTHAMBI: GUAYNABO