Kodi Mwalimbikitsapo Aliyense Posachedwapa?
ELENA anali chabe ndi zaka 17 pamene madokotala anapeza kuti anali ndi kansa m’chimake cha dzira. Amayi ake, a Mari, anavutika mtima poona kuzunzika kwa Elena.
Potsirizira pake, Elena anasamutsidwira ku chipatala china ku Madrid, Spain, pamtunda wa makilomita 1,900 kuchokera kwawo ku Canary Islands. Ku Madrid, gulu la madokotala linafuna kwambiri kuchita opaleshoni popanda mwazi. (Machitidwe 15:28, 29) Koma opaleshoni itangoyamba, kunakhala kodziŵikiratu kuti nthenda ya Elena inali ya ku imfa. Kansayo inali itafalikira kale m’thupi lake lonse, ndipo palibe chimene madokotala a opaleshoni akanachita. Elena anamwalira patapita masiku asanu ndi atatu kuchokera pamene anafika ku Madrid.
Mari sanali yekha poyang’anizana ndi tsoka lalikulu limenelo. Mwa kudzilipirira iwo eni, akulu aŵiri Achikristu anapita naye ku Madrid limodzi ndi mwana wake wamwamuna wamkulu nakakhala kumeneko kufikira imfa ya Elena. “Iwo anandithandiza kupirira kutaya mtima kosautsako kumene ndinali nako,” Mari akutero. “Sindidzaiŵala chilimbikitso chimene anandipatsa. Chichirikizo chawo chauzimu ndi chithandizo chawo chogwira ntchito zinali zamtengo wake. Iwo analidi ‘pobisalira mphepo.’”—Yesaya 32:1, 2.
Yehova amakondwera kuti abusa achikondi onga ameneŵa amasamalira nkhosa zake mwachifundo kwambiri. (Miyambo 19:17; 1 Petro 5:2-4) Komabe, kulimbikitsa ena sikuli thayo la akulu okha. Akristu onse amasonkhana pamodzi kuti alandire malangizo ndi ‘kudandaulirana wina ndi mnzake.’ (Ahebri 10:24, 25) Kulimbikitsa ena kuli kwachibadwa m’gulu Lachikristu.
Kodi Kulimbikitsa Ena Kumaphatikizapo Chiyani?
Mofanana ndi mmene duŵa limafotera litasoŵa madzi, anthu—m’banja ndi mumpingo momwe—angalefuke chifukwa cha kusoŵa chilimbikitso. Komabe, chilimbikitso chapanthaŵi yake chingalimbitse amene akuyesedwa, kutsitsimula opsinjika maganizo, ndi kupatsa mphamvu amene akutumikira Mulungu mokhulupirika.
Liwu Lachigiriki limene latembenuzidwa kuti “chilimbikitso” limaphatikizapo lingaliro la kukhazika mtima, kulangiza, ndi kutonthoza. Chotero, chilimbikitso sichili chabe kuuza wina kuti akuchita bwino. Chingaphatikizeponso kupereka chithandizo chakuthupi ndi chauzimu.
Kwenikweni, tanthauzo lenileni la liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kuti “chilimbikitso” ndilo “kuitana wina kuti mukhale naye.” Kuyendera limodzi ndi abale ndi alongo athu auzimu kumatikhozetsa kupereka chichirikizo mwamsanga ngati wina wa iwo walema kapena wakhumudwa. (Mlaliki 4:9, 10) Nkokondweretsa kuti anthu a Yehova ‘akumtumikira pheŵa ndi pheŵa.’ (Zefaniya 3:9, NW) Ndipo mtumwi Paulo anatcha Mkristu wina “mnzanga wa m’goli woona.” (Afilipi 4:3) Kugwirira ntchito pamodzi m’goli limodzi mwa kutumikira pheŵa ndi pheŵa kumapeputsa katundu, makamaka wa awo amene sali olimba mwauzimu.—Yerekezerani ndi Mateyu 11:29.
Analimbikitsa Ena
Popeza kuti chilimbikitso nchofunika kwambiri, tiyeni tipende zitsanzo zina za m’Malemba. Pamene mneneri wa Mulungu Mose anali kuyandikira mapeto a moyo wake, Yehova anasankha Yoswa kukhala mtsogoleri wa Aisrayeli. Imeneyi sinali ntchito yofeŵa, monga momwe Mose mwiniyo anadziŵira. (Numeri 11:14, 15) Chifukwa chake, Yehova anauza Mose ‘kulangiza Yoswa ndi kumlimbitsa mtima.’—Deuteronomo 3:28.
Panthaŵi ya oweruza a m’Israyeli, mwana wamkazi wa Yefita analabadira mofunitsitsa choŵinda cha atate wake mwa kulepa mwaŵi wa kukhala ndi banja kuti akatumikire pachihema cha Yehova. Kodi kudzipereka kwake nsembe kunanyalanyazidwa? Iyayi, pakuti Oweruza 11:40 amati: “Ana aakazi a Israyeli akamuka chaka ndi chaka kumliririra mwana wa Yefita wa ku Gileadi, masiku anayi pa chaka.” Maulendo amenewo ayenera kukhala atamlimbikitsa kwambiri mwana wamkazi wodzimanayo wa Yefita.
Nthaŵi zina kulimbikitsa wina kumafuna kulimba mtima. Paulendo wake woyamba waumishonale, mtumwi Paulo anakumana ndi chitsutso chowopsa m’mizinda ingapo ya m’Asia Minor. Anapitikitsidwa mu Antiokeya, anangotsala pang’ono kuphedwa mu Ikoniyo, ndipo anaponyedwa miyala nasiyidwa ali wokomoka ku Lustra. Komabe, patapita nthaŵi pang’ono pambuyo pa zimenezo, Paulo ndi mabwenzi ake anabwerera ku mizinda imeneyo, “nalimbikitsa mitima ya akuphunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m’chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kuloŵa m’ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.” (Machitidwe 14:21, 22) Paulo anali wokonzekera kutaya moyo wake kuti alimbikitse ophunzira atsopano ameneŵa.
Komabe, ophunzira atsopano sindiwo Akristu okha amene afunikira chilimbikitso. Zaka zambiri pambuyo pake, Paulo anakhala ndi ulendo wovuta wopita ku Roma, kumene anali kukaweruzidwa. Pamene anali kufika kumene anali kupita, angakhale anali atataya mtima. Koma pamene anafika pamtunda wa makilomita 74 kummwera koma chakummaŵa kwa Roma, analimbika mtima. Chifukwa? Chifukwa chakuti abale a ku Roma anadza kukumana naye ku Bwalo la Apiyo ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu. “Ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.” (Machitidwe 28:15) Pa zochitika zofanana ndi chimenechi, kungokhalapo kwathu kungakhale kolimbikitsa kwambiri kwa okhulupirira anzathu.
Gwiritsirani Ntchito Mipata Yolimbikitsira Ena
Palidi mipata yambiri yolimbikitsira ena. Kodi mtima wanu wakhudzidwa ndi nkhani yabwino ya wophunzira yokambidwa ndi mbale kapena mlongo m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki? Kodi muli wokondwa kuti mumpingo muli achinyamata olimba mwauzimu? Kodi mwachita chidwi ndi chipiriro cha okalamba? Kodi mwakondwera ndi njira imene wina wa apainiya wagwiritsirira ntchito Baibulo mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba? Pamenepo ayamikireni, ndipo nenani kanthu kolimbikitsa.
Chilimbikitso nchofunika kwambiri m’banja ndi mumpingo. Chingathandize makolo kulera ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].” (Aefeso 6:4) Kuuza mwana kuti wachita bwino, ndi kumuuza chifukwa chake, kungakhale kolimbikitsa kwambiri! M’zaka zaunyamata, pamene achichepere amayang’anizana ndi ziyeso ndi zitsenderezo zambiri, chilimbikitso chanthaŵi zonse nchofunika.
Kusoŵeka kwa chilimbikitso paubwana kungakhale kowononga kwambiri. Lerolino Michael, mkulu Wachikristu, ngwaubwenzi, koma akuti: “Atate sanandiuzepo kuti ndinachita bwino pa kanthu kalikonse. Chotero ndinakula ndilibe chidaliro chaumwini. . . . Ngakhale kuti ndili ndi zaka 50 tsopano, ndimayamikirabe kuuzidwa ndi mabwenzi kuti ndikuchita bwino monga mkulu. . . . Zimene zinandichitikira zandiphunzitsa kufunika kwake kwa kulimbikitsa ena, ndipo ndimayesetsa kuchita zimenezo.”
Kodi Ndani Amene Afunikira Chilimbikitso?
Akulu Achikristu amene amagwira ntchito kwambiri ayenerera chilimbikitso. Paulo analemba kuti: “Abale, tikupemphani, dziŵani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yawo.” (1 Atesalonika 5:12, 13) Nkosavuta kuona mopepuka ntchito yaikulu ya akulu. Koma mawu oyamikira ndi olimbikitsa angachititse katundu wawo kuoneka ngati wopepukirapo.
Ndiponso amene akupirira mikhalidwe yovuta pakati pathu afunikira chilimbikitso. “Limbikitsani amantha mtima; chirikizani ofooka,” Baibulo limalangiza motero. (1 Atesalonika 5:14) Makolo amene ali okha, akazi amasiye, achinyamata, okalamba, ndi odwala ali pakati pa awo amene amapsinjika maganizo kapena kufooka mwauzimu nthaŵi ndi nthaŵi.
María ali mkazi Wachikristu amene anangosiyidwa mwadzidzidzi ndi mwamuna wake. Iye akuti: “Mofanana ndi Yobu, ndinalakalaka kufa panthaŵi zina. [Yobu 14:13] Koma ndinapitirizabe wosafooka chifukwa cha chilimbikitso chimene ndinalandira. Akulu aŵiri, amene ndinali kudziŵa bwino, anataya maola ambiri akumandithandiza kuona kufunika kwake kwa kupitiriza mu utumiki wa nthaŵi yonse. Ndipo alongo aŵiri omvetsetsa nawonso ananditonthoza mtima, akumamvetsera moleza mtima pamene ndinali kuwauza zakukhosi. Mwa kugwiritsira ntchito Baibulo, iwo anandikhozetsa kuona zinthu malinga ndi mmene Yehova amazionera. Sindidziŵa kuti tinaŵerenga kangati Salmo 55:22, koma ndikudziŵa kuti mwa kugwiritsira ntchito lemba limeneli, ndinayamba pang’onopang’ono kupezanso nyonga yanga yauzimu ndi yamalingaliro. Zonsezi zinachitika zaka 12 zapitazo, ndipo ndili wokondwa kunena kuti ndapitiriza mu utumiki wa nthaŵi yonse mpaka lero. Moyo wanga uli wokhutiritsa ndi wachimwemwe ngakhale kuti nthaŵi zina ndimapsinjika mtima. Ndine wotsimikiza kuti chilimbikitso cha panthaŵi yotero chingathandize kwambiri m’moyo wa munthu.”
Ena amafuna chilimbikitso chifukwa chakuti achita zolakwa ndipo tsopano akulimbikira kuziwongolera. Mwinamwake alandira chidzudzulo chachikondi. (Miyambo 27:6) Akulu amene apereka chidzudzulocho ayenera kukhala atcheru kotero kuti awayamikire pamene aona kuti iwo akugwiritsira ntchito uphungu wa Malemba. Mawu awo olimbikitsa adzakhala ndi mapindu aŵiri—kutsimikiziritsa chikondi chawo pa wolakwayo kotero kuti asakhale ndi “chisoni chochuluka” ndi kumkumbutsa mapindu a kugwiritsira ntchito uphungu wotero.—2 Akorinto 2:7, 8.
Mkulu wina anachita cholakwa chachikulu natayikidwa mathayo ake a uyang’aniro mumpingo. “Pamene chilengezo chinaperekedwa cha kuchotsedwa kwanga pa ukulu, ndinaganiza kuti abale sakamva bwino kukhala nane,” iye akutero. “Komatu akulu anasunga kwambiri chinsinsi cha mlanduwo ndipo anachita zonse zotheka kundilimbikitsa. Mofananamo, mpingo wonse unasonyeza chikondi ndi ubwenzi, zimene zinachititsadi kuchira kwanga kwauzimu.”
Khalani Wolimbikitsa Ena
M’moyo wathu wotangwanitsidwa, nkosavuta kunyalanyaza kulimbikitsa ena. Koma kulimbikitsa ena kungakhaledi kopindulitsa! Kuti mupereke chilimbikitso chogwira mtima, muyenera kukumbukira zinthu ziŵiri. Choyamba, lingalirani zimene mudzakamba, kotero kuti chilimbikitso chanu chikhale cholunjika. Chachiŵiri, funafunani mpata wa kupita kwa munthu amene ayenera kuyamikiridwa kapena amene afunikira kulimbikitsidwa.
Ngati muchita zimenezi kaŵirikaŵiri, mudzakhala achimwemwe kwambiri. Ndi iko komwe, Yesu akutitsimikizira kuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Mwa kulimbikitsa ena, mudzadzilimbikitsa inu eni. Bwanji osadziikira chonulirapo cha kulimbikitsa wina tsiku lililonse?