Analandira Chitsogozo cha Mulungu
TINENE kuti mwana wangwiro anaikidwa m’manja mwanu kuti mumsamalire ndi kuti mumlere moyenera. Ha, nchitokoso chotani nanga chimenecho! Kodi ndimotani mmene munthu wina aliyense wopanda ungwiro angachitire zimenezo? Ndi kokha mwakulandira chitsogozo cha Mulungu ndi kuchigwiritsira ntchito m’moyo watsiku ndi tsiku.
Zimenezo nzimene Yosefe anachita kumene, atate wa Yesu womlera. Mosiyana ndi miyambo yopeka yofotokoza zambiri ponena za Yosefe, Baibulo silimanena zambiri ponena za mbali yake yochitidwa modzichepetsa m’moyo woyambirira wa Yesu. Timadziŵa kuti Yosefe ndi mkazi wake, Mariya, analera Yesu, ana aamuna anayi, ndi ana aakazinso.—Marko 6:3.
Yosefe anali mbadwa ya Mfumu Davide ya Israyeli kupyolera mu mzera wa Solomo. Iye anali mwana wa Yakobo ndi mpongozi wa Heli. (Mateyu 1:16; Luka 3:23) Monga mmisiri wa mitengo mu mzinda wa Nazarete ku Galileya, Yosefe analibe zinthu zochuluka. (Mateyu 13:55; Luka 2:4, 24; yerekezerani ndi Levitiko 12:8.) Koma anali wolemera mwauzimu. (Miyambo 10:22) Ndithudi zimenezi zinali chifukwa chakuti iye analandira chitsogozo cha Mulungu.
Mosakayikira, Yosefe anali Myuda wofatsa ndi wodzichepetsa amene anali ndi chikhulupiriro mwa Mulungu ndi amene anafunitsitsa kuchita chimene chinali chabwino. Zochitika zoŵerengeka za moyo wake zolembedwa m’Malemba zimasonyeza kuti iye nthaŵi zonse anali womvera malamulo a Yehova. Zimenezi zinali choncho mosasamala kanthu kuti ameneŵa anali m’Chilamulo kapena analandiridwa mwachindunji ndi Yosefe kudzera mwa angelo.
Munthu Wolungama Wokhala ndi Mavuto
Kodi munthu wowopa Mulungu ayenera kuchitanji pamene ayang’anizana ndi vuto lalikulu? Eya, ‘ayenera kusenza Yehova nkhaŵa zake’ ndi kutsatira chitsogozo cha Mulungu! (Salmo 55:22) Zimenezo nzimene Yosefe anachita. Pamene anapala ubwenzi Mariya, “asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa mzimu woyera.” Chifukwa chakuti Yosefe ‘anali wolungama, ndiponso sanafune kunyazitsa iye, anayesa m’mtima kumleka iye mtseri.’ Yosefe atasinkhasinkha za nkhaniyo, mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye m’kulota ndipo anati: “Yosefe, mwana wa Davide, usawope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha mzimu woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.” Atauka kutulo take, Yosefe “[a]nachita monga anamuuza mngelo wa [Yehova, NW], nadzitengera yekha mkazi wake; ndipo sanamdziŵa iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu.” (Mateyu 1:18-25) Yosefe analandira chitsogozo cha Mulungu.
Kaisara Augusto analamula kuti anthu alembetse m’kaundula m’mizinda yawo. Pomvera lamulolo, Yosefe ndi Mariya anamka ku Betelehemu ku Yudeya. Kumeneko Mariya anabala Yesu ndipo anamgoneka modyera ng’ombe chifukwa chakuti kunalibe malo ogona. Usikuwo abusa amene anamva chilengezo cha angelo cha kubadwa kumeneku kwapadera anadza kudzaona khandalo. Pafupifupi masiku 40 pambuyo pake, Yosefe ndi Mariya anachita mogwirizana ndi Chilamulo mwa kusonyeza Yesu ku kachisi ku Yerusalemu limodzi ndi nsembe. Onse aŵiriwo anadabwa pamene anamva mawu aulosi a Simeoni onena za zinthu zazikulu zimene Yesu adzachita.—Luka 2:1-33; yerekezerani ndi Levitiko 12:2-4, 6-8.
Ngakhale kuti Luka 2:39 angaonekere kukhala akusonyeza kuti Yosefe ndi Mariya anamka ku Nazarete nthaŵi yomweyo atasonyeza Yesu pakachisi, vesili lili mbali ya cholembedwa chofupikitsidwa. Kukuonekera kuti patapita nthaŵi ina pambuyo pa kusonyezedwa kwa pakachisiko, anzeru a Kummaŵa (Amagi) anadza kudzaona Mariya ndi Yesu m’nyumba ina ku Betelehemu. Kuloŵerera kwa Mulungu kunaletsa kudzaona Yesu kumeneku kuchititsa imfa yake. Amagiwo atachoka, mngelo wa Yehova anaonekera kwa Yosefe m’kulota ndi kumuuza kuti: “Herode adzafuna kamwana kukawononga iko.” Monga mwanthaŵi zonse, Yosefe anamvera chitsogozo cha Mulungu ndipo anatengera banja lake ku Aigupto.—Mateyu 2:1-14.
Herode atamwalira, mngelo anaonekera kwa Yosefe m’kulota ku Aigupto, akumati: “Tauka, nutenge kamwana ndi amake, nupite ku dziko la Israyeli.” Atamva kuti mwana wa Herode Arikelao anali kulamulira m’malo mwa atate wake, Yosefe anachita mantha kubwerera ku Yudeya. Pomvera chenjezo la Mulungu loperekedwa m’kulota, anamka m’dera la Galileya nakhala mu mzinda wa Nazarete.—Mateyu 2:15-23.
Munthu wa Mkhalidwe Wauzimu
Yosefe anali wotsimikizira kuona kuti banja lake linachita zinthu mogwirizana ndi lamulo la Mulungu ndi kuti linadyetsedwa mwauzimu. Chaka chilichonse iye anatengera banja lake lonse ku phwando la Paskha ku Yerusalemu. Pa imodzi ya nyengo zimenezi, Yosefe ndi Mariya anali kubwerera kumka ku Nazarete ndipo anali atatha ulendo watsiku limodzi kuchokera ku Yerusalemu pamene anatulukira kuti Yesu wa zaka 12 panalibepo. Akumabwereranso ku Yerusalemu, anamfunafunitsa ndipo potsirizira pake anampeza pa kachisi, akumamvetsera ndi kufunsa mafunso aphunzitsi amene anali pamenepo.—Luka 2:41-50.
Kukuonekera ngati kuti Yosefe analola mkazi wake kukhala woyambirira m’kuchita zinthu zina. Mwachitsanzo, pamene anabwereranso ku Yerusalemu ndi kupeza Yesu m’kachisi, anali Mariya amene analankhula kwa mwana wake wamwamuna wamng’onoyo ponena za nkhaniyo. (Luka 2:48, 49) Pamene anali kukula monga “mwana wa mmisiri wa mitengo,” Yesu analandira malangizo auzimu. Yosefe anamphunzitsanso umisiri wa mitengo, pakuti Yesu anatchedwa ‘mmisiri wa mitengo, mwana wa Mariya.’ (Mateyu 13:55; Marko 6:3) Lerolino makolo owopa Mulungu ayenera kugwiritsira ntchito mokwanira mipata yofananayo kulangiza ana awo, makamaka kuwapatsa maphunziro auzimu.—Aefeso 6:4; 2 Timoteo 1:5; 3:14-16.
Ziyembekezo za Yosefe
Malemba samanena chilichonse ponena za imfa ya Yosefe. Koma nkodziŵika kuti Marko 6:3 anatcha Yesu kuti “mwana wa Mariya,” osati Yosefe. Zimenezi zimasonyeza kuti panthaŵiyo Yosefe anali atamwalira. Ndiponso, ngati Yosefe akanakhala ndi moyo kufikira mu 33 C.E., nkwachionekere kuti Yesu wopachikidwayo sakanaikizira Mariya m’chisamaliro cha mtumwi Yohane.—Yohane 19:26, 27.
Motero, Yosefe, adzakhala pakati pa akufa amene adzamva mawu a Mwana wa munthu ndi kuukitsidwa. (Yohane 5:28, 29) Podziŵa za makonzedwe a Yehova a moyo wosatha, Yosefe mosakayikira anadzipereka kuti ayenerere ndipo adzakhala nzika yomvera ya Mfumu yaikulu yakumwamba, Yesu Kristu, monga momwe anachitira momvera chitsogozo cha Mulungu zaka zoposa 1,900 zapitazo.
[Chithunzi patsamba 31]
Yosefe anapatsa Yesu malangizo auzimu ndiponso anamphunzitsa umisiri wa mitengo