Mboni za Yehova Padziko Lonse—Zambia
WOTAKATA, wa zidikha zamapiri pa nthaka yathyathyathya yokwezeka kwa mamita 1,200—ndiye Zambia, dziko lokhala pakati pa chigawo chapakati koma chakummwera kwa Afirika. Kumpoto kwake koma chakummaŵa, kuli mapiri otchedwa Muchinga Mountains okwera mamita 2,100. Mtsinje wa Zambezi wamphamvuwo, umene umafuka mochititsa chidwi pamwamba pa mathithi ochedwa Victoria Falls otchuka padziko lonse, umapanga mbali yaikulu ya malire akummwera a dzikoli lochingidwa ndi maiko ena. Kunoko kuli anthu osiyanasiyana, ndi mitundu yosiyanasiyana yoposa 70. Kumalankhulidwa zinenero zazikulu zisanu ndi zitatu, koma zilipo zina zambiri.
Mu 1911 chinenero cha mtundu wina chinayamba kukhazikika ndi kufalikira m’Zambia. Alendo anabweretsa makope a Studies in the Scriptures, ndipo Mboni za Yehova kuyambira nthaŵiyo kumkabe mtsogolo zayesayesa kufalitsa “chinenero choyera” cha choonadi cha Baibulo m’Zambia. (Zefaniya 3:9, NW) Zovuta zawo makamaka ndizo zikhulupiriro zosagwirizana ndi Malemba za mkhalidwe wa akufa. Pamene anthu aphunzira choonadi ndi kuona mmene malaulo awaikira muukapolo, zotulukapo zake zimakhala chimasuko!—Yohane 8:32.
Mwachitsanzo, mlongo wina wokhulupirika akusimba: “Pamene amalume anamwalira mwadzidzidzi, amayi, chiwalo cholimba cha United Church of Zambia, anathedwa nzeru. Pambuyo pa mwambo wa kuika maliro wotenga mlungu umodzi, ndinabwerera kumudzi kukaona mmene analiri. Nditafika kumeneko, ndinapeza nkhalamba ina yachimuna m’nyumba, ndipo pamene inapita, ndinafunsa agogo aakazi kuti mwamunayo anali yani. Anati anali sing’anga. Amayi anafuna kumulipira kuti alipsire imfa ya alongo awo kuti mzimu wawo ugone. Iwo anakhulupirira kuti panthaŵiyo unali ‘kungoyendayenda,’ malinga ndi mmene ananenera.
“Agogowo anapitiriza kufotokoza kuti kufika kwangako kunali dalitso chifukwa chakuti banjalo linkafunafuna ndalama zolipira sing’angayo. Anandipempha kuthandiza, koma mwaluso ndinalongosola kuti monga Mkristu, sindikanatha kutengamo mbali. Ndinakambitsirana nawo Salmo 146:4, limene limasonyeza kuti akufa salingalira—chotero kulibe mzimu umene ‘ukuyendayenda.’ Tinakambitsirananso Aroma 12:19, ndikutchula kuti kubwezera ndi kwa Yehova osati ife ayi. Nditatero, ndinauza amayi za chiyembekezo cha chiukiriro chimene Yesu analankhula chimene chili pa Yohane 5:28, 29. Iwo anachita chidwi ndi chikhulupiriro changa cholimba m’malonjezo a Mulungu. Posapita nthaŵi anayamba kuphunzira ndi Mboni ina ndi kupita patsogolo mofulumira. Iwo analeka kugwirizana konse ndi chipembedzo chawo chakale ndi kusonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu mwa ubatizo. Tsopano ali mmodzi wa Mboni za Yehova.”
Mlongo wina akusimba kuti: “Ndinapita ku maliro a akazi a amalume. Nditafika, ndinapeza kuti amalume ndi msuwani wanga alikufa ndi njala. Iwo sanadye kanthu kuyambira tsiku limene apongozi anamwalira. Pamene ndinafunsa chifukwa chake, iwo anayankha kuti malinga ndi mwambo, sanaloledwe kukoleza moto kuti aphike chakudya. Ndinapempha kuti ndiphike ndine, koma ena abanja anawopa kuti ndikaswa mwambo wachikunja umenewo, aliyense akachita msala!
“Ndinafotokoza kuti monga mmodzi wa Mboni za Yehova, ndimalemekeza zimene Baibulo limanena pa Levitiko 18:30 ndipo sindimatsatira miyambo yosagwirizana ndi malemba. Ndiyeno ndinawasonyeza brosha lakuti Mizimu ya Akufa. Atamva zimenezo anafeŵa mtima, ndipo ndinaphikira chakudya amalume ndi anthu ena onse. Achibale a wakufayo anachita chidwi ndi kulimba mtima kwanga ndipo anavomereza kupitiriza kuphunzira Baibulo. Iwo ali kale ofalitsa osabatizidwa, ndipo banja lonselo likuyembekezera kubatizidwa posachedwapa.”
Timakhala okondwa chotani nanga pamene chinenero choyera cha choonadi chichotsa msokonezo wa zinyengo za chipembedzo, makamaka malingaliro ozama kwambiri amenewo amene amaika anthu osadziŵa kanthu muukapolo! Ndi dalitso la Yehova, chinenero choyera chikufalikira m’Zambia, monga momwe chikuchitira pa dziko lonse lapansi.—2 Akorinto 10:4.
[Bokosi patsamba 9]
ZIŴERENGERO ZA DZIKOLO
Chaka Chautumiki cha 1994
CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 82,926
KUGAŴA: Mboni 1 pa anthu 107
OFIKA PA CHIKUMBUTSO: 363,372
AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 10,713
AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 108,948
CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 3,552
CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 2,027
OFESI YA NTHAMBI: LUSAKA
[Chithunzi patsamba 9]
Nthambi ya Watch Tower kunja kwa mzinda wa Lusaka
[Chithunzi patsamba 9]
Kulalikira ku Shimabala, kummwera kwa Lusaka