Kuphunzira Kupeza Chisangalalo M’kuwopa Yehova
“Idzani ananu ndimvereni ine: ndidzakulangizani za kumuwopa Yehova.”—SALMO 34:11.
1. Kodi mantha adzachotsedwa motani ndi Ufumu wa Mulungu, koma kodi zimenezo zikutanthauza mantha onse?
ANTHU kulikonse amakhumba kumasuka ku mantha—mantha a upandu ndi chiwawa, mantha a ulova, mantha a matenda aakulu. Lidzakhala tsiku lalikulu chotani nanga pamene chimasuko chimenecho chidzachitikadi pansi pa Ufumu wa Mulungu! (Yesaya 33:24; 65:21-23; Mika 4:4) Komabe, mantha onse sadzachotsedwa panthaŵiyo, ndiponso sitiyenera kuyesa kuchotsa mantha onse m’miyoyo yathu. Pali mantha abwino ndi oipa.
2. (a) Kodi ndi mantha otani amene ali oipa, ndipo kodi ndi mtundu uti umene uli wabwino? (b) Kodi mantha aumulungu nchiyani, ndipo kodi malemba oikidwawo amasonyeza motani zimenezo?
2 Mantha angakhale poizoni yamaganizo, akumafooketsa mphamvu ya munthu ya kulingalira. Angafooketse kulimba mtima ndi kuwononga chiyembekezo. Mantha otero angakhale ndi wina amene akuwopsezedwa mwakuthupi ndi mdani. (Yeremiya 51:30) Angakhale ndi munthu amene amasamalira kwambiri kufunika kwa kukhala wovomerezedwa ndi anthu ena amene amalingaliridwa kukhala ndi ukumu waukulu. (Miyambo 29:25) Koma palinso mantha abwino, amene amatiletsa kuchita chinthu chilichonse mosasamala, chimene chingativulaze. Mantha aumulungu amaphatikizapo zoposa zimenezo. Ndiko kuwopa Yehova, ulemu waukulu kwa iye, limodzi ndi chinthenthe choyenera cha kusamkondweretsa. (Salmo 89:7) Mantha ameneŵa a kupeŵa kusakondweretsa Mulungu amakhalapo chifukwa cha kuyamikira kukoma mtima kwake ndi ukoma wake. (Salmo 5:7; Hoseya 3:5) Amaphatikizaponso kuzindikira kuti Yehova ndiye Woweruza Wamkulu ndi Wamphamvuyonse, amene ali ndi mphamvu ya kupereka chilango, ngakhale cha imfa, kwa awo amene amakana kumumvera.—Aroma 14:10-12.
3. Kodi ndimotani mmene kuwopa Yehova kulili kosiyana ndi kwa milungu ina yachikunja?
3 Mantha aumulungu ngabwino, osati oipa. Amasonkhezera munthu kukhala wolimba nji pa chabwino, wosagonja mwa kuchita cholakwa. Sali ngati mantha a kuwopa mulungu Wachigiriki Phobos, wofotokozedwa kukhala mulungu woipa amene anali wowopsa. Ndipo sali ngati mantha akuwopa mulungu wachikazi Wachihindu Kali, amene panthaŵi zina amasonyezedwa kukhala wachilope, akumagwiritsira ntchito mitembo, njoka, ndi zibade monga zokometsera. Mantha aumulungu amakopa; samawopseza. Amayendera limodzi ndi chikondi ndi chiyamikiro. Motero, mantha aumulungu amatikokera kwa Yehova.—Deuteronomo 10:12, 13; Salmo 2:11.
Chifukwa Chake Ena Ali Nawo Ndipo Ena Alibe
4. Monga momwe kwasonyezedwera ndi mtumwi Paulo, kodi mtundu wa anthu wafika pa mkhalidwe wotani, ndipo chikuchititsa zimenezi nchiyani?
4 Mtundu wa anthu wonse umene, sukusonkhezeredwa ndi mkhalidwe wa mantha aumulungu. Pa Aroma 3:9-18, mtumwi Paulo akufotokoza mlingo wa kutalikirana ndi ungwiro woyambirira umene anthu afikapo. Atanena kuti onse ali muuchimo, Paulo akugwira mawu a Masalmo, kuti: “Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi.” (Onani Salmo 14:1.) Ndiyeno akupereka maumboni mwa kutchula zinthu zonga kunyalanyaza kwa anthu kufuna Mulungu, kusoŵa kwawo kukoma mtima, mawu awo achinyengo, kutemberera, ndi kukhetsa mwazi. Zimenezo zikufotokoza molondola chotani nanga dziko la lerolino! Anthu ochuluka samafuna kudziŵa za Mulungu ndi zifuno zake. Kaŵirikaŵiri mkhalidwe wonga wachifundo umangochitidwa pamene pali kanthu kena koti apindule nawo. Kunama ndi kutukwana nzofala. Kukhetsa mwazi kumasonyezedwa osati pa nyuzi pokha komanso m’zosangulutsa. Kodi chimachititsa mkhalidwewo nchiyani? Nzoona kuti tonsefe ndife mbadwa za Adamu wochimwayo, koma pamene anthu asankha kuchita zinthu zofotokozedwa ndi mtumwi Paulo monga moyo wawo, kanthu kena koposa zimenezo kamaloŵetsedwamo. Vesi 18 likufotokoza za iko, likumati: “Kumuwopa Mulungu kulibe pamaso pawo.”—Onani Salmo 36:1.
5. Kodi nchifukwa ninji anthu ena ali ndi mantha aumulungu, pamene kuli kwakuti ena alibe?
5 Komabe, kodi nchifukwa ninji anthu ena ali ndi mantha aumulungu pamene ena alibe? Kunena mosavuta, nchifukwa chakuti anthu ena amawakulitsa, pamene kuli kwakuti ena samatero. Palibe aliyense wa ife amene amabadwa nawo, koma tonsefe tili ndi kukhoza kwakukhala nawo. Mantha aumulungu ali kanthu kena kamene tiyenera kuphunzira. Ndiyeno, kuti akhale mphamvu yaikulu yosonkhezera miyoyo yathu, tifunikira kuwakulitsa.
Pempho Lochonderera
6. Kodi ndani amene akupereka pempho kwa ife lolembedwa pa Salmo 34:11, ndipo kodi vesili limasonyeza motani kuti mantha aumulungu ayenera kuphunziridwa?
6 Pempho lochonderera la kudzaphunzira kuwopa Yehova likuperekedwa kwa ife m’Salmo 34. Limeneli ndi salmo la Davide. Ndipo kodi Davide anaphiphiritsira yani? Osatinso munthu wina koma Ambuye Yesu Kristu. Ulosi umene mtumwi Yohane anatchula molunjika kukhala ukunena za Yesu walembedwa m’vesi 20 la salmo limeneli. (Yohane 19:36) M’tsiku lathu, Yesu ndiye amene akupereka pempho longa lija la mu vesi 11: “Idzani ananu ndimvereni ine: ndidzakulangizani za kumuwopa Yehova.” Zimenezi zimasonyeza bwino kwambiri kuti mantha aumulungu ali kanthu kena kamene kangaphunziridwe, ndipo Yesu Kristu ali wokhoza bwino kwambiri kutiphunzitsa. Kodi nchifukwa ninji zili choncho?
7. Kodi nchifukwa ninji Yesu ndiye amene makamaka tiyenera kuphunzirako mantha aumulungu?
7 Yesu Kristu amadziŵa kufunika kwa mantha aumulungu. Ahebri 5:7 amati ponena za iye: “Ameneyo, m’masiku a thupi lake [Kristu NW] anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa iye mu imfa, ndipo anamveka popeza anawopa Mulungu.” Mantha aumulungu amenewo anali mkhalidwe umene Yesu Kristu anasonyeza ngakhale pamene anali asanayang’anizane ndi imfa pa mtengo wozunzirapo. Kumbukirani, m’Miyambo chaputala 8, Mwana wa Mulungu amafotokozedwa kukhala nzeru. Ndipo pa Miyambo 9:10, timauzidwa: “Chiyambi cha nzeru ndicho kuwopa Yehova.” Chotero mantha aumulungu ameneŵa anali mbali yaikulu ya umunthu wa Mwana wa Mulungu kalelo asanadze ku dziko lapansi.
8. Kodi nchiyani chimene timaphunzira ponena za kuwopa Yehova pa Yesaya 11:2, 3?
8 Ndiponso, ponena za Yesu monga Mfumu Yaumesiya, Yesaya 11:2, 3 amati: “Mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziŵa ndi wakuwopa Yehova; ndipo adzakondwera nako kumuwopa Yehova.” Zimenezo zikulongosoledwa bwino chotani nanga! Kuwopa Yehova sikuli chinthu choipa. Nkwabwino ndi kothandiza. Ndiko mkhalidwe umene udzafunga pa gawo lonse limene Kristu adzalamulira monga Mfumu. Iye akulamulira tsopano lino, ndipo kwa onse amene akusonkhanitsidwa kukhala nzika zake, akuwapatsa malangizo m’kuwopa Yehova. Motani?
9. Kodi ndimotani mmene Yesu Kristu akutiphunzitsira kuwopa Yehova, ndipo kodi iye akufuna kuti tiphunzirenji za iko?
9 Kupyolera m’misonkhano yathu ya mpingo, misonkhano yadera, ndi misonkhano yachigawo, Yesu, monga Mutu wa mpingo woikidwa ndipo monga Mfumu Yaumesiya, amatithandiza kumvetsetsa bwino lomwe chimene chili mantha aumulungu ndi chifukwa chake ali opindulitsa kwambiri. Motero amayesayesa kukulitsa chiyamikiro chathu kaamba ka iwo kotero kuti tiphunzire kupeza chisangalalo m’kuwopa Yehova monga momwe iye amachitira.
Kodi Mudzapanga Kuyesayesa?
10. Pamene tili pamisonkhano Yachikristu, kodi tiyenera kuchitanji ngati titi timvetsetse kuwopa Yehova?
10 Ndithudi, kungoŵerenga kwathu Baibulo kapena kufika pamisonkhano m’Nyumba Yaufumu sikudzatichititsa kukhala ndi mantha aumulungu. Taonani zimene tifunikira kuchita ngati titi timvetsetsedi kuwopa Yehova. Miyambo 2:1-5 imati: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwayira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuwopa Yehova ndi kumdziŵadi Mulungu.” Chotero pamene tifika pamisonkhano, tifunikira kutchera khutu ku zimene zikunenedwa, kuyesayesa mwakhama kusumika maganizo pa mfundo zazikulu ndi kuzikumbukira, kusinkhasinkha mwakuya ponena za mmene lingaliro lathu la Yehova liyenera kusonkhezera mkhalidwe wathu wamaganizo kulinga ku uphungu umene ukuperekedwa—inde, kutsegula mitima yathu. Pamenepo tidzazindikira kuwopa Yehova.
11. Kuti tikulitse mantha aumulungu, kodi tiyenera kuchitanji mwakhama ndiponso nthaŵi zonse?
11 Salmo 86:11 limasonyeza chinthu china chofunika, pemphero. “Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m’choonadi chanu,” anapemphera motero wamasalmo. “Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliwope dzina lanu.” Yehova anavomereza pemphero limenelo, pakuti analichititsa kulembedwa m’Baibulo. Kuti tikulitse mantha aumulungu, nafenso tifunikira kupemphera kwa Yehova kaamba ka thandizo lake, ndipo tidzapindula mwa kupemphera mwakhama ndiponso nthaŵi zonse.—Luka 18:1-8.
Mtima Wanu Ukuloŵetsedwamo
12. Kodi nchifukwa ninji mtima uyenera kupatsidwa chisamaliro chapadera, ndipo kodi zimenezi zimaphatikizaponji?
12 Palinso kanthu kena kamene tifunikira kuona pa Salmo 86:11. Wamasalmo sanali kungopempha kuti angodziŵa m’maganizo za kuwopa Mulungu. Iye akutchula mtima wake. Kukulitsa mantha aumulungu kumaloŵetsamo mtima wophiphiritsira, umene umafuna kupatsidwa chisamaliro chapadera chifukwa chakuti ndiwo munthu wamkati wosonyezedwa m’zochita zathu zonse za moyo ndipo umaphatikizapo malingaliro athu, mkhalidwe wathu wamaganizo, zikhumbo zathu, zolinga zathu, ndi zonulirapo zathu.
13. (a) Kodi nchiyani chimene chingasonyeze kuti mtima wa munthu uli wogaŵanika? (b) Pamene tikukulitsa mantha aumulungu, kodi tiyenera kumenyera nkhondo kulinga ku chonulirapo chotani?
13 Baibulo limatichenjeza kuti mtima wa munthu ungakhale wogaŵanika. Ungakhale wonyenga. (Salmo 12:2; Yeremiya 17:9) Ungatisonkhezere kukhala ndi phande m’zochita zabwino—kupita kumisonkhano ya mpingo ndi ku utumiki wakumunda—komanso ungakonde mbali zina za moyo wa dziko. Zimenezi zingatilepheretse kuchirikiza ndi mtima wonse zinthu za Ufumu. Pamenepo mtima wonyengawo ungayese kutisonkhezera kuti, ndi iko komwe, tikuchita zochuluka mofanana ndi ena ambiri. Mwina mwake kusukulu kapena pantchito, mtima ungasonkhezeredwe ndi kuwopa munthu. Monga chotulukapo chake, m’mikhalidwe imeneyo tingazengereze kudzidziŵikitsa kuti tili Mboni za Yehova ndipo mwina tingachitedi zinthu zimene zili zosayenera kwa Akristu. Komabe, pambuyo pake, chikumbumtima chathu chimatitsutsa. Sitikufuna kukhala munthu wamtundu umenewo. Chifukwa chake, timapemphera kwa Yehova mogwirizana ndi wamasalmo: “Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliwope dzina lanu.” Tikufuna kuti munthu yense wamkati, wosonyezedwa mu ntchito zathu zonse za m’moyo, asonyeze kuti ‘timawopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake.’—Mlaliki 12:13.
14, 15. (a) Poneneratu za kubwezeretsedwanso kwa Israyeli kuchokera ku ukapolo wa ku Babulo, kodi nchiyani chimene Yehova analonjeza kupatsa anthu ake? (b) Kodi Yehova anachitanji ali ndi cholinga cha kukhomereza kuwopa Mulungu m’mitima ya anthu ake? (c) Kodi nchifukwa ninji Israyeli anachoka m’njira za Yehova?
14 Yehova analonjeza kuti akapatsa anthu ake mtima wa kuwopa Mulungu wotero. Ananeneratu za kubwezeretsedwanso kwa Israyeli, ndipo monga momwe timaŵerengera pa Yeremiya 32:37-39 anati: “Ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika, ndipo adzakhala anthu anga, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo; ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiwope ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana awo pambuyo pawo.” Mu vesi 40, lonjezo la Mulungu likuchirikizidwa: “Ndidzalonga kuwopsa kwanga m’mitima yawo, kuti asandichokere.” Mu 537 B.C.E., Yehova anawabwezeranso ku Yerusalemu monga momwe analonjezera. Komano bwanji nanga za mbali yotsala ya lonjezo limenelo—lakuti akawapatsa ‘mtima umodzi kuti amuwope masiku onse’? Kodi nchifukwa ninji mtundu wa Israyeli wakale unachoka kwa Yehova ataubwezera kwawo kuchokera ku Babulo, kwakuti kachisi wawo anawonongedwa mu 70 C.E., wosadzamangidwanso?
15 Zimenezi sizinali chifukwa cha kulephera kulikonse kwa Yehova. Ndithudi, Yehova anatengadi masitepe a kuika kuwopa Mulungu m’mitima ya anthu ake. Mwa chifundo chimene anasonyeza powalanditsa ku Babulo ndi kuwabwezeretsa kudziko lawo, anawapatsa zifukwa zokwanira zomupatsira ulemu waukulu. Mulungu anachirikiza zonsezo ndi zikumbutso, uphungu, ndi chidzudzulo kupyolera mwa aneneriwo Hagai, Zekariya, ndi Malaki; ndi Ezara, amene anatumidwa kwa iwo monga mphunzitsi; kupyolera mwa Kazembe Nehemiya; ndi mwa Mwana wa Mulungu mwiniyo. Nthaŵi zina anthuwo anamvetsera. Anatero pamene anamanganso kachisi wa Yehova mofulumizidwa ndi Hagai ndi Zekariya ndi pamene anachotsa akazi achikunja m’masiku a Ezara. (Ezara 5:1, 2; 10:1-4) Koma nthaŵi zambiri iwo sanamvere. Si nthaŵi zonse pamene anali otchera khutu; sanapitirize kulabadira uphungu; sanasunge mitima yawo ili yotseguka. Aisrayeli sanali kukulitsa mantha aumulungu, ndipo chotero, sanali mphamvu yaikulu yosonkhezera miyoyo yawo.—Malaki 1:6; Mateyu 15:7, 8.
16. Kodi Yehova wakhomereza mantha aumulungu m’mitima ya ayani?
16 Komabe, lonjezo la Yehova la kuika mantha aumulungu m’mitima ya anthu ake silinalephere. Iye anapanga pangano latsopano ndi Israyeli wauzimu, Akristu amene anawaikira chiyembekezo chakumwamba pamaso pawo. (Yeremiya 31:33; Agalatiya 6:16) Mu 1919, Mulungu anawamasula ku ukapolo wa Babulo Wamkulu, ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Iye wakhomereza zolimba kumuwopa m’mitima yawo. Zimenezi zadzetsa mapindu ochuluka kwa iwo ndi kwa “khamu lalikulu,” limene lili ndi chiyembekezo cha moyo monga nzika za pa dziko lapansi za Ufumuwo. (Yeremiya 32:39; Chivumbulutso 7:9) Kuwopa Yehova kwakhala m’mitima yawo nawonso.
Mmene Mantha Aumulungu Amakhomerezekera m’Mitima Yathu
17. Kodi Yehova waika motani mantha aumulungu m’mitima yathu?
17 Kodi Yehova wakhomereza motani mantha aumulungu ameneŵa m’mitima yathu? Mwa kugwira ntchito kwa mzimu wake. Ndipo kodi nchiyani chimene tili nacho chimene chili chipatso cha mzimu woyera? Baibulo, Mawu a Mulungu ouziridwa. (2 Timoteo 3:16, 17) Mwa zimene wachita kumbuyoku, mwa zochita zake ndi atumiki ake zimene tsopano zikukwaniritsa Mawu ake aulosi, ndi mwa maulosi a zinthu zimene zilinkudza, Yehova amapereka kwa tonsefe maziko amphamvu okulitsirapo mantha aumulungu.—Yoswa 24:2-15; Ahebri 10:30, 31.
18, 19. Kodi ndimotani mmene misonkhano yachigawo, misonkhano yadera, ndi misonkhano ya mpingo imatithandizira kupeza mantha aumulungu?
18 Nkoyenerera kudziŵa kuti, monga momwe kwasimbidwira pa Deuteronomo 4:10, Yehova anati kwa Mose: “Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mawu anga, kuti aphunzire kundiwopa ine masiku awo onse akukhala ndi moyo pa dziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana awo.” Mofananamo lerolino, Yehova wapanga makonzedwe ochuluka kuthandiza anthu ake kuphunzira kumuwopa. Pamisonkhano yachigawo, misonkhano yadera, ndi misonkhano ya mpingo, timasimba za umboni wa kukoma mtima ndi ukoma wa Yehova. Zimenezo nzimene tinali kuchita pamene tinali kuphunzira buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Kodi ndimotani mmene phunziro limenelo linayambukirira inu ndi mkhalidwe wanu wamaganizo kulinga kwa Yehova? Pamene munaona mbali zosiyanasiyana za umunthu wabwino koposa wa Atate wathu wakumwamba zosonyezedwa mwa Mwana wake, kodi zimenezi sizinalimbitse chikhumbo chanu cha kusafuna kusakondweretsa Mulungu?—Akolose 1:15.
19 Pamisonkhano yathu, timaphunziranso mbiri za kulanditsa kwa Yehova anthu ake m’nthaŵi zakale. (2 Samueli 7:23) Pamene tiphunzira buku la Baibulo la Chivumbulutso, timadziŵa za masomphenya amene akwaniritsidwa kale m’zaka za zana la 20 zino ndiponso ponena za zochitika zina zowopsa zimene ziti zidze. Ponena za zochita za Mulungu zonsezo, Salmo 66:5 limati: “Idzani, muone ntchito za Mulungu; zochitira iye ana a anthu nzowopsa.” Inde, zitaonedwa moyenera, zochita za Mulungu zimenezi zimakhomereza m’mitima yathu kuwopa Yehova, ulemu waukulu. Motero timazindikira za mmene Yehova Mulungu amakwaniritsira lonjezo lake: “Ndidzalonga kuwopsa kwanga m’mitima yawo, kuti asandichokere.”—Yeremiya 32:40.
20. Kuti mantha aumulungu akhomerezeke kwambiri m’mitima yathu, kodi nchiyani chimene chikufunika kwa ife?
20 Komabe, kuli kwachionekere kuti mantha aumulungu samangokhala m’mitima mwathu popanda kuyesayesa kwathu. Zotulukapo zake sizimangokhalapo zokha. Yehova amachita mbali yake. Nafenso tiyenera kuchita mbali yathu mwa kukulitsa mantha aumulungu. (Deuteronomo 5:29) Israyeli wakuthupi analephera kuchita zimenezo. Koma modalira Yehova, Aisrayeli auzimu ndi atsamwali awo ayamba kale kupeza ochuluka a mapindu amene amadza kwa awo amene amawopa Mulungu. Tidzalingalira ena a mapindu ameneŵa m’nkhani yotsatira.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi mantha aumulungu nchiyani?
◻ Kodi ndimotani mmene tikuphunzitsidwira kupeza chisangalalo m’kuwopa Yehova?
◻ Kuti tikhale ndi mantha aumulungu, kodi nkuyesayesa kotani kumene kukufunika kwa ife?
◻ Kodi nchifukwa ninji kupeza mantha aumulungu kumaloŵetsamo mbali zonse za mtima wathu wophiphiritsira?
[Zithunzi pamasamba 12, 13]
Phunziro losamalitsa limafunika kuti timvetsetse kuwopa Yehova