Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 5/1 tsamba 4-7
  • Posachedwapa, Sikudzakhalanso Mmphaŵi!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Posachedwapa, Sikudzakhalanso Mmphaŵi!
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Thandizo kwa Amphaŵi
  • Thandizo la Kulimbana ndi Umphaŵi
  • Potsirizira Pake, Sipadzakhalanso Umphaŵi!
  • Mapeto a Umphaŵi Ayandikira
    Galamukani!—1998
  • Tsanzirani Yesu Poganizira Osauka
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Dziko Lopanda Umphawi Layandikira
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kupeza Njira Yothetseratu Umphaŵi
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 5/1 tsamba 4-7

Posachedwapa, Sikudzakhalanso Mmphaŵi!

“MUSAWOPE; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse.” (Luka 2:10) Mawu osangalatsa mtima ameneŵa anamvedwa ndi abusa odabwa pafupi ndi Betelehemu pa usiku umene Yesu anabadwa. Mogwirizana ndi chilengezo chimenecho, Yesu anagogomezera kwambiri za “uthenga wabwino” mu utumiki wake wa pa dziko lapansi. Lerolino, kodi ndimotani mmene uthenga wabwino wonena za Yesu ungatipindulitsire, pamene tikudalira kwambiri pa ndalama kuti tipeze zosoŵa zathu?

Yesu Kristu analengeza ‘uthenga wabwino kwa anthu osauka.’ (Luka 4:18) Malinga ndi Mateyu 9:35, “Yesu anayendayenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, namaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa ufumuwo.” Uthenga wake unalidi wolimbikitsa kwa amphaŵi. “Poona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Zoonadi, Yesu anati, “Osauka muli nawo pamodzi ndi inu nthaŵi zonse,” komatu sitiyenera kulingalira mawu amenewo kuti anatanthauza kuti palibe chiyembekezo kwa osauka. (Yohane 12:8) Padzakhalabe osauka malinga ngati dongosolo loipali lilipobe, mosasamala kanthu za chochititsa chake chilichonse. Mawu a Mulungu samanyalanyaza za kukhalapo kwa umphaŵi, koma samangonena za kuipa kwake. M’malo mwake, amapereka thandizo kwa amphaŵi lolimbanirana ndi nkhaŵa za moyo.

Thandizo kwa Amphaŵi

Mwachidziŵikire, kwanenedwa kuti: “Palibe chothodwetsa chimene chingasenzedwe ndi munthu kuposa cha kudziŵa kuti palibe aliyense amene amamusamala kapena kumumvetsetsa.” Komabe, ngakhale kuti anthu ambiri alibe chifundo, pali uthenga wabwinobe kwa amphaŵi​—patsopano lino ndi mtsogolo momwe.

Mwachisoni, ambiri samakonda kwambiri kuthandiza amphaŵi. Malinga ndi kunena kwa The World Book Encyclopedia, ena amakhulupirira kuti “anthu m’chitaganya chawo amachita mpikisano wa kukhala ndi moyo ndipo . . . opambana amakhala amphamvu ndi achuma.” Awo amene amakhulupirira nthanthi imeneyi, yotchedwa kuti lingaliro la kakhalidwe ka anthu la Darwin, angaone amphaŵi kungokhala anthu aulesi kapena owawanya zinthu. Komabe, antchito a m’mafamu, antchito akudza kuchokera kumaiko ena, ndi ena, ngakhale kuti amalipidwa ndalama zochepa, kaŵirikaŵiri amagwira ntchito zolimba kuti adyetse mabanja awo.

M’maiko ambiri umphaŵi ngwambiri. Chifukwa chake, amphaŵi​—amene ali ambiri​—samachititsidwa kulingalira kuti ali olephera kuchita zinthu. Chikhalirechobe, m’maiko otero muli anthu amene ali ndi moyo wa mwana alirenji pakati pa anthu aumphaŵi. Nyumba zabwino, zambambande zimamangidwa pamodzi ndi zithando za anthu ambirimbiri, zauve. Anthu olandira malipiro abwino kwambiri amayenda pagalimoto zokwera mtengo kwambiri m’misewu ya piringupiringu wa anthu aumphaŵi ndi okhala paulova. M’maiko otero amphaŵi amalingalira kwambiri za mkhalidwe wawo. Kwenikweni, “Amphaŵi amavutika osati kokha ndi chakudya chosamanga thupi, nyumba zoipa, ndi chisamaliro cha mankhwala chochepa, komanso ndi nkhaŵa yanthaŵi zonse ponena za mkhalidwe wawo,” ikutero The World Book Encyclopedia. “Pokhala osakhoza kupeza ntchito yabwino, amataya ulemu wonse ndi kudzilemekeza.” Nangano, kodi amphaŵi ena amalimbana motani ndi mkhalidwe wawo? Kodi uthenga wabwino wonena za Yesu uli wogwirizana motani ndi kulimbana ndi umphaŵi kumeneku?

Choyamba, kumbukirani kuti umphaŵi ungapangitsidwe kukhala woipirapo ndi zizoloŵezi zopusa. Lingalirani zitsanzo zina. Valdecir akuvomereza kuti ankawawanya ndalama pa moyo wa makhalidwe oipa, pamene kuli kwakuti mkazi wake ndi ana aang’ono anali ndi chakudya chochepa. Iye akuti: “Ngakhale kuti ndinali pantchito, sindinkakhala ndi ndalama koma nthaŵi zonse ndinali ndi matikiti osiyanasiyana a lotale m’thumba mwanga.” Milton anataya bizinesi yokhala ndi antchito 23 chifukwa cha kumwetsa zakumwa zaukali ndi kusuta fodya. Iye akuti: “Ndinkathera usiku wambiri m’misewu, wosakhoza kumka kunyumba, ndipo banja langa linavutika kwambiri chifukwa cha ine.”

Nayenso João anawawanya malipiro ake pa makhalidwe oipa. “Sindinkagona panyumba. Malipiro onse amene ndinkalandira sanali okwanira pa makhalidwe anga oipawo ndi akazi. Mkhalidwewo unafikira kukhala wosapiririka, ndipo mkazi wanga anafuna kuti tipumirane.” Kuwonjezera pa mavuto ake azandalama ndi a muukwati, panali enanso. Iye akuti: “Ndinkavutitsa achibale anga ndi anansi, ndipo makamaka ndinali ndi mavuto kuntchito. Chotero, nthaŵi zonse ndinali kuchotsedwa ntchito.” Júlio anali womwerekera ndi anamgoneka. Komabe, iye akufotokoza kuti: “Popeza kuti malipiro anga anali osakwanira kuchirikiza chizoloŵezi changa cha anamgoneka, ndinayamba kugulitsa anamgoneka kuti ndisamachita kugula.”

Pokhala wokulira m’banja laumphaŵi la ana asanu ndi atatu, José anafuna kukhala ndi kanthu kena ka iye mwini. Polingalira kuti panalibe chilichonse chimene akanataya, iye limodzi ndi achichepere ena anayamba kubera anthu. Chifukwa cha kuthedwa nzeru, wachichepere wina anakhala chiŵalo cha kagulu ka chiwawa kotchedwa Headbangers. Iye akufotokoza kuti: “Popeza kuti ambiri a ife tinali osauka kwambiri, tinapeza chikhutiro chenicheni mwa kuphwanya zinthu ndi kuukira anthu.”

Komabe, lerolino anthu ameneŵa ndi mabanja awo sakuvutikanso ndi kusoŵa zinthu kwakukulu kapena kuŵaŵidwa mtima ndi mkwiyo. Iwo salinso osoŵa thandizo kapena opanda chiyembekezo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anaphunzira uthenga wabwino umene Yesu analalikira. Anagwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo ndi kuyanjana ndi anthu a maganizo ofanana mu mipingo ya Mboni za Yehova. Ndipo anaphunzira zinthu zina zofunika kwambiri ponena za chuma ndi umphaŵi.

Thandizo la Kulimbana ndi Umphaŵi

Choyamba, iwo anaphunzira kuti ngati makhalidwe a Baibulo agwiritsiridwa ntchito, ziyambukiro zoipa za umphaŵi zingachepetsedwe. Baibulo limatsutsa chisembwere, kuledzera, kutchova juga, ndi anamgoneka. (1 Akorinto 6:9, 10) Zinthu zotero zimawonongetsa ndalama. Zingachititse munthu wachuma kukhala wosauka, ndipo munthu wosauka kukhala mmphaŵi weniweni. Kuleka makhalidwe oipa ameneŵa ndi ena ofanana nawo kumawongolera kwambiri mkhalidwe wa zandalama wa banja.

Chachiŵiri, iwo anapeza kuti pali zinthu zina zofunika kwambiri m’moyo kuposa chuma. Lingaliro labwino limafotokozedwa m’mawu awa ouziridwa: “Nzeru ichinjiriza monga ndalama zichinjiriza; koma kudziŵa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.” (Mlaliki 7:12) Inde, ndalama nzofunika. Koma nzeru ndi kudziŵa zifuno za Mulungu zozikidwa pa Baibulo nzothandiza kwambiri. Ndithudi, kwa munthu amene alibe nzeru, kukhala ndi ndalama zambirimbiri kungangokhalanso chothodwetsa mofanana ndi kukhala ndi ndalama zochepa kwambiri. Wolemba Baibulo wina mwanzeru anapemphera: “Musandipatse umphaŵi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.”​—Miyambo 30:8, 9.

Chachitatu, iwo anatulukira kuti ngati munthu akhala ndi moyo mogwirizana ndi uthenga wabwino umene Yesu analalikira, sadzaona kukhala wosiyidwa. Uthenga wabwino umalowetsamo Ufumu wa Mulungu. Uthengawo umatchedwa “uthenga . . . wabwino wa ufumu,” ndipo m’tsiku lathu ukulalikidwa pa dziko lonse lapansi lokhala anthu. (Mateyu 24:14) Yesu anatiuza kuti tidzachirikizidwa ngati tiika chiyembekezo chathu pa Ufumu umenewo. Iye anati: “Koma muthange mwafuna Ufumu [wa Mulungu] ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Mulungu sakulonjeza galimoto zambambande kapena nyumba za ampondamatiki. Yesu anali kulankhula za zofunika za moyo, zinthu zonga chakudya ndi zovala. (Mateyu 6:31) Koma lerolino anthu mamiliyoni ambiri angachitire umboni kuti lonjezo la Yesulo nlodalirika. Munthu, ngakhale wosauka kwambiri, samangosiyidwa ngati aika Ufumuwo pamalo oyamba.

Chachinayi, iwo anapeza kuti munthu amene amaika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba samapwetekedwa mtima ndi mavuto azandalama. Inde, munthu waumphaŵi afunikira kugwira ntchito zolimba. Koma ngati atumikira Mulungu, amakhala ndi unansi wapadera ndi Mlengi wake, za amene Baibulo limati: “Sanapeputsa ndipo sananyansidwa ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisira nkhope yake; koma pomfuulira iye, anamva.” (Salmo 22:24) Ndiponso, mmphaŵi amakhala ndi thandizo polimbana ndi mavuto a moyo. Amakhala paubwenzi wachikondi ndi Akristu anzake ndipo amadziŵa chifuniro cha Yehova chovumbulidwa ndipo ali ndi chidaliro pa icho. Zinthu zonga zimenezi “zifunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa.”​—Salmo 19:10.

Potsirizira Pake, Sipadzakhalanso Umphaŵi!

Potsirizira pake, anthu amene amalabadira uthenga wabwino amaphunzira kuti Yehova Mulungu walinganiza kuthetseratu vuto la umphaŵi ndi Ufumu wake. Baibulo limalonjeza kuti: “Sadzaiŵalika nthaŵi zonse waumphaŵi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzawonongeka kosatha.” (Salmo 9:18) Ufumuwo uli boma lenileni, lokhazikitsidwa kumwamba ndi Yesu Kristu monga Wolamulira wake. Posachedwapa, Ufumu umenewo udzaloŵa m’malo maboma a anthu amene akulamulira anthu. (Danieli 2:44) Pamenepo, Yesu, monga Mfumu yoikidwa pa mpando wachifumu “adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”​—Salmo 72:13, 14.

Poyembekezera nthaŵi imeneyo, Mika 4:3, 4 amati: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.” Kodi ndi ayani amene akunenedwa pano? Aha, awo onse amene amagonjera Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewo udzathetsa mavuto onse amene akukantha anthu​—ngakhale vuto la matenda ndi imfa. “Iye wameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.” (Yesaya 25:8; 33:24) Lidzakhala dziko lina chotani nanga limenelo! Ndipo kumbukirani kuti, tingakhulupirire malonjezo ameneŵa chifukwa chakuti ali ouziridwa ndi Mulungu mwiniyo. Iye akuti: “Anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.”​—Yesaya 32:18.

Kudalira Ufumu wa Mulungu kumathetsa kusadziŵerengera kumene kaŵirikaŵiri kumachititsidwa ndi umphaŵi. Mkristu wosauka amadziŵa kuti iye ali wofunikanso pamaso pa Mulungu monga momwe alili Mkristu amene ali wachuma. Mulungu amakonda onsewo mofanana, ndipo onsewo ali ndi chiyembekezo chofanana. Onsewo amayembekezera mwachidwi nthaŵiyo pamene, pansi pa Ufumu wa Mulungu, umphaŵi udzakhala chinthu chakale. Imeneyo idzakhala nthaŵi yabwino chotani nanga! Potsirizira pake, sipadzakhalanso mmphaŵi!

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi nkutayiranji ndalama pa kutchova juga, kusuta fodya, kumwetsa zakumwa zaukali, anamgoneka, kapena pa moyo wachisembwere?

[Chithunzi patsamba 7]

Yehova Mulungu adzathetsa mavuto a umphaŵi wa anthu ndi Ufumu wake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena