Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe”—Kodi Mudzakhalapo?
CHIMWEMWE! Kodi liwuli limamveka lachilendo, losazoloŵereka, m’nthaŵi ino yodzala mavuto? Ndithudi, manyuzipepala samakhala ndi nkhani zambiri zosangalatsa mitima yathu. Nkhondo za mafuko, njala zofalikira, ulova, kuipitsa kowopsa, zipolowe za ndale, upandu—zimenezi sindizo zinthu zotipatsa chimwemwe, sichoncho kodi?
Anthu ochuluka lerolino amasusukira chikondwerero chilichonse chimene angapeze m’moyo. Koma bwanji za chimwemwe? Chimwemwe chalongosoledwa kukhala “mkhalidwe wa kusangalala; kukondwa.” Si anthu ambiri amene akhalapo ndi chimwemwe chenicheni, ndipo pamene akhalapo nacho, kaŵirikaŵiri ndi kwakanthaŵi chabe.
Komabe, poneneratu za nthaŵi yathu, Baibulo linati: “Atero Ambuye Yehova, Taonani, atumiki anga adzasangalala. Taonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala.” (Yesaya 65:13, 14) Kodi zimenezi zingachitike motani?
Kuti mupeze yankho, tikukuitanirani ku umodzi wa misonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova imene idzachitika mu 1995. Mutu wankhani wa misonkhano imeneyo udzakhala wakuti “Atamandi Achimwemwe,” ndipo kuloŵa kudzakhala kwaulere. Programu ya msonkhanowo ya masiku atatu idzaphatikizapo nkhani za Baibulo, zitsanzo, makambitsirano, ndi zina zambiri. M’programu yonseyo, mutu wankhani wa chimwemwe udzagogomezeredwa.
Misonkhanoyo idzayambira ku United States mu June ndipo idzapitiriza m’mizinda ina kuzungulira dziko lonse kufikira mu 1996. Mwachionekere, udzakhalapo wina pafupi ndi inu. Bwanji osafunsa Mboni za Yehova za kwanuko? Tikukuitanani mwachikondi kudzapezekapo.