Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 6/1 tsamba 11-16
  • Chitonthozo Chochokera kwa “Mulungu wa Chitonthozo Chonse”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitonthozo Chochokera kwa “Mulungu wa Chitonthozo Chonse”
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova​—Mulungu wa Chitonthozo
  • Yesu ndi Paulo​—Otonthoza Achifundo
  • Mmene Tingatonthozere Olira
  • Zimene Tiyenera Kupeŵa
  • Malemba Amene Amatonthoza
  • “Lirani ndi Anthu Amene Akulira”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Tonthozani Amene ali ndi Chisoni
    Nsanja ya Olonda—2003
  • ‘Tonthozani Anthu Onse Olira’
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Mulungu Amatilimbikitsa Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 6/1 tsamba 11-16

Chitonthozo Chochokera kwa “Mulungu wa Chitonthozo Chonse”

“Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.”​—2 AKORINTO 1:3, 4.

1, 2. Kodi ndi chitonthozo chotani chimene anthu olira amafunikira?

ANTHU olira amafunikira chitonthozo chenicheni​—osati mawu wamba achisoni ndi ndemanga zachizoloŵezi chabe. Tonsefe tamvapo mawu akuti ‘mudzaiŵala pakapita nthaŵi,’ koma m’masiku oyambirira a kufedwa, kodi ndi munthu wanji wogwidwa ndi chisoni amene angatonthozedwe ndi lingaliro limenelo? Akristu amadziŵa kuti Mulungu walonjeza chiukiriro, koma zimenezo sizimaletsa kupweteka ndi kuvutika maganizo kwakukulu kwa imfa yadzidzidzi. Ndipotu ngati mwataya mwana, ana ena otsala sangatenge malo a wakufa wofunika kwambiriyo.

2 Panthaŵi ya imfa, timathandizidwa kwambiri ndi chitonthozo chenicheni, chitonthozo chimene chili ndi maziko olimba m’malonjezo a Mulungu. Timafunanso chifundo. Zimenezi zakhaladi zofunika kwa anthu a ku Rwanda, makamaka kwa mabanja mazana ambiri a Mboni za Yehova kumeneko amene anataya okondedwa awo m’kuphana kwa mafuko kwauchiŵanda. Kodi nkuti kumene onse olira angapeze chitonthozo?

Yehova​—Mulungu wa Chitonthozo

3. Kodi Yehova wapereka motani chitsanzo cha kupereka chitonthozo?

3 Yehova wapereka chitsanzo potipatsa chitonthozo tonsefe. Anatumiza Mwana wake wobadwa yekha, Kristu Yesu, kudziko lapansi kudzatipatsa chitonthozo chosatha ndi chiyembekezo. Yesu anaphunzitsa kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Iye anauzanso ophunzira ake kuti: “Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.” (Yohane 15:13) Panthaŵi ina iye anati: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Ndipo Paulo ananena kuti: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” (Aroma 5:8) Mwa malemba ameneŵa ndi ena ambiri, timaona chikondi cha Mulungu ndi cha Kristu Yesu.

4. Kodi nchifukwa ninji mtumwi Paulo anali woyamikira Yehova kwenikweni?

4 Mtumwi Paulo anali wodziŵa bwino lomwe za chisomo chachikulu cha Yehova. Iye analanditsidwa kumkhalidwe wa imfa yauzimu, pamene anali wozunza otsatira a Kristu wankhalwe ndi kukhala Mkristu wozunzidwa iye mwini. (Aefeso 2:1-5) Iye akufotokoza zomchitikira kuti: “Ine ndili wamng’ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Eklesia wa Mulungu. Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhala chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.”​—1 Akorinto 15:9, 10.

5. Kodi Paulo analembanji za chitonthozo cha Mulungu?

5 Chotero, kunali koyenera kwa Paulo kulemba kuti: “Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m’nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu. Pakuti monga masautso a Kristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Kristu. Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva. ndipo chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziŵa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi chitonthozo.”​—2 Akorinto 1:3-7.

6. Kodi liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “chitonthozo” limatanthauzanji?

6 Ha, ndi mawu olimbikitsa chotani nanga! Liwu Lachigiriki panopa lotembenuzidwa “chitonthozo” nlogwirizana ndi “pempho la kuima kumbali ya munthu.” Chotero, “ndiko kuima kumbali ya munthu ndi kumchirikiza pamene ali pachiyeso chachikulu.” (A Linguistic Key to the Greek New Testament) Katswiri wina wa Baibulo analemba kuti: “Liwulo . . . nthaŵi zonse limatanthauza zoposa kwambiri chifundo chokhazika mtima. . . . Chitonthozo Chachikristu chili chitonthozo chimene chimalimbikitsa, chitonthozo chimene chimakhozetsa munthu kupirira zonse zimene moyo ungamchitire.” Chimaphatikizaponso mawu otonthoza ozikidwa pa lonjezo lolimba ndi chiyembekezo​—chija cha kuukitsidwa kwa akufa.

Yesu ndi Paulo​—Otonthoza Achifundo

7. Kodi Paulo anali wotonthoza motani kwa abale ake Achikristu?

7 Ha, Paulo anali chitsanzo chabwino chotani nanga cha kupereka chitonthozo! Iye analembera abale ku Tesalonika kuti: “Tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha; kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si uthenga wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife. Monga mudziŵa kuti tinachitira yense wa inu payekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni.” Mofananadi ndi makolo achikondi ndi osamala, tonsefe tingasonyeze chikondi chathu ndi chifundo kwa ena panthaŵi ya kusoŵa kwawo.​—1 Atesalonika 2:7, 8, 11.

8. Kodi nchifukwa ninji chiphunzitso cha Yesu chili chitonthozo kwa olira?

8 Posonyeza chisamaliro chotero ndi kukoma mtima, Paulo ankangotsanzira Wompatsa Chitsanzo wamkulu, Yesu. Kumbukirani chiitano chachifundo chimene Yesu anapereka kwa onse cholembedwa pa Mateyu 11:28-30: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” Inde, chiphunzitso cha Yesu nchopatsa mpumulo chifukwa chakuti chimapereka chiyembekezo ndi lonjezo​—lonjezo la chiukiriro. Ichi ndicho chiyembekezo ndi lonjezo zimene timapereka kwa anthu, mwachitsanzo, pamene tiwasiira brosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Chiyembekezo chimenechi chingatithandize tonsefe, ngakhale ngati takhala tikulira kwanthaŵi yaitali.

Mmene Tingatonthozere Olira

9. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukhala osaleza mtima ndi anthu olira?

9 Chisoni chilibe nyengo yoikika imene chimatherapo mwamsanga pambuyo pa imfa ya wokondedwa. Anthu ena amasenzabe mtolo wa chisoni chawo kwa moyo wawo wonse, makamaka aja ofedwa ana. Akristu ena aŵiri okhulupirika okwatirana ku Spain anafedwa mwana wawo wamwamuna wazaka 11 mu 1963 amene anadwala meningitis. Kufikira lerolino, iwo amagwetsabe misozi pamene alankhula za Paquito. Madeti apachaka, zithunzithunzi, zikumbutso, zingakumbutse zachisoni. Chifukwa chake, sitiyenera kukhala osaleza mtima ndi kuganiza kuti chisoni cha ena chatha tsopano. Buku lina la zamankhwala likuvomereza kuti: “Kusinthasintha kwa maganizo opsinjika kungapitirizebe kwa zaka zingapo.” Motero, kumbukirani kuti monga momwe zipsera zachilonda pathupi zingakhalire nafe kwa moyo wonse, momwemonso zipsera zambiri zamalingaliro.

10. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tithandize olira?

10 Kodi ndi zinthu zina ziti zothandiza zimene tingachite kuti titonthoze olira mumpingo Wachikristu? Tinganene moona mtima kwa mbale kapena mlongo wofunikira chitonthozo kuti, “Ngati pali chilichonse chimene ndingachite kukuthandizani, tangondiuzani.” Koma kodi ndikangati pamene munthu wofedwa amatiitana ndi kunena kuti, “Ndalingalira chinthu china chimene mungachite kundithandiza”? Mwachionekere, ife tiyenera kuyamba kuchitapo kanthu moyenera ngati titi titonthoze wofedwa. Chotero, kodi tingachitenji mwa njira yothandiza? Nawa malingaliro angapo ogwira ntchito.

11. Kodi ndimotani mmene kumvetsera kwathu kungakhalire chitonthozo kwa ena?

11 Mvetserani: Chimodzi cha zinthu zothandiza kwambiri chimene mungachite ndicho kugaŵana chisoni cha wofedwayo mwa kumvetsera. Mungafunse kuti, “Kodi mungalole kulankhula za imfayo?” Lolani munthuyo anene zimene afuna. Mkristu wina akukumbukira pamene atate wake anamwalira: “Zinandithandiza kwambiri pamene ena anafunsa zimene zinachitika ndiyeno ndi kumvetsera mosamalitsa.” Monga momwe Yakobo analangizira, fulumirani kumva. (Yakobo 1:19) Mvetserani moleza mtima ndi mwachifundo. “Lirani nawo akulira,” likulangiza motero Baibulo pa Aroma 12:15. Kumbukirani kuti Yesu analira ndi Marita ndi Mariya.​—Yohane 11:35.

12. Kodi ndi chilimbikitso chotani chimene tingapereke kwa olira?

12 Perekani chitsimikiziro: Kumbukirani kuti munthu wofedwa poyamba angamve kukhala waliwongo, akumalingalira kuti mwinamwake pali zinanso zimene akanachita. Mtsimikiziritseni munthuyo kuti anachita zonse zimene anakhoza (kapena zina zilizonse zimene mudziŵa kukhala zoona ndi zabwino). Mtsimikiziritseni kuti mmene akumveramo sikwachilendo. Muuzeni za ena amene mudziŵa omwe achira bwino lomwe pa kutayikidwa kofananako. M’mawu ena, khalani wozindikira ndi wachifundo. Chithandizo chathu chokoma mtima chingachite zochuluka! Solomo analemba kuti: “Mawu oyenera a panthaŵi yake akunga zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.”​—Miyambo 16:24; 25:11; 1 Atesalonika 5:11, 14.

13. Kodi kukhala kwathu opezeka kungathandize motani?

13 Khalani wopezeka: Khalani wopezeka osati kwa masiku oŵerengeka chabe pamene mabwenzi ambiri ndi achibale akalipo koma kwa miyezi ingapo pambuyo pake ngati kuli kofunika, pamene ena atabwerera ku moyo wawo wa masiku onse. Nyengo yolira ingasiyane kwambiri, zikumadalira pa munthuyo. Chisamaliro chathu Chachikristu ndi chifundo zingathandize kwambiri panthaŵi iliyonse ya kusoŵa. Baibulo limanena kuti “lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.” Nchifukwa chake mawu akuti, “Bwenzi pakusoŵa ndilo bwenzi lenileni,” ali oona amene tiyenera kuwagwiritsira ntchito.​—Miyambo 18:24; yerekezerani ndi Machitidwe 28:15.

14. Kodi tingalankhule za chiyani kuti titonthoze ofedwa?

14 Lankhulani za mikhalidwe yabwino ya munthu wakufayo: Chimenechi chimakhala chithandizo china chachikulu pamene chiperekedwa panthaŵi yoyenera. Kambitsiranani za zochitika zosangalatsa zimene mukukumbukira ponena za munthuyo. Musawope kutchula dzina la munthuyo. Musachite monga ngati kuti wotayikayo sanakhaleko kapena sanali munthu. Kuli kotonthoza kudziŵa zimene buku lina la ku Harvard Medical School linanena: “Kuchira kwinakwake kumakhalapo pamene wofedwayo akhala wokhoza kulingalira za wakufayo popanda chisoni chopambanitsa . . . Pamene mkhalidwe watsopano uvomerezedwa ndi kulandiridwa, chisoni chimazimiririka ndi kukhala zikumbukiro zabwino.” “Zikumbukiro zabwino”​—ndi kotonthoza chotani nanga kukumbukira nthaŵi zosangalatsa zimenezo zimene munali pamodzi ndi wokondedwa! Mboni ina imene inafedwa atate wake zaka zingapo zapita inati: “Chinthu chabwino kwambiri chimene ndimakumbukira ndicho kuŵerenga Baibulo pamodzi ndi Atate atangoyamba kumene kuphunzira choonadi. Ndiponso pamene tinkagona m’mphepete mwa mtsinje tikumakambitsirana za mavuto anga ena. Ndinkangoonana nawo pambuyo pa zaka zitatu kapena zinayi, motero nthaŵi zimenezo zinali zapadera kwambiri.”

15. Kodi ndimotani mmene munthu angayambire iye mwini kuchitapo kanthu kuti athandize?

15 Yambani Ndinu kuchitapo kanthu pamene kuli koyenera: Anthu ena olira angathe kupirira bwinopo kuposa ena. Motero, malinga ndi mkhalidwe, chitanipo kanthu kuti muthandize. Mkristu wachikazi wina wolira anakumbukira kuti: “Ambiri anati, ‘Ngati pali chilichonse chimene ndingachite, ndiuzeni.’ Koma mlongo wina Wachikristu sanafunse. Iye anangoloŵa m’chipinda, anayalula bedi, ndi kukachapa zofunda zoipitsidwazo. Wina anatenga bekete, madzi, ndi zotsukira natsuka kapeti imene mwamuna wanga anasanzirapo. Aŵa anali mabwenzi enieni, ndipo sindidzawaiŵala konse.” Ngati paonekeratu kukhala pofunika kuthandiza, yambani ndinu kuchitapo kanthu​—mwinamwake mwa kukonza chakudya, kuthandiza kuyeretsa, kapena kutumikira ntchito zina. Ndithudi, tiyenera kukhala osamala kusasokoneza pamene munthu wofedwa akufuna kukhala yekha. Chifukwa chake, tiyenera kugwiritsira ntchito mawu a Paulo akuti: “Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.” Kukoma mtima, kuleza mtima, ndi chikondi sizimalephera.​—Akolose 3:12; 1 Akorinto 13:4-8.

16. Kodi nchifukwa ninji kalata kapena khadi ingapereke chitonthozo?

16 Lembani kalata kapena tumizani khadi lotonthoza: Chimene chimanyalanyazidwa kaŵirikaŵiri ndicho phindu la kalata yotonthoza maliro kapena khadi yachisoni yokongola. Kodi imathandizanji? Iyo ingaŵerengedwe mobwerezabwereza. Kalata yoteroyo siifunikira kukhala yaitali, koma iyenera kusonyeza chifundo chanu. Iyeneranso kusonyeza mawu auzimu koma osati ulaliki. Uthenga wokha wakuti “Tili nanu” ungakhale chitonthozo.

17. Kodi pemphero lingapereke motani chitonthozo?

17 Pempherani nawo: Musachepetse phindu la mapemphero anu opempherera pamodzi ndi Akristu anzanu ofedwa ndi aja owapempherera. Baibulo pa Yakobo 5:16 limati: “Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu.” Mwachitsanzo, pamene olira atimva tikuwapempherera, kumawathandiza kuchotsa malingaliro ovutitsa maganizo monga liwongo. Panthaŵi zimene tikhala ofooka, olefulidwa, Satana amayesa kutifooketsa ndi “machenjerero” ake, kapena “machitidwe onyenga.” Apa mpamene timafunikira chitonthozo ndi chichilikizo cha pemphero, monga momwe Paulo ananenera kuti: ‘Mwa mtundu uliwonse wa pemphero ndi pembedzero musaleke kupemphera pachochitika chilichonse mumzimu. Ndipo pamlingo umenewo khalani maso nthaŵi zonse limodzi ndi kupembedzera oyera mtima onse.’​—Aefeso 6:11, 18, Kingdom Interlinear; yerekezerani ndi Yakobo 5:13-15.

Zimene Tiyenera Kupeŵa

18, 19. Kodi tingasonyeze motani kusamala m’makambitsirano athu?

18 Pamene munthu alira, palinso zinthu zimene sitiyenera kuchita kapena kunena. Miyambo 12:18 imachenjeza kuti: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.” Nthaŵi zina, popanda kuzindikira, timalephera kukhala ochenjera. Mwachitsanzo, tinganene kuti, “Ndikudziŵa mmene mukumvera.” Koma kodi zimenezo nzoona? Kodi inakuchitikiranipo imfa imodzimodziyo? Ndiyenonso, anthu amakhudzidwa mosiyanasiyana. Mwina kukhudzidwa kwanu kunali kosiyana ndi kwa munthu wolirayo. Kungakhale kusonyeza kusamala kunena kuti, “Ndikukuchitiranidi chifundo chifukwa chakuti inenso inandichitikira imfa yofananayi pamene . . . wanga anamwalira kale.”

19 Kungakhalenso kusonyeza kusamala kupeŵa kulankhula zakuti kaya wakufayo adzaukitsidwa kapena iyayi. Abale ena ndi alongo akhumudwa kwambiri ndi ndemanga zoweruza ponena za zothekera za mtsogolo mwa mnzawo wa muukwati wakufa wosakhulupirira. Ife sitili oweruza pa amene adzaukitsidwa ndi amene sadzaukitsidwa. Tingatonthozedwe podziŵa kuti Yehova, amene amaona mtima, adzakhala wachifundo kwambiri kuposa mmene ochuluka a ife tingakhalire.​—Salmo 86:15; Luka 6:35-37.

Malemba Amene Amatonthoza

20, 21. Kodi ndi malemba ena ati amene angatonthoze ofedwa?

20 Chimodzi cha zinthu zopatsa chitonthozo chachikulu pa imfa, ngati chiperekedwa panthaŵi yoyenera, ndicho kukambitsirana za malonjezo a Yehova ponena za akufa. Malingaliro a Baibulo otsatirawa adzakhala othandiza kaya ngati munthu wofedwayo ali kale Mboni kapena ngati ali munthu amene tikumana naye mu utumiki. Kodi ena a malemba ameneŵa ndi ati? Timadziŵa kuti Yehova ali Mulungu wa chitonthozo chonse, pakuti iye anati: “Ine, inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako.” Iye anatinso: “Monga munthu amene amake amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu.”​—Yesaya 51:12; 66:13.

21 Wamasalmo analemba kuti: “Chitonthozo changa m’kuzunzika kwanga ndi ichi; pakuti mawu anu anandipatsa moyo. Ndinakumbukira maweruzo anu kuyambira kale, Yehova, ndipo ndinadzitonthoza. Chifundo chanu chikhaletu chakunditonthoza, ndikupemphani, monga mwa mawu anu kwa mtumiki wanu.” Onani kuti liwulo lakuti “chitonthozo” likutchulidwa mobwerezabwereza m’ndime zimenezo. Inde, tikhoza kupeza chitonthozo chenicheni kwa ife eni ndi kwa ena mwa kutembenukira ku Mawu a Yehova m’nthaŵi ya nsautso yathu. Zimenezi, kuphatikizapo chikondi cha abale athu, zingatithandize kupirira kutayikidwa kwathu ndi kudzazanso miyoyo yathu ndi ntchito zokondweretsa mu utumiki Wachikristu.​—Salmo 119:50, 52, 76.

22. Kodi patsogolo pathu pali chiyembekezo chotani?

22 Tingachepetsenso chisoni chathu mwa kukhala otanganitsidwa ndi kuthandiza ena m’nsautso yawo. Pamene tipereka chisamaliro chathu kwa ena ofunikira chitonthozo, ifenso timapeza chimwemwe chenicheni cha kupatsa m’lingaliro lauzimu. (Machitidwe 20:35) Tiyeni tikambitsirane nawo za chiyembekezo cha tsiku la chiukiriro pamene anthu a mitundu yonse yakale, mibadwo ndi mibadwo, adzakhala akulandira okondedwa awo kuchokera kwa akufa kubwera m’dziko latsopano. Ha, ndi chiyembekezo chabwino chotani nanga! Ndi misozi ya chisangalalo chotani nanga imene idzakhetsedwa panthaŵiyo pamene tikumbukira kuti Yehova alidi Mulungu “amene atonthoza ogona pansi”!​—2 Akorinto 7:6, NW.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi Yehova ali motani “Mulungu wa chitonthozo chonse”?

◻ Kodi Yesu ndi Paulo anatonthoza motani olira?

◻ Kodi ndi zinthu zina ziti zimene tingachite kuti titonthoze olira?

◻ Kodi tiyenera kupeŵanji pochita ndi olira?

◻ Kodi ndi malemba opatsa chitonthozo ati amene mumakonda panthaŵi ya imfa?

[Chithunzi patsamba 15]

Yambani ndinu kuchitapo kanthu mosamala kuti muthandize olira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena