Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 7/1 tsamba 26-29
  • Wokhala Ndekha Koma Wosasiyidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Wokhala Ndekha Koma Wosasiyidwa
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kudziŵa za Choonadi cha Baibulo Koyamba
  • Tsopano Wokhaladi Ndekha
  • Kuonana ndi Gulu
  • Msonkhano Ndipo, Potsirizira Pake, Ubatizo
  • Kubwerera ku Mount Gambier
  • Magawo Atsopano
  • Utumiki Wanthaŵi Yonse Wopitirizabe
  • Ndadalitsidwa Moyo Wanga Wonse Chifukwa Chosankha Bwino Zochita
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Ndinapeza Chuma Chamtengo Wopambana
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Moyo Wanga m’Gulu Lotsogozedwa ndi Mzimu la Yehova
    Nsanja ya Olonda—1988
Nsanja ya Olonda—1995
w95 7/1 tsamba 26-29

Wokhala Ndekha Koma Wosasiyidwa

YOSIMBIDWA NDI ADA LEWIS

Ndakhala wokonda kukhala ndekha nthaŵi zonse. Ndinenso wakhama kwambiri​—ena nthaŵi zina amaganiza kuti ndi kuuma khosi​—pa zonse zimene ndimachita. Ndimathanso kukhala wosabisa zinthu polankhula, ndipo mkhalidwe umenewu wandidzetsera mavuto kwa zaka zambiri.

KOMABE, ndikuthokoza kuti Yehova Mulungu sanandinyanyale chifukwa cha zifooko zanga za umunthu. Mwa kuphunzira Mawu ake, ndakhoza kusintha umunthu wanga ndipo motero ndatumikira pa zinthu za Ufumu wake kwa zaka pafupifupi 60. Kuyambira paubwana, ndimakonda akavalo, ndipo thandizo la Mulungu polamulira khalidwe langa longa louma khosilo kaŵirikaŵiri landikumbutsa za mmene chapakamwa chingagwiritsidwire ntchito kulamulilira kavalo.

Ndinabadwira pafupi ndi nyanja ina yokongola ku Mount Gambier ku South Australia mu 1908. Makolo anga anali ndi famu ya ng’ombe zamkaka, ndipo ndinali mwana wawo wamkazi wamkulu pa ana asanu ndi atatu. Atate wathu anamwalira pamene tonsefe tinali achichepere kwambiri. Zimenezo zinandisiyira thayo lalikulu la kuyang’anira famuyo, popeza kuti alongo anga aŵiri aakulu anali kugwira ntchito kutali ndi kwathu kuti apezere ndalama banjalo. Moyo wa pa famu unali wotanganitsa kwambiri, wofuna kugwira ntchito zolimba.

Kudziŵa za Choonadi cha Baibulo Koyamba

Banja lathu linali kuloŵa Tchalitchi cha Presbyterian, ndipo tinali ziŵalo zosaphonya kutchalitchi. Ndinakhala mphunzitsi wa Sande sukulu ndi kuona mwamphamvu ntchito yophunzitsa ana zimene ndinakhulupirira kukhala zinthu zauzimu ndi zamakhalidwe abwino.

Mu 1931 agogo anga aamuna anamwalira, ndipo pakati pa zinthu zawo panali mabuku angapo olembedwa ndi yemwe panthaŵiyo anali pulezidenti wa Watch Tower Society, J. F. Rutherford. Ndiyanamba kuŵerenga Zeze wa Mulungu ndi Creation, ndipo pamene ndinaŵerenga zambiri, mpamenenso ndinadabwa kwambiri kudziŵa kuti zinthu zambiri zimene ndinali kukhulupirira ndi zimene ndinali kuphunzitsa ana zinali zosachirikizidwa ndi Baibulo.

Ndinadabwa kwambiri kudziŵa kuti moyo wa munthu ukhoza kufa, kuti anthu ochuluka samapita kumwamba pamene amwalira, ndi kuti kulibe chizunzo chamuyaya cha anthu oipa mu moto wa helo. Ndinazunguzikanso mutu kupeza kuti kusunga sabata la pa Sande la mlungu ndi mlungu sikuli chinthu chofunika kwa Akristu. Chotero ndinafunikira kupanga chosankha chachikulu: kumamatira ku ziphunzitso zamwambo za Dziko Lachikristu kapena kuyamba kuphunzitsa choonadi cha Baibulo. Sizinanditengere nthaŵi yaitali kuti ndisankhe kuleka mayanjano anga ndi Tchalitchi cha Presbyterian.

Tsopano Wokhaladi Ndekha

Banja langa, mabwenzi, ndi omwe kale anali anzanga akutchalitchi sanakondwere mpang’ono pomwe pamene ndinadziŵikitsa cholinga changa cha kusiya tchalitchi ndi kusaphunzitsanso Sande sukulu. Ndipo pamene anadziŵa kuti ndinali kugwirizana ndi amene ankatchedwa kuti anthu a Judge Rutherford, zimenezo zinangowonjezeranso moto pa miseche yaikulu. Kuti ndinene zoona, si kuti ndinanyanyalidwa kwenikweni, koma ochuluka a m’banja langa ndi omwe kale anali mabwenzi anga anali opanda ubwenzi kwenikweni kwa ine.

Pamene ndinaphunzira zambiri ndi kupenda malemba oikidwa m’mabuku amene ndinali kuŵerenga, mpamenenso ndinayamba kuona kwambiri kufunika kwa kulalikira poyera. Ndinaphunzira kuti Mboni za Yehova zimamka kunyumba ndi nyumba monga mbali ya utumiki wawo wapoyera. Komano panthaŵiyo m’chigawo chathu munalibe Mboni. Chotero, panalibe amene anandilimbikitsa kapena kundisonyeza mmene munthu angalalikirire uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Ndinamvadi kukhala ndili ndekhandekha.

Komabe, lamulo la Baibulo la kulalikira kwa ena ndinali kulikumbukirabe, ndipo ndinalingalirabe kuti ndiyenera kuyamba kulalikira. Nditapemphera kwambiri, ndinaganiza za kuyamba kufikira nyumba za anansi anga kungoti ndiwauze zimene ndinadziŵa m’kuphunzira kwanga ndi kuyesa kuwasonyeza zinthu zimenezi m’ma Baibulo a iwo eni. Nyumba yanga yoyamba inali ya amene papitapo anali woyang’anira wanga wa Sande sukulu. Mchitidwe wake wonyalanyaza ndi ndemanga zake zonena za kusiya kwanga tchalitchi sizinalidi chiyambi changa chabwino. Koma ndinamva nyonga ina yachilendo mkati mwanga pamene ndinachoka panyumba pake ndi kupitiriza kufikira nyumba zina.

Panalibe chitsutso chachindunji chenicheni, koma ndinadabwa ndi kunyalanyazidwa ndi anthu ochuluka amene papitapo anali anzanga atchalitchi pamene ndinawafikira. Ndinadabwa mogwiritsidwa mwala, pamene ndinatsutsidwa mwamphamvu ndi mlongo wanga wamkulu, zikumandikumbutsa za mawu a Yesu akuti: “Mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a fuko lanu, ndi abwenzi anu; . . . Ndipo anthu onse adzadana ndi inu chifukwa cha dzina langa.”​—Luka 21:16, 17.

Ndinadziŵa kukwera kavalo pausinkhu waung’ono kwambiri, chotero ndinalingalira kuti njira yofulumira yofikira nyumba za anthu ikakhala ya kuyenda pa kavalo. Zimenezi zinandikhozetsa kumka kumalo akutali a dera la kumidzilo. Komabe, masana ena kavalo wangayo anaphunthwa ndi kugwa mu msewu woterera, ndipo ndinavulala kwambiri m’mutu. Anthu anawopa kwakanthaŵi kuti mwina ndidzafa. Pambuyo pa kugwa kumeneko, ngati msewu unali woterera, ndinkayenda pa ngolo ya magudumu aŵiri yokokedwa ndi kavalo m’malo mwa kukwera pakavalo.

Kuonana ndi Gulu

Panthaŵi ina ngozi yanga itachitika, kagulu kena ka alaliki anthaŵi yonse, tsopano kotchedwa kuti apainiya, kanafika ku chigawo cha Mount Gambier. Chotero, kwa nthaŵi yoyamba, ndinakhoza kulankhula mwachindunji ndi okhulupirira anzanga. Asanachoke, anandilimbikitsa kulembera kalata ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ndi kufunsa za mmene ndingakhalire ndi phande m’ntchito ya kulalikira poyera molongosoka kwambiri.

Nditalembera Sosaite, ndinalandira mabuku, timabuku, ndi makhadi aulaliki ogwiritsira ntchito podzidziŵikitsa pamakomo. Ndinaona kukhala ndili woyandikiranako ndi abale ndi alongo anga auzimu chifukwa cha kulemberana makalata ndi ofesi ya nthambi. Koma pamene kagulu ka apainiyako kanasamukira ku tauni ina yotsatira, ndinakhala wosukidwa kwambiri kuposa kale.

Monga chotulukapo cha chizoloŵezi cha kuchitira umboni kwanga tsiku lililonse​—makamaka ndi ngolo yokokedwa ndi kavalo​—ndinadziŵika kwambiri m’deralo. Panthaŵi imodzimodziyo, ndinkakhoza kugwira ntchito ya pafamu. Pamenepo nkuti banja langa litaleka kunditsutsa ndipo silinayesenso kundidodometsa. Kwa zaka zinayi ndinatumikira motero monga wolengeza uthenga wabwino wakutali, wosabatizidwa.

Msonkhano Ndipo, Potsirizira Pake, Ubatizo

Mu April 1938, Mbale Rutherford anachezera Australia. Chitsutso champhamvu cha atsogoleri achipembedzo chinachititsa kuletsedwa kwa pangano la kugwiritsira ntchito Sydney Town Hall. Komabe, pamapeto penipeni, panapezedwa chilolezo cha kukagwiritsira ntchito Sports Grounds. Kwenikweni kusintha makonzedwe koumirizako kunakhaladi kwaphindu, popeza kuti anthu zikwi zambiri anakwanira kuloŵa mu Sports Grounds yaikuluyo. Panadza anthu pafupifupi 12,000, mwachionekere ambiri anakopedwa ndi kutsutsa msonkhano wathu kosonkhezeredwa ndi atsogoleri achipembedzoko.

Ulendo wa Mbale Rutherford unagwirizanitsidwa ndi msonkhano wa masiku angapo umenenso unachitidwa mu mlanga wina wapafupi wa m’Sydney. Kunali kumeneko kumene potsirizira pake ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu ndi ubatizo wa m’madzi. Kodi mungalingalire mmene chimwemwe changa chinalili potsirizira pake pamene ndinasonkhana ndi abale ndi alongo ochokera mu kontinenti yonse yaikuluyi ya Australia?

Kubwerera ku Mount Gambier

Pamene ndinabwerera kwathu, ndinasukidwa kwambiri, komabe ndinali wotsimikiza kwambiri kuposa kale kuchita zonse zimene ndikatha mu ntchito ya Ufumu. Posapita nthaŵi ndinadziŵana ndi banja la a Agnew​—Hugh, ndi mkazi wake, ndi ana awo anayi. Anali kukhala m’tauni ya Millicent, makilomita 50 okha kuchokera ku Mount Gambier, ndipo ndinkayenda ulendo wa makilomita 50 kupita ndiponso chimodzimodzi kubwerera pa ngolo yokokedwa ndi kavalo kukachita nawo phunziro la Baibulo la nthaŵi zonse. Pamene analandira choonadi, kusukidwa kwangako kunachepa.

Posakhalitsa, tinalinganizidwa kukhala kagulu kochitira umboni. Ndiyeno, mosangalatsa, mayi wanga anayamba kukondwerera ndipo ankatsagana nane pa ulendo wa makilomita 100 umenewo kupita ndi kubwera kukaphunzira ndi kagulu kolinganizidwa chatsopano kumeneko. Kuyambira pamenepo, nthaŵi zonse Amayi anali olimbikitsa ndi othandiza, ngakhale kuti panapita zaka zingapo asanabatizidwe. Tsopano sindinali wosukidwanso!

Kagulu kathu kakang’onoko kanatulutsa apainiya anayi, atsikana atatu a m’banja la a Agnew​—Crystal, Estelle, ndi Betty​—ndi ineyo. Pambuyo pake, kuchiyambi kwa ma 1950, atsikana atatu onsewo anakaloŵa Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. Iwo anatumizidwa ku India ndi Sri Lanka monga amishonale, kumene akutumikirabe mokhulupirika.

Mu January 1941 ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa mu Australia, chotero tinachitapo kanthu mwamsanga. Tinaika zinthu zonse zimene tinali kugwiritsira ntchito mu utumiki​—mabuku, galamalafoni yaing’ono, malekodi a nkhani za Baibulo, ndi zina zotero​—m’bokosi lachitsulo lalikulu. Ndiyeno tinaika bokosilo m’chipinda chosungiramo zinthu ndi kuunjikamo udzu wouma kuti ulikwirire.

Ngakhale kuti panali chiletso, tinapitiriza ntchito yathu ya kulalikira kunyumba ndi nyumba, komano mosamala, tikumagwiritsira ntchito Baibulo lokha polankhula kwa eni nyumba. Ndinkabisa magazini ndi timabuku pansi pa chokhalira cha pa kavalo wanga ndi kuwatulutsa kokha pamene ndinapeza munthu wofunitsitsadi kumvetsera uthenga wa Ufumu. Potsirizira pake, mu June 1943, chiletsocho chinachotsedwa, ndipo kachiŵirinso tinali okhoza kugaŵira mabuku poyera.

Magawo Atsopano

Mu 1943, ndinakhala mpainiya, ndipo chaka chotsatira ndinachoka ku Mount Gambier kumka ku gawo lina. Choyamba, ndinapemphedwa kukatumikira kwakanthaŵi ku ofesi ya nthambi ya Sosaite ku Strathfield. Pambuyo pake, ndinalandiranso magawo ku matauni ena aang’ono kummwera kwa New South Wales ndi kumadzulo kwa Victoria. Komabe, limodzi la magawo anga ofupa koposa linali la ku mpingo wina waukulu wa mu mzinda wa Melbourne. Pokhala wochokera ku tauni yaing’ono yakutali, ndinaphunzira zambiri pamene ndinali kutumikira kumeneko.

M’gawo langa kumunsi kwa Gippsland chigawo cha Victoria, ine ndi mnzanga wochita naye upainiya, Helen Crawford, tinachititsa maphunziro ambiri a Baibulo, ndipo m’nyengo yaifupi, tinaona mpingo ukupangidwa. Chigawo chimenecho chinali ndi dera lalikulu la midzi, ndipo tinali ndi galimoto lakale losadalirika loyendera. Nthaŵi zina tinkayenda pa galimotolo, koma nthaŵi zambiri tinali kulikankha. Ha, mmene ndinalakalakira kavalo nanga! Nthaŵi zina, ndinkanenetsa kuti: “Ndikhoza kupatsa munthu chilichonse (kusiyapo Ufumu) ngati andipatsa kavalo!” Lerolino m’matauni ambiri a chigawo chimenecho, muli mipingo yolimba ndi Nyumba Zaufumu zabwino kwambiri.

Mu 1969, ndinalandira gawo lina ku Canberra, likulu la Australia. Ameneŵa anali malo ochitiramo umboni opereka chitokoso ndi a zochitika zosiyanasiyana, popeza kuti kaŵirikaŵiri tinkafikira ogwira ntchito m’malo ambiri a akazembe oimira maiko akwawo. Ndidakatumikirabe konkuno, koma m’zaka zaposachedwapa ndachitira umboni wanga mwapadera kudera la kumaindasitale la mzindawu.

Mu 1973, ndinali ndi mwaŵi wa kukaloŵa msonkhano waukulu ku United States. Chochitika china chosaiŵalika m’moyo wanga chinali cha kukhala nthumwi ya msonkhano mu 1979 ndi kukaona malo ku Israel ndi Jordan. Kufika kumalo enieniwo otchulidwa m’Baibulo ndi kusinkhasinkha pa zochitika zimene zinachitika kumeneko kunalidi chinthu chochititsa chidwi. Ndinali wokhoza kumva mmene kuyandama pa Dead Sea kulili, nyanja ya madzi okhuthala ndi mchere, ndipo mkati mwa ulendo wathu wa ku Petra mu Jordan, kachiŵirinso ndinali ndi mwaŵi wa kukwera kavalo. Zimenezi zinandikumbutsa za masiku akale pamene akavalo anandikhozetsa kufika kumadera otalikirana akumidzi ndi uthenga wa Ufumu.

Utumiki Wanthaŵi Yonse Wopitirizabe

Chikhumbo changa cha kupitirizabe mu utumiki wanthaŵi yonse ngakhale kuti ndili wokalamba chandisunga mwa njira ya makonzedwe onga Sukulu ya Utumiki wa Upaniya ndi misonkhano ya apainiya yochitidwa mogwirizana ndi misonkhano yadera, ndiponso chilimbikitso chosalekeza chimene ndimalandira kwa oyang’anira oyendayenda. Ndinganenedi kuti Yehova wandilinganizira zinthu kotero kuti masiku anga a kusukidwa ali chinthu chakale.

Tsopano ndili ndi zaka 87, ndipo pambuyo pa zaka pafupifupi 60 za kutumikira Yehova, ndikufuna kulimbikitsa ena amene angakhalenso osabisa zinthu polankhula ndi odziimira kwambiri kuti: Gonjerani zitsogozo za Yehova nthaŵi zonse. Yehova atithandizetu kulamulira mkhalidwe wathu wosabisa zinthu polankhula, ndipo nthaŵi zonse atikumbutsetu kuti ngakhale mwina tingakhale osukidwa, sadzatisiya konse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena