Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 7/15 tsamba 4-7
  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Munthu Weniweni Wotsutsana ndi Mulungu
  • Chifukwa Chake Satana Waloledwa Kulamulira
  • Nthaŵi ya Satana Njaifupi!
  • Kukondwera Pansi pa Ulamuliro wa Ufumuwo
  • Mdani wa Moyo Wosatha
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Satana Mdyerekezi
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Satana
    Galamukani!—2013
  • Khalani Maso Satana Akufuna Kukumezani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 7/15 tsamba 4-7

Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu

KODI ndani amalamulira dziko? Kodi pali munthu wina wauzimu amene amayang’anira? Kapena kodi Mulungu wangoleka anthu kuti adzionere okha? Pofunafuna mayankho a mafunso ameneŵa, choyamba tiyeni tilingalire za chochitika china chimene chinachitika mu utumiki wa pa dziko lapansi wa Yesu Kristu.

Atangobatizidwa, Yesu anayesedwa ndi cholengedwa chauzimu chosaoneka chotchedwa Satana Mdyerekezi. Posonyeza amodzi amayesowo, Baibulo limati: “Mdyerekezi anamuka [ndi Yesu] ku phiri lalitali, namuonetsa maiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo.” (Mateyu 4:8) Ndiyeno Satana anauza Yesu: “Ndidzapatsa inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wawo: chifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna. Chifukwa chake ngati inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu.”​—Luka 4:6, 7.

Satana ananena kuti anali ndi ulamuliro pa maufumu onse, kapena maboma, a dzikoli. Kodi Yesu anatsutsa mawuwo? Ayi. Iye kwenikweni anawavomereza panthaŵi ina mwa kutchula Satana kukhala “mkulu wa dziko lapansi.”​—Yohane 14:30.

Malinga ndi kunena kwa Baibulo, Satana ndi mngelo woipa wokhala ndi mphamvu yaikulu. Mtumwi Wachikristu Paulo amagwirizanitsa Satana ndi “magulu oipa amizimu” ndipo amalankhula za iwo monga “olamulira dziko a mdima uno.” (Aefeso 6:11, 12, NW) Ndiponso, mtumwi Yohane anati “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Buku la Baibulo la Chivumbulutso limati Satana ‘akunyenga dziko lonse.’ (Chivumbulutso 12:9) Mophiphiritsira, Chivumbulutso chimasonyezanso Satana kukhala chinjoka chimene chimapatsa magulu andale a dziko “mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.”​—Chivumbulutso 13:2.

Zochitika za dzikonso zimasonyeza kuti pali mphamvu ina yoipa imene ikugwira ntchito, ikumachititsa anthu kudzivulaza. Kodi chifukwa china nchiti chimene chimachititsa maboma a anthu kulephera kuchirikiza mtendere? Kodi nchiyaninso chimene chingachititse anthu kudana ndi kuphana? Atanyansidwa ndi kuphana ndi imfa mu nkhondo yachiŵeniŵeni, mboni ina yoona ndi maso inati: “Sindikumvetsetsa chifukwa chake zimenezi zinachitika. Si udani chabe. Ndi mizimu yoipa imene ikugwiritsira ntchito anthu ameneŵa kuwonongana.”

Munthu Weniweni Wotsutsana ndi Mulungu

Lerolino, ambiri samakhulupirira kuti kuli Satana Mdyerekezi. Komabe, iye sali chabe kuipa mwa anthu, monga momwe ena amakhulupirira. Baibulo ndi zochitika za dziko zomwe zimasonyeza kuti iye ndi munthu weniweni. Ndiponso, Satana ndi wotsutsana kotheratu ndi Yehova Mulungu. Zoonadi, Satana ali wosafanana ndi Mulungu. Popeza kuti Yehova ndi Mlengi wamphamvuyonse, iye ndiye Wolamulira woyenera pa chilengedwe chonse.​—Chivumbulutso 4:11.

Mulungu sanalenge cholengedwa choipa chomtsutsa. M’malo mwake, mmodzi wa ‘ana a Mulungu’ aungelo anakulitsa chikhumbo chadyera cha kufuna kulanda kulambira koyenera koperekedwa kwa Yehova. (Yobu 38:7; Yakobo 1:14, 15) Chikhumbo chimenechi chinamchititsa kutenga njira yopandukira Mulungu. Mwa kupanduka, cholengedwa chimenechi chauzimu chinadzipanga Satana (kutanthauza “wotsutsa”) ndi Mdyerekezi (kutanthauza “woneneza”). Polingalira zonsezi, inu mungadabwe kuti Satana waloledwa bwanji kulamulira dziko.

Chifukwa Chake Satana Waloledwa Kulamulira

Kodi mukukumbukira zimene Satana anauza Yesu ponena za ulamuliro wa pa dziko lonse lapansi? “Ndidzapatsa inu ulamuliro wonse umenewu . . . chifukwa unaperekedwa kwa ine,” anatero Satana. (Luka 4:6) Mawu amenewo akusonyeza kuti Satana Mdyerekezi amalamulira kokha chifukwa cha kuloledwa ndi Mulungu. Koma kodi nchifukwa ninji Mulungu amalekerera Satana?

Yankho la funso limenelo likukhudza zochitika za m’munda wa Edene, mmene Satana anayamba ntchito yake monga wolamulira wadziko. Mmenemo Satana ananena kuti Mulungu anali kulamulira m’njira yoipa mwa kumana kanthu kena kabwino mwamuna ndi mkazi oyambawo, Adamu ndi Hava. Malinga ndi kunena kwa Satana, ngati iwo akanadya chipatso choletsedwa ndi Mulungu, akanamasulidwa. Adamu ndi Hava akanakhala aufulu ndi osadalira Yehova. Akanakhala ngati Mulungu mwiniyo!​—Genesis 2:16, 17; 3:1-5.

Mwa kunama motere ndi kunyenga Hava ndipo kupyolera mwa iye kusonkhezera Adamu kuswa lamulo la Mulungu, Satana anachititsa anthu oyambawo kukhala pansi pa utsogoleri wake ndi ulamuliro. Motero Mdyerekezi anakhala mulungu wawo, wotsutsana ndi Yehova. Komabe, m’malo mwa chimasuko, Adamu ndi Hava anakhala akapolo a Satana, a uchimo, ndi a imfa.​—Aroma 6:16; Ahebri 2:14, 15.

Mogwirizana ndi chiweruzo chake changwiro, Yehova akanapha nthaŵi yomweyo Satana ndi omtsatira ake atsopano aŵiriwo. (Deuteronomo 32:4) Komabe, nkhani ya makhalidwe inaphatikizidwapo. Satana anabutsa zikayikiro ponena za kuyenera kwa njira ya kulamulira ya Yehova. Mwa nzeru yake, Mulungu analola kuti nthaŵi ipyole kotero kuti asonyeze kuti kudziimira kwa munthu popanda iye kumadzetsa tsoka. Yehova analola opandukawo kukhalabe ndi moyo kwa nthaŵi ina, akumalola Adamu ndi Hava kubala ana.​—Genesis 3:14-19.

Ngakhale kuti ana ambiri a Adamu sanagonjere ulamuliro wa Yehova, zochita za Mulungu ndi olambira Ake zasonyeza kupambana kwake. Kulemekeza ulamuliro wa Yehova kumadzetsa chimwemwe ndi chisungiko chenicheni. Komanso, nsautso ndi kusasungika zakhalapo chifukwa cha ulamuliro wa munthu pansi pa chisonkhezero cha Satana. Inde, “wina apweteka mnzake pomlamulira.” (Mlaliki 8:9) Anthu sanapeze chisungiko chenicheni ndi chimwemwe chokhalitsa mu ulamuliro wa munthu m’dziko lino logona mumphamvu ya Satana. Komabe, pali zifukwa zomveka zokhalira ndi chiyembekezo.

Nthaŵi ya Satana Njaifupi!

Chisonkhezero cha Satana pa dziko lapansi nchakanthaŵi. Yehova sadzalekerera ulamuliro wausatana kwa nthaŵi yaitali! Posachedwapa Mdyerekezi adzalandidwa mphamvu. Wolamulira watsopano adzayamba kulamulira dziko lapansi, mfumu yolungama yosankhidwa ndi Mulungu mwini. Mfumuyo ndiyo Yesu Kristu. Ponena za kuikidwa kwake pampando wachifumu kumwamba, Chivumbulutso chimati: “Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu [Yehova], ndi wa Kristu wake.” (Chivumbulutso 11:15) Kuŵerengera zaka kwa Baibulo, limodzi ndi kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Malemba, kumasonyeza kuti zimenezi zinachitika m’chaka cha 1914.​—Mateyu 24:3, 6, 7.

Baibulo limafotokozanso zimene zinachitika Yesu atangoikidwa kumene pampando wachifumu. Limati: “Munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli [Yesu Kristu] ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka [Satana Mdyerekezi]; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.”​—Chivumbulutso 12:7-9.

Kodi nchiyani chimene chinachitika pa kuthamangitsidwa kumwamba kwa Satana? Awo okhala kumwamba anakondwera, koma bwanji nanga za okhala pa dziko lapansi? “Tsoka mtunda ndi nyanja,” chimatero Chivumbulutso 12:12, “chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” Ndithudi, kuthamangitsidwa kwa Satana kumwamba kwadzetsa tsoka pa dziko lapansi. The Columbia History of the World imati: “Tsoka lalikulu la Nkhondo ya Zaka Zinayi ya 1914-1918 . . . linasonyeza maiko Akumadzulo kuti sangatetezere kutsungula pa kupusa kwake kapena pa chisonkhezero choipa. Maiko Akumadzulo sanapezebe mzimu umene anataya pa kusakazako.”

Masoka a mbadwo uno ali ndi zambiri, osati chabe mzimu wosweka. Yesu analosera kuti: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti.” Ananeneratunso za miliri. (Mateyu 24:7, 8; Luka 21:11) Ndiponso, Baibulo limanena kuti mu “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu la Satana, ambiri adzakhala “odzikonda okha, okonda ndalama, . . . osamvera akuwabala, . . . osayanjanitsika.” Anthu adzakhalanso “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.”​—2 Timoteo 3:1-5.

Nkhondo, miliri, njala, zivomezi, ndi kuipiraipira kwa makhalidwe​—zinthu zonsezo zachitika pamlingo wosayerekezeka ndi wina kuyambira 1914, monga momwedi Baibulo linaneneratu. Zimasonyeza kuti mdani wa Mulungu ndi wa anthu wokwiyayo​—Satana Mdyerekezi​—wathamangitsidwa kumwamba ndipo tsopano akusonyeza mkwiyo wake ku dziko lapansi. Koma Baibulo limasonyezanso kuti Satana sadzaloledwa kulamulira kwa nthaŵi yaitali. Iye wangotsala ndi “kanthaŵi” kufikira pa Armagedo, pamene Mulungu adzawononga dongosolo la dziko la Satana.

Nangano nchiyani chimene chidzachitika kwa Satana? Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndinaona mngelo anatsika kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake.” (Chivumbulutso 20:1-3) Ha, ndi mpumulo wabwino chotani nanga umenewo kwa anthu ovutika!

Kukondwera Pansi pa Ulamuliro wa Ufumuwo

Satana atachotsedwa, Ufumu wa Mulungu pansi pa Yesu Kristu udzalamulira anthu onse. M’malo mwa kukhala ndi maboma ambiri pa dziko lapansi, boma limodzi lokha lakumwamba lidzatsala kuti lilamulire pulaneti yonseyi. Nkhondo idzakhala chinthu chakale, ndipo mtendere udzakhala ponseponse. Pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, onse adzakhala pamodzi m’chikondi chapaubale.​—Salmo 72:7, 8; 133:1; Danieli 2:44.

Kodi Yesu adzakhala wolamulira wotani? Pamene anali pa dziko lapansi, anasonyeza chikondi chachikulu pa anthu. Yesu mwachifundo anapatsa chakudya anthu anjala. Anachiritsa odwala ndi kupenyetsa akhungu, kulankhulitsa osalankhula, ndi kuchiritsa opuwala ziŵalo. Yesu anaukitsadi akufa! (Mateyu 15:30-38; Marko 1:34; Luka 7:11-17) Zozizwitsa zimenezo zinali zitsanzo za zinthu zodabwitsa zimene ati adzachite monga Mfumu. Kudzakhala kwabwino kwambiri chotani nanga kukhala ndi wolamulira wabwino wotero!

Madalitso osatha adzalandiridwa ndi awo amene amagonjera ulamuliro wa Yehova. Malemba amalonjeza kuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzaimba.” (Yesaya 35:5, 6) Pofotokoza za tsiku labwino kwambiri lamtsogolo limenelo, mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndinamva mawu aakulu ochokera kumpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Zinthu zokondweretsa zoperekedwa ndi ulamuliro wa Yehova Mulungu kupyolera mwa Mwana wake, Yesu Kristu, zidzaposa mavuto alionse amene takumana nawo m’dongosolo limene lilipoli la zinthu lolamuliridwa ndi Satana Mdyerekezi. M’dziko latsopano la Mulungu lolonjezedwalo, anthu sadzafunsa modabwa kuti, ‘Kodi kwenikweni ndani amene akulamulira?’ (2 Petro 3:13) Anthu omvera adzakhala achimwemwe ndi osungika pa dziko lapansi mu ufumu wa Olamulira achikondi m’malo a mizimu, Yehova ndi Kristu. Bwanji nanga osalandira chiyembekezo cha kudzakhala pakati pa nzika zawo?

[Chithunzi patsamba 7]

Anthu adzakhala osungika pa dziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Chithunzithunzi cha NASA

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena