Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 9/1 tsamba 19-21
  • Kodi Mungakulitse Luntha Lowonjezereka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungakulitse Luntha Lowonjezereka?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusoŵa Luntha kwa Israyeli
  • Kupeza Luntha Lauzimu
  • Luntha ndi Chidziŵitso
  • Lozetsani Mtima Wanu ku Kuzindikira
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kuzindikira Kukuchinjirizeni
    Nsanja ya Olonda—1997
  • “Yehova Apatsa Nzeru”
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Khalani Olimba Mtima Ndiponso Ozindikira Ngati Yesu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 9/1 tsamba 19-21

Kodi Mungakulitse Luntha Lowonjezereka?

LUNTHA ndilo “mphamvu kapena luso limene maganizo amasiyanitsira chinthu china ndi chinzake.” Lingakhalenso “kulingalira kwatcheru” kapena “mphamvu ya kuona kusiyana kwa zinthu kapena malingaliro.” Nzimene imanena Webster’s Universal Dictionary. Mwachionekere, luntha ndi mkhalidwe wofunika kwambiri. Kufunika kwake kumaoneka m’mawu a Solomo akuti: “Pakuti nzeru idzaloŵa m’mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa, . . . [Luntha, NW] [li]dzakuchinjiriza; kukupulumutsa ku njira yoipa.”​—Miyambo 2:10-12.

Inde, luntha lidzatithandiza kukaniza “njira yoipa,” imene ili yowanda lerolino. Ndipo limadzetsanso mapindu ena ambiri. Mwachitsanzo, makolo kaŵirikaŵiri amamva ana awo akunena kuti, ‘Simukundimvetsa!’ Mwa kufunsitsa pang’ono, makolo aluntha amadziŵa mmene angachititsire ana awo kutulutsa zakukhosi ndi nkhani zimene zikuwavutitsa. (Miyambo 20:5) Mwamuna wa luntha amamvetsera kwa mkazi wake ndi kuzindikira zimene akulingalira ndi mmene akumvera m’malo mongogamula. Mkaziyo amachita chimodzimodzi kwa mwamuna wake. Mwakutero, “nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa.”​—Miyambo 24:3.

Luntha limathandiza munthu kukhoza kuchita ndi mikhalidwe. Miyambo 17:27 imati: “Wopanda chikamwakamwa apambana kudziŵa; ndipo wofatsa mtima ali [waluntha, NW].” Munthu waluntha sali waphuma, wofulumira kuloŵa m’nkhani iliyonse popanda kulingalira. Amasinkhasinkha mosamalitsa zimene zingachitike asanadziloŵetsemo. (Luka 14:28, 29) Amakhalanso pamtendere ndi ena chifukwa chakuti “kamwa lanzeru” limamchititsa kusankha mawu mosamalitsa. (Miyambo 10:19; 12:8, NW) Koma, chofunika koposa nchakuti, munthu waluntha amazindikira modzichepetsa kupereŵera kwake ndipo amafuna chitsogozo cha Mulungu osati cha munthu. Zimenezi zimakondweretsa Yehova ndipo ndicho chifukwa china chimene tiyenera kukulitsira luntha.​—Miyambo 2:1-9; Yakobo 4:6.

Kusoŵa Luntha kwa Israyeli

Chochitika cha kuchiyambi kwa mbiri ya Israyeli chimasonyeza ngozi ya kulephera kuchita mwaluntha. Ponena za panthaŵiyo, wamasalmo wouziridwa anati: “Makolo athu sanadziŵitsa zodabwiza zanu m’Aigupto; sanakumbukira zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.”​—Salmo 106:7.

Pamene Mose anatsogolera Israyeli kutuluka mu Aigupto, Yehova anali atasonyeza kale mphamvu yake ndi kutsimikiza mtima kwake kumasula anthu ake mwa kutsanulira milili khumi pa ulamuliro wadziko lonse wamphamvu umenewo. Farao atalola Aisrayeli kupita, Mose anawatsogolera kugombe la Nyanja Yofiira. Komabe, ankhondo a Aigupto anawalondola. Kunaoneka ngati kuti Aisrayeliwo anachingidwa ndi kuti amenewo ndiwo anali mathedwe a ufulu umene anangopeza kumene. Motero Baibulo limati: “Ana a Israyeli . . . anawopa kwambiri; . . . nafuulira kwa Yehova.” Ndipo anatembenukira Mose, nati: “Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa m’Aigupto? . . . Kutumikira Aaigupto kutikomera si kufa m’chipululu ayi.”​—Eksodo 14:10-12.

Mantha awo angaoneke kukhala ndi chifukwa chomveka kufikira titakumbukira kuti anali ataonapo kale zisonyezero khumi zapadera za mphamvu ya Yehova. Iwo anadziŵa bwino lomwe zimene Mose adzawakumbutsa pambuyo pa zaka 40: “Yehova anatitulutsa m’Aigupto ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi kuwopsa kwakukulu, ndi zizindikiro, ndi zodabwiza.” (Deuteronomo 26:8) Chifukwa chake, monga momwe wamasalmo analembera, pamene Aisrayeli anafulatira chitsogozo cha Mose, “sanadziŵitsa.” Komabe, Yehova, mogwirizana ndi lonjezo lake, anagonjetsa ankhondo a Aigupto kotheratu.​—Eksodo 14:19-31.

Chikhulupiriro chathu chingafooke mofananamo ngati tikayikira kapena kusakhala otsimikiza poyang’anizana ndi mayesero. Luntha lidzatithandiza kuona zinthu mwa lingaliro labwino nthaŵi zonse, tikumakumbukira kuti Yehova ali wamkulu kwambiri kuposa aliyense amene angatitsutse. Luntha lidzatithandizanso kukumbukira zimene Yehova watichitira kale. Lidzatithandiza kusaiŵala konse kuti iye ali Amene “asunga onse akukondana naye.”​—Salmo 145:18-20.

Kupeza Luntha Lauzimu

Luntha silimangofika ndi kukula kwa munthu. Tiyenera kulikulitsa. Mfumu yanzeru Solomo, imene inakhala yotchuka kwa mitundu yambiri chifukwa cha luntha lake, inati: “Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka.” (Miyambo 3:13, 14) Kodi Solomo anapeza kuti luntha lake? Kwa Yehova. Pamene Yehova anafunsa Solomo za dalitso limene anafuna, Solomo anayankha kuti: “Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa.” (1 Mafumu 3:9) Inde, Solomo anayang’ana kwa Yehova monga mthandizi wake. Anapempha luntha, ndipo Yehova anampatsa lalikulu. Chotulukapo chake? “Nzeru ya Solomo inaposa nzeru za anthu onse a Kummawa, ndi nzeru zonse za ku Aigupto.”​—1 Mafumu 4:30.

Chochitika cha Solomo chimatisonyeza kumene tingapite pamene tifuna luntha. Mofanana ndi Solomo, tiyenera kuyang’ana kwa Yehova. Motani? Chabwino, Yehova wapereka Mawu ake, Baibulo, amene amatipatsa chidziŵitso cha malingaliro ake. Pamene tiŵerenga Baibulo, timakhala tikukumba pamgodi wa chidziŵitso kuti tipeze miyala yomangira luntha lauzimu. Chidziŵitso chimene timasonkhanitsa mwa kuŵerenga Baibulo tiyenera kuchisinkhasinkha. Ndiyeno, tingachigwiritsire ntchito kupangira zosankha zoyenera. M’kupita kwa nthaŵi, mphamvu zathu za kulingalira zimakula kufikira titakhala ‘aakulu misinkhu m’chidziŵitso,’ okhoza “kusiyanitsa [kapena, kuzindikira] chabwino ndi choipa.”​—1 Akorinto 14:20; Ahebri 5:14; yerekezerani ndi 1 Akorinto 2:10.

Chokondweretsa nchakuti, tikhoza kupindulabe ndi luntha limene Yehova anapatsa Solomo. Motani? Solomo anakhala ndi luso la kusonyeza nzeru m’miyambi, imene kwenikweni inali mawu achidule a nzeru youziridwa ndi Mulungu. Yambiri ya miyambi imeneyi yasungidwa m’buku la Baibulo la Miyambo. Kuphunzira buku limenelo kumatithandiza kupindula ndi luntha la Solomo ndi kukulitsanso luntha lathu.

Tingagwiritsire ntchito magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! monga zotithandiza kuphunzira Baibulo. Kwa zaka zoposa 116, Nsanja ya Olonda yakhala ikulengeza Ufumu wa Yehova kwa anthu oona mtima. Magazini a Galamukani! limodzinso ndi anzake amene analipo poyamba, akhala akulongosola za mikhalidwe ya dziko chiyambire 1919. Magazini aŵiriŵa amapenda choonadi cha Baibulo ndi kupereka kuunikira kopita patsogolo kumene kumatithandiza kuzindikira zolakwa, kaya zophunzitsidwa ndi Dziko Lachikristu kapena zopezedwa m’kalingaliridwe kathu.​—Miyambo 4:18.

Chithandizo china pokulitsa luntha ndicho mayanjano oyenera. Umodzi wa miyambi ya Mfumu Solomo umati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Nzachisoni kuti Rehabiamu mwana wa Mfumu Solomo sanakumbukire mwambi umenewu panthaŵi yofunika kwambiri m’moyo wake. Atate wake atamwalira, mafuko khumi a Israyeli anafika kwa iye kukampempha kuti awapeputsire mavuto awo. Choyamba, Rehabiamu anafunsira kwa akulu, ndipo iwo anasonyeza luntha pamene anamlimbikitsa kuti amvetsere kwa anthu ake. Ndiyeno anapitanso kwa anyamata anzake. Iwoŵa anasonyeza chibwana ndi kupanda luntha, nalimbikitsa Rehabiamu kuyankha Aisrayeli ndi ziwopsezo. Rehabiamu anamvetsera anyamata anzake. Kodi chinachitika nchiyani? Israyeli anapanduka, ndipo Rehabiamu anataya chigawo chachikulu cha ufumu wake.​—1 Mafumu 12:1-17.

Mbali yaikulu yokulitsira luntha ndiyo kufuna chithandizo cha mzimu woyera. Popenda zochita za Yehova ndi Aisrayeli pambuyo pa kumasulidwa kwawo ku ukapolo mu Aigupto, mlembi wa Baibulo Nehemiya anati: “Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza.” (Nehemiya 9:20) Mzimu wa Yehova ukhoza kutithandiza kukhala ochenjera. Pamene mukupempherera mzimu wa Yehova kuti ukupatseni luntha, pempherani ndi chidaliro chifukwa chakuti Yehova “apatsa kwa onse modzala manja.”​—Yakobo 1:5; Mateyu 7:7-11; 21:22.

Luntha ndi Chidziŵitso

Mtumwi Paulo anasonyeza luntha pamene analalikira choonadi kwa anthu amitundu. Mwachitsanzo, nthaŵi ina pamene anali mu Atene, anali ‘kupita, ndi kuona’ zinthu zimene iwo anazipembedza. Paulo anazingidwa ndi mafano, ndipo anavutika mtima. Tsopano anayenera kupanga chosankha. Kodi atenge njira yopeŵa mavuto ndi kukhala chete? Kapena kodi alankhule molimba mtima za kulambira mafano kowandako kumene kunamvutitsa mtima, ngakhale kuti kutero kungapute ngozi?

Paulo anachita mwaluntha. Anaona guŵa la nsembe lolembedwapo kuti: “Kwa Mulungu Wosadziŵika.” Mochenjera, Paulo anathokoza kudzipereka kwawo ku mafano ndiyeno anagwiritsira ntchito guwa limenelo kuyambitsa nkhani ya “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo.” Inde, Yehova anali Mulungu amene sanamdziŵe! Motero Paulo anadziŵa kuti nkhaniyo inali yowatokosa ndipo anakhoza kupereka umboni wabwino kwambiri. Chotulukapo chake? Unyinji wa anthuwo analandira choonadi, kuphatikizapo “Dionisiyo [woweruza wa khoti la Areopagi, NW], ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nawo.” (Machitidwe 17:16-34) Ndi chitsanzo cha luntha chotani nanga chimene Paulo anali!

Mosakayika konse, luntha silimafika mofeŵa kapena mwachibadwa. Koma mwa kuleza mtima, pemphero, khama, mayanjano anzeru, kuphunzira Baibulo ndi kulisinkhasinkha, limodzi ndi kudalira mzimu woyera wa Yehova, inunso mungakulitse luntha.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena