Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 9/1 tsamba 22-26
  • “Chikondi Sichilephera”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chikondi Sichilephera”
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kagulu ka Phunziro la Baibulo Kapangidwa
  • Chitsutso cha Atsogoleri Achipembedzo
  • Ntchito Yathu Yolalikira
  • Zaka za Nkhondo
  • Miyezo ya Yehova ya Ukwati Imveketsedwa Bwino
  • Mathayo a Utumiki
  • Chikondi Chenicheni Sichilephera
  • Ndinali Mwana Wolowerera
    Galamukani!—2006
  • Kukhala Wokhutira ndi Zimene Mulungu Wandipatsa Kwandithandiza
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Makolo Anga Anandithandiza Kuti Ndizitumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Nsanja ya Olonda—1995
w95 9/1 tsamba 22-26

“Chikondi Sichilephera”

YOSIMBIDWA NDI SAMUEL D. LADESUYI

Ndimadabwa pamene ndilingalira za zaka zapitazo ndi kuona zonse zimene zachitidwa. Yehova wakhala akuchita zinthu zodabwitsa pa dziko lonse lapansi. Ku Ilesha, Nigeria, oŵerengeka a ife amene tinayamba kulalikira mu 1931 takhala mipingo 36. Anthu mwina ofikira 4,000 amene anali kufalitsa panthaŵiyo pamene omaliza maphunziro oyambirira a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower anafika ku Nigeria mu 1947 akhala oposa 180,000. Kale, sitinayembekezere kapena kulota za chiwonjezeko chimene chachitika. Ha, ndili woyamikira chotani nanga kuti ndakhala ndi phande m’ntchito yosangalatsa imeneyi! Lekani ndikusimbireni nkhaniyi.

ATATE anali kugulitsa mfuti ndi wonga m’matauni; kaŵirikaŵiri sanali kupezeka panyumba. Anali ndi akazi asanu ndi aŵiri amene ndikudziŵa, koma sanali kukhala ndi onsewo. Atate analoŵa chokolo kwa mayi wanga, mkazi wa akulu awo amene anamwalira. Iwo anakhala mkazi wawo wachiŵiri, ndipo ndinkakhala ndi mayiwo.

Tsiku lina Atate anafika panyumba kuchokera kwa akazi awo oyamba, amene anali kukhala m’mudzi wina wapafupi. Pamene anali kumeneko, anamva kuti mbale wanga wabere lina anali kuimba sukulu. Mbale wangayo anali ndi zaka khumi, mofanana nane. Chotero Atate ananena kuti nanenso ndinayenera kukaimba sukulu. Anandipatsa nainipenzi​—firipenzi ya mabuku ndipo sikisipenzi ya sileti. Mmenemo munali mu 1924.

Kagulu ka Phunziro la Baibulo Kapangidwa

Kuyambira pa ubwana wanga, ndinali kukonda Mawu a Mulungu, Baibulo. Ndinali kukonda maphunziro a Baibulo kusukulu ndipo nthaŵi zonse ndinayamikiridwa ndi aphunzitsi a Sande sukulu. Chotero, mu 1930, ndinapeza mwaŵi wa kukakhala pa nkhani imene inaperekedwa ndi mlendo wina Wophunzira Baibulo, mmodzi wa anthu oyamba kulalikira ku Ilesha. Nkhaniyo itatha, anandigaŵira kope la buku la Zeze wa Mulungu m’Chiyoruba.

Ndinapita ku Sande sukulu nthaŵi zonse. Motero ndinayamba kutenga buku la Zeze wa Mulungu ndi kukaligwiritsira ntchito kutsutsira ziphunzitso zina zimene anali kuphunzitsa kumeneko. Pankabuka mkangano, ndipo kaŵirikaŵiri ndinali kuchenjezedwa ndi atsogoleri atchalitchi pa kutsatira ‘chiphunzitso chatsopano’ chimenechi.

Chaka chotsatira, pamene ndinali kuyenda mu msewu, ndinapeza kagulu ka anthu amene anali kumvetsera kwa munthu wina amene anali kuwakambira nkhani. Wokamba nkhaniyo anali J. I. Owenpa, Wophunzira Baibulo. Anatumizidwa kumeneko ndi William R. Brown (kaŵirikaŵiri wotchedwa kuti Bible Brown), amene anali kuyang’anira ntchito yolalikira ali ku Lagos.a Anandiuza kuti ku Ilesha kunali kagulu ka phunziro la Baibulo komaphunzira Zeze wa Mulungu, chotero ndinagwirizana nako.

Ndinali wamng’ono m’kaguluko​—mwana wasukulu chabe, wazaka pafupifupi 16. Mwachibadwa ndinali wamanyazi, wamantha, kuyanjana kwambiri ndi amuna azaka za ku ma 30 ndi kuposa pamenepo. Koma iwo anakondwa kwambiri chifukwa cha kukhala nawo kwanga, ndipo anandilimbikitsa. Anali ngati atate kwa ine.

Chitsutso cha Atsogoleri Achipembedzo

Posapita nthaŵi tinayamba kutsutsidwa ndi atsogoleri achipembedzo. Akatolika, Aangilikani, ndi ena, amene poyamba anali kulimbana, tsopano anamvana kutitsutsa. Anachita chiŵembu ndi mafumu kuti atilefule. Anatumiza apolisi kudzatilanda mabuku athu, akumanena kuti adzasokoneza anthu. Komabe, ofesala wachigawocho anachenjeza anthuwo kuti analibe ulamuliro wolanda mabukuwo, ndipo patapita milingu iŵiri mabukuwo anabwezedwa.

Zimenezi zitachitika tinaitanidwa ku msonkhano kumene tinaonana ndi oba, kapena mfumu yaikulu, limodzi ndi anthu ena odziŵika a m’tauniyo. Tinali pafupifupi 30 panthaŵiyo. Cholinga chake chinali chofuna kutiletsa kuŵerenga mabuku “owopsa” amenewo. Anatifunsa ngati tinali anthu achilendo, koma pamene anapenyetsetsa nkhope zathu, anati, “Awa ndi ana athu, ngakhale kuti pakati pawo pali anthu ena achilendo.” Anatiuza kuti sanafune kuti tipitirize kuŵerenga mabuku a chipembedzo chimene chidzatisokoneza.

Tinapita kwathu popanda kunenapo kanthu, pakuti tinali titasankha kusamvera anthu odziŵika amenewo. Ambiri a ife tinali okondwa kwambiri ndi zimene tinaphunzira ndipo tinali otsimikiza kupitiriza kuphunzira. Chotero, ngakhale kuti oŵerengeka anawopa ndi kuchoka m’gulu lathu, ambiri a ife tinapitiriza kuphunzira m’shopo ina yaukalipentala. Tinalibe wochititsa phunziro. Tinali kuyamba ndi pemphero ndiyeno tinkasinthana kuŵerenga ndime za bukulo. Patapita ngati ola limodzi, tinali kupempheranso ndi kupita kwathu. Komano anali kutilonda mwachinsinsi, ndipo mafumu ndi atsogoleri achipembedzo anapitiriza kutiitana milingu iŵiri iliyonse ndi kutichenjeza kuleka kuphunzira mabuku a Ophunzira Baibulo.

Zikali choncho, tinali kuyesa kugwiritsira ntchito chidziŵitso chochepa chimene tinali nacho kuthandiza anthu, ndipo ambiri anali kuvomerezana nafe. Anthuwo anayamba kugwirizana nafe mmodzimmodzi. Tinali achimwemwe kwambiri, komabe sitinadziŵe zambiri ponena za chipembedzo chimene tinali kupitako.

Kuchiyambiyambi kwa 1932 mbale wina anafika kuchokera ku Lagos kudzathandiza kuti tikhale olinganizidwa, ndipo mu April nayenso “Bible” Brown anafika. Poona kuti panali gulu lofika pafupifupi 30, Mbale Brown anafunsa kuti adziŵe za kupita patsogolo kumene tinali kuchita m’kuŵerenga kwathu. Tinamuuza zonse zimene tinali kudziŵa. Iye anati tinali oyenerera kubatizidwa.

Popeza kuti inali nyengo yachilimwe, tinayenda ulendo wa makilomita 14 kumtsinje wina kuchokera ku Ilesha, ndipo pafupifupi 30 a ife tinabatizidwa. Kuyambira pamenepo tinakhala alaliki a Ufumu ndipo tinayamba kupita kunyumba ndi nyumba. Sitinayembekezere kuchita zimenezi, koma tsopano tinali okondwera kuuza ena zimene tinadziŵa. Tinafunikira kukonzekera bwino kuti Baibulo litichirikize kutsutsa ziphunzitso zonama zimene tinapeza. Chotero pamisonkhano yathu, tinkakambitsirana za ziphunzitso, kuthandizana pa zimene tinadziŵa.

Ntchito Yathu Yolalikira

Tinalalikira taunishipi yonse. Anthu ankatiseka ndi kutilalatira, koma sitinasamale zimenezo. Chimwemwe chathu chinali chachikulu chifukwa chakuti tinali ndi choonadi, ngakhale kuti tinafunikirabe kuphunzira zambiri.

Pa Sande paliponse tinali kumka kunyumba ndi nyumba. Anthu ankatifunsa mafunso, ndipo tinali kuyesa kuwayankha. Pa Sande madzulo tinali kupereka nkhani yapoyera. Tinalibe Nyumba Yaufumu, chotero tinkasonkhana pabwalo. Tinkasonkhanitsa anthu, kupereka nkhani, ndi kuwapatsa mwaŵi wa kufunsa mafunso. Nthaŵi zina tinkalalikira m’matchalitchi.

Tinkayendanso m’madera kumene anthu ake anali asanamvepo za Mboni za Yehova. Nthaŵi zambiri,tinkayenda panjinga, koma nthaŵi zina tinali kuhaya basi. Pamene tinafika pamudzi, tinkaliza lipenga mwamphamvu. Mudzi wonse unkatimva! Anthu ankatuluka kunja mofulumira kudzaona zimene zinali kuchitika. Ndiyeno tinkapereka uthenga wathu. Titamaliza, anthu analikulimbirana mabuku athu. Tinkagaŵira mabuku ambiri.

Tinayembekezera mwaphamphu kufika kwa Ufumu wa Mulungu. Ndikukumbukira kuti pamene tinalandira 1935 Yearbook, mbale wina, ataona mpambo wonse wa malemba a tsiku okambitsirana chakacho, anafunsa kuti: “Kodi zimenezi zikutanthauza kuti chaka chonse chitha Armagedo isanadze?”

Poyankha wochititsa phunziro anafunsa kuti: “Mbale wanga, kodi uganiza kuti ngati Armagedo ifika maŵa, tidzaleka kuŵerenga Yearbook?” Pamene mbaleyo anati ayi, wochititsa phunziroyo anati: “Nangano uvutikiranji?” Tinayembekezera, ndipo tikali kuyembekezera mwaphamphu tsiku la Yehova.

Zaka za Nkhondo

Mkati mwa nkhondo yachiŵiri, mabuku athu analetsedwa kuloŵa m’dziko. Mbale wina ku Ilesha mosadziŵa anasonyeza buku la Chuma kwa wapolisi wina. Wapolisiyo anamfunsa kuti: “Kodi mwini bukuli ndani?” Mbaleyo anati linali lake. Wapolisiyo anati linali buku loletsedwa, anamtengera ku polisi, ndi kukamtsekera.

Ndinapita kupolisiko ndipo, nditafunsa za nkhaniyo, ndinalipirira mbaleyo faindi yomtulutsira m’ndende. Ndiyeno ndinaimbira telefoni Mbale Brown ku Lagos kumdziŵitsa zimene zinachitika. Ndinamfunsanso ngati panali lamulo lililonse loletsa kufalitsa mabuku athu. Mbale Brown anandiuza kuti mabuku athu anangoletsedwa kuloŵa m’dziko, osati kuwafalitsa. Patapita masiku atatu, Mbale Brown anatuma mbale wina kuchokera ku Lagos kudzaona zimene zinali kuchitika. Mbale ameneyu anapereka lingaliro lakuti tonsefe tipite kuntchito yolalikira mmaŵa mwake tili ndi magazini ndi mabuku.

Tinamwazikana kumbali zosiyanasiyana. Patapita ngati ola limodzi, ndinalandira mbiri yakuti abale ochuluka amangidwa. Chotero ine ndi mbale amene anafikayo tinapita kupolisi. Apolisi anakana kuti tiwalongosolere kuti mabukuwo sanaletsedwe.

Abale 33 omangidwawo anatumizidwa ku Khoti la Mejasitiliti Wamkulu ku Ife, ndipo ndinatsagana nawo. Anthu a m’taunimo amene anationa titatengedwa anafuula kuti, “Lero anthu awa pawo patha. Sadzabweranso kuno.”

Mejasitiliti wamkuluyo, Mnaijeriya, anauzidwa mlanduwo. Mabuku onse ndi magazini anasonyezedwa. Anafuna kudziŵa kuti ndani amene analamulira mkulu wapolisi kugwira anthu ameneŵa. Mkulu wapolisi anayankha kuti anamvera malangizo ochokera kwa ofesala wa chigawocho. Mejasitiliti wamkuluyo anaitana mkulu wapolisiyo ndi nthumwi zathu zinayi, kuphatikizapo ineyo, m’chipinda chake.

Anafuna kudziŵa kuti a Brown anali ayani. Tinamuuza kuti anali woimira wa Watch Tower Society ku Lagos. Ndiyeno anatiuza kuti analandira telegalamu kwa a Brown yonena za ife. Anaimitsa mlanduwo tsikulo ndi kutulutsa abalewo pafaindi. Tsiku lotsatira anachotsera abale mlanduwo, nawamasula, ndipo analamulira apolisi kubwezera mabukuwo.

Tinabwerera ku Ilesha, tikumaimba. Anthu anayambanso kufuula, komano akumati, “Abweranso!”

Miyezo ya Yehova ya Ukwati Imveketsedwa Bwino

Munali mu 1947 pamene anthu atatu oyambirira omaliza maphunziro a Gileadi anafika mu Nigeria. Mmodzi wa abale ameneŵa, Tony Attwood, akali kutumikira konkuno, pa Beteli ya Nigeria. Kuyambira nthaŵiyo, tinaona masinthidwe aakulu m’gulu la Yehova mu Nigeria. Amodzi a masinthidwe aakuluwo anali onena za mitala.

Ndinakwatira Olabisi Fashugba mu February 1941 ndipo ndinadziŵa bwino kwambiri za kusakwatira akazi enanso. Koma kufikira 1947 pamene amishonale anafika, mitala inali yofala m’mipingo. Abale amitala anawauza kuti anali atakwatira akazi ambiri mosadziŵa. Chotero ngati anali ndi akazi aŵiri, kapena atatu kapena anayi, ngakhale asanu, awasamalire, koma sanayenera kukwatira enanso. Limenelo ndilo lamulo limene tinali nalo.

Anthu ambiri anafunitsitsa kugwirizana nafe, makamaka a Sosaite ya Akerubi ndi Aserafe ku Ilesha. Iwo anati Mboni za Yehova zinali anthu okha amene anaphunzitsa choonadi. Anavomereza ziphunzitso zathu ndipo anafuna kusintha matchalitchi awo kukhala Nyumba Zaufumu. Tinali kuyesayesa kwambiri kuti zimenezi zichitike. Tinalinso ndi malo ophunzitsira akulu awo.

Ndiyeno panadza malangizo atsopano ponena za mitala. Mmodzi wa amishonalewo anapereka nkhani pamsonkhano wadera mu 1947. Iye anafotokoza za khalidwe labwino ndi zizoloŵezi. Ndiyeno anagwira mawu 1 Akorinto 6:9, 10, amene amati osalungama sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu. Ndiyeno anawonjezera kuti: “Ndipo amitala sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu!” Anthu ena mwa omvetsera anafuula kuti: “Aaa, amitala sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu!” Panali magaŵano. Zinali ngati nkhondo. Atsopano ambiri analeka kuyanjana nafe, akumati: “Tili ndi mwaŵi, chifukwa chakuti sitinapite patali.”

Komabe, abale ambiri anayamba kukonza miyoyo yawo mwa kumasula akazi awo. Anawapatsa ndalama nanena kuti, ‘Poti ukali wanthete, pita ukakwatiwe ndi mwamuna wina. Ndinalakwa kukukwatira. Tsopano ndiyenera kukhala mwamuna wa mkazi mmodzi.’

Vuto lina linabuka posapita nthaŵi. Ena, pambuyo posankha kukhala ndi mkazi mmodzi ndi kumasula ena, anasintha maganizo awo nanena kuti anafuna kutenga mmodzi wa akazi amene anawachotsa mosinthanitsa ndi amene anatsala naye! Chotero mavuto anayambanso.

Malangizo owonjezereka anafika kuchokera ku Brooklyn, ozikidwa pa Malaki 2:14 (NW), pamene pamanena za “mkazi wa ubwana wako.” Malangizowo anati amuna anayenera kusunga akazi awo oyamba amene anakwatira. Umu ndimo mmene nkhaniyo inathetsedwera.

Mathayo a Utumiki

Mu 1947 Sosaite inayamba kulimbitsa mipingo ndi kuilinganiza kukhala madera. Anafuna kuika abale amene anali achidziŵitso ndi okhwima maganizo kukhala ‘atumiki a kwa abale,’ tsopano amene amatchedwa oyang’anira madera. Mbale Brown anandifunsa ngati ndingavomere thayolo. Ndinati ndinabatizidwa chifukwa cha kufuna kuchita chifuniro cha Yehova, ndikumawonjezera kuti: “Pajatu ndinu munandibatiza. Tsopano kodi muganiza kuti pamene pakhala mwaŵi wa kutumikira Yehova mochuluka ndingakane kodi?”

Mu October wa chaka chimenecho, asanu ndi aŵiri a ife tinaitanidwa ku Lagos ndipo tinalandira maphunziro tisanatumizidwe m’ntchito yadera. Masikuwo madera anali aakulu. Dziko lonse linagaŵidwa m’madera asanu ndi aŵiri okha. Mipingo inali yoŵerengeka.

Ntchito yathu monga atumiki a kwa abale inali yovuta. Tinkayenda mitunda yambiri tsiku lililonse, kaŵirikaŵiri kudutsa nkhalango zotentha kwambiri. Mlungu uliwonse tinkayenda m’midzi yosiyanasiyana. Nthaŵi zina miyendo yanga inali kufooka. Nthaŵi zina ndinkaganiza kuti ndidzafa! Koma panali chimwemwe chachikulu, makamaka poona chiŵerengero chomawonjezereka cha anthu olandira choonadi. Mwaona nanga, m’zaka zisanu ndi ziŵiri zokha, chiŵerengero cha ofalitsa m’dzikolo chinaŵirikiza kanayi!

Ndinachita ntchito yadera kufikira 1955 pamene matenda anandichititsa kubwerera ku Ilesha, kumene ndinaikidwa kukhala woyang’anira mzinda. Kukhala kumudzi kunandikhozetsa kuika mtima kwambiri pa kuthandiza banja langa mwauzimu. Lero ana anga onse asanu ndi mmodzi akutumikira Yehova mokhulupirika.

Chikondi Chenicheni Sichilephera

Pamene ndikumbukira za zaka zakumbuyoku, pali zambiri zimene ndimayamikira. Panali zolefula, nkhaŵa, ndi matenda, komanso panali chimwemwe chambiri. Ngakhale kuti chidziŵitso ndi kuzindikira kwathu zakula m’kupita kwa zaka, kupyolera mwa zokumana nazo ndazindikira thanthauzo la 1 Akorinto 13:8 (NW), amene amati: “Chikondi sichilephera.” Ngati mumakonda Yehova ndi kulimbikira mu utumiki wake, adzakuthandizani m’zovuta zanu ndipo adzakudalitsani kwambiri.

Kuunika kwa choonadi kukuwalilirabe. Masikuwo pamene tinayamba, tinaganiza kuti Armagedo idzafika mofulumira; nchifukwa chake tinali kuchita mofulumira zonse zimene tinakhoza. Koma zonsezo zinali zotipindulitsa. Nchifukwa chake ndikuvomereza mawu a wamasalmo akuti: “Ndidzalemekeza Yehova m’moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.”​—Salmo 146:2.

[Mawu a M’munsi]

a Mbale Brown anatchedwa kuti Bible Brown chifukwa cha chizoloŵezi chake cha kugwiritsira ntchito Baibulo monga ulamuliro wake.​—Onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 1992, patsamba 32, nkhani yakuti “Kututa kwa Mlaliki Wowona.”

[Chithunzi patsamba 23]

Samuel ndi Milton Henschel mu 1955

[Chithunzi patsamba 24]

Samuel ndi mkazi wake, Olabisi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena