Nsanje Inatsala Pang’ono Kuwononga Moyo Wanga
NSANJE inayamba kundikhudza moipa kwambiri pamene ndinakwatiwa ndi Mark,a mwamuna wanga wachiŵiri. Tinali kusamalira ana angapo opeza ndi kumachitira zinthu zina pamodzi ndi anzathu a mu ukwati akale. Nthaŵi zina mkhalidwewo unali wosapiririka. Nthaŵi zonse patabuka kusamvana pabanja, Mark sanali kundichirikiza. Ndinayamba kuganiza kuti iye anali kukondabe mkazi wake wakale. M’malo molamulira nsanje yanga, ndinailola kulamulira moyo wanga. Nthaŵi zonse ndikaona mkazi wakale wa Mark, zinali kundivutitsa maganizo.
Nthaŵi zonse ndinali kumpenya Mark, ngakhale kupenya maso ake kuti ndione kumene anali kuyang’ana. Ndinayesa kuti kuyang’ana kwake kunatanthauza kanthu kena kamene ngakhale iye sanakaganizire. Nthaŵi zina ndinali kumuuza poyera kuti anakondabe mkazi wake wakale. Nthaŵi ina anavutika nazo kwambiri zimenezi kwakuti ananyamuka ndi kuchoka pamsonkhano Wachikristu. Ndinamva liwongo pamaso pa Yehova. Ndinavutitsa moyo wa banja langa chifukwa chakuti ngakhalenso ana anakhudzidwa nazo zimenezi. Ndinadzida ndekha chifukwa cha zimene ndinali kuchita, koma ngakhale kuti ndinayesayesa mwamphamvu, sindinathe kulamulira nsanje yanga.
M’malo mwa kundithandiza, Mark anayamba kubwezera. Pamene ndinamuimba mlandu, anali kundizazira kuti, “Nsanje basi, ndiwe wansanje.” Ndipo anali kuyesa dala kundichititsa nsanje. Mwinamwake anaganiza kuti zimenezo zidzathetsa nsanje yanga, koma zinangoipitsa zinthu. Anayamba kumayang’ana akazi ena, akumakamba za kukongola kwawo. Zimenezi zinandichititsa kuganiza kuti ndinali wapansi kwambiri ndi wosafunika. Zinthu zinafika poti mkhalidwe wina—udani—unabuka. Panthaŵiyo, ndinali wosokonezekeratu kwakuti ndinangofuna kupatukana naye ndi banja lake lomwe.
Pamene Baibulo limati “nsanje ivunditsa mafupa,” limanenadi zoona. (Miyambo 14:30) Ndinayamba kudwalira. Ndinakhala ndi zilonda za m’mimba zimene zinatenga nthaŵi yaitali kupola. Ndinapitiriza kuvutitsa moyo wanga mwa kunyumwira kalikonse kamene Mark anachita. Ndinali kupisa m’matumba a zovala zake, ndipo nditapezamo manambala a telefoni, ndinali kuimba foni kuti ndione amene adzayankha. Pansi pa mtima ndinali ndi manyazi kwambiri, ndinali kulira chifukwa chochita manyazi pamaso pa Yehova. Komabe ndinalephera kudziletsa. Ndinadzida kowopsa.
Mkhalidwe wanga wauzimu unawonongeka kufika poti ndinasiya kupemphera. Ndinamkonda Yehova ndipo ndinafunadi kuchita chabwino. Ndinadziŵa malemba onse onena za amuna ndi akazi awo, koma sindinakhoze kuwatsatira. Kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wanga, sindinafunenso kukhala ndi moyo, ngakhale kuti ndinali ndi ana abwino kwambiri.
Akulu mumpingo Wachikristu anandilimbikitsa kwambiri ndipo anayesayesa kundithandiza. Koma atabutsa nkhani ya nsanje yanga, ndinali kukana chifukwa cha manyazi, osafuna kuvomereza kuti ndinali ndi vutolo.
M’kupita kwa nthaŵi, thanzi langa linaipa kwambiri kwakuti ndinaloŵa m’chipatala kukachitidwa opaleshoni. Ndili mmenemo, ndinazindikira kuti moyo suyenera kupitiriza choncho ayi. Ine ndi Mark tinasankha kupatukana miyezi itatu kuti tikalingalire za vuto lathu popanda kuvutitsana mtima kwambiri. Panthaŵiyi panachitika kanthu kena kabwino kwambiri. M’magazini a Galamukani! munatuluka nkhani yamutu wakuti “Chithandizo kwa Ana Achikulire a Zidakwa.”b
Mwaona nanga, amayi anali chidakwa. Ngakhale kuti sanandichitire nkhanza, makolo anga sanasonyezane chikondi ngakhale ine sanandisonyeze chikondi. Sindikukumbukira pamene amayi anandikumbatirapo kapena kundiuza kuti anandikonda. Chotero ndinakula wosadziŵa kwenikweni mmene ndingakondere wina, kapena chofunikanso kwambiri, mmene kukondedwa kulili.
Kaŵirikaŵiri amayi anali kundiuza za akazi amene atate anali kunyengana nawo ndi kuti iwo sanawakhulupirire. Ndiyesa kuti nanenso ndinakula wosakhulupirira amuna onse. Chifukwa cha mmene ndinakulira, ndinali kudziyesa wapansi kwa ena, makamaka kwa akazi anzanga. Kuŵerenga nkhani imeneyo mu Galamukani! kunandithandiza kuzindikira zimene zinthuzi zinatanthauza. Kwa nthaŵi yoyamba, ndinazindikira zochititsa zazikulu za vuto langa la nsanje.
Ndinasonyeza mwamuna wanga Mark nkhani ya mu Galamukani! imeneyo, ndipo nayenso inamthandiza kundimvetsa. Posapita nthaŵi ine ndi iye tinakhoza kutsatira uphungu wa Baibulo kwa okwatirana oganiza zopatukana. Tinabwererana. (1 Akorinto 7:10, 11) Tsopano ukwati wathu uli bwino kuposa mmene unalili kale. Timachitira pamodzi zinthu zochuluka, makamaka pamene zikuphatikizapo ntchito Zachikristu. Mark amandisonyeza chifundo kwambiri. Pafupifupi masiku onse iye amandiuza za mmene amandikondera, ndipo tsopano ndimakhulupiriradi.
Nthaŵi zonse ndikadziŵa kuti tidzaonana ndi mkazi wakale wa Mark, ndimapemphera kwa Yehova kuti andipatse nyonga, ndikumamupempha kundithandiza kuchita monga Mkristu wokhwima. Ndipo zimathandiza. Ngakhale udani wanga kulinga kwa iye ukuzimiririka. Sindimaganizanso zoipa kapena kulola zolingalira zanga kundilamulira.
Ndimakhalabe ndi nsanje yosayenera nthaŵi zina. Moyo wangwiro m’dziko latsopano la Mulungu ndiwo wokha umene udzaithetsa. Pakali pano, ndaphunzira kulamulira nsanje, m’malo mwa kuilola kundilamulira. Inde, nsanje inatsala pang’ono kuwononga moyo wanga, koma mwa chithandizo cha Yehova ndi gulu lake, tsopano ndine munthu wachimwemwe koposa, ndipo thanzi langa lakhala bwino. Ndakhalanso ndi ubwenzi wolimba ndi Yehova, Mulungu wanga.—Yoperekedwa.
[Mawu a M’munsi]
a Dzinalo lasinthidwa.