Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 11/15 tsamba 3-4
  • Moyo Wabwino Kwambiri Ulonjezedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo Wabwino Kwambiri Ulonjezedwa
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi ndi Moyo Uti Umene Mungakonde?
  • Mabwenzi a Mulungu Adzakhala M’paradaiso
    Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Dzikoli Lidzakhala Paradaiso
    Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • “Iwe Udzakhala ndi Ine m’Paradaiso”
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 11/15 tsamba 3-4

Moyo Wabwino Kwambiri Ulonjezedwa

KODI mungakonde kumasuka pa mavuto amene amapangitsa moyo kukhala wovuta? Kodi mukufuna kukhala m’dziko limene moyo wake uli wosangalatsa monga momwe wasonyezedwera pachikuto cha kumaso ndi kumbuyo kwa magazini ano? Yang’anitsitsani bwino chithunzithunzi chimenecho. Anthu ali ndi chakudya chambiri. Iwo adzasangalaladi ndi chakudya chokoma. Aliyense ngwachimwemwe. Anthu a mafuko osiyanasiyana ali pamtendere wina ndi mnzake. Ngakhale nyama zili pamtendere! Palibe amene akumenyana. Palibe amene ali wosauka. Palibe amene akudwala. Pali malo okongola, mitengo yokongola, ndi madzi abwino oyera. Ha, ndi mkhalidwe wabwino chotani nanga umenewu!

Kodi dzikoli lidzakhala lotero? Inde, lidzakhala paradaiso. (Luka 23:43) Mulungu, amene analenga dziko lapansi, walinganiza kuti anthu adzakhale ndi moyo wabwino kwambiri pa dziko lapansi la paradaiso. Ndipo inu mungathe kukhala mmenemo!

Kodi ndi Moyo Uti Umene Mungakonde?

Kodi Paradaiso wa pa dziko lapansi wamtsogolo adzakhala wosiyana motani ndi dziko limene tikukhalamo tsopano? Pakali pano, anthu oposa mamiliyoni chikwi chimodzi amakhala ndi njala tsiku lililonse. Koma m’Paradaiso amene Mulungu walinganiza kaamba ka dziko lapansi, aliyense adzakhala ndi chakudya chochuluka. Baibulo limalonjeza kuti: “Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe.” (Yesaya 25:6) Sipadzakhala kupereŵera kwa chakudya, pakuti Baibulo limati: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.”​—Salmo 72:16.

Lerolino, ambiri amakhala m’zithando, kapena amavutikira kulipirira lendi yawo. Ena alibe pokhala ndipo amagona m’mbali mwa misewu. Malinga ndi kunena kwa World Health Organization, ana ambiri a m’dziko ofikira 100 miliyoni alibe kwawo. Koma m’Paradaiso amene akudzayo, aliyense adzakhala ndi nyumba yakeyake. Mawu a Mulungu amati: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake.”​—Yesaya 65:21.

Ambiri amakhetsa thukuta pa ntchito zimene samakonda. Kaŵirikaŵiri amagwira ntchito zolimba kwa maola ambiri koma amalandira ndalama zochepa kwambiri. Pafupifupi munthu mmodzi mwa anthu asanu alionse m’dziko amakhalira moyo pa ndalama zosafika pa $500 pachaka. Komabe, m’Paradaiso amene akudzayo, anthu adzasangalala ndi ntchito yawo ndipo adzapindula nayo. Mulungu akulonjeza kuti: “Adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe.”​—Yesaya 65:22, 23.

Tsopano kudwala ndi matenda zili ponseponse. Ambiri ngakhungu. Ena ngogontha. Ena sangayende. Koma m’Paradaiso, anthu adzamasuka pakudwala ndi matenda. Yehova akunena kuti: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ponena za amene ali opunduka kale, lonjezo losangalatsa mtima nlakuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzaimba.”​—Yesaya 35:5, 6.

Panthaŵi ino, pali nsautso ndi zopweteka, chisoni ndi imfa. Koma m’Paradaiso wa pa dziko lapansi, zinthu zonsezi sizidzakhalako. Inde, ngakhale imfa idzachoka! Baibulo limati: “Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Motero, mwachionekere, Paradaiso wa pa dziko lapansi wolonjezedwayo wa Yehova adzatanthauza moyo wabwino kwambiri kwa anthu. Koma kodi tingatsimikizire motani kuti adzafika? Kodi adzafika liti, ndipo motani? Kodi muyenera kuchitanji kuti mudzakhalemo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena