Kodi Muli ndi Mzimu Wopatsa?
KODI mwazindikira kuti pali zochititsa zambiri zimene zimasonkhezera anthu kupereka mphatso? Mphatso ingakhale kusonyeza chikondi, kuoloŵa manja, kuyamikira. Komabe kodi simunaone kuti mphatso ingaperekedwe chifukwa cha chikhumbo cha munthu kuti aziyanjidwa? Kapena wina angaipereke chifukwa cha kuganiza kuti ali ndi thayo kapena chifukwa chakuti akufuna kupindula kanthu kena.
Mphatsoyo ingakhale ili m’chikuto chomangidwa ndi liboni yokongola. Koma kodi si zoona kuti tsadzi la maluŵa, chakudya, kapena mchitidwe wina wokoma mtima ungakhale mphatso yabwino? Kwenikweni, mphatso zimene zimayamikiridwa kwambiri kaŵirikaŵiri zimaphatikizapo kudzipereka kwa munthuwe.
Kodi Pali Aliyense Amene Mukufuna Kuti Akuyanjeni?
Si kwachilendo kuti munthu apereke mphatso kwa munthu wina amene akufuna kuti amuyanje. M’maiko ena mnyamata amene akufuna kukondedwa ndi msungwana amene akuyembekezera kudzakwatirana naye angampatse maluŵa. Komabe mkazi wanzeru amazindikira tanthauzo la mphatso. Amasinkhasinkha kuti aone ngati mzimu wa mphatso ya mnyamatayo uli wachikondi umene udzampangitsanso kukhala mwamuna wabwino. Mphatso yotero, ngati isonyeza mzimu waumulungu, ingabweretse chimwemwe chochuluka kwa wopereka ndi wolandira yemwe.
Baibulo limatiuza za chochitika china pamene Abigayeli, mkazi wa Nabala, mofulumira anakonzera Davide mphatso, amene anamzindikira kukhala munthu wosankhidwa ndi Mulungu kudzakhala mfumu yamtsogolo ya Israyeli. Iye anafunanso chiyanjo. Mwamuna wake anali atanyoza Davide ndipo ananenera anyamata a Davide zachipongwe. Gulu la amuna 400 onyamula malupanga linatsata Davide kuti likaphe Nabala ndi a m’nyumba yake. Abigayeli analoŵererapo, akumatumiza msanga mphatso ya chakudya kwa Davide cha anyamata ake. Mkaziyo anafika pambuyo pa mphatsoyo, ndipo atapepesa modzichepetsa pa zimene mwamuna wake anachita, anapereka umboni wakuti anali ndi luntha kwambiri pamene anakambitsirana nkhaniyo ndi Davide.
Cholinga chake chinali chabwino, ndipo chotulukapo chake chinali chabwino. Davide analandira mphatso yake nati kwa iye: “Ukwere kwanu mumtendere; ona, ndamvera mawu ako, ndavomereza nkhope yako.” Pambuyo pake, Nabala atamwalira, Davide anafunsira Abigayeli kukhala mkazi wake, ndipo iyeyo anavomera mokondwera.—1 Samueli 25:13-42.
Komabe, m’zochitika zina, chiyanjo chimene munthu amafuna chingaphatikizepo kusonyeza tsankhu, ngakhale kupotoza chiweruzo. Patachitika zotero, mphatsoyo imakhala chiphuphu. Woperekayo amaganiza kuti adzapindula, komatu amadzichotsera mtendere wamaganizo. Nthaŵi zonse pamakhala ngozi yakuti ena adzatulukira zimenezo, ndi kuti adzapatsidwa mlandu. Ngakhale ngati chiyanjo chimene akufuna chiperekedwa, munthu amene anachifunayo angapeze kuti iye tsopano ali ndi mbiri ya munthu amene zolinga zake zili zokayikitsa. Posonyeza nzeru yaumulungu, Baibulo limachenjeza za mphatso zotero.—Deuteronomo 16:19; Mlaliki 7:7.
Kodi Mphatsoyo Ikuchokera mu Mtima Wofunitsitsa?
Nzosakayikitsa—kupereka mphatso kwa munthu amene mumakonda chifukwa chakuti mukufuna kutero kumabweretsa chisangalalo chachikulu kuposa kupereka mphatso chifukwa chakuti ena akukuchititsani kumva kuti muyenera kutero.
Ponena za kusonkhanitsa katundu wachithandizo wa Akristu anzake amene anali osoŵa mwakuthupi, mtumwi Paulo anafotokoza njira zabwino kwambiri za kupereka mphatso kwaumulungu. “Ngati chivomerezocho chili pomwepo,” analemba motero, “munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsoŵa.” Anawonjezera kuti: “Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akorinto 8:12; 9:7) Motero, zambiri zikudalira pa inu. Kodi mumachita moyenererana ndi thumba lanu m’malo mwa kuloŵa m’ngongole pa nyengo ya kupereka mphatso zochuluka? Kodi mumachita zimene mwatsimikiza mumtima mwanu m’malo mwa kukakamizidwa kupereka mphatso makamaka chifukwa cha mabwenzi kapena amalonda? Ponena za Akristu oyambirira amene anagwiritsira ntchito njira zaumulungu zimenezo, Paulo analemba kuti: “Anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho [“mwaŵi wa kupatsa mokoma mtima,” NW], ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima.”—2 Akorinto 8:4.
Mosiyana ndi zimenezo, Royal Bank Letter ya November/December 1994 inati ponena za masabata oyandikira nyengo ya Krisimasi: “Nyengoyo ingaonedwe kukhala mkhalidwe wa chimwemwe chachiphamaso chosonkhezeredwa ndi amalonda olimbikitsa makasitomala kugula zinthu zimene mwina sakanagula.” Ngati kugulako kuli kwa ngongole, chikhutiro chilichonse chimene chingakhalepo chifukwa cha kupereka mphatso chimatha msanga pamene ngongolezo zifunikira kulipiridwa.
Nkhaŵa Yanu Yaikulu—Chochitika? Kapena Kusonyeza Chikondi?
Kodi zimachitika kuti mumapereka mphatso makamaka pa zochitika zimene zimafuna zimenezo? Ngati ndi choncho, mungakhale mukuphonya chimwemwe chochuluka chimene kupereka mphatso kodzifunira kumabweretsa.
Pali anthu ambiri amene samakondwera ndi zotulukapo za kupereka mphatso kochitidwa pamasiku ena apadera. Mayi wina yemwenso ndi wolemba mabuku akuvomereza kuti umbombo unaoneka mwa ana ake pamene tsiku loyembekezera mphatso linali kuyandikira. Akuvomereza kuti chisangalalo chake cha kulandira mphatso yokongola chinawonongedwa chifukwa chakuti anayembekezera kulandira kanthu kena. Malipoti ambiri akunena kuti maholide okhala ndi mapwando ndi kupatsana mphatso alinso nthaŵi pamene anthu amapsinjika kwambiri ndi kuledzera.
Pokhala ataona kuti kugogomezera kupereka mphatso panthaŵi ya holide nthaŵi zina kumayambukira ana moipa, profesa wa zamalingaliro wogwidwa mawu mu The New York Times akunena kuti: “Lingalirani za kupereka mphatso pamasiku ena kukhala njira yochepetsera kupsinjika.” Kodi muganiza kuti zimenezo zingakhale ndi zotulukapo zabwino?
Tammy, wazaka 12 wokhala m’banja limene silimasunga masiku a Krisimasi ndi a kubadwa, analemba kuti: “Kulandira mphatso mwadzidzidzi nkosangalatsa kwambiri.” Iye anati m’malo mwa kupereka mphatso kamodzi kokha kapena kaŵiri pachaka, makolo ake amapereka zimenezo kwa iye ndi mlongo wake chaka chonse. Koma pali kanthu kena kamene kali kofunika kwambiri kwa iye kuposa mphatso zimenezo. Monga momwe iye akunenera, “Ndili m’banja lachimwemwe kwambiri.”
Buku lotchedwa Secrets of Strong Families limanena mosabisa kuti: “Ambiri a ife timatha nthaŵi ndi ndalama kangapo pachaka tikumasankha mphatso zoyenera za masiku a kubadwa, masiku apadera apachaka, kapena maholide a anthu amene timakonda. Mphatso yeniyeni yabwino koposa sifuna ndalama zilizonse. Ndipo simufunikira kuikutira. Ngati mukhulupirira, monga momwe anthu ochuluka amachitira, kuti moyo wanu ndiwo chuma chamtengo wapatali chimene muli nacho, pamenepo mbali ina ya moyo wanu ndiyo mphatso yamtengo wapatali imene mungapereke. Timapereka mphatso yamtengo wapatali imeneyo mwa kuchuluka kwa nthaŵi yathu imene timapereka kwa okondedwa athu.”
Mungachite kupereka mphatso kumeneko kwa enanso amene sali a m’banja lanu. Kupereka mphatso kodzifunira kuthandiza ena pakusoŵa kwawo kungakupatseni chikhutiro chapadera. Yesu Kristu anatilimbikitsa kusonyeza nkhaŵa yachikondi yotero kwa osauka, opunduka, ndi akhungu, akumawonjezera kuti: “Udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe cha kubwezera iwe mphotho.”—Luka 14:12-14.
Rockland Journal-News (U.S.A.) posachedwapa inasimba za chitsanzo china cha kupatsa kwa mtundu umenewo. Pamene nyumba ya nkhalamba ina yachikazi yakhungu inagwa, mabwenzi ake anaimangira nyumba yatsopano. Makampani angapo akumaloko anapereka zopereka, ndipo ndalama zinaperekedwa ndi bungwe loimira boma lakumaloko. “Komabe, chofunika koposa,” inatero nyuzipepalayo, “chinali anthu pafupifupi 150, ochuluka a iwo amene amaloŵa mpingo wa Mboni za Yehova wa ku Haverstraw, amene anapereka nthaŵi ya kumangira nyumbayo.”
Nkhaniyo inapitiriza kunena kuti: “Pamalo omangawo panali miyulu ya zinthu imene inali pafupi ndi mathebulo odzaza chakudya. M’masiku aŵiri antchitowo anamanga nyumba ya zigawo ziŵiri, ya zipinda zosanja zitatu. . . . Mboni za Yehova nzodziŵika ndi luso lawo la kumanga nyumba mofulumira. . . . Komabe, kufulumira kumeneko nkosiyana kwambiri ndi cholinga chawo chachikulu: kuchititsa ntchito ya chikondi kukhala yachikhalire. Agogo aBlakely sangaone nyumba yawo yatsopanoyo, koma angathe kuikhudza ndi manja awo, ndipo mtima wawo wakhudzidwa kwambiri ndi mchitidwe umenewu wosadzikonda.”
Mzimu wa Kuoloŵa Manja Chaka Chonse
Awo amene alidi ndi mzimu wooloŵa manja samayembekezera masiku apadera. Samangosumika moyo wawo pa iwo eni. Pamene alandira kanthu kena kabwino, amafuna kukagaŵira ena. Zimenezi si zimatanthauza kuti iwo ali omwerekera pa kupereka mphatso kwa ena. Si zimatanthauza kuti amapereka mphatsozo momana mabanja awo. Si zimatanthauza kuti amapereka mphatso mosalingalira za mmene idzakhudzira woilandira. Komabe, iwo ndi anthu amene ‘amapatsa,’ monga momwe Yesu anaphunzitsira ophunzira ake kuchita.—Luka 6:38.
Amadziŵa za mikhalidwe ya mabwenzi awo ndi anansi amene ali okalamba, odwala, kapena ofuna chilimbikitso mwanjira ina. “Mphatso” yawo ingakhale kuwapitira ku sitolo kapena kuwathandiza ntchito ina yapanyumba. Ingakhale ntchito yoŵaza nkhuni kapena kuyeretsa ngalande. Chingakhale chakudya chophikaphika m’mbale kapena kupatula ola locheza nawo ndi kuŵerengera nawo pamodzi. Moyo wawo ungakhale wotanganitsa koma wosati nkulephera kuthandiza ena. Aphunzira mwa zochitika kuti ndithudi “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
Zoonadi, Mpatsi wamkulu kuposa onse ndiye Mlengi wathu, Yehova Mulungu. Iyeyo “apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25) M’Baibulo, iye amatipatsanso chidziŵitso chonena za chifuno chake cha kuthetsa kuipa, matenda, ndi imfa, ndi kupanga dziko lapansili kukhala paradaiso. (Salmo 37:10, 11; Chivumbulutso 21:4, 5) Atadziŵa zimenezi, awo amene ali ndi mzimu wooloŵa manja samangosunga uthenga wabwino umenewo. Chimodzi cha zinthu zimene zimawasangalatsa kwambiri ndicho kuuza ena zimenezi. Mzimu wawo wa kupatsawo ulidi waumulungu. Kodi umenewo ndiwo mzimu umene mukukulitsa?
[Zithunzi patsamba 7]
Mphatso zina zamtengo wapatali sizimafuna ndalama