Kodi Munapulumutsidwa?
JOHNNY anali ndi zaka khumi pamene mwamuna wina anamuimika kuchionetsero namfunsa kuti: “Mnyamata iwe, kodi ukuvomereza Yesu Kristu monga Ambuye ndi Mpulumutsi wako?” Funso limenelo linamveka lachilendo kwa Johnny, popeza iye anakhulupirira mwa Yesu nthaŵi zonse. Chotero, iye anayankha kuti: “Inde, ndimatero.” “Alemekezeke Ambuye!” mwamunayo anafuula kuti onse amve. “Moyo winanso wapulumutsidwa kaamba ka Kristu!”
Kodi chipulumutso chilidi chosavuta choncho? Kodi Johnny “anapulumutsidwa” kuyambira nthaŵi imene ananena mawuwo, ngakhale kuti akanachita zotani m’moyo wake wonse? Anthu ambiri oona mtima angayankhe kuti inde anatero. Matrakiti ena achipembedzo amalangiza munthu kulemba tsiku limene “anapulumutsidwa” kuti azilikumbukira.
Mtsogoleri wachipembedzo analemba kuti “nthaŵi imene munthu amasonyeza chikhulupiriro mwa kungovomereza Kristu . . . mtsogolo mwake mumakhazikika kosatha.” Iye anati Baibulo limanena kuti chipulumutso chimadalira pa “kusonyeza chikhulupiriro [kamodzi kwatha], osati chikhulupiriro chopitiriza.” Mlembi wina wachipembedzo analemba kuti: “Zimenezi ndi ntchito yomalizidwa. Inu mwachipeza kale chipulumutso . . . ‘Nkhondo [yanu] yatha.’ ‘Machimo [anu] achotsedwa.’” Koma ngakhale anthu amene akhulupiriradi kuti zimenezi nzoona angathe kuona chothetsa nzeru panopa. Nkwachionekere kuti anthu ambiri amene anauzidwa kuti “anapulumutsidwa” samakhala ndi moyo monga momwe Baibulo limanenera. Ambiri amanena kuti mwinamwake zimenezi zili chifukwa chakuti iwo ‘sanavomerezedi’ Kristu.
Chotero, kodi “kuvomereza” Yesu kumatanthauzanji kwenikweni? Kodi ndiko kusonyeza chikhulupiriro kamodzi kwatha, kapena ndiko njira ya moyo yopitiriza? Kodi chikhulupiriro chathu chiyenera kukhala cholimba kwakuti nkutisonkhezera kuchita ntchito? Kodi tingalandiredi mapindu a nsembe ya Yesu popanda kukhala ndi thayo la kumtsatira?
Anthu ambiri amafuna madalitso osati thayo la kumtsatira Yesu ndi kumumvera iye. Kwenikweni, liwu lakuti “kumvera” limawanyansa. Komabe Yesu anati: ‘Idza kuno, unditsate ine.’ (Luka 18:18-23) Ndipo Baibulo limati: “Iwo osamvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu; . . . adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.”—2 Atesalonika 1:8, 9; Mateyu 10:38; 16:24.
Baibulo limanena zinthu zambiri zimene zimadzutsa zikayikiro zazikulu ponena za zimene zaphunzitsidwa pa chipulumutso. Ngati mufuna kutsimikiza zimene Baibulo limanenadi pankhaniyi, mudzachita chidwi kwambiri ndi masamba otsatira. Tsegulani Baibulo lanu, ndipo ŵerengani malemba osonyezedwawo kuti muone zimene Yesu ndi atumwi ake anaphunzitsa pankhani yofunika kwambiri imeneyi.