Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 3/1 tsamba 23-27
  • Ogwirizana mu Utumiki wa Mulungu mu Nthaŵi Zabwino ndi Zoipa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ogwirizana mu Utumiki wa Mulungu mu Nthaŵi Zabwino ndi Zoipa
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kutumikira Kumene Alaliki Anafunika
  • Kutumikira ku South Pacific
  • Abale Athu Ngamtengo Wapatali
  • Ku Chisumbu ndi Chisumbu
  • Tifika mu Afirika Potsirizira!
  • Kulimbana ndi Kansa
  • Kubwerera ku Benin
  • Anadzipereka ndi Mtima Wonse Kumadzulo kwa Africa
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Tinadalitsidwa Chifukwa Chokonda Kwambiri Mulungu
    Galamukani!—2009
  • Kubwera kwa Matchalitchi ku Tahiti
    Galamukani!—2008
Nsanja ya Olonda—1996
w96 3/1 tsamba 23-27

Ogwirizana mu Utumiki wa Mulungu mu Nthaŵi Zabwino ndi Zoipa

Yosimbidwa ndi Michel ndi Babette Muller

“NDILI ndi uthenga wanu woipa,” anatero dokotala. “Iŵalani za ntchito yanu yaumishonale ku Afirika.” Poyang’ana mkazi wanga, Babette, iyeyo anati, “Muli ndi kansa yamaŵere.”

Tinachita kakasi kusoŵa chonena. Maganizo athu anasokonezeka. Tinali titalingalira kuti kuonana ndi dokotala kumeneku kudzangokhala kupima kwake kotsiriza. Matikiti athu a ulendo wobwerera ku Benin, West Africa, anali atagulidwa. Tinayembekezera kuti tidzakhala titabwerera mkati mwa mlungu umodzi. Mu ukwati wathu wazaka 23, tinali ndi nthaŵi zabwino ndi zoipa. Tili osokonezeka maganizo ndi amantha, tsopano tinavala chamuna kuti tilimbane ndi kansa.

Tiyeni tiyambire pachiyambi. Michel anabadwa mu September 1947, Babette mu August 1945. Tinakulira ku France ndipo tinakwatirana mu 1967. Tinkakhala ku Paris. Mmaŵa wina kuchiyambiyambi kwa 1968, Babette anachedwa kuntchito. Mkazi wina anafika pakhomo ndi kumgaŵira brosha lachipembedzo; analilandira. Ndiyeno mkaziyo anati: “Kodi ndingadzafikenso ndi mwamuna wanga kudzakambitsirana nanu ndi amuna anu?”

Babette anali kuganiza za ntchito yake. Anafuna kuti mkaziyo achoke, chotero anangoti, “Inde, chabwino.”

Michel akulongosola kuti: “Ndinalibe chidwi ndi chipembedzo, koma broshalo linanditenga mtima, ndipo ndinaliŵerenga. Patapita masiku angapo, mkaziyo, Joceline Lemoine, anafikanso ndi mwamuna wake, Claude. Mwamunayo anali waluso kwambiri pa Baibulo lake. Anayankha mafunso anga onse. Ndinachita chidwi.

“Babette anali Mkatolika wabwino koma analibe Baibulo, zimene sizinali zachilendo kwa Akatolika. Anakondwera kwambiri kuona ndi kuŵerenga Mawu a Mulungu. M’phunziro lathu tinaphunzira kuti malingaliro ambiri achipembedzo amene tinaphunzitsidwa anali onyenga. Tinayamba kuuza achibale athu ndi mabwenzi zinthu zimene tinkaphunzira. Mu January 1969 tinakhala Mboni za Yehova zobatizidwa. Posapita nthaŵi achibale ndi mabwenzi athu asanu ndi anayi anabatizidwa pambuyo pake.”

Kutumikira Kumene Alaliki Anafunika

Titangobatizidwa, tinalingalira kuti: ‘Tilibe ana. Bwanji ngati titaloŵa utumiki wanthaŵi yonse?’ Chotero mu 1970 tinasiya kugwira ntchito zathu, kulembetsa monga apainiya okhazikika, ndi kusamukira ku tauni yaing’ono ya Magny-Lormes, kufupi ndi Nevers, pakati pa France.

Linali gawo lovuta. Kupeza anthu amene anafuna kuphunzira Baibulo kunali kovuta. Sitinathe kupeza ntchito yolembedwa, chotero tinali ndi ndalama zochepa. Nthaŵi zina tinkangodya mbatata za kachewere. M’nyengo yozizira tempichala inali kutsika kufikira pa -22 digirii Celsius. Nthaŵi imene tinathera kumeneko tinaitcha kuti nyengo ya ng’ombe zisanu ndi ziŵiri zowonda.​—Genesis 41:3.

Koma Yehova anatithandiza. Tsiku lina pamene chakudya chinatsala pang’ono kutithera, wamakalata wina anabweretsa bokosi lalikulu la tchizi lochokera kwa mchemwali wake wa Babette. Tsiku linanso titalalikira tinafika panyumba ndi kupeza mabwenzi athu ena amene anayenda ulendo wa makilomita  500 kudzationa. Atamva za mmene zinthu zinalili, abale ameneŵa analongedza chakudya kaamba ka ife m’galimoto zawo ziŵiri.

Patatha chaka chimodzi ndi theka, Sosaite inatiika kukhala apainiya apadera. M’zaka zinayi zotsatira, tinatumikira ku Nevers, ndiyeno tinamka ku Troyes, ndipo potsirizira ku Montigny-lès-Metz. Mu 1976, Michel anaikidwa kuti atumikire monga woyang’anira dera kumpoto chakumadzulo kwa France.

Patapita zaka ziŵiri, mkati mwa sukulu ya oyang’anira madera, tinalandira kalata kuchokera ku Watch Tower Society yotiitana kumka kunja monga amishonale; kalatayo inati tiyenera kusankha pakati pa Chad ndi Burkina Faso (panthaŵiyo Upper Volta). Tinasankha Chad. Posakhalitsa tinalandira kalata ina, yotiuza kukagwira ntchito pansi pa uyang’aniro wa nthambi ya Tahiti. Tinali titapempha kumka ku Afirika, kontinenti yaikulu, koma posapita nthaŵi tinali pachisumbu chaching’ono!

Kutumikira ku South Pacific

Tahiti ndi chisumbu cha m’dera lotentha chokongola cha ku South Pacific. Pamene tinafika, abale pafupifupi zana anadzatichingamira pa bwalo la ndege. Anatilandira ndi magango amaluŵa, ndipo ngakhale kuti tinali otopa chifukwa chaulendo wautali kuchokera ku France, tinali achimwemwe kwambiri.

Patapita miyezi inayi titafika ku Tahiti, tinakwera boti laling’ono lodzala ngole zouma. Patapita masiku asanu tinafika kugawo lathu latsopano​—chisumbu cha Nuku Hiva ku Marquesas Islands. Anthu pafupifupi 1,500 anali kukhala pachisumbucho, koma panalibe abale. Tinali ife tokha.

Mikhalidwe yake inali yachikale panthaŵiyo. Tinkakhala m’kanyumba kopangidwa ndi konkire ndi nsungwi. Kanalibe magetsi. Tinali ndi mpope wamadzi umene nthaŵi zina unali kugwira ntchito, koma madzi ake anali athope. Nthaŵi zambiri, tinkagwiritsira ntchito madzi a mvula amene anali kudzala m’thanki. Kunalibe misewu yaphula, kunali tinjira tosalambulira chabe.

Kuti tifike kumbali zakutali za chisumbucho, tinkabwereka akavalo. Zokhalira zake zinali zamitengo​—zopweteka, makamaka kwa Babette, amene anali asanakwerepo kavalo. Tinkanyamula chikwanje chodulira nsungwi zimene zinapingasa m’njira. Kunali kusintha kwakukulu pa moyo wa ku France.

Tinkachita misonkhano ya pa Sande, ngakhale kuti tinkangokhala tili aŵiri chabe. Poyamba sitinachite misonkhano ina popeza kuti tinali ife aŵiri chabe. M’malo mwake tinkaŵerengera pamodzi nkhani za misonkhanoyo.

Patapita miyezi yoŵerengeka, tinaona kuti sikunali bwino kupitiriza mwa njira imeneyo. Michel akusimba kuti, “Ndinati kwa Babette: ‘Tiyenera kuvala moyenera. Iweyo ukhale apo, ndipo ine ndikhala pano. Ndidzayamba ndi pemphero, ndiyeno tidzachita Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi Msonkhano Wautumiki. Ndizifunsa mafunso, ndipo iwe uziyankha, ngakhale kuti ndiwe munthu wina yekha m’chipinda chino.’ Ndi bwino kuti tinachita zimenezo chifukwa kuli kosavuta kukhala waulesi mwauzimu pamene kulibe mpingo.”

Kunatenga nthaŵi kuti anthu ayambe kufika pamisonkhano yathu yachikristu. Aŵirife tinali tokhatokha kwa miyezi isanu ndi itatu yoyamba. Pambuyo pake, munthu mmodzi, aŵiri, kapena nthaŵi zina atatu anayamba kugwirizana nafe. Chaka china, aŵiri tokhafe tinayamba kuchita Chakudya Chamadzulo cha Ambuye cha chaka ndi chaka. Mphindi khumi zitatha, anthu ena anafika, chotero ndinaleka kulankhula ndi kuyambiranso.

Lerolino, mu Marquesas Islands muli ofalitsa 42 ndi mipingo itatu. Ngakhale kuti mbali yaikulu koposa ya ntchitoyo inachitidwa ndi amene anabwera pambuyo pathu, anthu ena amene kale tinawafikira tsopano ali obatizidwa.

Abale Athu Ngamtengo Wapatali

Tinaphunzira kuleza mtima ku Nuku Hiva. Tinafunikira kuyembekezera zonse kusiyapo zinthu zazikulu zofunika. Mwachitsanzo, ngati munafuna buku, munafunikira kulemba kalata yake, ndiyeno kuyembekezera kwa miyezi iŵiri kapena itatu lisanafike.

Phunziro lina limene tinapeza linali lakuti abale athu ngamtengo wapatali. Pamene tinakacheza ku Tahiti ndi kufika pamisonkhano ndi kumva abale akuimba, tinalira. Nzoona kuti abale ena ngovuta kugwirizana nawo, koma pamene muli nokha, mumazindikira mmene kukhala ndi ubale kulili kwabwino. Mu 1980 Sosaite inasankha kuti tibwerere ku Tahiti ndi kukatumikira m’ntchito yadera. Kumeneko tinalimbikitsidwa kwambiri ndi ufulu wa abale ndi kukonda kwawo ntchito yolalikira. Tinathera zaka zitatu mu ntchito yadera ku Tahiti.

Ku Chisumbu ndi Chisumbu

Kenako tinagaŵiridwa kukakhala ku nyumba ya amishonale ku Raïatéa, chisumbu china cha Pacific, ndipo tinakhala kumeneko pafupifupi zaka ziŵiri. Titachoka ku Raïatéa, tinagaŵiridwa ntchito yadera ku gulu la zisumbu za Tuamotu. Tinafika pa zisumbu 25 mwa 80 ndi boti. Zinali zovuta kwa Babette. Nthaŵi iliyonse pamene anayenda paboti, anali kudwala.

Babette akuti: “Zinali zowopsa! Nthaŵi zonse ndinkadwala tikayenda ndi boti. Titayenda panyanja kwa masiku asanu, ndinali kudwala kwa masiku asanu. Panalibe mankhwala amene anandithandiza. Komabe, ngakhale kuti ndinali kudwala, ndinaganiza kuti nyanjayo inali yokongola. Inali chinthu chokondweretsa kuona. Madolofini anali kuthamangira boti. Kaŵirikaŵiri anali kudumpha m’madzi utawomba m’manja!”

Patapita zaka zisanu tili m’ntchito yadera, tinagaŵiridwa ku Tahiti kwa zaka ziŵiri ndipo kachiŵirinso tinasangalala m’ntchito yolalikira. Mpingo wathu unakula kuŵirikiza kaŵiri kuchokera pa ofalitsa 35 kufikira pa 70 m’chaka chimodzi ndi theka. Khumi ndi aŵiri a amene tinaphunzira nawo Baibulo anabatizidwa titatsala pang’ono kuchoka. Ena a iwo ndi akulu tsopano mumpingo.

Tinathera zaka 12 ku South Pacific. Ndiyeno tinalandira kalata kuchokera ku Sosaite yonena kuti zisumbuzo sizinafunikirenso amishonale popeza kuti mipingo yake tsopano inali yolimba. Panali ofalitsa pafupifupi 450 pamene tinafika mu Tahiti ndipo tinasiya oposa 1,000 pamene tinachoka.

Tifika mu Afirika Potsirizira!

Tinabwerera ku France, ndipo patapita mwezi ndi theka, Sosaite inatipatsa gawo latsopano​—Benin, ku West Africa. Tinafuna kupita ku Afirika zaka 13 poyamba paja, chotero tinali achimwemwe kwambiri.

Tinafika mu Benin pa November 3, 1990, ndipo tinali pakati pa amishonale oyamba kufika chiletso cha zaka 14 pa ntchito yolalikira Ufumu chitachotsedwa. Zinali zokondweretsa. Sizinativute kuti tizoloŵereko chifukwa chakuti moyo wake uli wofanana ndi uja wa ku zisumbu za Pacific. Anthu ake ngaubwenzi kwambiri ndi aufulu. Mungathe kuima ndi kulankhula ndi aliyense m’khwalala.

Patangopita masabata oŵerengeka okha titafika mu Benin, Babette anapeza chotupa m’bere lake. Chotero tinamka kuchipatala china chaching’ono pafupi ndi ofesi yanthambi yongokhazikitsidwa kumene. Dokotala anampima nanena kuti anafunikira opaleshoni mwamsanga. Tsiku lotsatira tinamka ku chipatala chinanso chaching’ono kumene tinakaonana ndi dokotala wachizungu, katswiri wa nthenda za akazi wa ku France. Nayenso ananena kuti tifunikira kupita ku France mwamsanga kuti Babette akachitidwe opaleshoni. Patapita masiku aŵiri tinali paulendo wa pandege kumka ku France.

Tinali ndi chisoni kuchoka m’Benin. Pokhala ndi ufulu wachipembedzo wobwezeretsedwa m’dzikolo, abale anakondwera kulandira amishonale atsopano ndipo nafenso tinakondwera kukhala kumeneko. Chotero tinakhumudwa chifukwa chakuti tinafunikira kuchoka titangokhala masabata oŵerengeka okha m’dzikolo.

Pamene tinafika ku France, dokotala wa opaleshoni anapima Babette ndi kuvomereza kuti anafunikira opaleshoni. Madokotala anachitapo kanthu mwamsanga, anachita opaleshoni yaing’ono, ndi kutulutsa Babette m’chipatala tsiku lotsatira. Tinaganiza kuti vutolo linathera pamenepo.

Patapita masiku asanu ndi atatu, tinaonana ndi dokotala wa opaleshoniyo. Ndi panthaŵiyo pamene anatiuza uthenga wakuti Babette anali ndi kansa yamaŵere.

Pofotokoza mmene anamvera panthaŵiyo, Babette akuti: “Choyamba, sindinazunguzike kwambiri maganizo ngati Michel. Komano mmaŵa mwake, ndinauma thupi. Sindinathe kulira. Sindinathe kumwetulira. Ndinaganiza kuti ndidzafa. Kwa ine, kansa inali yofanana ndi imfa. Maganizo anga anali akuti, Tiyenera kuchita zomwe tingathe.”

Kulimbana ndi Kansa

Tinamva uthenga woipawo pa Lachisanu, ndipo anali atalinganiza kuti Babette achitidwe opaleshoni yachiŵiri pa Lachiŵiri. Tinali kukhala ndi mkulu wake wa Babette, koma nayenso anali wodwala, chotero sitinapitirize kukhala naye m’nyumba yake yaing’ono.

Tinasoŵa kopita. Ndiyeno tinakumbukira Yves ndi Brigitte Merda, banja lina limene tinakhala nalo kumbuyoko. Banja limeneli linatilandira mwaufulu kwambiri. Chotero tinaimbira telefoni Yves ndi kumuuza kuti Babette adzafunikira kuchitidwa opaleshoni ndipo tinasoŵa kokhala. Tinamuuzanso kuti Michel anafunanso ntchito.

Yves anapezera Michel ntchito panyumba pake. Abale anatichirikiza ndi kutilimbikitsa ndi machitidwe ambiri okoma mtima. Anatipatsanso thandizo la ndalama. Sosaite inalipirira ndalama za kuchipatala za Babette.

Opaleshoniyo inali yaikulu. Madokotala anayenera kuchotsa anabere ndi bere. Anayamba kupereka chithandizo cha mankhwala a makhemikolo nthaŵi yomweyo. Patapita sabata, Babette anatuluka m’chipatala, koma anali kupitako pa masabata atatu alionse kukalandirabe mankhwala.

Panthaŵiyo imene Babette anali kulandira mankhwala, abale mumpingo anali othandiza kwambiri. Mlongo wina amene nayenso anadwalapo kansa yamaŵere anali wolimbikitsa kwambiri. Anauza Babette zimene anayenera kuyembekezera ndi kumtonthoza kwambiri.

Chikhalirechobe, tinali ndi nkhaŵa yonena za mtsogolo mwathu. Pozindikira zimenezi, Michel ndi Jeanette Cellerier anatitengera ku lesitilanti kukadya kumeneko.

Tinawauza kuti tidzaleka utumiki waumishonale ndi kuti sitidzapitanso ku Afirika. Komabe, Mbale Cellerier anati: “Chiyani? Ndani amene akuti muleke? Bungwe Lolamulira? Abale m’France? Ndani watero?”

“Palibe amene watero,” ndinayankha motero, “ndine amene ndikutero.”

“Iyayi, ayi!” anatero Mbale Cellerier. “Mudzabwerera!”

Chithandizo cha mankhwala a makhemikolo chinatsatiridwa ndi cha rediyeshoni, chimene chinatha chakumapeto kwa August 1991. Madokotala anati sanaone vuto lililonse pa kubwerera kwathu ku Afirika, kusiyapo kuti Babette azifika ku France kaamba ka kupimidwa kwanthaŵi zonse.

Kubwerera ku Benin

Chotero tinalembera kumalikulu ku Brooklyn, tikumapempha chilolezo chakuti tibwerere mu utumiki waumishonale. Tinafunitsitsa kumva yankho lawo. Masiku anali kuchedwa. Potsirizira pake, Michel sanathe kuyembekezera, chotero anaimbira telefoni ku Brooklyn ndi kufunsa ngati analandira kalata yathu. Iwo anati analingalirapo za nkhaniyo​—tidzabwerera ku Benin! Tinali othokoza chotani nanga kwa Yehova!

Banja la a Merda linalinganiza phwando lokondwerera mbiriyo. Mu November 1991 tinabwerera ku Benin, ndipo abale anatilandira ndi phwando!

Babette akuoneka kuti ali bwino tsopano. Timapita ku France panthaŵi ndi nthaŵi kuti akapimidwe, ndipo madokotala samapeza chizindikiro chilichonse cha kansa. Tikukondwera kukhalanso m’gawo lathu laumishonale. Tikulingalira kuti tikufunika ku Benin, ndipo Yehova wadalitsa ntchito yathu. Kuyambira pamene tinabweranso kuno tathandiza anthu 14 kufikira atabatizidwa. Asanu a iwo tsopano ndi apainiya okhazikika, ndipo mmodzi waikidwa kukhala mtumiki wotumikira. Taonanso mpingo wathu waung’ono ukukula ndi kugaŵidwa kukhala mipingo iŵiri.

M’zaka zonsezi, tatumikira Yehova monga mwamuna ndi mkazi ndipo talandira madalitso ambiri ndipo tadziŵana ndi anthu abwino kwambiri ambiri. Komanso taphunzitsidwa ndi kulimbikitsidwa ndi Yehova kupirira bwinobwino pamavuto. Monga Yobu, nthaŵi zonse sitinamvetse chifukwa chimene zinthu zinachitikira motero, koma tinadziŵa kuti Yehova analipo nthaŵi zonse kuti atithandize. Zili monga momwe Mawu a Mulungu amanenera kuti: “Taonani, mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lake silili logontha, kuti silingamve.”​—Yesaya 59:1.

[Chithunzi patsamba 23]

Michel ndi Babette Muller atavala zovala za ku Benin

[Zithunzi patsamba 25]

Ntchito yaumishonale pakati pa Apoloneziya m’Tahiti wa m’chigawo chotentha

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena