Timafunikira Mabwenzi Enieni
JENNY ndi Sue akukambitsirana mwachisangalalo. Pali kumwetulirana, maso akusonyeza kukondwa—kalikonse mumkhalidwe wake kakusonyeza chidwi cha kufuna kumva zimene wina akunena. Ngakhale kuti ali ndi makulidwe osiyana, mwachionekere ali ofanana m’zinthu zambiri ndipo ali ndi ulemu waukulu kwa wina ndi mnzake.
Kwinanso, Eric ndi Dennis akugwirira pamodzi ntchito inayake, imodzi ya zambiri zimene achita kwa zaka. Iwo ali odekha, akumaseka bwino lomwe. Pamene makambitsirano awo afika pankhani zazikulu, apatsana malingaliro moona mtima. Amalemekezana. Monga Jenny ndi Sue, Eric ndi Dennis ali mabwenzi enieni.
Malongosoledwe ameneŵa angakusangalatseni mtima, kukuchititsani kuganiza za mabwenzi anu. Kapena, angakuchititseni kulakalaka mabwenzi oterowo. Inunso mungakhale nawo!
Chifukwa Chake Timafunikira Mabwenzi Enieni
Maubwenzi abwino ali ofunika kwambiri kuti tikhale ndi thanzi labwino ndi maganizo abwino. Komabe, pamene tisungulumwa, sikumatanthauza kuti chinachake ncholakwika kwa ife. Ofufuza ena amanena kuti kusungulumwa ndi chikhumbo, chizindikiro chachibadwa chakuti mukufuna bwenzi. Mulimonse mmene zingakhalire, monga momwe chakudya chimachepetsera njala kapena kuithetsa, maubwenzi oyenera angachepetse kusungulumwa kapena kukuthetsadi. Ndiponso, kukhala ndi mabwenzi abwino amene amatiŵerengera sikuli chinthu chosatheka.
Anthu analengedwa ndi chikhumbo cha kukhala ndi wina. (Genesis 2:18) Baibulo limanena kuti bwenzi lenileni, ‘limathandiza pooneka tsoka.’ (Miyambo 17:17) Chifukwa chake, mabwenzi enieni ayenera kukhala okhoza kupemphana thandizo pamene lili lofunika. Koma ubwenzi umaloŵetsamo zoposa chabe kukhala ndi munthu wofunako thandizo kapena mnzanu wogwira naye ntchito kapena woseŵera naye. Mabwenzi abwino amathandizana kukhala ndi makhalidwe abwino koposa. Miyambo 27:17 imati: “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.” Monga momwe chitsulo chingagwiritsidwe ntchito kunolera mpeni wofulidwa ku chitsulo chimodzimodzicho, bwenzi lingakhoze kunola nzeru ndi uzimu wa mnzake. Ngati tipsinjika chifukwa cha kugwiritsidwa mwala, kapenyedwe ka bwenzi kachifundo ndi chilimbikitso cha m’Malemba zingatilimbikitse kwambiri.
M’Baibulo, ubwenzi umagwirizanitsidwa ndi chikondi, kuzoloŵerana, kusungirana chinsinsi, ndi kuchitira zinthu pamodzi. Mabwenzi angakhale achinansi, ogwira nawo ntchito, ndi ena otero. Ena amaonanso achibale ena kukhala pakati pa mabwenzi awo apamtima. Komabe, kupeza mabwenzi enieni ndi kuwasunga nkovuta kwa anthu ambiri lerolino. Chifukwa ninji? Kodi mungakhale ndi mabwenzi enieni ndi okhalitsa?