Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 3/15 tsamba 8-9
  • Kulabadira Mawu a Yesu Otsazikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulabadira Mawu a Yesu Otsazikira
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Chitani Ichi Chikumbukiro Changa”
  • ‘Ndikupatsani Lamulo Latsopano’
  • “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Chakudya Chamadzulo cha Ambuye Ndi Mwambo Umene Umalemekeza Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuchita Chikumbutso cha Mgonero wa Ambuye?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Mgonero wa Ambuye uli ndi Tanthauzo Lalikulu kwa Inu
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 3/15 tsamba 8-9

Anachita Chifuniro cha Yehova

Kulabadira Mawu a Yesu Otsazikira

MADZULO a Nisani 14, 33 C.E., Yesu Kristu ndi atumwi ake 11 okhulupirika anaseyama pagome m’chipinda chapamwamba mu Yerusalemu. Pozindikira kuti imfa yake inali pafupi, iye anati kwa iwo: “Katsala kanthaŵi ndikhala ndi inu.” (Yohane 13:33) Kwenikweni, Yudasi Isikariote anali kale paulendo wokapangana za chiŵembu ndi anthu oipa omwe anafuna kuti Yesu aphedwe.

Palibe aliyense m’chipinda chapamwambacho amene anazindikira kufulumira kwa mkhalidwewo mofanana ndi Yesu. Iye anadziŵa bwino lomwe kuti anali pafupi kuvutika. Yesu anadziŵanso kuti atumwi ake adzamsiya usiku womwewo. (Mateyu 26:31; Zekariya 13:7) Popeza kuti umenewu unali mpata womaliza wakuti Yesu alankhule kwa atumwi ake asanamwalire, tikhoza kukhala otsimikiza kuti mawu ake otsazikira anasumika pankhani zofunika kwambiri.

“Chitani Ichi Chikumbukiro Changa”

Pamodzi ndi atumwi ake okhulupirikawo, Yesu anayambitsa phwando latsopano limene linaloŵa m’malo Paskha wachiyuda. Mtumwi Paulo analitcha “mgonero wa Ambuye.” (1 Akorinto 11:20) Atatenga mkate wopanda chotupitsa, Yesu anapereka pemphero. Ndiyeno ananyema mkatewo naugaŵira atumwi ake. “Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa,” anatero iye. Ndiyeno anatenga chikho cha vinyo, napereka pemphero loyamika nachipatsa kwa atumwi ake, akumati: ‘Mumwere ichi inu nonse, pakuti ichi ndicho mwazi wanga wa pangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri kuchotsa machimo.’​—Mateyu 26:26-28.

Kodi chochitika chimenechi chinatanthauzanji? Monga momwe Yesu anasonyezera, mkate unaimira thupi lake losachimwa. (Ahebri 7:26; 1 Petro 2:22, 24) Vinyo anaphiphiritsira mwazi wa Yesu wokhetsedwa, umene unatheketsa chikhululukiro cha machimo. Mwazi wake wansembe unachititsanso kugwira ntchito kwa pangano latsopano pakati pa Yehova Mulungu ndi anthu a 144,000, amene potsirizira pake adzalamulira pamodzi ndi Yesu kumwamba. (Ahebri 9:14; 12:22-24; Chivumbulutso 14:1) Mwa kuitana atumwi ake kudzadya chakudya chimenechi, Yesu anasonyeza kuti iwo adzakhala naye mu Ufumu wakumwamba.

Ponena za chakudya chachikumbukiro chimenechi, Yesu analamula kuti: “Chitani ichi chikhumbukiro changa.” (Luka 22:19) Inde, Chakudya Chamadzulo cha Ambuye chinakhala chochitika cha pachaka, monga momwe Paskha inalili. Pamene kuli kwakuti Paskha anali chikumbukiro cha chilanditso cha Aisrayeli ku ukapolo wa mu Aigupto, Mgonero wa Ambuye unaimira chilanditso chokulirapo kwambiri​—chiwomboledwe cha anthu ku uchimo ndi imfa. (1 Akorinto 5:7; Aefeso 1:7) Ndiponso, awo amene amadya mkate ndi vinyo wophiphiritsira amakumbutsidwa za mwaŵi wawo wamtsogolo wakukhala mafumu ndi ansembe mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu.​—Chivumbulutso 20:6.

Imfa ya Yesu Kristu inalidi chochitika chofunika koposa m’mbiri ya anthu. Awo amene amayamikira zimene Yesu anachita amamvera lamulo lake lonena za Mgonero wa Ambuye kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” Mboni za Yehova zimachita chikumbutso cha imfa ya Yesu chaka chilichonse patsiku lolingana ndi Nisani 14. Mu 1996 deti limeneli lidzakhala pa April 2, dzuŵa litaloŵa. Mukuitanidwa mwachikondi kufika pa Nyumba ya Ufumu ya kwanuko.

‘Ndikupatsani Lamulo Latsopano’

Kuwonjezera pakuyambitsa Mgonero wa Ambuye, Yesu anali ndi uphungu wotsazikira kwa atumwi ake. Mosasamala kanthu za kuphunzitsidwa kwawo kwabwino, amunaŵa anali ndi zambiri zoti aphunzirebe. Sanazindikire mokwanira chifuno cha Mulungu kwa Yesu, kwa iwo, kapena chamtsogolo. Koma Yesu sanayese kulongosola nkhani zonsezi panthaŵiyo. (Yohane 14:26; 16:12, 13) M’malo mwake, analankhula za kanthu kena kofunika kwambiri. “Ndikupatsani inu lamulo latsopano,” anatero iye, “kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.” Ndiyeno Yesu anaonjeza kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”​—Yohane 13:34, 35.

Kodi limeneli linali “lamulo latsopano” m’njira yotani? Chabwino, Chilamulo cha Mose chinalamula kuti: “Uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha.” (Levitiko 19:18) Komabe, Yesu anauza otsatira ake kusonyeza chikondi chodzimana chimene chimafika pamlingo wakupereka moyo wa munthu mwini kaamba ka Akristu anzake. Ndithudi, ‘lamulo la chikondi’ lingagwirenso ntchito m’mikhalidwe yosakhala yovuta kwambiri. M’mikhalidwe yonse wotsatira wa Yesu Kristu ayenera kuchitapo kanthu kuti asonyeze chikondi mwa kuthandiza ena mwauzimu ndi mwakuthupi.​—Agalatiya 6:10.

Pa usiku womalizira umenewu wa moyo wa Yesu, chikondi chinasonkhezera Yesu kupempherera ophunzira ake kwa Yehova Mulungu. Pakati pa zinthu zina anapemphera kuti: “Iwo ali m’dziko lapansi, ndipo ine ndidza kwa inu, Atate Woyera, sungani awa m’dzina lanu amene mwandipatsa ine, kuti akhale mmodzi, monga ife.” (Yohane 17:11) Nkoonekeratu kuti m’pempho lake limeneli kwa Atate wake, Yesu anapempherera umodzi wachikondi wa otsatira ake. (Yohane 17:20-23) Iwo anafunikira ‘kukondana wina ndi mnzake monga momwe Yesu anawakondera iwo.’​—Yohane 15:12.

Atumwi okhulupirikawo analabadira mawu a Yesu otsazikira. Ifenso tiyenera kumvera malamulo ake. Mu “masiku otsiriza” ano oŵaŵitsa, chikondi ndi chigwirizano pakati pa alambiri oona nzofunika kwambiri kuposa ndi kalelonse. (2 Timoteo 3:1) Ndithudi, Akristu oona amamvera malamulo a Yesu ndi kusonyeza chikondi chaubale. Zimenezi zimaphatikizapo kumvera lamulo lake la kuchita chikumbutso cha Mgonero wa Ambuye.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena